Kodi Atate Wathu wa Kumwamba Ndi Wotani Kwenikweni?
Kodi Atate Wathu wa Kumwamba Ndi Wotani Kwenikweni?
ANTHU ambiri amatha kunena pamtima Pemphero la Ambuye limene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake. (Mateyo 6:9-13) Nthawi zonse akamanena pempheroli, Mulungu amam’tchula kuti “Atate Wathu.” Komano kodi ndi anthu angati amene anganene kuti amam’dziwa bwino Mulungu?
Kodi inuyo mungati mumam’dziwa bwino Mulungu? Kodi muli paubwenzi wolimba ndi Mulungu moti mumalankhula naye, n’kumamuuza zinthu zimene zimakusangalatsani ndi zimene zimakusautsani? Kodi kudziwa Mulungu kumatanthauza chiyani kwenikweni?
“Dzina Lake Ndiye Yehova”
Mwana wamng’ono amangodziwa kuti awa ndi ababa basi. Komano akamakula, amadziwa dzina la bambo akewo komanso makhalidwe awo ndipo nthawi zambiri amawanyadira. Kodi n’chimodzimodzinso ndi Mlengi wathu wakumwamba, amene anatipatsa moyo? Kodi mumadziwa dzina lake lenileni ndiponso tanthauzo lake?
Ngakhale kuti anthu ambiri akamanena Pemphero la Ambuye, amatchula mawu akuti “dzina lanu liyeretsedwe,” iwo sangathe kuyankha ngati mutawafunsa kuti, “Kodi dzina limene mukuti liyeretsedwelo ndi liti?” Tikamaona nyenyezi kumwamba, mapiri akuluakulu, zamoyo zokongola za pansi pa nyanja, sitikayika ngakhale pang’ono kuti kuli Mulungu. Komatu zinthu zimenezi sizitiuza dzina lake. Kuti tidziwe dzina limenelo, tiyenera kufufuza m’Baibulo. Baibulo limanena mwachidule kuti: “Dzina lake ndiye Yehova.”—Eksodo 15:3.
Mulungu amafuna kuti tidziwe dzina lake, lakuti Yehova. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti dzinali limasonyeza umunthu wake. Tanthauzo lenileni la dzina limeneli ndi lakuti “Amachititsa Kukhala,” kutanthauza kuti iye angathe kukhala china chilichonse kuti akwaniritse cholinga chake. Kuti mumvetse zimenezi taganizira
izi: Pofuna kusamalira banja lake, bambo angathe kukhala mlangizi, mkhalapakati, woweruza, mtetezi, mphunzitsi, ndiponso munthu wopezera banjalo zonse zofunikira. N’chimodzimodzinso ndi Mulungu. Dzina lake lakuti Yehova, limatitsimikizira kuti zivute zitani, iye angathe kuchita chilichonse pokwaniritsa cholinga chake kuti adalitse anthu onse amene amam’tumikira.Tiyeni tione zinthu zosiyanasiyana zimene Mulungu wathu wachikondiyu amatha kukhala, mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lakeli. Kudziwa zimenezi kukuthandizani kumvetsetsa kuti Yehova ndi Mulungu wotani, komanso kudziwa zimene muyenera kuchita kuti mukhale naye paubwenzi.
“Mulungu Wachikondi ndi Wamtendere”
Mtumwi Paulo anati Mlengi wathuyu ndi “Mulungu wachikondi ndi wamtendere.” (2 Akorinto 13:11) N’chifukwa chiyani anatero? Paulo asananene zimenezi, Yesu Khristu anali atanena kale kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Chifukwa chokonda kwambiri anthu, Mulungu anapereka Mwana wake wapamtima kuti akhale nsembe yowombolera anthu. Zimenezi zinachititsa kuti anthu onse okhulupirira iye adzapeze moyo wosatha, wopanda mavuto ndi masautso amene anabwera chifukwa cha uchimo. N’chifukwa chake Paulo anati: “Malipiro a uchimo ndiwo imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndiyo moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Kodi zimenezi siziyenera kutichititsa kuti tiyambe kukonda Mulungu?
