Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ankaona Malonjezo Ali Patali

Ankaona Malonjezo Ali Patali

“Sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo. Koma anawaona ali patali.”—AHEB. 11:13.

1. Kodi kukhala ndi luso loona zinthu m’maganizo mwathu kungatithandize bwanji? (Onani chithunzi pamwambapa.)

YEHOVA anatilenga ndi luso loona m’maganizo mwathu zinthu zimene sitinazione. Zimenezi zimatithandiza kuchita zinthu mwanzeru komanso kuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. Yehova amadziwa zomwe zidzachitike ndipo Baibulo limatithandiza kudziwa zam’tsogolo. Choncho timatha kuona zinthuzo m’maganizo mwathu n’kumakhulupirira kuti zidzachitikadi.—2 Akor. 4:18.

2, 3. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Hana ankachita? (b) Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhaniyi?

2 Koma zinthu zina zimene timaona m’maganizo mwathu sizikhala zenizeni. Mwachitsanzo, kamtsikana kangamayerekezere m’maganizo mwake katakwera pamsana pa gulugufe n’kumauluka. Koma Hana ankaganizira zinthu zenizeni zimene zingachitike atapereka mwana wake Samueli kuti azikatumikira pa chihema. Kuganizira kwambiri zimenezi kunamuthandiza kuti asasinthe maganizo. (1 Sam. 1:22) Tikamaona m’maganizo mwathu zimene Mulungu walonjeza ndiye kuti tikuganizira zinthu zimene zidzachitikadi.—2 Pet. 1:19-21.

3 N’zosakayikitsa kuti atumiki akale a Yehova ankaona m’maganizo mwawo zimene Mulungu anawalonjeza. Kodi zimenezi zinkawathandiza bwanji? Kodi kuganizira zinthu zosangalatsa zimene Mulungu watilonjeza kungatithandize bwanji?

KUGANIZIRA MALONJEZO KUNAWALIMBIKITSA

4. Kodi ndi mawu ati amene anachititsa Abele kukhala ndi chiyembekezo komanso chikhulupiriro?

4 Kodi Abele ankaona m’maganizo mwake zimene Yehova analonjeza? Abele sankadziwa zimene Yehova adzachite pokwaniritsa mawu amene anauza njoka akuti: “Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Mbewu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.” (Gen. 3:14, 15) Koma Abele ayenera kuti ankaiganizira kwambiri nkhaniyi ndipo ankadziwa kuti winawake ayenera ‘kuvulazidwa chidendene’ kuti athu akhalenso angwiro ngati mmene Adamu ndi Hava analili poyamba. Kaya ankaona zotani m’maganizo mwake, iye ankakhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova ndipo izi zinathandiza kuti Yehovayo alandire nsembe yake.—Werengani Genesis 4:3-5; Aheberi 11:4.   

5. Kodi Inoki ayenera kuti ankaona chiyani m’maganizo mwake?

5 Inoki anali ndi chikhulupiriro ngakhale kuti ankakhala limodzi ndi anthu onyoza Mulungu. Mulungu anauzira Inoki kunena ulosi wakuti Yehova adzabwera ‘ndi miyandamiyanda ya oyera ake, kudzapereka chiweruzo kwa onse. Adzagamula kuti onse osaopa Mulungu apezeka ndi mlandu chifukwa cha ntchito zawo zonyoza Mulungu zimene anazichita mosaopa Mulungu. Adzawaweruzanso chifukwa cha zinthu zonse zonyoza koopsa zimene ochimwa osaopa Mulungu anamunenera.’ (Yuda 14, 15) Inoki ayenera kuti ankaona m’maganizo mwake dziko lopanda anthu osaopa Mulungu.—Werengani Aheberi 11:5, 6.

