Ndimayesetsa Kukhala ndi Zochita Zambiri M’gulu la Yehova
Ndimayesetsa Kukhala ndi Zochita Zambiri M’gulu la Yehova
Yosimbidwa ndi Vernon Zubko
NDINAKULIRA pa famu inayake pafupi ndi mudzi wotchedwa Stenen m’chigawo cha Saskatchewan, ku Canada. Makolo anga, Fred ndi Adella, ankayesetsa kwambiri kusamalira mwauzimu ndiponso mwakuthupi, ineyo, mchemwali wanga dzina lake Aurellia, m’ng’ono wanga Alvin, mchemwali wanga wina Allegra ndi mng’ono wanga winanso Daryl. Mpaka pano, timayamikirabe makolo athu chifukwa chotiphunzitsa choonadi.
Bambo omwe anali Mkhristu wodzozedwa ankalalikira mopanda mantha. Iwo ankagwira ntchito mwakhama kuti apeze zofunika pa moyo koma ankachitanso zinthu zochititsa kuti aliyense azidziwa kuti ndi a Mboni. Iwo nthawi zonse ankakonda kulankhula za choonadi. Ndimalimbikitsidwabe ndikaganizira za khama ndiponso kulimba mtima kwawo. Iwo ankakonda kundiuza kuti, “Uziyesetsa kukhala ndi zochita zambiri m’gulu la Yehova ndipo udzapewa mavuto ambiri.”
Nthawi zambiri tinkalalikira mumsewu ku Stenen komanso m’madera ozungulira. Kawirikawiri izi sizinali zophweka kwa ineyo. M’tawuni iliyonse munali anthu okonda kuvutitsa anzawo makamaka anafe. Tsiku lina ndili ndi zaka 8 ndinaima pakona penapake nditatenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndipo panabwera gulu la anyamata. Iwo anandivula chipewa n’kuchikoleka pa mtengo umene unaimikidwa pafupi. Mwamwayi m’bale wina wachikulire amene ankandiyang’anira anaona zimene zinkachitikazi. Iye anabwera pafupi n’kufunsa kuti, “Vern, chikuchitika n’chiyani?” Nthawi yomweyo anyamata aja anathawa. Ngakhale kuti izi zinandikhumudwitsa, ndinaphunzirapo kuti ukamalalikira mumsewu si bwino kungoima pamalo amodzi ngati chipilala. Zinthu zimene zinandichitikira ndili wamng’ono zinandithandiza kuti ndikhale wolimba mtima polalikira khomo ndi khomo.
Ine ndi Alvin tinabatizidwa mu May 1951. Pa nthawiyi ndinali ndi zaka 13. Ndimakumbukirabe kuti M’bale Jack Nathan amene anakamba nkhani ya ubatizo anatilimbikitsa kuti tisamalole mwezi kutha tisanalankhulepo za Yehova. * M’banja lathu tinkaona kuti upainiya ndiye ntchito yabwino imene munthu ungagwire. Choncho mu 1958 nditamaliza sukulu ndinasamukira kumzinda wa Winnipeg ku Manitoba kukachita upainiya. Ngakhale kuti bambo anga ankasangalala tikamagwira limodzi ntchito yopala matabwa, iwo ndi mayi anga anandilimbikitsa kwambiri kuti ndizichita utumiki wa nthawi zonse ndipo anavomera zoti ndisamuke.
Nyumba Yatsopano Ndiponso Mnzanga Watsopano
Mu 1959, ofesi ya nthambi inapempha aliyense amene angathe kusamukira ku chigawo cha Quebec komwe kunkafunika olengeza 1 Akor. 9:22, 23.
Ufumu ambiri. Ine ndinapita kukachita upainiya mumzinda wa Montreal. Zinthu zinasinthiratu. Ndinayamba kuphunzira Chifalansa komanso chikhalidwe cha kumeneko. Tsiku lina woyang’anira dera anandiuza kuti, “Osamanena kuti ‘Ife kwathu tinkatere.’” Awa anali malangizo abwino kwambiri.—Pa nthawi imene ndinkasamukira ku Quebec ndinalibe munthu wochita naye upainiya. Koma mu February 1961 ndinakwatira Shirley Turcotte, mlongo amene ndinakumana naye ku Winnipeg. Apa tsopano ndinapeza mnzanga weniweni wochita naye upainiya nthawi zonse. Iyenso anachokera ku banja lokonda Yehova. Pa nthawiyi sindinkadziwa kuti iye adzandithandiza ndiponso kundilimbikitsa kwambiri zaka zotsatira.
