Mungamasangalale Ngakhale Mukukumana ndi Zokhumudwitsa
Mungamasangalale Ngakhale Mukukumana ndi Zokhumudwitsa
PALIBE munthu amene sanakhumudwitsidwepo. Ngakhale Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu, anakhumudwitsidwapo. Mwachitsanzo, iye anamasula Aisiraeli mu ukapolo ku Iguputo ndipo anawadalitsa kwambiri. Koma Baibulo limati: “Pakuti anabwerera m’mbuyo, nayesa Mulungu, nachepsa Woyerayo wa Isiraeli.” (Salmo 78:41) Ngakhale zili choncho, Yehova wapitirizabe kukhala “Mulungu wa chisangalalo.”—1 Timoteyo 1:11.
N’zoona kuti pali zinthu zambiri zimene zingatikhumudwitse. Koma kodi tingatani kuti tikhalebe osangalala zinthu zimenezi zikatichitikira? Nanga tingaphunzirepo chiyani tikaona mmene Yehova Mulungu anachitira zinthu atakhumudwitsidwa?
Zinthu Zimene Zingatikhumudwitse
Mawu a Mulungu amati tonsefe timakumana ndi zotigwera mwadzidzidzi. (Mlaliki 9:11) Nthawi zina anthu ena angatichitire zachiwawa, kapena tingachite ngozi, mwinanso tingadwale mwadzidzidzi ndipo zimenezi zingatikhumudwitse kwambiri. Komanso Baibulo limati: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.” (Miyambo 13:12) Timasangalala kwambiri tikamayembekezera zinthu zabwino. Koma tingakhumudwe ngati zimene tikuyembekezerazo sizikuchitika. Mwachitsanzo, Duncan * ankafunitsitsa kupitiriza ntchito yake ya umishonale. Koma atagwira ntchitoyi kwa zaka zambiri, iye ndi mkazi wake anafunika kusiya ntchitoyi n’kubwerera kwawo. Iye anati: “Inali nthawi yoyamba pamoyo wanga wonse kuti ndisokonezeke maganizo kwambiri chonchi ndipo ndinalibiretu cholinga chilichonse pamoyo. Palibe chilichonse chomwe chinkandisangalatsa.” Munthu angavutikenso kwa nthawi yaitali chifukwa cha kukhumudwa ngati momwe zinalili ndi mayi wina dzina lake Claire. Iye anati: “Ndinapita padera ndili ndi pakati pa miyezi 7. Ngakhale kuti zimenezi zinachitika zaka zambiri zapitazo, ndimakumbukirabe, makamaka ndikaona mnyamata akukamba nkhani ku mpingo. Zikatero ndimaganiza kuti ‘Bwenzi pano mwana wanga ali ngati mnyamatayu.’”
Zingakhalenso zopweteka ndiponso zokhumudwitsa kwambiri makamaka ngati chibwenzi chanu chatha, ukwati wanu watha, kapena ngati mwana wanu wakugalukirani. Zingateronso ngati mwamuna kapena mkazi wanu ndi wosakhulupirika, ndiponso ngati mnzanu ndi wosayamikira. Pali zinthu zambiri zimene zingatikhumudwitse popeza kuti tikukhala m’nthawi yovuta ndiponso anthu amene tikukhala nawo ndi opanda ungwiro.
Mungakhumudwenso chifukwa cha zinthu zina zimene mwalephera kuchita. Mwachitsanzo, mungakhumudwe ngati mwalephera mayeso, mwalephera kupeza ntchito, kapenanso ngati wina wakana kuti mukhale naye pachibwenzi. Komanso mungakhumudwe ngati wachibale wanu wasiya kukonda kwambiri Yehova. Mayi wina dzina lake Mary anati: “Mwana wanga wamkazi ankaoneka kuti ndi Mkhristu wolimbikira kwambiri. Ndipo ndinkaona kuti akutsatira chitsanzo changa chabwino. Koma atasiya kutimvera ndiponso kutumikira Yehova Mulungu, ndinaona kuti ndine wolephera. Ngakhale ndichite bwino pa zinthu zina, ndinkangoonabe kuti ndine wolephera basi. Ndipo zimenezi zinkandikhumudwitsa kwambiri.”
Kodi tingatani kuti tipirire zinthu zokhumudwitsa ngati zimenezi? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione mmene Yehova anachitira zinthu atakhumudwitsidwa.
