Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumathandiza Kuti Misonkhano Yachikhristu Ikhale Yolimbikitsa?

Kodi Mumathandiza Kuti Misonkhano Yachikhristu Ikhale Yolimbikitsa?

Kodi Mumathandiza Kuti Misonkhano Yachikhristu Ikhale Yolimbikitsa?

“Mukasonkhana pamodzi, . . . zochitika zonse zikhale zolimbikitsa.”​—1 AKOR. 14:26.

1. Malinga ndi 1 Akorinto chaputala 14, kodi cholinga chachikulu cha misonkhano yathu yachikhristu n’chiyani?

‘KOMA ndiye tinali ndi misonkhano yolimbikitsa.’ Kodi munayamba mwanenapo mawu ngati amenewa pambuyo pa misonkhano ku Nyumba ya Ufumu? Muyenera kuti munanenapo. N’zosadabwitsa kuti misonkhano ya mpingo imakhala yolimbikitsa kwambiri. Ndipotu, mofanana ndi nthawi ya Akhristu oyambirira, cholinga chachikulu cha misonkhano yathu ndi kulimbikitsa mwauzimu anthu amene asonkhana. Taonani mmene mtumwi Paulo anatsindikira mfundo imeneyi, yokhudza misonkhano yachikhristu, m’kalata yake yoyamba yopita kwa Akorinto. M’chaputala 14 chonse cha buku limeneli, Paulo anafotokoza mobwerezabwereza mfundo yakuti cholinga cha nkhani iliyonse pa misonkhano chizikhala ‘kumanga mpingo.’​—Werengani 1 Akorinto 14:3, 12, 26. *

2. (a) Kodi n’chiyani chimachititsa kuti misonkhano yathu izikhala yolimbikitsa? (b) Kodi tikambirana funso liti?

2 Timadziwa kuti mzimu wa Mulungu makamaka ndi umene umathandiza kuti misonkhano yathu izikhala yolimbikitsa ndiponso yothandiza. N’chifukwa chake timayamba misonkhano yathu ndi pemphero lochokera pansi pa mtima kupempha Atate wathu wakumwamba Yehova kuti adalitse misonkhano yathu ndi mzimu wake woyera. Komabe, timadziwanso kuti munthu aliyense mu mpingo angathandize kuti misonkhano ikhale yolimbikitsa kwambiri. Ndiyeno kodi aliyense angachite chiyani kuti misonkhano ya mlungu uliwonse ku Nyumba ya Ufumu izikhala yolimbikitsa ndiponso yotsitsimula mwauzimu?

3. Kodi misonkhano yachikhristu ndi yofunika bwanji?

3 Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane mbali zina zokhudza misonkhano yathu zimene anthu otsogolera pa misonkhanoyi ayenera kukumbukira. Tikambirananso zimene mpingo wonse ungachite pofuna kuthandiza kuti anthu onse amene afika pa misonkhano alimbikitsidwe. Nkhani imeneyi ndi yofunika kwambiri chifukwa chakuti misonkhano yathu ndi yopatulika. Ndipotu kupezeka pa misonkhano ndi kutenga nawo mbali ndi zinthu zofunika kwambiri pa kulambira kwathu Yehova.​—Sal. 26:12; 111:1; Yes. 66:22, 23.

Msonkhano Womwe Cholinga Chake Ndi Kuphunzira Baibulo

4, 5. Kodi cholinga cha Phunziro la Nsanja ya Olonda n’chiyani?

4 Tonsefe timafuna kuti tizipindula kwambiri ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda lomwe limachitika mlungu uliwonse. Choncho, kuti timvetse bwino cholinga chachikulu cha msonkhano umenewu, tiyeni tikambirane zinthu zina ndi zina zimene zasintha m’magazini ya Nsanja ya Olonda ndiponso mu nkhani zophunzira.

5 Kuyambira ndi Nsanja ya Olonda yophunzira ya January 15, 2008, pachikuto cha magaziniyi panaikidwa chinthu china chofunika kwambiri. Kodi mwachiona? Tayang’anani bwinobwino chikuto cha magazini imene mwatengayi. M’munsi mwa nsanjayo muli chithunzi cha Baibulo lotsegula. Chithunzi chimenechi chikutsindika cholinga cha Phunziro la Nsanja ya Olonda. Cholinga chake ndi kuphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito magazini amenewa. Mlungu uliwonse pa Phunziro la Nsanja ya Olonda, Mawu a Mulungu ‘amafotokozedwa’ ndipo mofanana ndi nthawi ya Nehemiya, anthu amathandizidwa ‘kumvetsa tanthauzo’ la mawuwo.​—Neh. 8:8; Yes. 54:13.

6. (a) Kodi n’chiyani chimene chasinthidwa pa Phunziro la Nsanja ya Olonda? (b) Kodi tiyenera kukumbukira chiyani pa malemba osonyezedwa kuti “werengani”?

