Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amatiteteza Kuti Tidzapulumuke

Yehova Amatiteteza Kuti Tidzapulumuke

Yehova Amatiteteza Kuti Tidzapulumuke

“Mulungu akukutetezani ndi mphamvu yake chifukwa muli ndi chikhulupiriro. Mulungu akukutetezani kuti mudzalandire chipulumutso, ndipo chipulumutso chimenechi chidzaonekera mu nthawi ya mapeto.”​—1 PET. 1:5.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi Yehova anatikoka bwanji kuti tiyambe kumulambira?

Kodi tingalole bwanji Yehova kutitsogolera ndi malangizo ake?

Kodi Yehova amatilimbikitsa bwanji?

1, 2. (a) Kodi timadziwa bwanji kuti Mulungu adzatithandiza kuti tikhalebe okhulupirika? (b) Kodi Yehova amadziwa zinthu ziti zokhudza munthu aliyense payekha?

YESU anati: “Amene adzapirire mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.” (Mat. 24:13) Mawu amenewa akusonyeza kuti tifunika kukhalabe okhulupirika mpaka mapeto kuti tidzapulumuke pamene Mulungu akuwononga dziko la Satanali. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova amangotisiya kuti tizipirira pogwiritsa ntchito nzeru kapena mphamvu zathu. Baibulo limalonjeza kuti: “Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.” (1 Akor. 10:13) Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani?

2 Yehova sadzalola kuti tiyesedwe kufika pamene sitingapirire. Koma kuti achite zimenezi ayenera kutidziwa bwino. Ayenera kudziwa mavuto amene tikukumana nawo, mmene zinthu zimatikhudzira ndiponso kuti tikhoza kupirira kufika pati. Koma kodi Mulunguyo amatidziwadi bwino? Inde. Malemba amasonyeza kuti Yehova amadziwa aliyense payekha. Amadziwa zimene timachita tsiku lililonse. Iye amatha kudziwa ngakhale maganizo ndi zolinga zonse za mumtima mwathu.​—Werengani Salimo 139:1-6.

3, 4. (a) Kodi zimene zinachitikira Davide zikusonyeza bwanji kuti Yehova amachita chidwi ndi munthu aliyense? (b) Kodi ndi zinthu ziti zochititsa chidwi zimene Yehova akuchita masiku ano?

3 Kodi n’zothekadi kuti Mulungu angakhale ndi chidwi choterechi kwa anthu wamba ngati ifeyo? Wamasalimo Davide anaganizirapo zimenezi ndi kufunsa Yehova kuti: “Ndikayang’ana kumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga, ndimaganiza kuti: Munthu ndani kuti muzimuganizira?” (Sal. 8:3, 4) N’kutheka kuti Davide anafunsa funso limeneli chifukwa cha zimene zinamuchitikira. Iye ndi amene anali wamng’ono pa ana onse a Jese, koma Yehova anaona kuti ndiye “munthu wapamtima pake” ndipo ‘anamutenga kubusa, kumene anali kusamalira nkhosa kuti akhale mtsogoleri’ wa Aisiraeli. (1 Sam. 13:14; 2 Sam. 7:8) Taganizirani mmene Davide anamvera atazindikira kuti Mlengi wa chilengedwe chonse ankachita chidwi ndi zimene iye, monga kam’busa kachinyamata, anali kuganiza mumtima mwake.

4 N’zochititsa chidwi kudziwa kuti Yehova amatiganiziranso masiku ano. Iye akusonkhanitsa anthu omwe ali ngati “zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse” kuti amulambire ndipo akuwathandiza kuti akhalebe okhulupirika. (Hag. 2:7) Kuti timvetse mmene Yehova amatithandizira kukhalabe okhulupirika, tiyeni tione mmene Iye amakokera anthu kuti ayambe kumulambira.

MULUNGU NDI AMENE WATIKOKA

5. Kodi Yehova amakoka bwanji anthu kuti abwere kwa Mwana wake? Perekani chitsanzo.

5 Yesu anati: “Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma.” (Yoh. 6:44) Mawu amenewa akutanthauza kuti Mulungu ndi amene amatithandiza kuti tikhale ophunzira a Khristu. Kodi Yehova amakoka bwanji anthu kuti abwere kwa Mwana wake? Iye amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera komanso ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, pamene Paulo ndi amishonale anzake anali ku Filipi, anakumana ndi mayi wina dzina lake Lidiya n’kuyamba kumuuza uthenga wabwino. Baibulo limati: “Yehova anatsegula kwambiri mtima wake kuti atchere khutu ku zimene Paulo anali kunena.” Mulungu anamupatsa mzimu wake kuti umuthandize kumvetsa uthengawo ndipo zotsatira zake zinali zakuti iye ndi a m’banja lake anabatizidwa.​—Mac. 16:13-15.