Ganizirani za Njira Yothetsera Vutolo
Mwachikondi, Yehova Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava zinthu zonse zofunikira pa moyo wawo koma iwo sanayamikire zimenezi ndipo anamugalukira. (Genesis, chaputala 2 ndi 3) Ndiyeno mwana wawo Kaini, anayamba kuganiza zinthu zoipa mumtima mwake. Iye ananyalanyaza chenjezo la Yehova mpaka anapha m’bale wake. (Genesis 4:1-8) Taganizirani mmene zimenezi zinakhumudwitsira Yehova.
N’chifukwa chiyani Mulungu anakhalabe wosangalala ngakhale kuti anakhumudwa kwambiri ndi zimenezi? N’chifukwa choti iye anali ndi cholinga choti dziko lapansi lidzaze ndi anthu angwiro, ndipo iye anali wofunitsitsa kuti akwaniritse zimenezi. (Yohane 5:17) Kuti zimenezi zitheke, iye anapereka Mwana wake nsembe ya dipo ndiponso anakhazikitsa Ufumu wake. (Mateyo 6:9, 10; Aroma 5:18, 19) Choncho Yehova Mulungu sanafooke ndi vutolo koma anaganizira kwambiri za njira yolithetsera.
Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tiziganizira kwambiri mmene tingathetsere mavuto athu, m’malo modziimba mlandu. Baibulo limati: “Chomalizira abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse za chikondi, zilizonse zoneneredwa zabwino, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.”—Afilipi 4:8.
Onani Moyenera Zinthu Zokhumudwitsa
Pali zinthu zambiri zimene zingasinthiretu moyo wathu. Mwachitsanzo, ntchito ikhoza kutithera mwadzidzidzi, mwamuna kapena mkazi wathu akhoza kumwalira, kapenanso maudindo ena omwe tili nawo mumpingo akhoza kutha. Tikhozanso kudwala, kupezeka kuti tilibe pokhala ndiponso anzathu. Kodi tingapirire bwanji mavuto ngati amenewa?
Anthu ena aona kuti kuika zinthu zofunika kwambiri pamalo oyamba n’kothandiza. Duncan yemwe tam’tchula koyamba uja anati: “Ine ndi mkazi wanga tinakhumudwa kwambiri titazindikira kuti sitingathenso kupitiriza umishonale. Komano tinaika patsogolo zinthu ziwiri zofunika kwambiri. Choyamba, tinakonza zoti tizisamalira mayi anga, ndipo chachiwiri, tinakonza zopitiriza kugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino nthawi zonse. Pakafunika kusankha zochita, choyamba timaganizira kaye mmene zosankhazo zingakhudzire zinthu zathu zofunikazo. Zimenezi zimatithandiza kwambiri.”
Ambirife timakonda kukokomeza zinthu tikakhumudwa. Mwachitsanzo, tingakhumudwe ngati talephera kulera bwino mwana wathu, talephera kupeza ntchito, kapena anthu sakumvetsera uthenga wabwino umene tikulalikira m’dziko lina. Tingaganize kuti, ‘Ine ndiye ndi wolephera basi.’ Komabe zimene Adamu ndi Hava anachita sizinasonyeze kuti Mulungu ndi wolephera. Ifenso ngati Deuteronomo 32:4, 5.
zinthu zina sizinatiyendere bwino, sitinganene kuti ndife olephera.—Kawirikawiri n’zosavuta kuti tikwiye kwambiri makamaka anthu ena akatikhumudwitsa. Koma Yehova satero. Yehova anakhumudwa kwambiri Mfumu Davide itachita chigololo ndiponso kupha mwamuna wa mkaziyo. Komabe Yehova anaona kuti Davide analapa moona mtima ndipo anapitiriza kum’gwiritsira ntchito monga mtumiki wake. Mofanana ndi zimenezi, Mfumu Yehosafati yemwe anali wokhulupirika analakwa kwambiri pamene anachita pangano ndi adani a Mulungu. Mneneri wa Yehova anati: “Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova. Koma zapezeka zokoma mwa inu.” (2 Mbiri 19:2, 3) Yehova anazindikira kuti kulakwa kamodzi kwa Yehosafati sikunatanthauze kuti iyeyo wasiya kum’konda. Mofanana ndi zimenezi tingakhalebe ndi anzathu ambiri ngati tipewa kupsa mtima kwambiri anzathuwo akatilakwira. Anzathu amene angatikhumudwitse, amakhalabe ndi makhalidwe ena abwino.—Akolose 3:13.
