Kodi Yehova Amaona Bwanji Kupereka Zifukwa Pofuna Kudzikhululukira?
Kodi Yehova Amaona Bwanji Kupereka Zifukwa Pofuna Kudzikhululukira?
“MKAZI amene munandipatsayu ndi amene wandipatsa chipatso cha mtengowo, ndipo ine ndadya.” Anatero mwamuna. Ndipo mkazi anati: “Njoka ndi imene inandinyenga, ndipo ine ndadya.” Awa ndi mawu amene makolo athu oyambirira Adamu ndi Hava anauza Mulungu ndipo chinali chiyambi cha khalidwe lokonda kupereka zifukwa pofuna kudzikhululukira.—Gen. 3:12, 13.
Chiweruzo chimene Yehova anapereka kwa Adamu ndi Hava chifukwa chosamvera mwadala lamulo lake, chinasonyeza kuti zifukwa zimene anapereka zinali zosamveka kwa iye. (Gen. 3:16-19) Kodi izi zikutanthauza kuti zifukwa zilizonse zimene tingapereke zimakhala zosamveka kwa Yehova? Kapena kodi pali zifukwa zina zimene iye amaona kuti n’zomveka? Ngati ndi choncho, tingadziwe bwanji zifukwa zomveka ndi zosamveka? Tiyeni tiyankhe mafunso amenewa.
Nthawi zina munthu amapereka zifukwa pofuna kufotokoza chifukwa chake wachitira kanthu kena, sanachitire kanthu kena kapena sadzachitira kanthu kena. Zifukwa zolepherera kuchita zinthuzo zikhoza kukhala zomveka ndipo zingachititse munthu kukomeredwa mtima ndiponso kukhululukidwa chifukwa chakuti wapepesa. Komabe monga zinalili ndi Adamu ndi Hava, nthawi zambiri zifukwazi zingakhale zabodza ndiponso zachinyengo. Ndiye poti kawirikawiri anthu amapereka zifukwa zabodza, nthawi zambiri anthu amakayikira munthu akapereka zifukwa zomulepheretsa kuchita zinazake.
Pa nkhani yopereka zifukwa zodzikhululukira makamaka zikakhala zokhudza kutumikira Mulungu, tiyenera kupewa ‘kudzinyenga ndi maganizo onama.’ (Yak. 1:22) Tiyeni tikambirane zitsanzo ndi mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuti ‘nthawi zonse tizitsimikizira kuti chovomerezeka kwa Ambuye n’chiti.’—Aef. 5:10.
Zimene Mulungu Amafuna Kuti Tizichita
M’Mawu a Mulungu timapezamo malamulo amene anthu a Yehovafe tiyenera kutsatira. Mwachitsanzo, mawu a Khristu akuti “pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga,” ndi lamulo limene likugwirabe ntchito kwa otsatira a Khristu. (Mat. 28:19, 20) Ndipotu kumvera lamulo limeneli n’kofunika kwambiri moti mtumwi Paulo ananena kuti: “Tsoka kwa ine ngati sindilengeza uthenga wabwino!”—1 Akor. 9:16.
Pali anthu ena amene akhala akuphunzira nafe Baibulo kwa nthawi yaitali koma amachitabe manyazi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mat. 24:14) Palinso anthu ena amene poyamba ankalalikira koma anasiya. Kodi nthawi zina, anthu amene salalikirawa amapereka zifukwa ziti? M’mbuyomu, pamene anthu anazengereza kumvera malamulo ena a Yehova, kodi iye anachita chiyani?
Zifukwa Zimene Mulungu Amaona Kuti N’zosamveka
“N’zovuta Kwambiri.” Makamaka anthu omwe ndi amantha mwachibadwa, amaona kuti ntchito yolalikira ndi yovuta kwambiri. Komabe taganizirani zimene tikuphunzira pa nkhani ya Yona. Iye anapatsidwa ntchito imene anaiona kuti ndi yovuta koopsa. Yehova anamuuza kuti akalengeze kuti mzinda wa Nineve udzawonongedwa. Tikhoza kumvetsa chifukwa chimene Yona anaopera kugwira ntchito imeneyi. Yona 1:1-3; 3:3, 4, 10.