6 Popeza kuti Baibulo ndi buku lalikulu limene timaphunzira, Phunziro la Nsanja ya Olonda linasinthidwa zina ndi zina. Malemba ena m’nkhani yophunzira amalembedwa kuti “werengani.” Tonsefe tikulimbikitsidwa kuti malemba amenewa akamawerengedwa ifenso tiziwawerenga m’Baibulo lathu. (Mac. 17:11) N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika? Tikaona malangizo a Mulungu m’Baibulo lathu, timakhudzidwa mtima kwambiri. (Aheb. 4:12) Choncho, malembawa asanawerengedwe, wochititsa phunziroli ayenera kudikira kuti onse apeze lembalo n’cholinga chakuti azitsatira likamawerengedwa.

Timakhala ndi Nthawi Yambiri Yofotokoza Chikhulupiriro Chathu

7. Kodi timakhala ndi mwayi wochita chiyani pa Phunziro la Nsanja ya Olonda?

7 Chinthu chinanso chimene chasintha, ndi chakuti m’zaka za posachedwapa nkhani zophunzira mu Nsanja ya Olonda ndi zazifupi. Choncho, pa Phunziro la Nsanja ya Olonda, nthawi yambiri sithera kuwerenga ndime koma kuyankha. Anthu ambiri mu mpingo amakhala ndi mwayi wofotokoza zimene amakhulupirira. Iwo amachita zimenezi mwa kuyankha mafunso, kusonyeza kugwirizana pakati pa lemba ndi nkhani, kupereka chitsanzo chosonyeza ubwino wogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo komanso mwa njira zina. Pamafunikanso kugwiritsa ntchito nthawi ina pokambirana zithunzi.​—Werengani Masalimo 22:22; 35:18; 40:9.

8, 9. Kodi amene amachititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda ali ndi udindo wotani?

8 Komabe, kuti pakhale nthawi yokwanira kuti anthu osiyanasiyana apereke ndemanga, pamafunika kuti anthu azipereka ndemanga zazifupi. Pamafunikanso kuti wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda azipewa kulankhula zambiri. Ndiyeno kodi n’chiyani chingathandize wochititsa phunziroli kuti agawe bwino nthawi yolankhula iyeyo, komanso yoti anthu ena apereke ndemanga, n’cholinga choti phunziroli likhale lolimbikitsa kwa anthu onse?

9 Kuti tiyankhe funsoli taganizirani fanizo ili. Phunziro la Nsanja ya Olonda lochititsidwa bwino limakhala ngati ndiwo zophikidwa bwino. Chimene chimachititsa kuti ndiwozi zikhale zokoma n’chakuti amaikamo zinthu zosiyanasiyana monga nsinjiro ndi tomato. N’chimodzimodzinso ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda. Chimene chimachititsa kuti likhale losangalatsa, ndi ndemanga zosiyanasiyana zimene abale ndi alongo amapereka. Nanga kodi udindo wa wochititsa phunziroli ndi wotani? Ndemanga zimene amapereka mwa apa ndi apo zili ngati mchere umene timathira m’ndiwo. Mcherewu sukhala wambiri koma umachititsa kuti ndiwozo zikhale zokoma. Mofanana ndi zimenezi, wochititsa phunziroli ayenera kukumbukira kuti udindo wake si kulankhula mfundo zambirimbiri koma kungolankhula mwa apa ndi apo n’cholinga choti phunzirolo liyende bwino ndiponso kuti ndemanga za abale ndi alongo zigwirizane ndi nkhaniyo. Motero, ndemanga zosiyanasiyana zimene abale ndi alongo amapereka limodzi ndi mawu a apa ndi apo amene wochititsa amanena, zimachititsa kuti phunziro lonselo likhale losangalatsa ngati ndiwo zophikidwa bwino.

‘Tiyeni Nthawi Zonse Tizipereka Nsembe Yotamanda Mulungu’

10. Kodi Akhristu oyambirira ankaiona bwanji misonkhano yampingo?

10 Mmene Paulo anafotokozera misonkhano yachikhristu pa 1 Akorinto 14:26-33, zimatithandiza kudziwa mmene misonkhano inkachitikira m’nthawi ya atumwi. Pofotokoza mavesi amenewa, katswiri wina wa Baibulo analemba kuti: “N’zochititsa chidwi kuti pa misonkhano ya Tchalitchi choyambirira, pafupifupi aliyense akamapita ku misonkhano ankadziwa kuti ali ndi mwayi ndiponso udindo wochitapo kenakake. Palibe amene ankabwera kuti azidzangomvetsera. Aliyense ankabwera osati kudzangolandira koma kuti nayenso adzapereke kenakake.” Choncho, Akhristu oyambirira ankaona kuti misonkhano yampingo inkawapatsa mwayi wofotokoza chikhulupiriro chawo.​—Aroma 10:10.