Mulungu amasonyeza chikondi chake kwa anthu onse komanso kwa munthu aliyense wokhulupirika. Mose ananena mawu otsatirawa kwa Aisiraeli akale, amene nthawi zambiri sankamvera Mulungu. Iye anati: “Kodi mubwezera Yehova chotero, anthu inu opusa ndi opanda nzeru? Kodi sindiye Atate wanu, Mbuye wanu; anakulengani, nakukhazikitsani?” (Deuteronomo 32:6) Kodi mawu amenewo mwawamvetsa bwinobwino? Popeza Yehova ndi Tate wachikondi, iye ankaganizira anthu ake, ngakhale kuti ankaona zolakwa zawo. Ndipotu ankawapatsa zinthu zimene ankafunikira kuti akhale ndi moyo, kuti akhale osangalala, ndiponso kuti akhale paubwenzi wabwino ndi iyeyo.
Tonsefe timakumana ndi zinthu zosiyanasiyana pamoyo wathu ndipo nthawi zina zimenezi zimatisautsa mtima mwinanso kutifoola kwambiri. Zikatero timafuna wina wotithandiza kuti tithe kupirira vutolo. Kodi ndani angatithandize? Kudzera m’Mawu ake, Baibulo, Yehova amatha kukhala Mlangizi wachikondi ndiponso Wotisamalira. Baibulo ndi buku lopatulika limene limatiuza chifukwa chake timakumana ndi mavuto ochuluka chonchi ndiponso zimene tingachite kuti tiwapirire. Monga mmene tate wachikondi amathandizira mwana wake akagwa n’kudzipweteka, tingati mwachikondi chake chachikulu, Yehova amawerama n’kutithandiza tikagwa m’mavuto. Ndithu, dzanja la Yehova si lalifupi kwa anthu amene amamukhulupirira.—Yesaya 59:1.
Timaonanso chikondi cha Mulungu poganizira kuti iye ndi “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Kodi chikondi chimenechi chimaonekera bwanji? Mtumwi Paulo anati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Mukamapemphera kwa Mulungu mochokera pansi pamtima ndi kutsatira malangizo amene iye amapereka m’Mawu ake, nanunso mungapeze “mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira.”
“Mulungu Wanzeru”
Baibulo limafotokoza kuti Yehova Mulungu ndi “wakudziwitsa mwangwiro.” Chifukwa choti Yobu 36:4; 1 Samueli 2:3) Kudzera mwa mtumiki wake Mose, iye ananena kuti: “Munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m’kamwa mwa Yehova.” (Deuteronomo 8:3; Mateyo 4:4) Zimenezi zikutanthauza kuti kukhala ndi zinthu zambiri sikungatipangitse kukhala osangalala pamoyo wathu.
ndi “Mulungu wanzeru,” iye amatidziwa bwino anthufe ndiponso amadziwa zosowa za anthu kuposa wina aliyense. (Mlengi wathu amatipatsa malangizo ofunika kwambiri kudzera m’Mawu ake, Baibulo. Tikamawerenga Baibulo n’kumagwiritsira ntchito malangizo ake m’moyo wathu, timathandizidwa ndi “zonse zakutuluka m’kamwa mwa Yehova.” Mwachitsanzo, mayi wina wachikhristu, dzina lake Zuzanna, anati: “Chimene chinalimbitsa banja lathu ndicho kuwerenga Baibulo limodzi, kupita limodzi ku misonkhano yachikhristu, ndiponso kuuza ena zimene timaphunzira. Chifukwa chotsatira malangizo a m’Baibulo, tonse tili ndi zolinga zofanana ndipo timagwirizana kwambiri.”
Kodi mungapindule bwanji ndi malangizo ochokera kwa Mulungu amenewa? Mulungu angathe kukudalitsani mukamaphunzira Baibulo nthawi zonse ndi kutsatira malangizo ake.—Aheberi 12:9
“Mulungu wa Chipulumutso”
Masiku ano dzikoli lili ndi mavuto adzaoneni. Palibe munthu amene amadziwa za mawa. Ngati kwanuko kuli nkhondo, mumalakalaka kwambiri mtendere. M’madera ambiri a padziko pano, anthu amangokhala mwamantha chifukwa cha zachiwawa zosiyanasiyana, mavuto a zachuma, ndiponso uchigawenga. Kodi ndani angatichotsere mavuto onsewa? Panopo, kuposa kale lonse, anthufe tikufunika kwambiri kutetezedwa ndiponso kupulumutsidwa.