6. Kodi tonsefe tinakokedwa bwanji ndi Mulungu kuti tizimulambira?

6 Kodi zimenezi zinangochitikira Lidiya yekha? Ayi. Ngati ndinu Mkhristu wobatizidwa ndiye kuti Mulungu anakukokaninso kuti muzimulambira. Atate wathu wakumwamba anaona makhalidwe abwino mumtima wa Lidiya ndipo n’chimodzimodzi ndi inuyo. Iye anaonanso makhalidwe abwino mumtima mwanu. Mutangomva uthenga wabwino, Yehova anakupatsani mzimu woyera kuti ukuthandizeni kumvetsa bwino uthengawo. (1 Akor. 2:11, 12) Mutayamba kuyesetsa kutsatira zimene mukuphunzira iye anakudalitsani kuti mukwanitse kuchita chifuniro chake. Yehova anasangalala kwambiri pamene munadzipereka kwa iye. Kuyambira pamene munayamba kuyenda pa njira yopita ku moyo, Yehova wakhala akukuthandizani nthawi zonse.

7. Tikudziwa bwanji kuti Mulungu adzatithandiza kukhalabe okhulupirika?

7 Yehova akatithandiza kuti tiyambe kuyenda naye samangotisiya. Amapitiriza kutithandiza kuti tikhalebe okhulupirika. Iye amadziwa kuti ngati anachita kutithandiza kuti tilowe m’choonadi ndiye kuti patokha sitingapitirize kukhala m’choonadi. Mtumwi Petulo analembera Akhristu odzozedwa kuti: “Mulungu akukutetezani ndi mphamvu yake chifukwa muli ndi chikhulupiriro. Mulungu akukutetezani kuti mudzalandire chipulumutso, ndipo chipulumutso chimenechi chidzaonekera mu nthawi ya mapeto.” (1 Pet. 1:5) Mfundo imeneyi imagwira ntchito kwa Akhristu onse ndipo aliyense wa ife ayenera kuimvetsa. Tikutero chifukwa chakuti tonsefe timafuna kuti Mulungu atithandize kukhalabe okhulupirika kwa iye.

AMATITHANDIZA KUTI TISALOWERE NJIRA YOLAKWIKA

8. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kuti tisalowere njira yolakwika?

8 Mavuto amene timakumana nawo komanso kupanda ungwiro kwathu zingachititse kuti tisokonezeke mwauzimu. Kenako tikhoza kuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira. (Werengani Agalatiya 6:1.) Chitsanzo pa nkhani imeneyi ndi zimene zinachitikira Davide.

9, 10. Kodi Yehova anathandiza bwanji Davide kuti asalowere njira yolakwika ndipo amatithandiza bwanji masiku ano?

9 Pa nthawi imene ankasakidwa ndi Sauli, Davide anadziletsa kwambiri ndipo sanabwezere mfumu yansanjeyi. (1 Sam. 24:2-7) Koma patangopita nthawi yochepa, analephera kudziletsa. Iye ankafuna thandizo la chakudya cha anthu ake. Choncho anapita mwaulemu kukapempha kwa Nabala, yemwe anali Mwisiraeli mnzake. Nabala atayankha zachipongwe, Davide anakwiya kwambiri n’kukonza zoti akaphe Nabala ndi amuna onse a m’nyumba yake. Iye anaiwala kuti ngati atapha anthu osalakwa, adzakhala ndi mlandu wamagazi pa maso pa Mulungu. Abigayeli, yemwe anali mkazi wa Nabala, akanapanda kuchitapo kanthu Davide akanachimwa koopsa. Davide atazindikira zoti Yehova ndi amene wamuthandiza, anauza Abigayeli kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene wakutumiza kudzakumana nane lero! Iwenso udalitsike chifukwa cha kulingalira bwino kwako. Udalitsike chifukwa cha kundigwira lero kuti ndisapalamule mlandu wamagazi ndi kudzipulumutsa ndekha ndi dzanja langa.”​—1 Sam. 25:9-13, 21, 22, 32, 33.

10 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi? Yehova anagwiritsa ntchito Abigayeli pofuna kuthandiza Davide kuti asayambe kulowera njira yolakwika. Ndi mmene amachitiranso ndi ife masiku ano. Koma sikuti tiziyembekezera kuti Mulungu azitumiza munthu kudzatichenjeza nthawi iliyonse imene tatsala pang’ono kulakwitsa zinazake. Tisaganizenso kuti tingadziwe zimene Mulungu angachite pa nkhani iliyonse kapena zimene angalole kuti zichitike pokwaniritsa cholinga chake. (Mlal. 11:5) Ngakhale zili choncho, sitiyenera kukayikira zoti nthawi zonse Yehova amaona zimene zikutichitikira ndipo adzatithandiza kukhalabe okhulupirika kwa iye. Iye amatilonjeza kuti: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo. Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.” (Sal. 32:8) Kodi Yehova amatilangiza bwanji? Kodi tingatani kuti tipindule ndi malangizo ake? Nanga n’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira zoti Yehova akutsogolera anthu ake masiku ano? Tiyeni tipeze mayankho a mafunso amenewa m’buku la Chivumbulutso.

