Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiziganizirana Ndiponso Kulimbikitsana

Tiziganizirana Ndiponso Kulimbikitsana

“Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.”—AHEB. 10:24.

1, 2. N’chiyani chinathandiza a Mboni za Yehova okwana 230 kuti asafe pa ulendo umene anawayendetsa?

ULAMULIRO wa chipani cha Hitler utangotsala pang’ono kutha, pambuyo pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, akuluakulu a chipanichi analamula kuti anthu ambirimbiri amene anali m’ndende zawo aphedwe. Anakonza zoti anthu amene anali kundende ina apite nawo kumadoko enaake. Ankafuna kuti akawakweze sitima zapamadzi n’kukazimiza m’nyanja.

2 Anakonza zoti akaidi okwana 33,000 amene anali kundendeyo ayende mtunda wa makilomita 250 kupita kudoko la mumzinda wa Lübeck ku Germany. Pagululi panali a Mboni za Yehova okwana 230 ochokera m’mayiko 6. Aliyense pa gululi anali atafooka chifukwa cha njala ndi matenda. N’chiyani chinathandiza kuti abale athu apulumuke pa ulendowu? M’bale wina anati: “Sitinasiye kulimbikitsana kuti tipirire.” Iwo anapulumuka chifukwa chakuti ankakondana kwambiri komanso Mulungu anawapatsa “mphamvu yoposa yachibadwa.”—2 Akor. 4:7.

3. N’chifukwa chiyani timafunika kulimbikitsana?

3 Ife sitikuyenda pa ulendo woterewu, koma timakumana ndi mavuto ambirimbiri. Ufumu wa Mulungu utakhazikitsidwa kumwamba mu 1914, Satana anaponyedwa padziko lapansi. Iye “ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chiv. 12:7-9, 12) Pamene Aramagedo ikuyandikira, Satana akuyesetsa kutifooketsa potibweretsera mavuto ndi mayesero. Palinso zinthu zambirimbiri zimene zimatidetsa nkhawa tsiku ndi tsiku. (Yobu 14:1; Mlal. 2:23) Mavuto oterewa akachuluka, tingafooke ndipo patokha zingakhale zovuta kuti tipirire. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina amene kwa zaka zambiri anathandiza anthu ochuluka kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Atakalamba, iye ndi  mkazi wake anadwala ndipo m’baleyo anafooka kwambiri moti ankafunika “mphamvu yoposa yachibadwa” yochokera kwa Yehova kuti apirire. Nafenso timafunika mphamvu imeneyi komanso kulimbikitsidwa ndi anzathu.

4. Kuti tilimbikitse ena, kodi tiyenera kuganizira mawu ati a mtumwi Paulo?

4 Kuganizira mawu amene mtumwi Paulo analembera Akhristu achiheberi kungatithandize kuti tizilimbikitsa anzathu. Iye anati: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.” (Aheb. 10:24, 25) Kodi tingagwiritse ntchito bwanji malangizo amene ali m’mavesi amenewa?

‘TIZIGANIZIRANA’

5. Kodi mawu a Paulo akutilimbikitsa kuchita chiyani, ndipo tingachite bwanji zimenezi?

5 Mawu a Paulo akutilimbikitsa kuti tiziganizira anthu ena komanso mavuto amene akukumana nawo. Sitingadziwe kapena kuganizira zimene zikuchitikira abale athu ngati timangowapatsa moni mwachidule ku Nyumba ya Ufumu kapena kungocheza nawo nkhani zosafunika kwenikweni. N’zoona kuti timafunika kusamala kuti ‘tisamalowerere nkhani za eni.’ (1 Ates. 4:11; 1 Tim. 5:13) Komabe, ngati tikufunitsitsa kulimbikitsa abale athu, tiziyesetsa kuti tiwadziwe bwino. Tiziyesetsa kuti tidziwe mmene zinthu zilili pa moyo wawo, tidziwe makhalidwe awo, moyo wawo wauzimu, zimene amachita bwino komanso zimene zimawavuta. Tizichita zinthu zoti azitiona kuti ndife anzawo ndiponso azidziwa kuti timawakonda. Zimenezi zikusonyeza kuti tizipeza nthawi yocheza nawo, osati kumangopita kukawaona akakhala m’mavuto kapena akafooka.—Aroma 12:13.

