Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalanibe Tcheru Ngati Yeremiya

Khalanibe Tcheru Ngati Yeremiya

Khalanibe Tcheru Ngati Yeremiya

“[Ine Yehova] ndikhalabe wogalamuka kuti ndikwaniritse mawu anga.”​—YER. 1:12.

1, 2. N’chifukwa chiyani ‘kugalamuka’ kwa Yehova kukuyerekezeredwa ndi mtengo wa amondi?

M’MWEZI wa January ndi February ku Lebanon ndi ku Israel kumakhala kozizira. Nthawi imeneyi mitengo sichita maluwa koma mtengo wa amondi umachita maluwa. Maluwa ake amakhala apinki kapena oyera ndipo amakhala okongola kwambiri. Mtengo wa amondi ndi umodzi mwa mitengo imene imachita maluwa nyengo yotentha isanayambe. Choncho n’chifukwa chake m’Chiheberi dzina la mtengowu limatanthauza “wogalamuka.”

2 Pamene Yehova anaika Yeremiya kukhala mneneri wake, anayerekezera zimene mtengo wa amondi umachita pofotokoza mfundo yofunika kwambiri. Pa nthawi imene ankayamba utumiki wake, Mulungu anaonetsa mneneriyu masomphenya a mphukira ya mtengo umenewu. Kodi zimenezi zinatanthauza chiyani? Yehova anafotokoza kuti: “Ndikhalabe wogalamuka kuti ndikwaniritse mawu anga.” (Yer. 1:11, 12) Mofanana ndi mtengo wa amondi, umene tingati ndi “wogalamuka” chifukwa chochita maluwa msanga, Yehova mophiphiritsira anali “kudzuka m’mawa kwambiri” kuti atumize aneneri ake kukachenjeza anthu za kuopsa kwa kusamvera kwawo. (Yer. 7:25) Iye sankapuma, kapena kuti ‘ankakhalabe wogalamuka,’ mpaka pamene mawu ake aulosi anakwaniritsidwa. Ndipo pa nthawi yake yeniyeni, mu 607 B.C.E., Yehova anapereka chiweruzo pa mtundu wa Yuda womwe unali wampatuko.

3. Kodi ndi mfundo iti yokhudza Yehova imene sitiyenera kukayikira?

3 Masiku anonso Yehova ndi wogalamuka, kapena kuti ali tcheru, kuti akwaniritse cholinga chake. N’zosatheka kuti alephere kukwaniritsa mawu ake. Kodi mfundo yakuti Yehova ali tcheru ingakuthandizeni bwanji? Kodi mukukhulupirira kuti chaka chino cha 2011, Yehova ndi “wogalamuka” kuti akwaniritse malonjezo ake? Ngati timakayikira ngakhale pang’ono za malonjezo odalirika a Yehova, ino ndi nthawi yoti tisiye kuodzera mwauzimu. (Aroma 13:11) Potumikira monga mneneri wa Yehova, Yeremiya anakhalabe tcheru. Kupenda zimene zinathandiza Yeremiya ndiponso chifukwa chimene anapitirizirabe kukhala tcheru pa ntchito imene Mulungu anamupatsa kungatithandize kuona zimene tingachite kuti tipitirize kugwira ntchito imene Yehova watipatsa.

Uthenga Wofunika Kulengezedwa Mwachangu

4. Kodi Yeremiya anakumana ndi mavuto ati polengeza uthenga wake, nanga n’chifukwa chiyani anafunika kuulengeza mwachangu?

4 Yeremiya ayenera kuti anali ndi zaka pafupifupi 25 pa nthawi imene Yehova anamupatsa ntchito ya ulonda. (Yer. 1:1, 2) Koma iye ankadziona kuti ndi mwana ndiponso kuti sakanatha kulankhula kwa akulu a mtunduwo, amene anali achikulire ndiponso audindo. (Yer. 1:6) Iye anafunika kutsutsa mwamphamvu komanso kulengeza ziweruzo zoopsa. Anafunika kuchita zimenezi makamaka kwa ansembe, aneneri onyenga, olamulira ndiponso anthu amene ankangotsatira ‘njira imene anthu ambiri ankatsatira’ komanso kwa amene anakhalabe “osakhulupirika kwa nthawi yaitali.” (Yer. 6:13; 8:5, 6) Kachisi wokongola wa Mfumu Solomo, amene anali chimake cha kulambira koona kwa zaka pafupifupi 400, anali kudzawonongedwa. Yerusalemu ndi Yuda anali kudzakhala bwinja ndipo anthu ake anali kudzatengedwa kupita ku ukapolo. Apa n’zachidziwikire kuti Yeremiya anapatsidwa uthenga wofunika kulengezedwa mwachangu.

