Kodi Imfa ya Yesu Ingatipulumutse Bwanji?
PAFUPIFUPI zaka 2,000 zapitazo, panthawi ya Pasika wa Ayuda m’chaka cha 33 C.E., munthu wosalakwa anaphedwa n’cholinga choti anthu ena akhale ndi moyo. Kodi munthu ameneyo anali ndani? Anali Yesu wa ku Nazarete. Ndipo kodi ndi ndani amene angapindule ndi imfa yakeyi? Ndi anthu onse. Vesi lodziwika bwino la m’Baibulo limanena mwachidule za nsembe yopulumutsa moyo imeneyi kuti: “Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
Ngakhale kuti anthu ambiri amadziwa vesi limeneli, ndi ochepa okha amene amamvetsa tanthauzo lake. Iwo amadzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani tikufunikira nsembe ya Khristu? Kodi zingatheke bwanji kuti imfa ya munthu mmodzi ipulumutse anthu onse ku imfa?’ Baibulo limayankha mafunso amenewa momveka bwino ndiponso mogwira mtima.
Kodi Imfa Inayamba Bwanji Kulamulira Anthu?
Anthu ena amakhulupirira kuti anthu analengedwa kuti azikhala nthawi yochepa padzikoli, azivutika, azisangalala pang’ono, kenako n’kumwalira ndiyeno n’kupita kudziko la mtendere. Maganizo amenewa amasonyeza ngati kuti cholinga cha Mulungu chinali choti anthu azifa. Komabe Baibulo limanena chifukwa chenicheni chimene chimachititsa kuti anthu azifa. Limati: “Uchimo [unalowa] m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo, imfayo nifalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Vesili likusonyeza kuti anthu amafa chifukwa cha uchimo. Nangano “munthu mmodzi” amene imfa ndi uchimo zinalowa kudzera mwa iye n’ndani?
Buku lina lotchuka (The World Book Encyclopedia) limati asayansi ambiri amakhulupirira kuti anthu anachokera ku chinthu chimodzi. Ndipo Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti chinthucho ndi “munthu mmodzi.” Lemba la Genesis 1:27 limati: “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adam’lenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.” Choncho Baibulo limati anthu awiri oyambirira anali apadera kwambiri pa zinthu zonse zimene Mulungu Wamphamvuyonse analenga.
Nkhani ya m’buku la Genesis imafotokozanso za moyo wa anthu ena omwe anabadwa Yehova Mulungu atalenga anthu oyambirira. N’zochititsa Genesis 2:16, 17) Iye anafuna kuti anthu azikhala kosatha mosangalala ndiponso a thanzi labwino padziko lapansi la paradaiso. Sanafune kuti anthu azivutika ndi ukalamba kenako n’kumwalira. Nangano kodi zinatheka bwanji kuti imfa iyambe kulamulira anthu onse?
chidwi kuti m’nkhani yonseyi Mulungu sananene kuti anthu azifa. Koma iye anati anthu adzayamba kufa akadzasiya kumumvera. (Chaputala 3 cha buku la Genesis chimafotokoza mmene anthu awiri oyambirira anasankhira mwadala kusamvera Mlengi wawo, Yehova Mulungu. Motero Mulungu anawaweruza mogwirizana ndi zimene anawauziratu. Iye anauza mwamunayo kuti: “Chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Mogwirizana ndi zimene mawu a Mulungu ananena, anthu awiri osamverawo m’kupita kwa nthawi anafadi.
Koma uchimo wa anthu awiri oyamba aja unafalikira kwa anthu onse. Kusamvera kwawoku kunachititsa kuti mbadwa zawo zonse zisakhale ndi mwayi wodzasangalala ndi moyo wosatha. Zimene Yehova analonjeza Adamu ndi Hava zikanakhudzanso ana awo. Iye anawauza kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.” (Genesis 1:28) M’kupita kwa nthawi, anthuwo akanadzaza dziko lonse lapansi ndiponso akanasangalala ndi moyo wosatha. Koma kholo lawo Adamu, yemwe ndi “munthu mmodzi,” anawagulitsa n’kukhala akapolo a uchimo ndipo pamapeto pake anayamba kumwalira. Mtumwi Paulo, yemwenso anali mbadwa ya munthu woyambayo, analemba kuti: “Ine ndine wa kuthupi, wogulitsidwa ku uchimo.”—Aroma 7:14.