Mzinda wa Nineve unali likulu la Asuri ndipo anthu a kumeneko ankadziwika kuti anali ankhanza koopsa. N’kutheka kuti Yona anaganiza kuti: ‘Kodi kumeneko zikandithera bwanji? Kodi anthu sakandipha?’ Pasanapite nthawi yaitali, iye anathawa. Koma zifukwa zimene Yona anali nazozi, zinali zosamveka kwa Yehova. Choncho Yehova anamutumizabe kuti akalalikire ku Nineve. Pa nthawiyi, Yona anagwira ntchito yake molimba mtima ndipo Yehova anadalitsa zotsatira za ntchitoyo.—Ngati mumaganiza kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino ndi yovuta kwambiri, kumbukirani kuti “zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu.” (Maliko 10:27) Dziwani kuti Yehova adzakuthandizani ngati mupitirizabe kumupempha kuti akuthandizeni. Dziwaninso kuti mukamayesetsa kulimba mtima kuti mugwire ntchito yake, iye adzakudalitsani.—Luka 11:9-13.
“Sindifuna.” Kodi mungatani ngati mukuona kuti mulibe mtima wofuna kuchita utumiki wachikhristu? Dziwani kuti Yehova angakuthandizeni kusintha maganizo anu. Paulo anati: “Mulungu amachita zinthu m’njira imene imamusangalatsa. Iye amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.” (Afil. 2:13) Choncho, muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kuti muzifuna kuchita zimene iye amafuna. Izi n’zimene Mfumu Davide anachita. Iye anapempha Yehova kuti: “Ndiyendetseni m’choonadi chanu.” (Sal. 25:4, 5) Inunso mungachite chimodzimodzi. Muyenera kupempha Yehova kuchokera pansi pa mtima kuti akuthandizeni kufuna kuchita zimene zingamusangalatse.
Nthawi zambiri tikatopa kapena tikakhumudwa ndi zinthu zina, timafunika kuchita kudzikakamiza kuti tipite ku Nyumba ya Ufumu kukasonkhana ndiponso kuti tipite mu utumiki. Kodi zikatere ndiye kuti tiyenera kuganiza kuti sitikonda Yehova ndi mtima wonse? Ayi. Kale atumiki ena a Mulungu ankachitanso kudzikakamiza kuti achite chifuniro cha Mulungu. Mwachitsanzo, Paulo ananena kuti ‘anamenya thupi lake’ n’cholinga chakuti amvere malamulo a Mulungu. (1 Akor. 9:26, 27) Choncho ngakhale pa nthawi imene tachita kudzikakamiza kuti tichite utumiki, tiyenera kudziwa kuti Yehova adzatidalitsa. Chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti timadzikakamiza kuchita chifuniro cha Mulungu pa chifukwa chabwino chomwe ndi kukonda Yehova. Tikamachita zimenezi, timatsutsa zimene Satana amanena zakuti atumiki a Mulungu akhoza kukana Mulunguyo ngati atayesedwa.—Yobu 2:4.
“Ndine wotanganidwa.” Ngati mumalephera kulalikira chifukwa choona kuti ndinu wotanganidwa, ndi bwino kuti muganizirenso zinthu zimene mumaziika pa malo oyamba. Yesu ananena kuti: “Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba.” (Mat. 6:33) Kuti mutsatire mfundo imeneyi, mwina muyenera kuyamba kukhala moyo wosalira zambiri kapena muyenera kuchepetsa nthawi imene mumachita zosangalatsa n’cholinga chakuti muzipeza nthawi yochita utumiki. N’zoona kuti zinthu monga zosangalatsa ndiponso zinthu zina zimene timakonda kuchita n’zofunika, koma zisamakhale zifukwa zotilepheretsa kuchita utumiki. Mtumiki wa Mulungu amaika patsogolo zinthu za Ufumu.