6. N’chiyani chingathandize mkulu kuti ‘aziganizira’ nkhosa?

6 Akulu mumpingo amalimbikitsidwa ‘kuweta gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwawo,’ ndipo ayenera kuchita zimenezi mofunitsitsa komanso ndi mtima wonse. (1 Pet. 5:1-3) Ndipotu kuti iwo awete bwino nkhosa za Mulungu amafunika kuzidziwa bwino. (Werengani Miyambo 27:23.) Akulu akamapeza nthawi yocheza ndi Akhristu anzawo, Akhristuwo amakhala omasuka kupempha kuti awathandize. Iwo angakhalenso omasuka kuwauza zakukhosi kwawo komanso zinthu zimene zikuwadetsa nkhawa. Zimenezi zingathandize akuluwo ‘kuganizira’ nkhosazo n’kuona mmene angazithandizire.

7. Kodi tizitani anthu amene akhumudwa akatilankhula “zopanda pake”?

7 M’kalata imene analembera Akhristu a ku Tesalonika, Paulo anati: “Thandizani ofooka.” (Werengani 1 Atesalonika 5:14.) Tinganene kuti anthu “amtima wachisoni” komanso amene akhumudwa amakhala ofooka. Lemba la Miyambo 24:10 limati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” Ndipotu munthu amene wakhumudwa kwambiri angalankhule “zopanda pake.” (Yobu 6:2, 3) ‘Poganizira’ anthu oterewa, tisamaiwale kuti nthawi zina anganene zinthu zosiyana ndi zimene zili mumtima mwawo. Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Rachelle, amene mayi ake ankavutika kwambiri maganizo, anati: “Nthawi zambiri mayi anga ankanena zinthu zokhumudwitsa kwambiri. Zimenezi zikachitika, ndinkayesetsa kuganizira makhalidwe abwino amene mayi anga ali nawo. Ndinkakumbukira kuti iwo ndi munthu wachikondi, wokoma mtima ndiponso wowolowa manja. Ndinazindikira kuti anthu amene akhumudwa kapena omwe akuvutika maganizo amalankhula zinthu zambiri asanaganizire. Ndipo kubwezera anthu oterewa n’kulakwa kwambiri.” Lemba la Miyambo 19:11 limati:  “Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola.”

8. Kodi ndi anthu otani amene tiyenera ‘kuwatsimikizira’ kuti timawakonda, ndipo n’chifukwa chiyani?

8 Anthu ena angamachitebe manyazi mwinanso kukhumudwa chifukwa cha machimo amene anachita m’mbuyomu, ngakhale kuti analapa. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘timaganizira’ anthu oterewa? Ponena za munthu wina wa ku Korinto, amene anali wochimwa koma kenako analapa, Paulo analemba kuti: “Mukhululukireni ndi mtima wonse ndi kumutonthoza, kuopera kuti mwina wotereyu angamezedwe ndi chisoni chake chopitirira malire. Choncho ndikukudandaulirani kuti mumutsimikizire kuti mumamukonda.” (2 Akor. 2:7, 8) Malinga ndi zimene buku lina lotanthauzira mawu limanena, mawu amene anawamasulira kuti ‘kutsimikizira’ amatanthauza “kuvomereza kapena kusainira.” Sitiyenera kungoganiza kuti munthu winawake akudziwa kuti timamukonda komanso kumuganizira. Munthuyo amafunika kuona zimene ifeyo tikumuchitira posonyeza kuti timamuganizira.

“TILIMBIKITSANE PA CHIKONDI NDI NTCHITO ZABWINO”

9. Kodi tingatani kuti ‘tilimbikitse ena pa chikondi ndi ntchito zabwino’?

9 Paulo analemba kuti: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.” Tiyenera kulimbikitsa Akhristu anzathu kuti akhale achikondi ndiponso kuti azichita ntchito zabwino. Ngati tikufuna kuti moto usazime, timasonkhezera komanso kukupizira. (2 Tim. 1:6) Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kulimbikitsa abale athu kuti azisonyeza kuti amakonda Mulungu komanso anthu ena. Kuti tilimbikitse ena kuchita ntchito zabwino, tiyenera kuwayamikira pa zinthu zimene akuchita bwino.