5, 6. (a) Kodi Yehova akugwiritsa ntchito bwanji Akhristu odzozedwa masiku ano? (b) Kodi m’nkhani ino tikambirana za chiyani kwenikweni?

5 Masiku ano, Yehova wapereka gulu la Akhristu odzozedwa amene ali ngati alonda kuti achenjeze anthu zoti Mulungu adzapereka chiweruzo pa dzikoli. Iye wachita zimenezi chifukwa chokonda anthu. Kwa zaka zambiri, odzozedwa amenewa, omwe akugwira ntchito yofanana ndi ya Yeremiya, akhala akuchenjeza anthu za nthawi imene tikukhalamoyi. (Yer. 6:17) Baibulo limatsindika mfundo yakuti Yehova amasunga nthawi yochitira zimene wakonza ndipo sachedwa. Tsiku lake lidzafika pa nthawi yeniyeni, koma pa ola limene anthu sakuyembekezera.​—Zef. 3:8; Maliko 13:33; 2 Pet. 3:9, 10.

6 Tizikumbukira kuti Yehova ndi wogalamuka ndiponso kuti adzabweretsa dziko lake lolungama pa nthawi yake yeniyeni. Kudziwa zimenezi kuyenera kulimbikitsa odzozedwa kupitiriza ntchito yawo. Anzawo a nkhosa zina amalimbikitsidwanso kukhala tcheru pa ntchito yawo yolengeza uthenga wawo mwachangu. Kodi zimenezi ziyenera kutikhudza bwanji? Yesu analimbikitsa aliyense kusonyeza kuti ali ku mbali ya Ufumu wa Mulungu. Choncho tiyenera kuchita khama pa ntchito yolalikira kuti tithandize anthu kuchita zimenezi. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene zinathandiza Yeremiya kukhala tcheru pa ntchito yake ndiponso zimene zingatithandize ifeyo.

Ankakonda Anthu

7. Kodi chikondi chinalimbikitsa bwanji Yeremiya kulalikirabe ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto?

7 Kodi n’chiyani chinalimbikitsa Yeremiya kulalikirabe ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto? Iye ankakonda anthu. Yeremiya ankadziwa kuti abusa achinyengo ndi amene ankayambitsa mavuto amene anthu ankakumana nawo. (Yer. 23:1, 2) Kudziwa zimenezi kunamuthandiza kugwira ntchito yake mwachikondi ndiponso mwachifundo. Iye ankafuna kuti anthu a m’dziko lake amve mawu a Mulungu n’kukhala ndi moyo. Iye ankawadera nkhawa kwambiri moti analira poganizira tsoka limene anali kudzakumana nalo. (Werengani Yeremiya 8:21; 9:1.) Buku la Maliro limasonyeza bwino kuti Yeremiya ankakonda kwambiri ndiponso kuganizira dzina la Yehova komanso anthu ake. (Maliro 4:6, 9) Mukaona anthu masiku ano ali “onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa,” kodi simulakalaka kuwauza uthenga wolimbikitsa wa Ufumu wa Mulungu?​—Mat. 9:36.

8. N’chiyani chikusonyeza kuti Yeremiya sankangokhala wokwiya chifukwa chozunzidwa?

8 Yeremiya anazunzidwa ndi anthu amene ankafuna kuwathandiza koma sanabwezere kapena kukhala wokwiya. Iye anali woleza mtima ndiponso wokoma mtima ngakhale kwa Mfumu Zedekiya yomwe inali yoipa. Zedekiya atamupereka kwa anthu kuti amuphe, Yeremiya anachondererabe mfumuyi kuti imvere mawu a Yehova. (Yer. 38:4, 5, 19, 20) Kodi nafenso timakonda kwambiri anthu ngati mmene Yeremiya ankachitira?

