Kodi Mukudziwa?
Kodi Mukudziwa?
N’chifukwa chiyani Yudasi anapatsidwa ndalama 30 zasiliva kuti apereke Yesu?
Yudasi Isikariyoti atapita kwa ansembe aakulu kukafunsa ndalama zimene angamupatse atati apereke Yesu, iwo anamuuza kuti adzamupatsa “ndalama 30 zasiliva.” (Mateyo 26:14, 15) Mtengo umenewu anautchula pofuna kusonyeza kuti iwo ankanyansidwa kwambiri ndi Yesu ndipo ankamuona kuti ndi wosanunkha kanthu.
N’kutheka kuti ndalama zasiliva zimenezi zinali masekeli amene Ayuda ankagwiritsa ntchito panthawiyo. Kodi mphamvu ya ndalama zimenezi inali yotani? Chilamulo cha Mose chinati masekeli 30 ndi mtengo wogulira kapolo. Ndiponso munthu akanatha kugula munda ndi ndalama zimenezi.—Eksodo 21:32; Mateyo 27:6, 7.
Mneneri Zekariya atauza Aisiraeli osakhulupirika kuti amupatse malipiro ake pantchito imene anagwira monga m’busa wa anthu a Mulungu iwo anamupatsa “ndalama zasiliva makumi atatu.” Iwo anachita dala zimenezi pofuna kunyoza mneneri wa Mulunguyo kuti aoneke ngati wachabechabe, mofanana ndi kapolo. N’chifukwa chake Yehova analamula Zekariya kuti: “Kaziponye kwa woumba mbiya, mtengo wake wokometsetsa anandiyesawo.” (Zekariya 11:12, 13) Zekariya anamvera Mulungu ndipo zimene anachitazo zikutikumbutsa zimene Yudasi anadzachita ndi ndalama zimene analandira atapereka Yesu, amene Mulungu anamutumiza kuti adzakhale m’busa wa mtundu wa Isiraeli.—Mateyo 27:5.
Kodi ‘Kalata ya Chilekanitso’ Yotchulidwa M’Baibulo N’chiyani?
Chilamulo cha Mose chinanena kuti: “Munthu akatenga mkazi akhale wake, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pake, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, am’lembere kalata wa chilekanitso, ndi kum’pereka uyu m’dzanja lake, ndi kum’tulutsa m’nyumba mwake.” (Deuteronomo 24:1) Kodi cholinga cha kalatayi chinali chiyani? Malemba sanena kuti m’kalatayi munkalembedwa zotani, koma iyenera kuti inkateteza ufulu komanso katundu wa mkazi wosiyidwayo.
Mu 1951 ndi 1952, ofufuza anapeza zinthu zambirimbiri zamakedzana m’mapanga a kumpoto kwa mtsinje wopanda madzi, wotchedwa Wadi Murabbaat, womwe uli m’chipululu cha Yudeya. Pamipukutu imene anapeza kumeneku panalinso kalata ya chilekanitso yomwe inalembedwa cha m’ma 71 kapena 72 C.E. Kalatayi inalembedwa m’Chialamu. Kalatayo imafotokoza zimene zinachitika pa tsiku loyamba la mwezi wa Malaheshivan, patatha zaka 6 kuchokera pamene Ayuda anagalukira Aroma. Yosefe, mwana wa Nakisani, yemwe ankakhala ku Masada, anasudzula Miriamu, mwana wa Yonatani wa ku Hanabulata. Motero Miriamuyo anali ndi ufulu wokwatiwa ndi mwamuna aliyense wachiyuda amene akanakonda. Yosefe uja anabweza ndalama zonse za malowolo ndipo anam’patsanso Miriamuyo katundu wowirikiza kanayi polipira katundu wake yense amene anawonongeka. Kalata ya chilekanitsoyo inasayinidwa ndi Yosefeyo komanso mboni zina zitatu, Eliezere, mwana wa Malika, Yosefe, mwana wa Malika, komanso Eleazara, mwana wa Hanana.
[Chithunzi patsamba 25]
Mapanga a ku WadI Murabbaat
[Chithunzi patsamba 25]
Kalata ya Chilekanitso Yolembedwa mu 71 Kapena 72 C.E.
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Caves: Todd Bolen/Bible Places.com; certificate: Clara Amit, Courtesy of the Israel Antiquities Authority