Amene Angabwezeretse Moyo
Yandikirani Mulungu
Amene Angabwezeretse Moyo
KODI munaferedwapo wachibale wanu kapena mnzanu? Ngati zili choncho, n’zosakayikitsa kuti zimenezi zinakupwetekani kwambiri. Mlengi wathu amatimvetsa kwambiri tikakhala ndi chisoni chotere. Kuwonjezera pamenepa, iye angathetse mavuto onse amene amabwera wina akamwalira. M’Baibulo muli nkhani za anthu amene anaukitsidwa zosonyeza kuti iye sikuti wangokhala Wopereka moyo koma ndi Wobwezeretsanso moyowo. Tiyeni tione imodzi mwa nkhani za anthu amene Mulungu anawaukitsa kudzera mwa Mwana wake, Yesu Khristu. Nkhani imeneyi yalembedwa pa Luka 7:11-15.
Chinali chaka cha 31 C.E., ndipo Yesu anapita ku mzinda wotchedwa Naini, ku Galileya. (Vesi 11) Zikuoneka kuti mdima unali utayamba kugwa pamene iye amafika mu mzindawu. Baibulo limati: “Atayandikira pa chipata cha mzindawo, anakumana ndi anthu atanyamula maliro. Womwalirayo anali mwana wamwamuna yekhayo kwa mayi wakeyo. Komanso mayiyu anali mkazi wamasiye. Panali khamu lalikulu ndithu la anthu ochokera mu mzindawo limodzi ndi mayiyo.” (Vesi 12) Tangoganizani chisoni chimene mayiyo anali nacho. Iye anali kale ndi chisoni chachikulu chifukwa mwamuna wake anali atamwalira, ndipo panthawi iyi mwana wake mmodzi yekhayo yemwe akanamusamalira anamwaliranso.
Yesu anakhudzidwa mtima kwambiri kuona mzimayi wachisoniyo, yemwe mwina ankayenda pafupi ndi chithatha chomwe panali mtembo wa mwanayo. Nkhaniyi imati: “Pamene Ambuye anaona mayiyo, anamumvera chifundo, ndipo anati kwa iye: ‘Lekani kulira mayi.’” (Vesi 13) Yesu anakhudzidwa mtima kwambiri ndi chisoni cha mayi wamasiyeyu. Mwina anakumbukira za amayi ake om’bereka omwe panthawiyi ayenera kuti anali amasiye, ndiponso amadziwa kuti posachedwapa amayi ake adzakhala ndi chisoni ngati chimenechi iye akamwalira.
Yesu anafika pomwe panali anthuwa osati n’cholinga choti apite nawo kumanda. Koma atalamula anthuwo kuti aime ‘anagwira chithathacho.’ Kenako, monga munthu amene anapatsidwa mphamvu zogonjetsa imfa, anati: “‘Mnyamatawe, ndikunena ndi iwe, Tadzuka!’ Pamenepo wakufayo anadzuka nakhala tsonga, ndi kuyamba kulankhula. Kenako anam’pereka kwa mayi wake.” (Mavesi 14, 15) Mnyamatayu atamwalira sanalinso m’manja mwa mayi ake. Koma Yesu atam’pereka mnyamatayu, anakakhalanso limodzi ndi mayi ake. N’zoonekeratu kuti chisoni chimene mayiyu anali nacho chinasanduka chisangalalo.
Kodi mumalakalaka kudzasangalala pokumananso ndi achibale anu amene anamwalira? Dziwani kuti Mulungu amafuna kuti mudzatero. Chifundo chimene Yesu anali nacho pa mayi uja chimasonyezanso mmene Mulungu amamvera. Chifukwa Yesu amatsanzira ndendende umunthu wa Atate wake. (Yohane 14:9) Baibulo limatiphunzitsa kuti Mulungu amalakalaka kuukitsa anthu amene akuwakumbukira. (Yobu 14:14, 15) Mawu ake Baibulo amatipatsa chiyembekezo chosangalatsa chodzakhala ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi ndiponso kudzaona achibale athu akuukitsidwa. (Luka 23:43; Yohane 5:28, 29) Tikukulimbikitsani kuti muphunzire zambiri zokhudza Wobwezeretsa moyo ndiponso za mmene mungakhalire ndi chiyembekezo choti achibale anu adzaukitsidwa.
[Chithunzi patsamba 23]
“Wakufayo anadzuka nakhala tsonga, ndi kuyamba kulankhula. Kenako anam’pereka kwa mayi wake”