AMATITETEZA POTIPATSA MALANGIZO

11. Kodi Yehova amadziwa zinthu ziti zokhudza mipingo ya anthu ake?

11 Masomphenya amene ali m’chaputala 2 ndi 3 cha buku la Chivumbulutso amasonyeza Yesu Khristu monga Mfumu akuyendera mipingo 7 ya ku Asia Minor. Masomphenyawa amasonyeza kuti Khristu ankaona zinthu zenizeni zimene zinkachitika m’mipingoyo. M’mipingo ina iye ankatchula ngakhale mayina a anthu. Mpingo uliwonse ankauyamikira pa zimene ukuchita bwino kapena kupereka malangizo oyenera. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Pa kukwaniritsidwa kwa masomphenyawa, mipingo 7 ikuimira Akhristu odzozedwa kuyambira mu 1914 koma malangizo amene anaperekedwa ku mipingo imeneyi amagwira ntchito ku mipingo yonse ya anthu a Mulungu masiku ano. Choncho tikhoza kunena kuti Yehova akutsogolera anthu ake pogwiritsa ntchito Mwana wake. Kodi tingalole bwanji kuti Yehova azititsogolera?

12. Kodi tingalole bwanji Yehova kutitsogolera?

12 Kuphunzira Baibulo patokha ndi njira imodzi imene ingathandize kuti Yehova azititsogolera. Yehova amatipatsa malangizo ambiri ochokera m’Malemba kudzera m’mabuku ofalitsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. (Mat. 24:45) Kuti tipindule ndi malangizowa tiyenera kuphunzira mwakhama komanso kugwiritsa ntchito zimene taphunzirazo. Kuphunzira Baibulo patokha ndi njira imodzi imene Yehova ‘amatitetezera kuti tisapunthwe.’ (Yuda 24) Kodi munaphunzirapo zinthu zina m’mabuku athu zimene zinkaoneka ngati alembera inuyo? Muyenera kulandira malangizowo monga ochokera kwa Yehova. Nthawi zina, mnzathu amatikodola paphewa kuti atiuze zinazake. Nayenso Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake kuti atiuze zinazake zimene tiyenera kusintha pa khalidwe kapena zochita zathu. Tikamamvera zimene mzimu woyera ukutiuza ndiye kuti tikulola Yehova kutitsogolera. (Werengani Salimo 139:23, 24.) Choncho tiyeni tione ngati timachita khama kuphunzira Baibulo.

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira mozama Mawu a Mulungu?

13 Kugwiritsa ntchito nthawi yambiri kuchita zosangalatsa kungatiwonongere nthawi yophunzira Baibulo patokha. M’bale wina anati: “N’zosavuta kulephera kuphunzira Baibulo. Masiku ano, zosangalatsa zimapezeka mosavuta ndipo n’zotchipa kusiyana ndi kale. Zimapezeka pa TV, pa kompyuta, pa foni, tingoti paliponse.” Ngati sitisamala, tikhoza kusiya kuphunzira mozama mwapang’onopang’ono mpaka kusiyiratu. (Aef. 5:15-17) Aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndi kangati pamene ndimaphunzira mozama Mawu a Mulungu? Kodi ndimangochita zimenezi ndikapatsidwa nkhani yoti ndikonzekere?’ Ngati zili choncho, tiyenera kusintha n’kumagwiritsa ntchito nthawi ya kulambira kwa pabanja kapena yophunzira Baibulo patokha kuti tizifufuza nzeru za Yehova ngati mmene tingachitire pofufuza chuma chamtengo wapatali. Nzeru zimenezi zingatithandize kuti tidzapulumuke.​—Miy. 2:1-5.

AKATILIMBIKITSA TIMATHA KUPIRIRA

14. Kodi Malemba amasonyeza bwanji kuti Yehova amadziwa mmene timamvera mumtima mwathu?

14 Davide anakumana ndi mavuto ambiri pa moyo wake. (1 Sam. 30:3-6) Mawu ake ouziridwa amasonyeza kuti Yehova ankadziwa mmene Davide ankamvera. (Werengani Salimo 34:18; 56:8.) Mulungu amadziwanso mmene ife timamvera. Iye amatiyandikira tikakhala ndi “mtima wosweka” kapena ‘tikamadzimvera chisoni mumtima.’ Zimenezi zingatilimbikitse ngati mmene zinalimbikitsira Davide. Iye anaimba kuti: “Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha, pakuti mwaona kusautsika kwanga. Mwadziwa zowawa zimene zandigwera.” (Sal. 31:7) Koma sikuti Yehova amangoona pamene tikuvutika n’kusiyira pomwepo. Iye amatitonthoza ndiponso kutilimbikitsa kuti tipirire. Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndi kudzera m’misonkhano yachikhristu.

15. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Asafu?

15 Ubwino wopezeka pa misonkhano umaonekera pa zimene zinachitikira wamasalimo Asafu. Kuganizira kwambiri zinthu zopanda chilungamo kunachititsa Asafu kuona kuti kutumikira Mulungu n’kosathandiza kwenikweni. Asafu anakhumudwa kwambiri ndipo anafotokoza kuti: “Mtima unandipweteka ndipo ndinamva ululu mu impso zanga.” Iye anangotsala pang’ono kusiya kutumikira Yehova. N’chiyani chinamuthandiza kuti ayambenso kuona zinthu moyenera? Iye anati: “Ndinalowa m’malo opatulika aulemerero a Mulungu.” Atakhala pakati pa atumiki a Yehova anzake, m’pamene anayambanso kuona zinthu moyenera. Anazindikira kuti chisangalalo cha anthu oipa n’chakanthawi ndipo Yehova adzakonza zinthu. (Sal. 73:2, 13-22) N’chimodzimodzi ndi ifeyo. Tikhoza kufooka chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene timaona m’dziko la Satanali. Kusonkhana ndi abale athu kumatitsitsimula ndiponso kumatithandiza kuti tizitumikira Yehova mosangalala.

16. Kodi chitsanzo cha Hana chingatithandize bwanji?

16 Koma bwanji ngati zinthu zina mu mpingo zikuchititsa kuti muzivutika kupezeka pa misonkhano? Tinene kuti mukuchita manyazi chifukwa chakuti mwaimitsidwa pa udindo mu mpingo kapena mwasemphana maganizo ndi m’bale kapena mlongo. Ngati zili choncho, chitsanzo cha Hana chingakuthandizeni. (Werengani 1 Samueli 1:4-8.) Iye ankavutika kwambiri mumtima chifukwa cha mkazi mnzake dzina lake Penina. Zinthu zinkaipa kwambiri ikafika nthawi yokapereka nsembe kwa Yehova ku Silo. Zinkamupweteka kwambiri Hana moti “anali kulira ndiponso sankadya.” Koma sanalole kuti izi zimulepheretse kupita kukalambira Yehova. Yehova anaona kukhulupirika kwake ndipo anamudalitsa.​—1 Sam. 1:11, 20.

17, 18. (a) Kodi timalimbikitsidwa bwanji pa misonkhano ya mpingo? (b) Kodi mumamva bwanji mukaganizira zimene Yehova amachita potisamalira mwachikondi kuti tidzapulumuke?

17 Akhristu masiku ano angachite bwino kutsanzira Hana pa nkhani yopezeka pa misonkhano nthawi zonse. Monga tikudziwira, misonkhano imatilimbikitsa kwambiri. (Aheb. 10:24, 25) Mwachitsanzo, pa misonkhano timaona chikondi cha abale ndi alongo athu ndipo timalimbikitsidwa. Komanso mfundo inayake m’nkhani kapena ndemanga ingatifike pamtima. Apo ayi, pocheza ndi anzathu misonkhano isanayambe kapena itatha, Mkhristu mnzathu akhoza kumvetsera mavuto athu kapena kutiuza mawu olimbikitsa. (Miy. 15:23; 17:17) Ndiponso tikamaimbira Yehova nyimbo, timasangalala. Makamaka tikamavutika ndi “malingaliro osautsa” timafuna kwambiri kulimbikitsidwa pa misonkhano. Kumeneko Yehova amatilimbikitsa ndi ‘mawu ake otonthoza’ n’kutithandiza kuti tikhalebe okhulupirika.​—Sal. 94:18, 19.

18 Popeza Mulungu amatisamalira mwachikondi, timamva ngati wamasalimo Asafu, yemwe anaimbira Yehova kuti: “Mwandigwira dzanja langa lamanja. Mudzanditsogolera ndi malangizo anu.” (Sal. 73:23, 24) Timayamikira kwambiri kuti Yehova amatiteteza kuti tidzapulumuke.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 28]

Inunso Yehova anakukokani

[Chithunzi patsamba 30]

Timatetezedwa tikamagwiritsa ntchito malangizo a Mulungu

[Chithunzi patsamba 31]

Tikamalimbikitsidwa timatha kupirira