Kodi Mwana Wanu Angayankhe Bwanji?
Kodi Mwana Wanu Angayankhe Bwanji?
MAKOLO: Mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2010, pamasamba 16 mpaka 20, tinanena ubwino woyeserera zinthu ndi ana anu. Nkhani ino ili ndi malangizo amene angakuthandizeni kukonzekeretsa ana anu kuti azitha kulimbana ndi mavuto amene amakumana nawo kusukulu. Mwina mungakonze zoti muziyeserera zimenezi pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja.
ANA a Mboni za Yehova amakumana ndi mavuto ambiri. Nthawi zambiri anzawo kusukulu amawafunsa chifukwa chake sachita zinthu monga kuimba nawo nyimbo yafuko, kukondwerera tsiku lobadwa ndi maholide ena. Kodi mwana wanu atafunsidwa mafunso amenewa angayankhe bwanji?
Ana ena achikhristu amangoyankha kuti: “Sindingachite zimenezo. Chipembedzo changa sichindilola kuchita zimenezo.” Ana oterewa tiyenera kuwayamikira kwambiri. Kuyankha kwawo mwa njira imeneyi kungachititse kuti anzawo asafunse zambiri. Koma Baibulo limatilangiza kuti tiyenera kukhala ‘okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene watifunsa za chiyembekezo chimene tili nacho.’ (1 Pet. 3:15) Zimenezi sizitanthauza kungonena kuti, “Sindingachite zimenezo.” Ngakhale amene akutitsutsa angafunike kuwafotokozera zifukwa zimene tasankhira kuchita kapena kusachita zinthu zina.
Ana ambiri a Mboni anafotokozerapo anzawo a kusukulu nkhani za m’Baibulo pogwiritsa ntchito mabuku ngati la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Nkhani zimenezi zingathandize anzawo kudziwa chifukwa chake iwo amasankha kuchita kapena kusachita zinthu zina. Ana ena amamvetsera mwachidwi nkhani za m’Baibulo zoterezi ndipo ambiri ayamba kuphunzira Baibulo kudzera m’njira imeneyi. Koma ana ena akhoza kuvutika kuti amvetsere nthawi yaitali nkhani ya m’Baibulo. Ana a sukulu sangamvetse nkhani zina za m’Baibulo popanda kuzifotokoza bwinobwino. Mwana wina wazaka 11, dzina lake Minhee, ataitanidwa ndi mnzake kuti apite kuphwando lokondwerera tsiku lobadwa anauza mnzakeyo kuti: “Baibulo sililola kuti tizikondwerera tsiku lobadwa. Munthu wina wotchulidwa m’Baibulo dzina lake Yohane M’batizi, anaphedwa pa chikondwerero cha tsiku lobadwa.” Koma Minhee ananena kuti mnzakeyo ankaoneka kuti sanamvetse zimene anamuuza.
Nthawi zina ndi bwino kusonyeza mwana wa sukulu chithunzi china kapena nkhani ina ya m’mabuku athu. Koma bwanji ngati oyang’anira pasukulu atanena kuti safuna kuti ana azipatsana mabuku a chipembedzo? Kodi ana athu akhoza kulalikira mogwira mtima popanda mabuku alionse? Kodi mungathandize bwanji ana anu kuti achite zimenezi?
Muziyeserera
Kuyeserera zimene zingakuchitikireni n’kothandiza kwambiri. Makolo anu angayerekezere kukhala anzanu a kusukulu. Pamene ana akufotokoza zimene amakhulupirira makolo ayenera kuwayamikira ndiponso kuwathandiza kudziwa njira zina zabwino zoyankhira, komanso ayenera 1 Akor. 14:9.