Mulungu Anamulimbitsa Mtima

9. Tikudziwa bwanji kuti Mulungu ndi amene anathandiza Yeremiya kukhala wolimba mtima?

9 Nthawi imene Yehova anamuuza koyamba za utumiki wake, Yeremiya anafuna kukana. Zimenezi zikutisonyeza kuti ngakhale kuti Yeremiya analimba mtima ndiponso kulankhula mwamphamvu sanali choncho mwachibadwa. Yeremiya anagwira ntchito yake yonenera mwamphamvu kwambiri chifukwa chodalira Mulungu ndi mtima wonse. Kunena zoona, Yehova anali ndi mneneriyo ngati “msilikali wamphamvu ndi woopsa” ndipo anamuthandiza komanso kumupatsa mphamvu kuti agwire bwino ntchito yake. (Yer. 20:11) Anthu ankadziwa kuti Yeremiya anali wolimba mtima kwambiri moti pa nthawi imene Yesu ankachita utumiki wake padziko lapansi, ena ankaganiza kuti Yeremiya wauka.​—Mat. 16:13, 14.

10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti otsalira a odzozedwa apatsidwa “mphamvu pa mitundu ya anthu ndi maufumu”?

10 Monga “Mfumu ya mitundu yonse,” Yehova anauza Yeremiya kuti akalengeze uthenga wachiweruzo ku mitundu ya anthu ndi maufumu. (Yer. 10:6, 7) Koma n’chifukwa chiyani tinganene kuti otsalira a odzozedwa apatsidwanso “mphamvu pa mitundu ya anthu ndi maufumu”? (Yer. 1:10) Mfumu ya chilengedwe chonse yapereka ntchito kwa Akhristu odzozedwa ngati mmene inachitira ndi mneneri wakaleyu. Choncho odzozedwa a Mulungu amenewa apatsidwa mphamvu yolengeza uthenga wachiweruzo ku mitundu ya anthu ndi maufumu padziko lonse lapansi. Odzozedwa amalengeza kuti mitundu ya anthu ndiponso maufumu a masiku ano adzazulidwa n’kuwonongedwa pa nthawi imene Mulungu wasankha ndiponso mmene Mulunguyo akufunira. Iwo amalengeza zimenezi chifukwa apatsidwa mphamvu ndi Mulungu Wam’mwambamwamba ndipo amagwiritsa ntchito chinenero chomveka bwino cha m’Mawu ouziridwa a Mulungu. (Yer. 18:7-10; Chiv. 11:18) Akhristu odzozedwa ndi otsimikiza mtima kuti asasiye ntchito yawo yochokera kwa Mulungu yolengeza mauthenga achiweruzo a Yehova padziko lonse lapansi.

11. Kodi n’chiyani chingatithandize kupitirizabe kulalikira pamene tikukumana ndi mavuto?

11 Nthawi zina munthu amakhumudwa chifukwa chokumana ndi anthu otsutsa, opanda chidwi kapena chifukwa chokumana ndi mavuto ena. (2 Akor. 1:8) Mofanana ndi Yeremiya, sitiyenera kubwerera m’mbuyo kapena kutaya mtima. Choncho tiyeni tonse tipitirize kupemphera mochonderera kwa Mulungu, kumudalira ndiponso kuyang’ana kwa iye kuti atithandize kukhala ‘olimba mtima.’ (1 Ates. 2:2) Popeza ndife olambira oona, tiyenera kupitiriza kukhala tcheru pa ntchito imene Mulungu watipatsa. Tiyenera kukhala otsimikiza kupitirizabe kulalikira kuti Matchalitchi Achikhristu adzawonongedwa. Ndipotu kuwonongedwa kwa Yerusalemu wosakhulupirika kunaimira chiwonongeko cha Matchalitchi amenewa. Akhristu odzozedwa apitiriza kulengeza za “chaka cha Yehova chokomera anthu mtima” komanso za “tsiku lobwezera la Mulungu wathu.”​—Yes. 61:1, 2; 2 Akor. 6:2.