“Sindingathe.” Mwina mukhoza kumaona kuti si inu woyenerera kulalikira uthenga wabwino. M’nthawi za Baibulo, atumiki a Yehova ena ankaona kuti sangathe kugwira bwino ntchito imene Yehova wawapatsa. Mwachitsanzo, taganizirani za Mose. Yehova atam’patsa ntchito yoti achite, Mose anati: “Pepani Yehova, ine sinditha kulankhula, kuyambira kalekale, kapena pamene mwalankhula ndi ine mtumiki wanu. Pakuti ndimalankhula movutikira ndipo ndine wa lilime lolemera.” Yehova atamulimbikitsa Mose ananenabe kuti: “Pepani Yehova. Chonde, tumizani wina aliyense amene mungam’tumize.” (Eks. 4:10-13) Kodi Yehova anachita chiyani?
Yehova sanalole kuti Mose asagwire ntchito imene anam’patsayi. M’malomwake, iye anauza Aroni kuti athandize Mose pa ntchito imeneyi. (Eks. 4:14-17) M’zaka zotsatira, Yehova anathandiza Mose ndipo anamupatsa zinthu zonse zofunika kuti agwire bwino ntchito imene anamupatsa. Masiku anonso muyenera kukhulupirira kuti Yehova adzagwiritsa ntchito Akhristu anzanu aluso kuti akuthandizeni kuchita utumiki. Koposa zonse, Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti Yehova adzatithandiza kukhala oyenera kugwira ntchito imene iye watipatsa.—2 Akor. 3:5; onani bokosi lakuti, “Zaka Zimene Ndinasangalala Kwambiri pa Moyo Wanga.”
“Wina wake anandikhumudwitsa.” Ena amasiya kulalikira kapena kupezeka pa misonkhano chifukwa chokhumudwa ndipo amaganiza kuti zifukwa zimenezi n’zomveka kwa Yehova. N’zoona kuti nthawi zina timakhumudwa chifukwa cha zochita za ena. Koma kodi chimenechi ndi chifukwa chomveka chisiyira kuchita Mac. 15:39) Koma kodi iwo anasiya kulalikira chifukwa cha zimenezi? Ayi sanatero.
zinthu zimene timayenera kuchita monga Akhristu? Paulo ndi Baranaba ayenera kuti anakhumudwa kwambiri, pakati pawo ‘patabuka mkangano woopsa.’ (Mkhristu mnzanu akakukhumudwitsani muzikumbukira kuti mdani wanu si Mkhristu wopanda ungwiroyo koma Satana yemwe akufuna kuti akumezeni. Cholinga cha Mdyerekezi sichidzatheka ngati ‘mukhala olimba m’chikhulupiriro ndiponso kulimbana naye.’ (1 Pet. 5:8, 9; Agal. 5:15) Ngati muli ndi chikhulupiriro cholimba ‘simudzakhumudwa’ ngakhale pang’ono.—Aroma 9:33.
Kodi Tingatani Ngati Sitingakwanitse Kuchita Zambiri?
Malinga ndi zimene takambiranazi, n’zoonekeratu kuti palibe chifukwa cha m’Malemba chotilepheretsa kumvera malamulo a Yehova kuphatikizapo lamulo la kulalikira uthenga wabwino. Komabe, mwina pangakhale zifukwa zomveka zomwe zingatilepheretse kuchita zambiri mu utumiki. Maudindo ena a m’Malemba angachititse kuti tisamakhale ndi nthawi yambiri yolalikira. Ndiponso nthawi zina tikhoza kutopa kwambiri kapena kudwala zedi moti sitingathe kuchita zonse zimene timafuna potumikira Yehova. Koma Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti Yehova amadziwa zimene timafuna kuchita kuchokera pansi pa mtima komanso zimene sitingakwanitse.—Sal. 103:14; 2 Akor. 8:12.
