Kodi Mukudziwa?
N’chifukwa chiyani anthu ena otchulidwa m’Baibulo ankang’amba zovala zawo?
BAIBULO limafotokoza nthawi zosiyanasiyana pamene anthu ankang’amba zovala zawo. Anthu masiku ano amadabwa akamva zimenezi. Koma Ayuda ankachita zimenezi posonyeza kuti akudandaula, akumva chisoni, achita manyazi, akwiya kapena akulira.
Mwachitsanzo, Rubeni “anang’amba zovala zake” atazindikira kuti cholinga chake chofuna kupulumutsa Yosefe chalephereka ndipo wagulitsidwa. Nayenso Yakobo “anang’amba zovala zake” poganiza kuti mwana wake wakhadzulidwa ndi chilombo. (Gen. 37:18-35) Yobu atamva zoti ana ake onse aphedwa, anaimirira “n’kung’amba malaya ake akunja.” (Yobu 1:18-20) Mwamuna wina anafika kwa Mkulu wa Ansembe dzina lake Eli “atang’amba zovala zake.” Iye anabwera kudzanena uthenga woti Aisiraeli agonjetsedwa, ana awiri a Eli aphedwa ndiponso likasa la pangano lalandidwa. (1 Sam. 4:12-17) Nayenso Yosiya atamva mawu a m’Chilamulo akuwerengedwa n’kuzindikira kuti anthu ake achimwa, ‘anang’amba zovala zake.’—2 Maf. 22:8-13.
Pamene Yesu ankazengedwa mlandu, Mkulu wa Ansembe dzina lake Kayafa “anang’amba malaya ake akunja” poganiza kuti Yesu wanyoza Mulungu. (Mat. 26:59-66) Arabi ankalamulanso kuti munthu aliyense akamva dzina la Mulungu likunyozedwa azing’amba zovala zake. Koma lamulo lina la arabi limene analikhazikitsa kachisi wa ku Yerusalemu atawonongedwa, linkanena kuti “masiku ano munthu amene wamva wina akunyoza Dzina la Mulungu, sayenera kung’amba zovala zake chifukwa zingachititse kuti munthu akhale ndi usiwa.”
Koma kung’amba zovala sikunali kokwanira pamaso pa Mulungu chifukwa iye ankadziwa ngati munthu akumvadi chisoni mumtima mwake. N’chifukwa chake Yehova anauza anthu ake kuti: ‘Ng’ambani mitima yanu osati zovala zanu ndipo bwererani kwa ine.’—Yow. 2:13.