kuwafotokozera ubwino wa njira zinazo. Mwachitsanzo, muyenera kukambirana mawu amene ana a misinkhu yawo angamve mosavuta. Mnyamata wina wazaka 9, dzina lake Joshua, ananena kuti anzake akusukulu sadziwa mawu monga “chikumbumtima.” Choncho anafunika kugwiritsa ntchito mawu osavuta pokambirana nawo.—Ana ena amene amafunsa funso angasiye kumvetsera ngati yankho lake ndi lalitali. Kufotokoza zinthu m’njira yokambirana kungathandize kuti azimvetserabe ana a Mboni akamacheza nawo. Mtsikana wina wazaka 10, dzina lake Haneul, ananena kuti: “Anzanga a kusukulu amafuna kukambirana osati kuwafotokozera zinthu.” Kuti mukambirane ndi munthu muyenera kufunsa mafunso ndi kumvetsera bwino akamafotokoza maganizo ake.
Chitsanzo cha makambirano chimene chili m’munsichi chikusonyeza mmene ana Achikhristu angayankhire mafunso a anzawo a kusukulu. Ana sayenera kuloweza mfundozi chifukwa anzawo a kusukulu ndi osiyanasiyana ndiponso angafunike kuwayankha mogwirizana ndi zimene
akumana nazo. Choncho, mwana wa Mboni ayenera kumvetsa mfundozi, n’kuzinena m’mawu akeake mogwirizana ndi zimene mnzake wa kusukulu wafunsa. Ngati muli ndi ana a pa sukulu, muyenera kuyeserera zimenezi.Kuphunzitsa ana kumafuna nthawi ndiponso khama. Makolo achikhristu ayenera kukhomereza mfundo za m’Baibulo mwa ana awo ndiponso kuwathandiza kuti azizitsatira pa moyo wawo.—Deut. 6:7; 2 Tim. 3:14.
Pa kulambira kwanu kwa pabanja mlungu wotsatira, mungachite bwino kuyeserera ndi ana anu mfundo zimene zili m’munsizi. Mudzaona kuti n’zothandiza kwambiri. Koma musaiwale kuti cholinga si kuloweza mawu kapena mayankho. Ndipotu mukhoza kuyeserera kangapo n’kumayankha mosiyanasiyana kuti muone zimene ana anu anganene. Anawo akamafotokoza zimene amakhulupirira muziwathandiza kuti aziyankha mwanzeru komanso mosamala. Mukamachita zimenezi mudzathandiza ana anu kuti azitha kufotokoza zimene amakhulupirira kwa anzawo a kusukulu, oyandikana nawo nyumba ndiponso aphunzitsi awo.
[Bokosi/Chithunzi pamasamba 4, 5]
KUKONDWERERA TSIKU LOBADWA
Mary: John ulipo. Ndakonza phwando lokondwerera tsiku lobadwa, ndiye ndikufuna kuti udzabwere.
John: Zikomo kwambiri pondiganizira. Koma n’chifukwa chiyani ukufuna kudzakondwerera tsiku lobadwa?
Mary: Ndikungofuna kudzakumbukira tsiku limene ndinabadwa. Kodi iwe sukondwerera tsiku limene unabadwa?
John: Ayi.
Mary: Chifukwa? Inetu anthu akwathu anasangalala nditabadwa.
John: N’chimodzimodzinso anthu akwathu. Anasangalala ine nditabadwa. Koma ndimaona kuti chimenechi si chifukwa chomveka chochitira chikondwerero chaka chilichonse. Anthu ambiri amaona kuti iwo ndi anthu ofunika kwambiri pa tsiku lawo lobadwa. Koma kodi Mulungu si ndiye wofunika kwambiri? Ndipotu tiyenera kumuyamikira iyeyo chifukwa chotipatsa moyo eti?
Mary: Kodi ukufuna kundiuza kuti ndisakachite chikondwerero cha tsiku langa lobadwa?