Masiku ano, anthu okonda kuwononga zinthu angawononge chithunzi chojambulidwa mwaluso kwambiri. Mofanana ndi zimenezi, Adamu, chifukwa choti anachimwa, anawononga kwambiri anthu omwe analengedwa mwaluso ndi Mulungu. Kuchokera pa ana a Adamu, panayamba kukhala mibadwo yosiyanasiyana ya anthu ndipo mbadwo uliwonse anthu ake amavutika kenako n’kumwalira. N’chifukwa chiyani anthu onsewa amafa? N’chifukwa choti onse anachokera kwa Adamu. Baibulo limati: “Mwa uchimo wa munthu mmodzi ambiri anafa.” (Aroma 5:15) Choncho zinthu monga matenda, ukalamba, mtima wokonda kuchita zoipa ndiponso imfa yeniyeniyo zinayamba chifukwa cha tchimo la Adamu lomwe linakhudza anthu onse. Ena mwa anthu amenewa ndi ifeyo.
M’kalata yomwe analembera Akhristu a ku Roma, mtumwi Paulo anatchula zoti anthu, Aroma 7:14-25) Ndithudi, Mlengi wathu wakonza njira yotipulumutsira kudzera mwa Mwana wake, Yesu Khristu.
kuphatikizapo iyeyo, ndi omvetsa chisoni chifukwa cha kupanda ungwiro ndiponso kuvutika kwawo chifukwa cha uchimo. Iye anati: “Munthu wovutika ine! Ndani adzandipulumutsa ku thupi limene likufa imfa imeneyi?” Limeneli ndi funso labwino kwambiri. Kodi ndani amene akanapulumutsa Paulo ndi anthu ena onse kuukapolo wa uchimo ndi imfa? Paulo yemweyo anayankha kuti: “Mulungu adzatero kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.” (Udindo wa Yesu Pantchito Yopulumutsa Anthu
Yesu anafotokoza bwino za udindo umene ali nawo pantchito yopulumutsa anthu kuukapolo wa uchimo. Iye anati: “Mwana wa munthu [anabwera] . . . kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyo 20:28) Kodi zinatheka bwanji kuti moyo wa Yesu ukhale dipo lowombola anthu? Nanga ifeyo timapindula bwanji ndi imfa yake?
Baibulo limati Yesu ndi “wopanda uchimo” ndiponso “wolekanitsidwa kwa ochimwa.” Pamoyo wake wonse, Yesu anamvera malamulo a Mulungu mokhulupirika. (Aheberi 4:15; 7:26) Choncho, Yesu sanafe chifukwa choti anachimwa ngati mmene zinalili ndi Adamu. (Ezekieli 18:4) M’malo mwake, Yesu analolera kufa kuti akwaniritse cholinga cha Atate wake, chopulumutsa anthu kuuchimo ndi imfa. Monga mmene taonera, Yesu analolera “kudzapereka moyo wake dipo” kuti anthu ambiri apulumuke. Yesu analolera ‘kulawa imfa kaamba ka munthu aliyense,’ ndipo palibe munthu wina aliyense amene angasonyeze chikondi kuposa chimenechi.—Aheberi 2:9.
Moyo umene Yesu anaupereka nsembe unali wofanana ndendende ndi umene Adamu anautaya. Ndiyeno kodi chinachitika n’chiyani Yesu atapereka moyo wake? Yehova analandira nsembeyo monga dipo “lolinganiza m’malo mwa onse.” (1 Timoteyo 2:6) Motero, Mulungu anagwiritsa ntchito mtengo wa moyo wa Yesu pogula, kapena kuti powombola anthu kuukapolo wa uchimo ndi imfa.
Baibulo limanena mobwerezabwereza za chikondi chachikulu chimenechi chomwe Mlengi wathu anatisonyeza. Paulo anakumbutsa Akhristu kuti iwo ‘anagulidwa ndi mtengo wake.’ (1 Akorinto 6:20; 7:23) Nayenso Petulo analemba kuti Mulungu sanagwiritse ntchito golide kapena siliva koma anagwiritsa ntchito magazi a Mwana wake kuti awombole Akhristu ku imfa. (1 Petulo 1:18, 19) Mwa kugwiritsa ntchito nsembe ya dipo ya Khristu, Yehova adzapulumutsa anthu ku imfa.