6. Kodi Nowa ayenera kuti ankaganizira za chiyani pambuyo pa Chigumula?

6 Nayenso Nowa anali ndi chikhulupiriro ndipo anapulumuka Chigumula. (Aheb. 11:7) Madzi ataphwera, iye asonyeza chikhulupiriro chake popereka nsembe ya nyama. (Gen. 8:20) Iye ayenera kuti ankakhulupiriranso zoti tsiku lina anthu adzamasulidwa ku uchimo ndi imfa. Pambuyo pa Chigumula, zinthu zinavutanso chifukwa chakuti Nimurodi anayamba kuchita zinthu zosemphana ndi cholinga cha Yehova. Koma Nowa anakhalabe ndi chikhulupiriro komanso chiyembekezo. (Gen. 10:8-12) N’kutheka kuti mtima wake unkakhala m’malo akaganizira zoti anthu adzamasulidwa ku uchimo ndi imfa. Panopa nthawi yomasulidwayi yatsala pang’ono kufika ndipo nafenso tikhoza kumaona m’maganizo mwathu mmene zinthu zidzakhalire pa nthawiyo.—Aroma 6:23.

ANKAONA M’MAGANIZO MWAWO MALONJEZO ATAKWANIRITSIDWA

7. Kodi Abulahamu, Isaki ndi Yakobo ankaganizira zinthu ziti?

7 Abulahamu, Isaki ndi Yakobo ayenera kuti ankaona m’maganizo mwawo zinthu zimene Mulungu analonjeza. Tikutero chifukwa iye anawalonjeza kuti mitundu yonse idzadalitsidwa kudzera mwa mbewu yawo. (Gen. 22:18; 26:4; 28:14) Anawauzanso kuti ana awo adzachuluka ndipo adzakhala m’dziko limene Mulungu anawalonjeza. (Gen. 15:5-7) Chikhulupiriro chinawathandiza ndipo ankaona malonjezowo atakwaniritsidwa. Kuyambira kale, Yehova wakhala akutsimikizira atumiki ake okhulupirika kuti adzabwezeretsa madalitso amene Adamu anataya.

8. Kodi n’chiyani chinathandiza Abulahamu kukhala ndi chikhulupiriro cholimba?

8 Abulahamu ankaona m’maganizo mwake zimene Mulungu analonjeza. Zimenezi zinamuthandiza kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri. Baibulo limati Abulahamu ndiponso atumiki ena a Yehova “sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo. Koma anawaona ali patali ndi kuwalandira.” (Werengani Aheberi 11:8-13.) Abulahamu anali ndi chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zam’tsogolo ndiponso umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.

9. Kodi kukhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova kunathandiza bwanji Abulahamu?

9 Abulahamu ankatumikira Mulungu mwakhama chifukwa chakuti ankakhulupirira kwambiri malonjezo ake. Chikhulupirirochi chinamuthandiza kuchoka mumzinda wa Uri ndiponso kuti asakhazikike m’mizinda ya Kanani. Maziko a mizinda yonseyi anali osalimba chifukwa olamulira ake anali osaopa Mulungu. (Yos. 24:2) Pa moyo wake wonse, Abulahamu “anali kuyembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.” (Aheb. 11:10) Abulahamu ankaona m’maganizo mwake ali mumzinda wolamulidwa ndi Yehova. Abele, Inoki, Nowa, Abulahamu ndi atumiki ena a Yehova ankakhulupirira kuti akufa adzauka. Iwo ankayembekezera Ufumu wa Mulungu womwe ndi “mzinda wokhala ndi maziko enieni.” Kuganizira zinthu zimenezi kunawathandiza kukhulupirira kwambiri Yehova.—Werengani Aheberi 11:15, 16.

10. Kodi chiyembekezo chimene Sara anali nacho chinamuthandiza bwanji?

10 Chitsanzo china pa nkhaniyi ndi Sara. Ali ndi zaka 90, analibe mwana koma anali ndi chiyembekezo ndipo ankakhulupirira Mulungu. Iye ankaona m’maganizo mwake ana ake akudalitsidwa ndi Yehova. (Aheb. 11:11, 12) Ankakhulupirira zimenezi chifukwa Yehova anali atauza mwamuna wake kuti: ‘Sara ndidzamudalitsa ndipo iwe ndidzakupatsa mwana wamwamuna wochokera mwa iye. Ndidzamudalitsa ndipo adzakhala mayi wa mitundu yambiri ya anthu ndi wa mafumu a mitundu yambiri ya anthu.’ (Gen. 17:16) Sara atabereka Isaki, zinamulimbikitsa kukhulupirira kwambiri malonjezo ena onse a Mulungu. Nafenso tili ndi mwayi woona m’maganizo mwathu kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu.