Muzipempha anthu ena kuti mulowe nawo mu utumiki

10, 11. (a) Kodi ndi anthu ati amene tiyenera kuwayamikira? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kuyamikira munthu amene wafooka kungam’thandize.

10 Kaya takhumudwa kapena ayi, tonsefe timafuna kuti anthu azitiyamikira. Mkulu wina analemba kuti: “Bambo anga sanandiyamikirepo ngakhale kamodzi. Choncho ndinkadzikayikira kwambiri. . . . Ngakhale kuti panopa ndili ndi zaka 50, ndimasangalala anzanga  akandiuza kuti udindo wanga monga mkulu ndikuukwanitsa. . . . Zimene zandichitikira pa moyo wanga zandithandiza kuona kuti kulimbikitsa ena n’kofunika kwambiri, ndipo ndimayesetsa kuchita zimenezi.” Aliyense amamva bwino akayamikiridwa, kaya akhale apainiya, achikulire kapena anthu amene afooka.—Aroma 12:10.

11 Pamene abale “oyenerera mwauzimu” akuthandiza ‘munthu amene wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika,’ ayenera kumulangiza mwachikondi komanso kumuyamikira pa zinthu zimene akuchita bwino. (Agal. 6:1) Akatero, munthuyo angalimbikitsidwe n’kuyambanso kuchita ntchito zabwino. Izi n’zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Miriam. Iye analemba kuti: “Pa nthawi ina ndinasokonezeka kwambiri anzanga ena atasiya choonadi ndiponso bambo anga atadwala kwambiri. Pofuna kuiwala mavuto, ndinayamba chibwenzi ndi mnyamata wosakhulupirira.” Zimenezi zinam’chititsa kuti azidziona kuti si woyenera kukondedwa ndi Yehova ndipo anaganiza zosiya kumutumikira. Koma analimbikitsidwa pamene mkulu wina anamukumbutsa kuti m’mbuyomu ankatumikira Yehova mokhulupirika kwambiri. Iye anamvetseranso pamene akulu ankamutsimikizira kuti Yehova amamukonda. Zimenezi zinam’thandiza kuti ayambenso kukonda Yehova. Choncho anathetsa chibwenzi ndi mnyamata wosakhulupirira uja ndipo anapitiriza kutumikira Yehova.

Muzilimbikitsa ena pa chikondi ndi ntchito zabwino

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala polimbikitsa anthu kuti azichita zambiri potumikira Mulungu?

12 Koma tiyenera kusamala tikamalimbikitsa anthu kuti azichita zambiri potumikira Mulungu. Si bwino kuwayerekezera ndi ena, kuwadzudzula kuti sakuchita bwino zinthu zina kapena kuwachititsa kuganiza kuti akulephera. N’kutheka kuti zimenezi zingam’chititse kuti ayambe kuchita khama kwa nthawi yochepa. Koma kuyamikira munthu pa zimene akuchita bwino ndiponso kumulimbikitsa kuti azichita zinthu chifukwa chokonda Mulungu, n’kumene kungamuthandize kwambiri kuti azitumikira Mulungu mwakhama.—Werengani Afilipi 2:1-4.

‘TIZILIMBIKITSANA’

13. Kodi tingalimbikitse bwanji anthu ena? (Onani chithunzi patsamba 18.)

13 Tiyenera ‘kulimbikitsana makamaka pamene tikuona kuti tsikulo likuyandikira.’ Polimbikitsa ena, timafunika kuwathandiza kuti apitirize kutumikira Mulungu mwakhama. Kulimbikitsa munthu kuli ngati kusonkhezera moto kuti usazime kapena kuti uyake kwambiri. Tiyenera kulimbikitsanso kapena kutonthoza anthu amene afooka kapena amene ali ndi chisoni. Pothandiza anthu oterewa, tizilankhula mokoma mtima ndiponso moleza mtima. (Miy. 12:18) Tiyenera kukhala ‘ofulumira kumva ndiponso odekha polankhula.’ (Yak. 1:19) Tikamamvetsera mwachifundo, tingadziwe zimene zikudetsa nkhawa Mkhristu mnzathu n’kuona mmene tingamuthandizire pa mavuto akewo.