John: Ayi Mary. Chimenecho ndi chosankha chako. Koma taganizira mfundo iyi. Anthu ambiri amasangalala akalandira mphatso pa tsiku lawo lobadwa, koma Baibulo limati munthu amakhala wosangalala kwambiri chifukwa chopatsa osati kulandira. M’malo mongodziganizira pa tsiku lobadwa, kodi sizingakhale bwino kuthokoza Mulungu, kuganizira anthu ena, n’kuona mmene tingawathandizire?
Mary: Komadi eti? Koma kodi ukutanthauza kuti makolo ako sakupatsa mphatso iliyonse?
John: Ayi amandipatsa. Koma sadikira kuti lifike tsiku langa lobadwa. Iwo amandipatsa mphatso pa nthawi iliyonse imene afuna. Ndakumbukiranso mfundo ina. Kodi ungakonde kudziwa mmene phwando lokondwerera tsiku lobadwa linayambira?
Mary: Linayamba bwanji?
John: Mawa ndidzakuuza nkhani yosangalatsa yofotokoza za phwando lokumbukira tsiku lobadwa limene linachitika kalekale.
NYIMBO YA FUKO
Tadala: N’chifukwa chiyani suimba nawo nyimbo ya fuko?
Chifundo: Wachita bwino kufunsa. Koma poyamba n’chifukwa chiyani iwe umaimba nawo?
Tadala: Ndimakonda dziko lathu.
Chifundo: Inenso ndimakonda dziko lathu, koma kodi mayiko enanso si abwino?
Tadala: Ee ndi abwino.
Chifundo: Koma kodi timaimbira nyimbo munthu kapena chinthu china chilichonse chimene timakonda?
Tadala: Ayi. Kaya n’chifukwa chiyani ndimaimba kaya. Mwina chifukwa aliyense amaimba basi.
Chifundo: Anthu ambiri amaimba nyimbo yafuko chifukwa amaona kuti dziko lawo ndi labwino kwambiri ndipo akhoza kulichitira china chilichonse. Koma ine sindiona choncho. Sindingapereke moyo wanga pomenyera nkhondo dzikoli chifukwa Mulungu ndi amene anandipatsa moyo. Choncho ndingakonde kupereka moyo wanga kwa Mulungu. Ngakhale kuti ndimakonda dziko lathu ndikuona kuti si bwino kuimba nawo nyimbo ya fuko.
Tadala: Kuteroku.
Chifundo: Eetu. Koma wachita bwino kufunsa. Ngati ungafune kudziwa chifukwa chimene ndimachitira kapena sindichitira zinthu zina ukhoza kundifunsa nthawi iliyonse. Baibulo limanenanso kuti kalekale mfumu ya ku Babulo inalamula anthu kuti aziweramira fano. Koma panali anthu ena amene sanalole kuchita zimenezi ngakhale kuti akanatha kuphedwa.
Tadala: Ndiyeno chinawachitikira n’chiyani?
Chifundo: Ndikuuza pa nthawi yopuma.
NKHANI ZA NDALE
Mike: Tim, utaloledwa kuvota, ungavotere ndani?
Tim: Palibe amene ndingavotere.
Mike: Chifukwa?
Tim: Ndinavota kale.
Mike: Zatheka bwanji poti sunafike msinkhu wovota?
Tim: Pali boma labwino kwambiri kuposa lina lililonse ndipo n’zotheka kulivotera pa msinkhu uliwonse.
Mike: Ndi boma liti limenelo?
Tim: Boma la Mulungu. Ndipo Mulungu ndi wolamulira wabwino kwambiri. Ungakonde kuti ndikuuze chifukwa chake ndikutero?
Mike: Aa. Usavutike.
Tim: Chabwino nthawi ina ukadzafuna kudziwa ukhoza kudzandifunsa.
[Chithunzi]
“John, ndikukuitana kuti udzabwere pa phwando lokumbukira tsiku langa lobadwa”
[Chithunzi patsamba 3]
“N’chifukwa chiyani suimba nawo nyimbo ya fuko?”