ANAYANG’ANITSITSA PA MPHOTO YAKE

11, 12. N’chiyani chinathandiza kuti Mose azikonda kwambiri Yehova?

11 Mose ankakonda kwambiri Yehova ndiponso kumukhulupirira. Iye anakulira m’banja lachifumu ndipo zinali zosavuta kuti ayambe kukonda udindo ndi chuma. Koma zikuoneka kuti makolo ake anamuphunzitsa kuti Yehova akufuna kulanditsa Aheberi ku ukapolo n’kupita nawo ku Dziko Lolonjezedwa. (Gen. 13:14, 15; Eks. 2:5-10) N’kutheka kuti Mose ankaganizira kwambiri zimenezi pa moyo wake ndipo zinamuchititsa kuti azikonda kwambiri Yehova osati kukhala ndi udindo m’dzikoli.

12 Baibulo limanena kuti: “Mwa chikhulupiriro, Mose atakula anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao, ndipo anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu, m’malo mochita zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo. Iye anachita zimenezi chifukwa anaona kutonzedwa kwake monga Wodzozedwa kukhala chuma chochuluka kuposa chuma cha Iguputo, pakuti anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandire.”—Aheb. 11:24-26.

13. Kodi kuganizira kwambiri malonjezo a Yehova kunathandiza bwanji Mose?

13 Kuganizira kwambiri malonjezo a Yehova kunachititsa Mose kumukonda kwambiri komanso kumukhulupirira ndi mtima wonse. N’kutheka kuti nayenso ankaganizira nthawi imene Yehova adzathetse imfa. (Yobu 14:14, 15; Aheb. 11:17-19) M’pomveka kuti Mose ankakonda Yehova chifukwa Yehovayo anasonyeza kuti amamvera chisoni Aheberi komanso anthu onse. Kukonda Mulungu komanso kumukhulupirira kunathandiza Mose pa moyo wake wonse. (Deut. 6:4, 5) Pa nthawi ina, Farao ananena kuti adzapha Mose koma iye sanachite mantha. Izi zinatheka chifukwa chakuti ankakhulupirira Mulungu, kumukonda ndiponso ankaona m’maganizo mwake zinthu zabwino zimene Mulungu analonjeza.—Eks. 10:28, 29.

MUZIGANIZIRA MADALITSO A UFUMU WA MULUNGU

14. Kodi anthu amayembekezera zinthu ziti?

14 Masiku ano, anthu amaganizira kwambiri zinthu zosatheka. Ambiri amavutika kupeza zinthu zofunika pa moyo koma amaganiza kuti adzalemera. Chomvetsa chisoni n’chakuti moyo wa anthu ndi ‘wodzaza ndi mavuto ndi zopweteka.’ (Sal. 90:10) Anthu ena amaganiza kuti maboma a anthu adzathetsa mavuto awo onse. Koma Baibulo limasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto a anthu. (Dan. 2:44) Ambiri amaganizanso kuti Mulungu sadzawononga anthu oipa koma Baibulo limanena zinthu zosiyana ndi zimenezi. (Zef. 1:18; 1 Yoh. 2:15-17) Zinthu zimene anthu osaopa Mulungu amayembekezerazi n’zosatheka.

Muziyerekezera muli m’dziko latsopano (Onani ndime 15)

15. (a) Kodi kuona m’maganizo mwathu zimene tikuyembekezera kungatithandize bwanji? (b) Kodi mumalakalaka zinthu ziti pa nthawi imene Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake?