Ndi bwino kuona zinthu zokhumudwitsa ngati zotithandiza kuti tiyesetse kukwaniritsa zimene tikufuna. Nthawi zina tingakhumudwe ndi zochita zathu zomwe, makamaka tikachimwa. Komabe tingayambenso kusangalala ngati titayesetsa kuchita zonse zomwe tingathe kuti tithane ndi vutolo. Mfumu Davide atakhumudwa kwambiri ndi zomwe anachita, analemba kuti: “Mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku Salmo 32:3-5) Ngati tazindikira kuti talakwa, tiyenera kupempha Mulungu kuti atikhululukire ndiponso tiyenera kusintha njira zathu n’kuyamba kutsatira kwambiri malangizo a Mulungu.—1 Yohane 2:1, 2.
lonse. . . . Ndinavomera choipa changa kwa inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa [Yehova] . . . , ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.” (Khalani Okonzekeratu Kuthana ndi Zokhumudwitsa
Mosakayikira aliyense waife adzakhumudwapo nthawi ina m’tsogolomu. Kodi tingachite chiyani kuti tikhale okonzekeratu? Zimene Mkhristu wina wachikulire dzina lake Bruno ananena n’zothandiza kwambiri. Iye anakumana ndi zinthu zina zokhumudwitsa kwambiri zimene zinasintha moyo wake. Iye anati: “Zimene zinandithandiza kwambiri kuthana ndi mavuto anga n’zoti ndinkapitirizabe kuchita zinthu zimene ndakhala ndikuchita nthawi zonse kuti ubwenzi wanga ndi Mulungu ukhale wolimba. Ndinazindikira chifukwa chake Mulungu walola kuti zinthu zoipa zipitirizebe kuchitika m’dzikoli. Ndinatha zaka zambiri ndikuyesetsa kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ndipo ndinasangalala kwambiri kuti ndinakwanitsa kuchita zimenezi. Kudziwa kokha kuti Yehova ali ndi ine kunandithandiza kwambiri kupilira mavuto onse omwe ndinkakumana nawo.”
Tikamaganizira zinthu za m’tsogolo, timatsimikiza mfundo yakuti: Ngakhale kuti nthawi zina tingakhumudwe ndi zochita zathu zomwe kapena anzathu angatikhumudwitse, koma Mulungu sadzatikhumudwitsa ngakhale pang’ono. Ndipotu Mulungu ananena kuti dzina lake lakuti Yehova limatanthauza kuti, “Ine ndine yemwe ndili ine.” (Eksodo 3:14) Zimenezi zimatipangitsa kumudalira kwambiri chifukwa choti iye amatha kukhala chilichonse chimene wafuna n’cholinga choti akwaniritse zimene analonjeza. Iye walonjeza kuti kudzera mu Ufumu wake, chifuniro chake chidzachitika ‘pansi pano monga mmene zilili kumwamba.’ N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakuti ndatsimikiza mtima kuti imfa, kapena moyo, kapena angelo, kapena maboma, . . . kapena cholengedwa china chilichonse, sichidzatha kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”—Mateyo 6:10; Aroma 8:38, 39.
Tikuyembekezera mwachidwi kuti zimene Mulungu analonjeza kudzera mwa mneneri Yesaya zidzakwaniritsidwa. Iye anati: “Taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.” (Yesaya 65:17) Posachedwapa tidzasangalala kwambiri pamene zinthu zonse zokhumudwitsa zidzakhala mbiri yakale.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Tasintha maina ena m’nkhani ino.
[Mawu Otsindika patsamba 13]
Ngati zinthu zina sizinatiyendere bwino, sitinganene kuti ndife olephera
[Mawu Otsindika patsamba 14]
Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tiziganizira kwambiri mmene tingathetsere mavuto athu, m’malo modziimba mlandu
[Zithunzi patsamba 15]
Ngakhale kuti anthu amakhumudwitsa Mulungu, iye ndi wosangalala chifukwa choti akudziwa kuti adzakwaniritsa chifuniro chake
[Chithunzi patsamba 16]
Kuika zinthu zauzimu pamalo oyamba m’moyo wathu kumatithandiza kupirira zinthu zokhumudwitsa