Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anabala Zipatso Chifukwa Chokonzekera Bwino

Anabala Zipatso Chifukwa Chokonzekera Bwino

María Isabel ndi mtsikana amene amakhala mumzinda wa San Bernardo m’dziko la Chile ku South America ndipo ndi wofalitsa wakhama. Iye limodzi ndi a m’banja lake ndi a fuko la Amapuche. Anthu onse a m’banjali akuyesetsa mwakhama kuthandiza kuti kukhale mpingo wa chinenero cha Amapuche chomwenso ndi Chimapudunguni.

María Isabel anamva kuti Chikumbutso cha imfa ya Khristu chidzakhala mu chinenero cha Chimapudunguni ndiponso kuti pali timapepala toitanira anthu tokwanira 2,000 ta m’chinenerochi. Atamva zimenezi, anaganiza mofatsa n’kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ndithandize nawo ntchito imeneyi?’ Iye anakumbukira zinthu zabwino zimene achinyamata ena anakumana nazo polalikira kwa ana asukulu anzawo ndiponso aphunzitsi. María Isabel anafotokozera makolo ake zimenezi. Kenako anagwirizana zoti María Isabel akonze zokagawira timapepalato kusukulu kwawo. Kodi iye anakonza zotani?

Poyamba, María Isabel anapempha akuluakulu a pasukulupo ngati angamuloleze kuti akakhome kapepala koitaniraka pakhomo pasukuluyo. Iwo anavomera ndipo anamuyamikira chifukwa cha khama lake. Tsiku lina m’mawa pa nthawi yoitana mayina, mphunzitsi wamkulu pasukulupo analengeza zokhudza kapepala koitanira anthu kaja.

Kenako María Isabel anapempha kuti ayende kalasi iliyonse n’kufotokozera anzake za timapepalato. Aphunzitsi atamulola, anayenda kalasi iliyonse n’kufunsa ngati muli anthu a fuko la Amapuche. Iye anati: “Ndinkaganiza kuti pasukulupo pangakhale mwina anthu 10 kapena 15 amene ndi Amapuche. Koma ndinadabwa kuona kuti anali ambiri moti ndinagawira timapepala tokwana 150.”

ANKAGANIZA KUTI KUBWERA MUNTHU WAMKULU

Mzimayi wina ataona kapepala kamene kanakhomedwa pakhomo kaja, anapempha kuti aonane ndi munthu amene angamufotokozere zambiri. Iye anadabwa kwambiri atam’bweretsera mtsikana wa zaka 10 kuti amuthandize. Mzimayiyu ankaganiza kuti kubwera munthu wamkulu. María Isabel anamupatsa kapepala komuitanira ku Chikumbutso ndiponso kumufunsa kumene amakhala. Anatero n’cholinga choti adzapiteko ndi makolo ake kukamufotokozera zambiri za Ufumu wa Mulungu. Ofalitsa okwana 20 amene amatumikira m’gawo la chinenero cha Chimapudunguni anasangalala kwambiri kuona mzimayi uja ndiponso anthu ena 26 achimapuche atabwera pa Chikumbutso. Panopa mpingowu ukukula kwambiri.

Kaya muli ndi zaka zingati, mungachite bwino kuyesetsa kuitanira anzanu akusukulu kapena akuntchito kuti abwere ku Chikumbutso, nkhani ya onse kapena ku msonkhano wachigawo. Mungachitenso bwino kufufuza m’mabuku athu kuti mudziwe njira zabwino zoitanira anthu zimene anthu ena anagwiritsapo ntchito. Muyeneranso kupempha Yehova kuti akupatseni mzimu wake woyera kuti ukuthandizeni kulankhula za iye molimba mtima. (Luka 11:13) Mukachita zimenezi ndiponso kukonzekera bwino, inunso mungasangalale komanso kulimbikitsidwa kuona kuti ntchito yanu yabala zipatso.