Muzipeza nthawi yocheza ndi ena

14. Kodi m’bale wina amene anafooka anathandizidwa bwanji?

14 Tiyeni tikambirane zimene mkulu wina  wachifundo anachita pothandiza m’bale amene poyamba anali mkulu koma kenako anafooka kwa zaka zambiri. Mkuluyo anamvetsera pamene m’baleyo ankafotokoza mavuto ake ndipo anazindikira kuti m’baleyo ankakondabe kwambiri Yehova. Iye ankaphunzira mwakhama Nsanja ya Olonda iliyonse ndipo ankayesetsa kufika pa misonkhano. Koma zimene anthu ena mumpingo anachita zinamukhumudwitsa kwambiri. Mkuluyo anamvetsera mwachifundo popanda kumuweruziratu ndipo anasonyeza kuti amakonda kwambiri m’baleyo limodzi ndi banja lake. Kenako m’baleyo anazindikira kuti akulola zinthu zoipa zimene zinachitika kale kuti zizimulepheretsa kutumikira Mulungu yemwe amamukonda. Mkuluyo anapempha m’baleyo kuti ayende naye mu utumiki. Zimene mkuluyu anachita zinamuthandiza kuti ayambirenso kulalikira ndipo patapita nthawi, anayenereranso kukhala mkulu.

Muzimvetsera moleza mtima munthu wina akamafotokoza mavuto ake (Onani ndime 14 ndi 15)

15. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yehova pa nkhani yolimbikitsa anthu amene afooka?

15 Nthawi zambiri, munthu amene wafooka samangosinthiratu pa nthawi imene tamuthandizayo. Tingafunike kupitiriza kumuthandiza. Paja mtumwi Paulo ananena kuti: “Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.” (1 Ates. 5:14, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.) M’malo mongowathandiza pang’ono n’kuwasiya, tiyenera kupitiriza ‘kuwachirikiza’ kuti asagwe. M’mbuyomu, Yehova ankachitanso zinthu moleza mtima ndi atumiki ake amene anafooka. Mwachitsanzo, Eliya atafooka, Mulungu anamvetsa mmene ankamvera mumtima mwake ndipo anamuthandiza mwachifundo. Yehova anapatsa mneneriyu zinthu zonse zimene ankafunikira kuti apitirize utumiki wake. (1 Maf. 19:1-18) Davide atachimwa n’kulapa ndi mtima wonse, Yehova anamukomera mtima n’kumukhululukira. (Sal. 51:7, 17) Mulungu anathandizanso munthu amene analemba Salimo 73 pamene anatsala pang’ono kusiya kumutumikira. (Sal. 73:13, 16, 17) Yehova amatithandiza mokoma mtima makamaka pamene tafooka kapena kukhumudwa. (Eks. 34:6) Baibulo limanena kuti chifundo chake “chimakhala chatsopano m’mawa uliwonse” ndipo “sichidzatha.” (Maliro 3:22, 23) Yehova amafuna kuti nafenso tizikhala achifundo n’kumathandiza mokoma mtima anthu amene afooka kapena kukhumudwa.

TIZILIMBIKITSANA KUTI TIPITIRIZE KUYENDA PAMSEWU WA KU MOYO

16, 17. Kodi tiyenera kuchita chiyani pamene mapeto akuyandikira, ndipo n’chifukwa chiyani?

16 Pa akaidi 33,000 amene tawatchula pandime yachiwiri aja, anthu masauzande ambiri anamwalira. Koma a Mboni za Yehova onse okwana 230 anapulumuka. Iwo ankalimbikitsana ndi kuthandizana pa ulendowo. Zimenezi zinawathandiza kwambiri kuti apulumuke.

17 Masiku ano tikuyenda ‘pamsewu wolowera ku moyo’ wosatha. (Mat. 7:14) Posachedwapa atumiki a Yehova onse adzayenda mogwirizana kulowa m’dziko latsopano la chilungamo. (2 Pet. 3:13) Tiyeni tiziyesetsa kuthandizana pamene tikuyenda pamsewu umenewu.