Choncho, tiyenera kusamala kuti tisamadziimbe mlandu kwambiri kapena kuweruza ena pa nkhani zimenezi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndiwe ndani kuti uweruze wantchito wapakhomo wa mnzako? Ndi udindo wa bwana wake kumuweruza kuti ndi wolakwa kapena wosalakwa.” (Aroma 14:4) M’malo modziyerekezera ndi anthu ena, tiyenera kukumbukira kuti “aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.” (Aroma 14:12; Agal. 6:4, 5) Aliyense akamapemphera kwa Yehova n’kumuuza zifukwa zomulepheretsa kuchita zinthu zina, ayenera kuchita zimenezo ndi “chikumbumtima choona.”—Aheb. 13:18.
Kutumikira Yehova Kumatithandiza Kukhala Osangalala
Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tonsefe tikhoza kutumikira Yehova mosangalala kwambiri chifukwa zimene amafuna kuti tizichita n’zotheka. N’chifukwa chiyani tikunena choncho?
Mawu a Mulungu amati: “Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo, pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.” (Miy. 3:27) Kodi taphunzirapo chiyani pa lemba limeneli pa zimene Mulungu amafuna? Yehova satiuza kuti tiziyesetsa kuchita zinthu zofanana ndi zimene dzanja la m’bale wathu lingathe kuchita. Koma iye akutiuza kuti tizimutumikira mogwirizana ndi zimene ‘dzanja lathu lingathe kuchita.’ Kaya ndife ofooka kapena amphamvu, tonsefe tikhoza kutumikira Yehova ndi mtima wonse.—Luka 10:27; Akol. 3:23.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 14]
“Zaka Zimene Ndinasangalala Kwambiri pa Moyo Wanga”
Ngakhale pamene tikudwala kwambiri, sitiyenera kuganiza mwamsanga kuti zimenezi zingatilepheretse kuchita mokwanira utumiki wathu. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina wa ku Canada dzina lake Ernest.
M’bale Ernest anali ndi vuto la kulankhula ndipo anali wamanyazi kwambiri. Iye atavulala msana sakanathanso kugwira ntchito yake ya zomangamanga. Ngakhale kuti anali atalumala, izi zinachititsa kuti akhale ndi nthawi yambiri yochita utumiki. Mfundo zolimbikitsa anthu kuchita upainiya wothandiza, zimene anamva pa misonkhano ya mpingo, zinamukhudza kwambiri. Koma iye ankaona kuti sangakwanitse kuchita upaniya wothandiza.
Kuti atsimikizire ngati sangakwanitsedi kuchita utumikiwo, analembetsa upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi. Iye anadabwa kwambiri kuona kuti wakwanitsa bwinobwino. Kenako anaganiza kuti, ‘Ndikuona kuti nditalembetsanso sindingakwanitse.’ Kuti atsimikizire zimenezi, iye analembetsanso upainiyawu kachiwiri ndipo anakwanitsanso bwinobwino.
M’bale Ernest anachita upainiya wothandiza kwa chaka koma ankaganiza kuti, “N’zodziwikiratu kuti sindingakwanitse kukhala m’painiya wokhazikika.” Pofunanso kutsimikizira zimenezi, iye analembetsa upainiya wokhazikika. Ernest anadabwa kwambiri kuona kuti watha chaka akuchita upainiya wokhazikika. Iye anachitabe upainiyawu kwa zaka ziwiri ndipo ankasangalala kwambiri mpaka pamene anamwalira ndi matenda ake a msana. Koma asanamwalire ankauza anthu amene ankabwera kudzamuona m’maso muli misozi kuti, “Zaka zimene ndatumikira Yehova monga m’painiya ndi zaka zimene ndinasangalala kwambiri pa moyo wanga.”
[Chithunzi patsamba 13]
Tikhoza kuthana ndi mavuto alionse amene angatilepheretse kuchita utumiki
[Chithunzi patsamba 15]
Yehova amasangalala kwambiri tikamamutumikira ndi mtima wonse malinga ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu