Tiziona Kuti Kutumikira Yehova Ndi Chinthu Chofunika Kwambiri
Tiziona Kuti Kutumikira Yehova Ndi Chinthu Chofunika Kwambiri
“Zinthu zilizonse . . . zofunika kwambiri, . . . pitirizani kuganizira zimenezi.”—AFIL. 4:8.
1, 2. Kodi n’chiyani chimachititsa anthu ambiri kukhala ndi mtima wongofuna kusangalala, nanga ndi mafunso ati amene tingadzifunse?
M’DZIKOLI tikukumana ndi mavuto aakulu ndiponso oopsa kuposa kale lonse. Anthu omwe si olimba mwauzimu angavutike kwambiri kuti apirire mavuto amene timakumana nawo “m’nthawi yapadera komanso yovuta” ino. (2 Tim. 3:1-5) Anthu oterewa amayesa kulimbana ndi mavutowa mwa mphamvu zawo zokha koma nthawi zambiri amalephera. Anthu ambiri amangokhalira kufunafuna zosangalatsa n’cholinga chofuna kuiwala mavuto awo.
2 Pofuna kuchepetsa nkhawa, anthu ambiri amaona kuti chofunika n’kumangochita zosangalatsa. Ngati Akhristu sangasamale akhoza kutengeka ndi moyo umenewu. Ndiyeno kodi tingapewe bwanji zimenezi? Kodi tiyenera kupeweratu zosangalatsa zilizonse? Kodi tingatani kuti tizikwaniritsa maudindo athu komanso kuchita zosangalatsa mosapitirira malire? Kodi ndi mfundo za m’Malemba ziti zimene zingatithandize kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani imeneyi?
Kudziwa Zofunika Kwambiri M’dziko Lokonda Zosangalatsa
3, 4. Kodi Malemba amatithandiza bwanji kumvetsa ubwino wozindikira zinthu zofunika kwambiri?
3 Anthu ambiri m’dzikoli ali ndi mtima ‘wokonda zosangalatsa.’ (2 Tim. 3:4) Mtima umenewu ukhoza kutisokoneza mwauzimu. (Miy. 21:17) N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba malangizo okhudza kukhala oganiza bwino ndiponso opanda chibwana m’kalata yake yopita kwa Timoteyo ndi Tito. Kutsatira malangizo amenewa kungatithandize kupewa mtima umene anthu ambiri ali nawo m’dzikoli.—Werengani 1 Timoteyo 2:1, 2; Tito 2:2-8.
4 Zaka zambiri Paulo asanalembe makalata amenewa, Solomo analemba za ubwino wosiya zinthu zosangalatsa nthawi zina n’cholinga choti tichite zinthu zofunika kwambiri. (Mlal. 3:4; 7:2-4) Popeza moyo ndi waufupi, ndi bwino ‘kuyesetsa mwamphamvu’ kuti tidzapulumuke. (Luka 13:24) Choncho tiyenera kupitiriza kuganizira zinthu zilizonse “zofunika kwambiri.” (Afil. 4:8, 9) Izi zikutanthauza kuti tiyenera kuganizira mofatsa za mbali iliyonse ya moyo wathu wachikhristu.
5. Kodi ndi nkhani iti imene tiyenera kuiona kuti ndi yofunika kwambiri?
5 Potengera chitsanzo cha Yehova ndi Yesu, Akhristu amaona kuti kugwira ntchito mwakhama ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri. (Yoh. 5:17) Izi zimachititsa kuti aziyamikiridwa chifukwa cha khama ndiponso kudalirika kwawo pa ntchito. Makamaka mitu ya mabanja imaona kuti kugwira ntchito mwakhama pofuna kusamalira banja lawo n’kofunika kwambiri. Pajatu munthu amene sasamalira banja kwenikweni akukana Yehova.—1 Tim. 5:8.
Tiziona Kulambira Kwathu Kukhala Kofunika Komanso Kosangalatsa
6. Kodi tikudziwa bwanji kuti tiyenera kuona kulambira Yehova kukhala nkhani yofunika kwambiri?
6 Kuyambira kale, Yehova amaona kuti kulambira koona ndi nkhani yofunika kwambiri. Mwachitsanzo, pa nthawi imene Chilamulo cha Yos. 23:12, 13) Akhristu oyambirira ankayesetsa mwakhama kuti kulambira koona kusasokonezedwe ndi ziphunzitso ndiponso maganizo opotoka. (2 Yoh. 7-11; Chiv. 2:14-16) Masiku anonso, Akhristu oona amaona kuti kulambira Mulungu ndi nkhani yofunika kwambiri.—1 Tim. 6:20.
Mose chinkagwira ntchito, Aisiraeli ankakumana ndi zovuta kwambiri akasiya kulambira Yehova m’njira yoyenera. (7. Kodi Paulo ankakonzekera bwanji utumiki wake?
7 Utumiki wathu wakumunda ndi wosangalatsa kwambiri. Koma kuti tipitirize kusangalala nawo tiyenera kuuona kuti ndi wofunika kwambiri ndiponso kukonzekera bwino. Paulo anafotokoza zimene ankachita poganizira anthu amene ankawaphunzitsa. Iye analemba kuti: “Ndakhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana, kuti mulimonse mmene zingakhalire ndipulumutseko ena. Koma ndikuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndiugawirenso kwa ena.” (1 Akor. 9:22, 23) Paulo ankasangalala kwambiri kuthandiza anthu mwauzimu ndipo ankaganizira mmene angathandizire anthu osiyanasiyana amene ankawaphunzitsa. Izi zinathandiza kuti awalimbikitse ndiponso kuti awathandize kukhala ndi mtima wofuna kulambira Yehova.
8. (a) Kodi tiyenera kuona bwanji anthu amene timawaphunzitsa mu utumiki wathu? (b) Kodi kuchititsa phunziro la Baibulo kungatithandize bwanji kuti tizisangalala ndi utumiki?
8 Kodi Paulo ankaona bwanji utumiki wake? Iye ankafunitsitsa ‘kutumikira Yehova monga kapolo’ ndiponso kukhala kapolo wa anthu onse amene ankamvetsera uthenga wa choonadi. (Aroma 12:11; 1 Akor. 9:19) Tikamaphunzitsa Mawu a Mulungu pa phunziro la Baibulo la panyumba, pa misonkhano yachikhristu kapena pa Kulambira kwa Pabanja, kodi timazindikira udindo wathu kwa anthu amene tikuwaphunzitsawo? Zikhoza kutheka kumaona kuti kukhala ndi phunziro la Baibulo ndi udindo waukulu moti sitingakwanitse. N’zoona kuti tikamachititsa phunziro la Baibulo timafunika kusiya kaye kuchita zinthu zathuzathu n’kugwiritsa ntchito nthawi imeneyo kuti tithandize ena. Komatu kuchita zimenezi ndiko kupatsa kumene Yesu ankatanthauza pamene ananena kuti “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Ntchito yophunzitsa anthu za njira yopezera chipulumutso imabweretsa chimwemwe kuposa ntchito ina iliyonse.
9, 10. (a) Kodi kuzindikira zinthu zofunika kwambiri kumatanthauza kuti sitingacheze ndi anzathu n’kumasangalala? Fotokozani. (b) Kodi n’chiyani chingathandize mkulu kukhala wolimbikitsa ndiponso wochezeka?
9 Kuzindikira zinthu zofunika kwambiri sikutanthauza kuti sitingacheze ndi anzathu n’kumasangalala. Yesu anali chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yopatula nthawi yoti aphunzitse anthu. Koma ankapezanso nthawi yoti acheze momasuka ndi anthu ena n’kukhala nawo pa ubwenzi wabwino. (Luka 5:27-29; Yoh. 12:1, 2) Kuzindikira zinthu zofunika kwambiri sikutanthauzanso kuti tizingokhala osamasuka ndiponso osaseka ndi anthu. Yesu akanakhala wokhwimitsa zinthu komanso wosaseka ndi anthu si bwenzi anthu akumasuka naye. Koma ngakhale ana ankamasuka naye. (Maliko 10:13-16) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani imeneyi?
10 Ponena za mkulu wina, m’bale wina ananena kuti, “Amene uja ndi munthu woti amayesetsa kuchita bwino zinthu koma sayembekezera anthu ena kuchita zinthu mwangwiro.” Kodi anthu ena anganene zimenezi pofotokoza za inuyo? Si kulakwa kuyembekezera kuti anthu ena achite zinthu mwa njira inayake. Mwachitsanzo, ana amalimbikitsidwa ngati makolo awo amayembekezera kuti anawo achite zinazake ndiponso ngati amawathandiza kuchita zinthuzo. Izi n’zimenenso zimachitika mu mpingo. Akulu amatha kulimbikitsa anthu kuti apite patsogolo mwauzimu n’kuwafotokozera zimene zingawathandize kuti achite zimenezi. Mkulu akamadziona moyenerera, amathadi kulimbikitsa anthu ndipo anthuwo amamasuka naye. (Aroma 12:3) Mlongo wina ananena kuti: “Sindisangalala mkulu akamangoona nkhani iliyonse mwanthabwala. Koma akakhalanso wosachezeka kapena wosaseka ndi anthu, zimakhala zovuta kumasuka naye.” Mlongo wina ananena kuti akulu ena “amakhala oopsa chifukwa chakuti amangooneka okwiya.” Khalidwe kapena zochita za akulu siziyenera kuchititsa anthu kuiwala mfundo yakuti kulambira Yehova, yemwe ndi “Mulungu wa chisangalalo,” n’kosangalatsa.—1 Tim. 1:11.
Landirani Udindo mu Mpingo
11. Kodi m’bale angachite chiyani ‘poyesetsa kuti akhale woyang’anira’ mu mpingo?
11 Pamene Paulo analimbikitsa amuna kuti ayesetse kukhala ndi udindo mu mpingo, sanatanthauze kuti achite zimenezi ndi cholinga choti atchuke kapena akhale apamwamba. M’malomwake analemba kuti: “Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anira, akufuna ntchito yabwino.” (1 Tim. 3:1, 4) M’bale amene “akuyesetsa kuti akhale woyang’anira” amafunika kukhala ndi mtima wofunitsitsa kugwira ntchito mwakhama kuti akhale ndi makhalidwe auzimu. Amachita zimenezi n’cholinga choti atumikire abale ake. Ngati m’bale watha chaka chimodzi kuchokera pamene anabatizidwa ndipo akukwaniritsa ziyeneretso za m’Malemba za atumiki othandiza zimene zafotokozedwa pa 1 Timoteyo 3:8-13, akulu akhoza kuvomereza kuti aikidwe pa udindowu. Onani kuti vesi 8 ikunena mwachindunji kuti, “nawonso atumiki othandiza akhale opanda chibwana,” kapena kuti ozindikira zinthu zofunika kwambiri.
12, 13. Fotokozani zimene abale achinyamata angachite poyesetsa kuti akhale ndi udindo.
12 Kodi ndinu m’bale wobatizidwa wa zaka za m’ma 17 kapena 18 ndipo mumaona kuti kulambira Yehova ndi nkhani yofunika kwambiri? Ngati zili choncho, pali zinthu zingapo zimene mungachite poyesetsa kuti mukhale ndi udindo mu mpingo. Chinthu chimodzi ndi kuchita khama kwambiri mu utumiki wakumunda. Kodi mumakonda kulowa mu utumiki ndi abale ndi alongo a misinkhu yosiyanasiyana? Kodi mukuyesetsa kuti mupeze munthu amene mungaphunzire naye Baibulo? Mukamachititsa phunziro la Baibulo motsatira malangizo amene timapatsidwa pa misonkhano yachikhristu, mudzatha kuphunzitsa anthu mwaluso njira za Yehova. Mudzayambanso kuchita zinthu mowaganizira kwambiri ndiponso mwachifundo. Wophunzira wanu akayamba kuzindikira kufunika kosintha zinthu pa moyo wake, mudzadziwa mmene mungamuthandizire moleza mtima ndiponso mwaluso kuti atsatire mfundo za m’Baibulo.
13 Abale achinyamatanu mungachite bwino kuthandiza achikulire mu mpingo m’njira iliyonse imene mungakwanitse. Mungachitenso bwino kuganizira za mmene Nyumba ya Ufumu ikuonekera n’kuthandiza kuti nthawi zonse izioneka mwaukhondo. Mukamayesetsa kuthandiza mu mpingo m’njira iliyonse imene mungakwanitse, mtima wanu wodziperekawu umasonyeza kuti mumaona kutumikira Yehova kukhala kofunika kwambiri. Mofanana ndi Timoteyo, mungaphunzire kusamaladi moona mtima zinthu zofunika zokhudza mpingo.—Werengani Afilipi 2:19-22.
14. Kodi abale achinyamata angayesedwe bwanji “ngati ali oyenerera” kupatsidwa udindo mu mpingo?
14 Akulu, muzipereka ntchito kwa abale achinyamata amene akuyesetsa ‘kuthawa zilakolako zaunyamata’ ndiponso kutsatira “chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, ndi mtendere” komanso makhalidwe ena ofunika kwambiri. (2 Tim. 2:22) Kupatsa achinyamatawo ntchito zina mu mpingo kumapereka mpata woti “ayesedwe kaye ngati ali oyenerera” kukhala ndi udindo. Kuchita zimenezi kungathandize kuti ‘anthu onse aone kuti akupita patsogolo.’—1 Tim. 3:10; 4:15.
Kuzindikira Zinthu Zofunika mu Mpingo Ndiponso M’banja
15. Mogwirizana ndi 1 Timoteyo 5:1, 2, kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza ena?
15 Munthu wozindikira zinthu zofunika kwambiri amalemekezanso abale ndi alongo. M’malangizo ake opita kwa Timoteyo, Paulo anasonyeza kuti tiyenera kulemekeza anthu ena. (Werengani 1 Timoteyo 5:1, 2.) Izi ndi zofunika kwambiri ngati tikuchita zinthu zina ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzathu. Pa nkhani yolemekeza akazi, makamaka amene tili nawo m’banja, tiyenera kutengera chitsanzo cha Yobu. Iye ankayesetsa kuti asamayang’ane mosirira akazi ena. (Yobu 31:1) Kulemekeza abale ndi alongo athu kumathandiza kuti tisamakopane nawo kapena kuwachititsa kuti azimangika akakhala nafe. Kulemekezana n’kofunika kwambiri makamaka kwa anthu amene ali pa chibwenzi ndipo akuyembekeza kuti adzakwatirane. Mkhristu waulemu sangayambe kukopa munthu wina alibe cholinga chodzakwatirana naye.—Miy. 12:22.
16. Kodi zimene Baibulo limanena zokhudza udindo wa mwamuna kapena bambo zimasiyana bwanji ndi maganizo amene anthu ena ali nawo m’dzikoli?
16 Tiyenera kusamala kuti tisasiye kuona udindo umene Mulungu watipatsa m’banja kukhala wofunika kwambiri. Satana akusokoneza maganizo a anthu n’cholinga choti asamaone moyenera udindo wa mwamuna kapena bambo m’banja. Mafilimu, mapulogalamu a pa TV ndiponso zosangalatsa zina zimanyoza amuna ndipo zimachititsa kuti anthu asamalemekeze mutu wa banja. Koma Malemba amasonyeza kuti mwamuna ndi “mutu wa mkazi” ndipo uwu ndi udindo waukulu kwambiri.—Aef. 5:23; 1 Akor. 11:3.
17. Kodi zimene timachita pa nkhani ya Kulambira kwa Pabanja zimasonyeza bwanji kuti timaona udindo wathu m’banja kukhala wofunika?
17 Amuna ena amapezera banja lawo zinthu zakuthupi koma osalisamalira mwauzimu. Kuchita zimenezi n’kupanda nzeru. (Deut. 6:6, 7) N’chifukwa chake lemba la 1 Timoteyo 3:4 limanena kuti ngati mwamuna, yemwe ndi mutu wa banja, akuyesetsa kuti akhale ndi udindo mu mpingo, ayenera kukhala “woyang’anira bwino banja lake. Wa ana omumvera ndi mtima wonse.” Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimapatula nthawi ya Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse?’ N’zomvetsa chisoni kuti amuna ena amachita kuchondereredwa ndi akazi awo kuti azitsogolera pa zinthu zauzimu. Mwamuna aliyense angachite bwino kuganizira mofatsa ngati akukwaniritsa bwino udindo wake. Nayenso mkazi wachikhristu ayenera kuthandiza mwamuna wake kuti Kulambira kwa Pabanja kuzichitika bwinobwino.
18. Kodi ana angaphunzire bwanji kuzindikira zinthu zofunika?
18 Ananso amalimbikitsidwa kuti azizindikira zinthu zofunika kwambiri pa moyo. (Mlal. 12:1) Si nkhanza kuphunzitsa ana kuti azigwira ntchito mwakhama. Akhoza kumagwira ntchito za pakhomo zimene angakwanitse komanso zimene ndi zogwirizana ndi msinkhu wawo. (Maliro 3:27) Mfumu Davide anaphunzira kukhala m’busa wabwino ali mnyamata. Iye anaphunziranso kupeka ndi kuimba nyimbo ndipo izi zinachititsa kuti adzakatumikire kwa mfumu ya Isiraeli. (1 Sam. 16:11, 12, 18-21) N’zosakayikitsa kuti Davide ali mwana ankasewera koma anaphunziranso maluso amene anadzawagwiritsa ntchito potamanda Yehova. Maluso amene anaphunzira ku ubusa anamuthandiza kutsogolera mtundu wa Isiraeli moleza mtima. Kodi ananu, ndi maluso ati amene mukuphunzira omwe angadzakuthandizeni kutumikira Mlengi ndiponso kukonzekera maudindo anu a m’tsogolo?
Tizikhala ndi Maganizo Oyenera
19, 20. Kodi inuyo mukufunitsitsa kudziona motani ndiponso kukhala ndi maganizo otani pa nkhani ya kulambira Mulungu?
19 Tonsefe tiyenera kuyesetsa kudziona moyenerera ndiponso kukhala omasuka ndi anthu ena. Ndi bwino kupewa kukhala “wolungama mopitirira muyezo.” (Mlal. 7:16) Kukhala omasuka ndiponso ochezeka kungathandize pamene zinthu zavuta kunyumba, kuntchito kapena pochita zinthu ndi abale ndi alongo athu. M’banja aliyense ayenera kusamala kuti asamangotsutsa anzake chifukwa zimenezi zimasokoneza mtendere. Anthu onse mu mpingo angachite bwino kukhala omasuka ndiponso ochezeka. Iwo ayenera kuonetsetsa kuti zokambirana zawo ndiponso kaphunzitsidwe kawo ndi zolimbikitsa.—2 Akor. 13:10; Aef. 4:29.
20 Tikukhala m’dziko limene anthu saganizira za Yehova ndiponso saona kuti malamulo ake ndi ofunika. Koma anthu a Yehova amaona kuti kumvera ndiponso kukhala okhulupirika kwa Mulungu ndi kofunika kwambiri. N’zosangalatsa kwambiri kukhala m’gulu lalikulu la anthu amene amaona kuti kulambira Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri. Tiyeni tiziyesetsabe kukhala ndi maganizo oyenerera ndiponso kuona kulambira kwathu kukhala kofunika kwambiri.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa mtima wokonda kwambiri zosangalatsa umene wafala m’dzikoli?
• Kodi tingatani kuti tiziona utumiki wathu kukhala wosangalatsa komanso wofunika kwambiri?
• Kodi kuyesetsa kuti tikhale ndi udindo mu mpingo kumasonyeza bwanji kuti timazindikira zinthu zofunika kwambiri?
• N’chifukwa chiyani kulemekeza anthu mu mpingo ndiponso m’banja n’kofunika kwambiri?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 12]
Mwamuna ayenera kusamalira banja lake mwakuthupi ndiponso mwauzimu