Anakhalabe Wosangalala

12. Tikudziwa bwanji kuti Yeremiya anakhalabe wosangalala ndipo n’chiyani chinamuthandiza kuchita zimenezi?

12 Yeremiya ankakhala wosangalala pogwira ntchito yake. Iye anauza Yehova kuti: “Mawu anu anandipeza ndipo ndinawadya. Mawu anu amandikondweretsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimatchedwa ndi dzina lanu, inu Yehova.” (Yer. 15:16) Yeremiya ankaona kuti kuimira Mulungu woona ndiponso kulalikira mawu ake unali mwayi waukulu. N’zochititsa chidwi kudziwa kuti Yeremiya akamaganizira kwambiri za chipongwe chimene anthu ankamuchitira sankasangalala. Koma akayamba kuganizira za kusangalatsa ndi kufunika kwa uthenga wake ankayambiranso kukhala wosangalala.​—Yer. 20:8, 9.

13. Kodi kuphunzira mfundo zozama za choonadi kungatithandize bwanji kukhalabe osangalala?

13 Kuti tizikhala osangalala pa ntchito yolalikira masiku ano, tiyenera kudya “chakudya chotafuna,” chomwe ndi mfundo zozama za m’Mawu a Mulungu. (Aheb. 5:14) Chikhulupiriro chathu chimalimba tikamaphunzira zinthu zozama. (Akol. 2:6, 7) Kuchita zimenezi kumatithandiza kumvetsa bwino mmene zochita zathu zimakhudzira mtima wa Yehova. Ngati tikusowa nthawi yowerenga ndiponso kuphunzira Baibulo, tiyenera kuonanso bwino zochita zathu za tsiku ndi tsiku. Ngakhale kungophunzira ndi kusinkhasinkha kwa mphindi zochepa zokha tsiku lililonse kungatithandize kuyandikira Yehova. Kungatithandizenso kukhala ‘okondwera ndi osangalala,’ ngati mmene zinalili ndi Yeremiya.

14, 15. (a) Popeza Yeremiya sanasiye kugwira ntchito yake mokhulupirika, kodi zotsatira zake zinali zotani? (b) Kodi anthu a Mulungu masiku ano amadziwa mfundo iti yokhudza ntchito yolalikira?

14 Yeremiya anapitirizabe kulengeza uthenga wochenjeza ndiponso wachiweruzo wochokera kwa Yehova, komabe sanaiwale ntchito yake ‘yomanga ndi kubzala.’ (Yer. 1:10) Ntchito yake yomanga ndi kubzala inakhala ndi zotsatira zabwino. Ayuda ena ndiponso anthu ena amene sanali Aisiraeli anapulumuka pamene Yerusalemu ankawonongedwa mu 607 B.C.E. Ena mwa anthu amenewa anali Ebedi-meleki, Baruki ndiponso mtundu wa Arekabu. (Yer. 35:19; 39:15-18; 43:5-7) Anzake a Yeremiyawa, amene anali okhulupirika ndiponso oopa Mulungu, akuimira anthu okhala ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi ndiponso amene amagwirizana ndi Akhristu odzozedwa. Odzozedwa amenewa amasangalala kwambiri ndi ntchito yomanga, kapena kuti kulimbitsa mwauzimu, “khamu lalikulu” limeneli. (Chiv. 7:9) Nawonso a khamu lalikulu amasangalala kwambiri kuthandiza anthu a mtima wabwino kuphunzira choonadi.

15 Anthu a Mulungufe timadziwa kuti kulalikira uthenga wabwino si ntchito yongothandiza chabe anthu amene amamvetsera koma ndi mbali ya kulambira Mulungu wathu. Kaya anthu atimvere kapena ayi, kuchitira Yehova utumiki wopatulika mwa kulalikira kumatithandiza kukhala osangalala kwambiri.​—Sal. 71:23; werengani Aroma 1:9.

Khalani Tcheru pa Ntchito Yanu

16, 17. Kodi malemba a Chivumbulutso 17:10 ndiponso Habakuku 2:3 amasonyeza bwanji kuti nthawi imene yatsala yafupika?