Kodi Inuyo Mudzapindula ndi Dipo la Khristu?
Ponena za madalitso osaneneka a dipo la Khristu, mtumwi Yohane analemba kuti: “[Yesu Khristu] ndiye nsembe yachiyanjanitso yophimba machimo athu. Osati athu okha, komanso a dziko lonse.” (1 Yohane 2:2) N’zoona, wina aliyense angapindule ndi dipo la Khristu. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti munthu aliyense adzapindula ndi nsembeyi ngakhale kuti sanachitepo chilichonse? Ayi. Kumbukirani anthu amene anapulumutsidwa mu mgodi amene tawatchula mu nkhani yoyamba ija. Anthu opulumutsa anzawo pangozi anangolowetsa chinthu choti anthu omwe anali mu mgodiwo alowemo. Koma kuti anthuwa apulumuke anafunika kulowa mu chinthucho. Mofanana ndi zimenezi, onse amene akufuna kudzapindula ndi dipo la Khristu sayenera kungokhala phee, n’kumadikira madalitso a Mulungu. Koma ayenera kuchitapo kanthu.
Kodi Mulungu amafuna kuti anthu achite chiyani? Lemba la Yohane 3:36 limati: “Iye wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha; wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu udzakhalabe pa iye.” Mulungu amafuna kuti tikhulupirire nsembe ya Khristu. Komatu sizokhazi chifukwa lemba la 1 Yohane 2:3 limati: “Ngati tipitiriza kusunga malamulo ake ndiye kuti tikum’dziwa [Yesu].” Choncho kuti munthu apulumutsidwe ku uchimo ndi imfa, zikuonekeratu kuti afunika kukhulupirira dipo la Khristu ndi kumvera malamulo ake.
Njira imodzi yofunika kwambiri yosonyezera kuti timakhulupirira dipo la Yesu ndiyo kuyamikira imfa yake mwa kupezeka pa mwambo wokumbukira imfa yakeyo, monga mmene iye analamulira. Yesu asanafe anayambitsa mwambo woti anthu azikumbukira imfa yake. Pamwambowu, iye anadyera pamodzi ndi atumwi ake okhulupirika chakudya chomwe chimaimira zinthu zinazake. Ndiyeno anauza ophunzirawo kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira ine.” (Luka 22:19) Mboni za Yehova zimaona ubwenzi wawo ndi Mwana wa Mulungu kukhala wofunika kwambiri ndipo zimamvera lamulo limeneli. Chaka chino, mwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu udzachitika Loweruka, pa March 22, dzuwa litalowa. Tikukuitanani ndi mtima wonse kuti mudzafike pa mwambo wapadera umenewu. Mukachita zimenezi mudzasonyeza kuti mukumvera lamulo la Yesu. Funsani Mboni za Yehova za m’dera lanu kuti zikuuzeni nthawi ndiponso malo kumene kukachitikire mwambowu. Pamwambo umenewu, mudzaphunzira zambiri zimene mufunika kuchita kuti dipo la Khristu likupulumutseni ku uchimo ndi imfa imene Adamu anatipatsira.
Masiku ano, ndi anthu ochepa okha amene amayamikira nsembe yaikulu imene Mlengi wathu ndi Mwana wake anapereka kuti atipulumutse. Anthu amene amakhulupirira nsembeyi amakhala osangalala kwambiri. Mtumwi Petulo analembera Akhristu anzake kuti: “Mumakhulupirira mwa [Yesu] ndipo mukusangalala kwambiri ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka, pamene mukulandira chipulumutso cha miyoyo yanu.” (1 Petulo 1:8, 9) Mwa kukonda Yesu Khristu ndiponso kukhulupirira nsembe yake ya dipo, mungakhale wosangalala kwambiri panopo komanso mungakhale ndi chiyembekezo chodzapulumutsidwa kuti uchimo ndi imfa.