15 Koma Akhristufe timalimbikitsidwa tikamaganizira kwambiri zimene tikuyembekezera, kaya ndi zapadziko lapansi kapena kumwamba. Tiyenera kuona m’maganizo mwathu tikusangalala ndi madalitso amene Mulungu watilonjeza. Tidzasangalala kwambiri tikamaganizira zimene tidzachite Yehova akadzakwaniritsa malonjezo ake. Mwina panopa mumaganizira za nthawi imene mudzakhala ndi moyo wosatha. Mwina mumaona m’maganizo mwanu mukugwira ntchito ndi anzanu posintha dzikoli kukhala Paradaiso. Aliyense pa nthawiyo adzakhala wokonda Yehova. Mudzakhala amphamvu ndipo simudzadwala kapena kuda nkhawa. Mudzasangalala kugwiritsa ntchito luso lanu polemekeza Yehova ndiponso pothandiza anthu ena. Mwachitsanzo, mudzasangalala kuthandiza anthu oukitsidwa kuti aphunzire za Yehova. (Yoh. 17:3; Mac. 24:15) Baibulo limanena kuti zimenezi zidzachitikadi ndipo sizidzalephereka.—Yes. 11:9; 25:8; 33:24; 35:5-7; 65:22.

MUZIKAMBIRANA ZIMENE TIKUYEMBEKEZERA

16, 17. Kodi kukambirana zimene tikuyembekezera kungatithandize bwanji?

16 Kukambirana ndi anzathu zimene tingafune kudzachita pa nthawi imene Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake, kumathandiza kuti tiziona zinthuzo m’maganizo mwathu. N’zoona kuti sitidziwa mmene zinthu zonse zidzakhalire pa nthawiyo. Koma tikamakambirana zimene tikuganizira timalimbikitsana ndipo timasonyeza kuti timakhulupirira kwambiri zimene Mulungu walonjeza. Paulo atafika ku Roma analimbikitsana ndi abale a kumeneko. (Aroma 1:11, 12) Nafenso tiyenera kulimbikitsana m’masiku ovutawa.

17 Kuona m’maganizo mwathu zinthu zimene tikuyembekezera kumathandizanso kuti tisiye kuganizira kwambiri mavuto amene tikukumana nawo. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chinachititsa Petulo kufunsa Yesu kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatirani, kodi tidzapeza chiyani?” N’kutheka kuti anali ndi nkhawa poganizira zam’tsogolo. Koma Yesu analimbikitsa onse amene analipo pa nthawiyo powauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Pa nthawi ya kulenganso zinthu, pamene Mwana wa munthu adzakhala pampando wachifumu waulemerero, inu amene mwatsatira ine mudzakhalanso m’mipando yachifumu 12, kuweruza mafuko 12 a Isiraeli. Aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, abambo, amayi, ana kapena minda chifukwa cha dzina langa adzalandira zochuluka kwambiri kuposa zimenezi, ndipo adzapeza moyo wosatha.” (Mat. 19:27-29) Mawuwa ayenera kuti anathandiza Petulo ndi anzakewo kuona m’maganizo mwawo akulamulira dziko n’kumathandiza anthu omvera kupeza madalitso osaneneka.

18. Kodi kuganizira zimene zidzachitike Yehova akadzakwaniritsa malonjezo ake kungatithandize bwanji?

18 Anthu a Yehova amasangalala kwambiri akamaganizira zimene zidzachitike pamene Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake. Zinthu zimene Abele ankadziwa zokhudza cholinga cha Mulungu zinamuthandiza kuona kuti ali ndi tsogolo labwino ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Nayenso Abulahamu anali ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa choti ankaona m’maganizo mwake malonjezo onse a Yehova okhudza mbewu yake atakwaniritsidwa. (Gen. 3:15) Mose “anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandire” ndipo izi zinamuthandiza kukonda kwambiri Yehova komanso kumukhulupirira kwambiri. (Aheb. 11:26) Ifenso tikamaona m’maganizo mwathu zimene Mulungu watilonjeza tidzayamba kumukonda kwambiri ndiponso kumukhulupirira ndi mtima wonse. M’nkhani yotsatira tidzakambirana zimene tingachite kuti tizigwiritsa ntchito bwino luso loona zinthu m’maganizo mwathu.