16 Ulosi wa pa Chivumbulutso 17:10 umatithandiza kumvetsa zoti nthawi imene yatsala yafupika kwambiri. Mfumu ya nambala 7, yomwe ndi ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America, ikulamulira panopa. Palembali timawerenga kuti: “[Mfumu ya nambala 7] ikafika, ikufunika kudzakhala kanthawi kochepa.” Panopa “kanthawi kochepa” kameneka kayenera kuti katsala pang’ono kutha. Ponena za mapeto a nthawi yoipa ino, mneneri Habakuku amatitsimikizira kuti: “Masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu . . . Uziwayembekezerabe chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu. Iwo sadzachedwa.”​—Hab. 2:3.

17 Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi moyo wanga umasonyezadi kuti ndimazindikira zoti ino ndi nthawi yokhala wachangu potumikira Mulungu? Kodi mmene ndimachitira zinthu zimasonyeza kuti ndikuyembekezera kuti mapeto abwera posachedwapa? Kapena kodi zosankha zanga ndiponso zinthu zimene ndimaika patsogolo pa moyo wanga zimasonyeza kuti sindikuyembekezera kuti mapeto abwera posachedwapa? Kodi mwina zimasonyeza kuti sindikukhulupirira ngati mapetowo abweradi?’

18, 19. N’chifukwa chiyani ino si nthawi yogwa ulesi?

18 Ntchito ya Akhristu odzozedwa, amene ali ngati alonda, sinathe. (Werengani Yeremiya 1:17-19.) N’zosangalatsa kwambiri kuona kuti otsalira a odzozedwa aima nji ngati “mzati wachitsulo” ndiponso ngati “mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.” Iwo ‘amanga kwambiri choonadi m’chiuno mwawo’ mwa kulola kuti Mawu a Mulungu awalimbikitse mpaka pamene adzamalize ntchito yawo. (Aef. 6:14) Nawonso a khamu lalikulu ndi otsimikiza mtima kuthandiza Akhristu odzozedwa kukwaniritsa ntchito imene Mulungu wawapatsa.

19 Ino si nthawi yogwa ulesi pa ntchito za Ufumu koma ndi nthawi yoganizira mofatsa malangizo a pa Yeremiya 12:5. (Werengani.) Tonsefe timakumana ndi mayesero amene tiyenera kupirira. Mayesero amenewa tingawayerekezere ndi “anthu oyenda pansi” amene tiyenera kuthamanga nawo. Koma pamene “chisautso chachikulu” chikuyandikira tiyembekezere kuti mavuto athu aziwonjezeka. (Mat. 24:21) Kulimbana ndi mavuto akuluakulu amene tikumane nawo m’tsogolomu tingakuyerekezere ndi ‘kupikisana ndi mahatchi.’ Munthu angafunike kupirira kwambiri kuti apikisane ndi mahatchi amene akuthamanga. Choncho tifunika kupirira mayesero amene tikukumana nawo panopa chifukwa angatithandize kukonzekera mayesero amene akubwera.

20. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?

20 Tonsefe tikhoza kutsanzira Yeremiya ndi kugwira bwinobwino ntchito yathu yolalikira. Chikondi, kulimba mtima ndiponso kukhala wosangalala zinathandiza Yeremiya kuchita utumiki wake mokhulupirika kwa zaka 67. Maluwa okongola a mtengo wa amondi amatikumbutsa mfundo yakuti Yehova adzakhalabe “wogalamuka” kuti akwaniritse mawu ake. Ifenso tiyenera kukhalabe ‘ogalamuka,’ kapena kuti atcheru. Ngati Yeremiya anakwanitsa kukhalabe tcheru, nafenso tingakwanitse kuchita zimenezi.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi chikondi chinathandiza bwanji Yeremiya kukhalabe tcheru pa ntchito imene anapatsidwa?

• N’chifukwa chiyani tifunika kuthandizidwa ndi Mulungu kuti tikhale olimba mtima?

• N’chiyani chinathandiza Yeremiya kukhalabe wosangalala?

• N’chifukwa chiyani mukuona kuti kukhalabe tcheru n’kofunika?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 31]

Kodi mupitirizabe kulalikira ngakhale pamene mukutsutsidwa?