Kodi Ndani Angadziwe Zam’tsogolo?
Kodi Ndani Angadziwe Zam’tsogolo?
“Ine ndine Mulungu . . . , ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe.”—Yesaya 46:9, 10.
M’NTHAWI zovuta zino, akatswiri a zandale, zachuma, ndi chikhalidwe cha anthu amafufuza mbiri yakale komanso zimene zikuchitika masiku ano n’cholinga choti adziwe zam’tsogolo. Chifukwa chofunitsitsa kudziwa zimene zidzawachitikire m’tsogolo, anthu ena amapita kwa okhulupirira nyenyezi kapena amatsenga. Anthu otere nthawi zambiri amakhumudwa ndi zimene amapeza. Kodi n’zosatheka ngakhale pang’ono kudziwa zimene zidzachitikire dzikoli, mabanja athu, ndiponso aliyense payekha? Kodi pali amene angadziwe zam’tsogolo?
Posonyeza kuti amatha kuneneratu zam’tsogolo, Yehova Mulungu Wamphamvuyonse analankhula mawu amene alembedwa pamwambawa kwa mneneri Yesaya. Iye analosera zoti Aisiraeli adzamasulidwa ku ukapolo wa ku Babulo n’kubwerera kukamanga mzinda wa Yerusalemu ndiponso kachisi. Kodi ndi zinthu ziti zimene ulosiwu unanena mwachindunji? Padakali zaka 200, Yesaya ananeneratu molondola kuti Koresi ndi amene adzagonjetse Babulo. Iye anafotokozanso zimene Koresi adzachite. Anati adzapatutsa madzi a mumtsinje wa Firate umene unkateteza mzindawo. Ananeneratunso kuti Koresi adzapeza zitseko za zipata za mumzindawo zitangosiyidwa zosatseka moti adzagonjetsa mzindawo mosavuta.—Yesaya 44:24–45:7.
Poyerekezera ndi Mulungu, munthu alibiretu mphamvu yoona zam’tsogolo. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Usanyadire zamawa, popeza sudziwa tsiku lina lidzabala chiyani?” (Miyambo 27:1) Mawu amenewa adakali oona. Palibe munthu amene angadziwe ngakhale za tsogolo lake. Koma n’chifukwa chiyani Mulungu ali wosiyana ndi anthu? N’chifukwa choti iye amadziwa bwino za cholengedwa chake chilichonse kuphatikizapo zochita za munthu aliyense ndiponso zimene zili mu mtima mwake. Mulungu atafuna, angathe kudziwa bwino lomwe zimene munthu kapena mitundu ya anthu ikufuna kudzachita. Komanso, ali ndi mphamvu zotha kuletsa zinthu zina kuti zisachitike. Akalosera kudzera mwa aneneri ake kuti chinachake chichitika, iye ‘amalimbitsa mawu a mtumiki wake, kuchita uphungu wa amithenga ake,’ kutanthauza kuti amachititsa kuti mawu onse amene mtumiki wake wanena akwaniritsidwe. (Yesaya 44:26) Yehova Mulungu yekha ndi amene angathe kuchitadi zimenezi.
Yesaya anakhalako zaka 700, Yesu yemwe ali Mesiya, asanabwere koma analosera za kubwera kwa Mesiyayo. Komabe, kuyambira zaka za m’ma 1700 kupita m’tsogolo, anthu otsutsa Baibulo ankanena kuti buku la Yesaya si lolondola. Iwo ankanena kuti nkhani za mu ulosi wa Yesaya zinalembedwa pambuyo poti zinthuzo zachitika. Koma kodi zimenezi n’zoona? Mu 1947 mpukutu wa buku la Yesaya unapezeka m’phanga la pafupi ndi Nyanja Yakufa, limodzi ndi mipukutu ina yakale. Akatswiri
ena anatsimikiza kuti mpukutu umenewo unalembedwa zaka zoposa 100, Khristu kapena kuti Mesiya woloseredwayo asanabadwe. N’zoonadi kuti Baibulo limaneneratu zam’tsogolo.Yesaya ndiponso olemba Baibulo ena sakanatha kuneneratu zam’tsogolo mwa nzeru zawo. Koma iwo “analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” (2 Petulo 1:21) M’nkhani zotsatirazi tiona zochitika zosiyanasiyana zokhudza moyo wa Yesu zimene Mulungu analosera kudzera mwa Yesaya. Kenako tikambirana zinthu zimene Yesu ndi ophunzira ake analosera kuti zidzachitika m’nthawi yathu ino ndiponso m’tsogolo.