Kulalikira M’dera Latsopano la Gaspé
Patangotha zaka ziwiri kuchokera pamene tinakwatirana, tinatumizidwa ku Rimouski, m’chigawo cha Quebec kukachita upainiya wapadera. Chaka chotsatira, ofesi ya nthambi inatipempha kuti tikalalikire kudera latsopano la Gaspé, m’mphepete mwa nyanja kum’mawa m’dziko la Canada. Ntchito yathu inali kukafesa mbewu zambiri za choonadi kuderali. (Mlal. 11:6) Tinapakira m’galimoto yathu magazini oposa 1,000, mabuku pafupifupi 400, chakudya, ndi zovala ndipo tinayamba ulendo wokalalikira kwa mwezi wathunthu kudera latsopano. Tinalalikira m’midzi ing’onoing’ono yonse ya ku Gaspé. Wailesi ya kuderali inalengeza kuti kukubwera a Mboni za Yehova ndipo inachenjeza anthu kuti asamalandire mabuku athu. Koma anthu ambiri sanamvetse chilengezochi, ndipo anaganiza kuti akuitanira mabuku athu, choncho ankalandira mabukuwa.
M’masiku amenewo tinali titangopatsidwa kumene ufulu wolalikira m’madera ena a ku Quebec, ndipo nthawi zambiri apolisi ankatiimitsa. Izi n’zimene zinachitika mumzinda wina tikugawira magazini pafupifupi khomo lililonse. Wapolisi wina anatiuza kuti tipite naye kupolisi ndipo tinapita nayedi. Ndinamva kuti loya wina mumzindawu analamula kuti tisiye kulalikira. Popeza tsikulo, mkulu wa apolisi anali atachoka ndinasonyeza loyayo kalata yochokera ku ofesi ya nthambi ku Toronto, yomwe inafotokoza mwatsatanetsatane za ufulu wathu wolalikira. Loyayu atawerenga kalatayi anati: “Inetu ndilibe nanu vuto. Ndi wansembe wina amene anandiuza kuti ndikuletseni kulalikira.” Popeza tinkafuna kuti anthu adziwe zoti ntchito yathu si yoletsedwa, nthawi yomweyo tinabwereranso kudera limene apolisi anatiletsalo n’kukapitiriza kulalikira.
M’mawa wa tsiku lotsatira titapita kukaonana ndi mkulu wa apolisi, iye anakhumudwa atamva kuti anatiletsa kulalikira. Pamene ankalankhula ndi loya uja pafoni ankachita kumvekeratu kuti wakwiya kwambiri. Mkulu wa apolisiyu anatiuza kuti tikakumana ndi vuto lililonse tizimuimbira foni ndipo analonjeza kuti azitithandiza. Ngakhale kuti tinali alendo ndipo sitinkadziwa bwinobwino Chifalansa, tinkaona kuti anthu ankatikomera mtima ndiponso ankatilandira bwino. Koma tinkadzifunsa kuti, ‘Koma anthu amenewa adzadziwadi choonadi?’ Yankho la funsoli linapezeka patapita zaka zingapo titapita kukamanga Nyumba za Ufumu m’dera lonse la Gaspé. Tinapeza kuti anthu ambiri amene tinawalalikira tsopano ndi abale athu. N’zoonadi kuti Yehova ndi amene amakulitsa.—1 Akor. 3:6, 7.