Baibulo limati: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.” (Miyambo 18:10) Kudziwa ndi kudalira dzina la Mulungu kumatithandiza kuganizira zimene watichitira ndiponso zimene adzachite populumutsa anthu amene amamukhulupirira. Yehova Mulungu watipatsa umboni wonse wotsimikizira kuti angathe kupulumutsa anthu ake. Mwachitsanzo, iye anapulumutsa Aisiraeli powononga asilikali ndiponso magaleta ankhondo a Farao. Pamenepa Yehova anaperekanso umboni wotsimikizira kuti ndi Mulungu wokhulupirika, yemwe saiwala anthu ovutika ndipo amafunitsitsa kuwathandiza.—Eksodo 15:1-4.
Komanso kuti tikhale ndi moyo wosatha m’pofunika kukhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova Mulungu ndi Mpulumutsi. Mfumu Davide ya mtundu wa Isiraeli, yomwe pamoyo wake inakumana ndi mikwingwirima yadzaoneni, inasonyeza chikhulupiriro chotere ponena za Yehova, kuti: “Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa.” (Salmo 25:5) Nayenso mtumwi Petulo ananena mosakayika kuti: “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye m’mayesero.”—2 Petulo 2:9.
Ponena za munthu amene amadalira thandizo lake, Mulungu analonjeza kuti: ‘Ndidzam’pulumutsa popeza adziwa dzina langa.’ (Salmo 91:14) Masiku ano, atumiki a Mulungu aona lonjezo limeneli likukwaniritsidwa. Henryk wa ku Poland wakhala akutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka 70, ngakhale kuti pamoyo wake wakumana ndi masautso ambiri komanso anazunzidwa kwadzaoneni. Ali ndi zaka 16, chipani cha Nazi chinaponya bambo ake m’ndende yozunzirako anthu ya Auschwitz. Koma iyeyo ndi mkulu wake anaponyedwa m’ndende ya ana. Kenako ankangomusamutsira m’ndende zozunzirako anthu zosiyanasiyana. Pokumbukira masiku amenewo, Henryk anati: “Pamayesero anga onse, Yehova sanandisiye ngakhale pang’ono. Nthawi zonse ankandithandiza kuti ndikhalebe wokhulupirika, ngakhale kuti nthawi zingapo moyo wanga unali pangozi.” Inde, Yehova amapereka mphamvu ndi chikhulupiriro kuti atumiki ake athe kupirira.
Posachedwapa Mulungu adzaperekanso umboni wotsimikizira kuti ndi Mpulumutsi wa anthu onse amene amamukhulupirira ndi kumudalira. Iye anati: “Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma ine ndekha.” (Yesaya 43:11) Pa “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse,” iye adzaseseratu anthu onse oipa padziko pano n’kupulumutsa olungama. (Chivumbulutso 16:14, 16; Miyambo 2:21, 22) Yehova akutitsimikizira kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:11.
Khalani “Ana a Mulungu”
M’masiku a mneneri Malaki, Aisiraeli ankanena kuti Yehova ndi Atate wawo. Koma m’malo moti adzipereke kwa iye n’kumamulemekeza, iwo ankamupatsa nsembe za mkate wodetsedwa ndiponso ziweto zakhungu ndi zopunduka. N’chifukwa chake Yehova anawafunsa kuti: “Ngati ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga?”—Malaki 1:6.
Musachite zangati zimene anachita Aisiraeli osakhulupirikawa. Koma limbikirani kuphunzira za Yehova Mulungu ndi kumuyandikira. Mtumwi Yakobe anati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobe 4:8.
Yehova akakhala Atate wathu timakhalanso ndi udindo wosiyanasiyana. Mukamayesetsa kulemekeza Mulungu mokhulupirika potsatira mfundo zake za makhalidwe abwino pa zochita zanu zonse, iye sangaiwale ngakhale pang’ono zimene mukuchitazo. M’malo mwake, amakuthandizani kuyenda m’njira yowongoka yopita ku dziko lapansi latsopano limene iye walonjeza. M’dziko limeneli “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Chivumbulutso 21:4) Panthawiyo, anthu onse okhulupirika ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda ndi kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.’—Aroma 8:21.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Mulungu amafuna kuti tidziwe dzina lake, lakuti Yehova ndipo dzinali limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala”
[Mawu Otsindika patsamba 6]
“Pamayesero anga onse, Yehova sanandisiye ngakhale pang’ono.”—ANATERO HENRYK
[Mawu Otsindika patsamba 7]
“Chimene chinalimbitsa banja lathu ndicho kuwerenga Baibulo limodzi, kupita limodzi ku misonkhano yachikhristu, ndiponso kuuza ena zimene timaphunzira.”—ANATERO ZUZANNA