Tinalandira Mphatso
Mwana wathu wamkazi dzina lake Lisa anabadwa m’chaka cha 1970. Mphatso yochokera kwa Yehova imeneyi inawonjezera chisangalalo chathu. Ine, Shirley, ndi Lisa tinkagwira pamodzi ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Lisa atamaliza sukulu anati: “Bambo ndi mayi, popeza ndinakusiyitsani utumiki wa nthawi zonse kwa kanthawi, ndibweza ngongole imeneyi mwa kuchita upainiya.” Lisa wakhala akuchita upainiya kwa zaka 20 ndipo panopa akuchita upaniniyawu limodzi ndi mwamuna wake Sylvain. Iwo akhala ndi mwayi wogwira ntchito ya zomangamanga m’mayiko osiyanasiyana. Cholinga cha banja lathu n’chakuti tizikhala moyo wosalira zambiri ndiponso kukhala odzipereka kutumikira Yehova. Sindiiwala mawu amene Lisa ananena
atangoyamba upainiya aja. Iye anandilimbikitsa kuti ndiyambirenso utumiki wa nthawi zonse mu 2001 ndipo mpaka pano ndikuchitabe upainiya. Upainiya umandithandizabe kukhulupirira Yehova pa zinthu zonse zimene ndimachita ndiponso kukhala moyo wosalira zambiri koma wachimwemwe.Ntchito Zomangamanga Zimafuna Chikondi, Kumvera ndi Kukhulupirika
Yehova wandiphunzitsa kuti tikakhala odzipereka n’kuvomera kuchita utumiki uliwonse umene angatipatse, iye amatidalitsa kwambiri. Ndi mwayi wosaneneka kutumikira mu Komiti Yomanga Yachigawo ndiponso kugwira ntchito ya zomangamanga limodzi ndi abale ndi alongo m’madera onse a ku Quebec.
Ngakhale kuti Akhristu ena amene amagwira ntchito zomangamanga alibe luso lokamba nkhani, iwo ali ndi luso logometsa pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Abale okondedwa amenewa amagwira ntchito ndi mtima wonse ndipo luso lawo limaonekera. Zotsatira zake zimakhala nyumba yokongola kwambiri imene anthu amalambiriramo Yehova.
Anthu ena andifunsapo kuti, “Kodi makhalidwe ofunika kwambiri kwa anthu odzipereka pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi ati?” Ine ndaona kuti choyamba, munthu ayenera kukonda Yehova, Mwana wake ndiponso abale onse. (1 Akor. 16:14) Chachiwiri n’chakuti, munthuyo ayenera kukhala womvera ndiponso wokhulupirika. Nthawi zina zinthu siziyenda mmene munthu ukufunira. Zikatere, ngati ndiwe munthu womvera umapitirizabe kutsatira dongosolo la Mulungu. Kukhulupirika n’kumene kungamuthandize munthu kuvomeranso kugwira ntchito zina zomangamanga m’tsogolo.
Timayamikira Kwambiri Yehova
Ngakhale kuti bambo anga anamwalira m’chaka cha 1985, malangizo awo akuti ndiyenera kuyesetsa kukhala ndi zochita zambiri m’gulu la Yehova ndimawakumbukirabe mpaka pano. Mofanana ndi anthu ena onse amene akutumikira mbali yakumwamba ya gulu la Yehova, sindikukayikira kuti ali ndi zochita zambiri kumeneko. (Chiv. 14:13) Panopa mayi anga ali ndi zaka 97. Iwo akudwala matenda opha ziwalo ndipo satha kulankhula bwino, koma amalidziwabe bwino Baibulo. Iwo akamalemba makalata, amagwira mawu malemba ndipo amatilimbikitsa kuti tipitirize kutumikira Yehova mokhulupirika. Anafe timayamikira kwambiri kukhala ndi makolo achikondi chonchi.
Ndikuthokozanso kwambiri Yehova chifukwa chondipatsa Shirley, mkazi wokhulupirika yemwenso ndi mnzanga weniweni. Iye nthawi zonse amakumbukira malangizo amene mayi ake anamupatsa. Iwo anamuuza kuti, “Vern azikhala wotanganidwa kwambiri pa nkhani zokhudza Ufumu. Choncho uyenera kudziwiratu kuti nthawi zina suzikhala naye chifukwa azikhala akuthandiza anthu ena.” Titangokwatirana zaka 49 zapitazo tinalumbira kuti tidzakhala limodzi mpaka kukalamba tikutumikira Yehova ndipo ngati tonse tidzapulumuke mapeto a dongosolo lino, tidzabwerera ku unyamata n’kupitiriza kutumikira Yehova limodzi mpaka muyaya. Anthufe takhaladi ndi ‘zochita zambiri mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Yehova wakhala akutisamaliradi kwambiri ndipo wakhala akuonetsetsa kuti sitikusowa chilichonse.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Kuti mudziwe mbiri ya moyo wa M’bale Jack Halliday Nathan, onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 1990, masamba 10-14.
[Chithunzi patsamba 31]
“Cholinga cha banja lathu n’chakuti tizikhala moyo wosalira zambiri ndiponso kukhala odzipereka kutumikira Yehova.”