11. (a) Kodi n’chiyani chimathandiza kwambiri kuti misonkhano yathu ikhale yolimbikitsa ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kuti tizipereka ndemanga zabwino pa misonkhano? (Onani mawu a m’munsi.)

11 Kufotokoza chikhulupiriro chathu pa misonkhano yampingo kumathandiza kwambiri kuti ‘timange mpingo.’ Inunso mungavomereze kuti kaya takhala tikupezeka pa misonkhano kwa zaka zingati, timasangalalabe kwambiri tikamamva ndemanga zimene abale ndi alongo amapereka. Timakhudzidwa kwambiri Mkhristu mnzathu wachikulire akapereka ndemanga yochokera mumtima. Timalimbikitsidwanso kwambiri ngati mkulu wachikondi watchula mfundo yothandiza kwambiri ndipo timachita chidwi kwambiri kamwana kakakhudzidwa mtima n’kupereka ndemanga yosonyeza kuti kamakonda kwambiri Yehova. Apatu n’zoonekeratu kuti ndemanga za tonsefe zimathandiza kuti misonkhano yachikhristu ikhale yolimbikitsa. *

12. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzo za Mose ndi Yeremiya? (b) Kodi pemphero lingatithandize bwanji pa nkhani yopereka ndemanga?

12 Anthu amene mwachibadwa ndi amantha amavutika kwambiri kuti apereke ndemanga. Ngati inu mumachita mantha musaganize kuti muli nokha. Ndipotu atumiki a Mulungu okhulupirika monga Mose ndi Yeremiya ankadzionanso kuti sangathe kulankhula bwinobwino pa gulu. (Eks. 4:10; Yer. 1:6) Yehova anathandiza atumiki akalewa kumutamanda pa gulu ndipo angathandizenso inuyo kuti muzipereka nsembe zomutamanda. (Werengani Aheberi 13:15.) Kodi mungatani kuti Yehova akuthandizeni kuthana ndi vuto la mantha popereka ndemanga? Choyamba, muyenera kukonzekera bwino misonkhano. Ndiyeno musanapite ku Nyumba ya Ufumu, muzipemphera kwa Yehova n’kutchula mwachindunji kuti akulimbitseni mtima kuti mukapereke ndemanga. (Afil. 4:6) Pemphero lotereli ‘n’logwirizana ndi chifuniro chake,’ choncho musamakayike zoti pemphero lanu liziyankhidwa.​—1 Yoh. 5:14; Miy. 15:29.

Misonkhano Imene Cholinga Chake Ndi ‘Kutithandiza, Kutilimbikitsa Ndiponso Kutitonthoza’

13. (a) Kodi misonkhano yathu iyenera kukhudza bwanji anthu? (b) Tchulani funso lofunika kwambiri kwa akulu.

13 Paulo ananena kuti cholinga chachikulu cha misonkhano ya mpingo ndi ‘kutithandiza, kutilimbikitsa ndiponso kutitonthoza.’ * (1 Akor. 14:3) Kodi akulu achikhristu masiku ano angatani kuti mbali zawo pa misonkhano zizikhala zolimbikitsa ndiponso zotonthoza kwa abale ndi alongo? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione za msonkhano umene Yesu anachititsa atangoukitsidwa kumene.

14. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinachitika Yesu asanachititse msonkhano? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mitima ya atumwi inakhala m’malo ‘Yesu atayandikira ndi kulankhula nawo’?

14 Choyamba, ganizirani zimene zinachitika Yesu asanachititse msonkhanowu. Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, atumwi “anathawa ndi kumusiya yekha” ndipo mogwirizana ndi ulosi iwo ‘anabalalika aliyense kupita kunyumba kwake.’ (Maliko 14:50; Yoh. 16:32) Ndiyeno ataukitsidwa, Yesu anaitana atumwi, omwe pa nthawiyo anali achisoni, ku msonkhano wapadera. * ‘Atumwi 11 anapita ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anakonza zoti akakumane nawo.’ Ndiyeno atafika, “Yesu anayandikira ndi kulankhula nawo.” (Mat. 28:10, 16, 18) Taganizirani mmene atumwiwo anamvera Yesu atachita zimenezi. Kodi Yesu anakambirana nawo za chiyani?

15. (a) Kodi Yesu anakambirana nkhani ziti ndi ophunzira ake nanga ndi zinthu ziti zimene sanatchule? (b) Kodi msonkhano umenewu unakhudza bwanji atumwi?

15 Yesu anayamba ndi mawu akuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine.” Kenako anawapatsa ntchito yoti achite. Iye anati: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.” Ndiyeno pomaliza anawauza mawu olimbikitsa akuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse.” (Mat. 28:18-20) Kodi mwaona zimene Yesu sanachite? Iye sanakalipire atumwiwo, kapena kupezerapo mwayi pa msonkhanowu kuti akayikire zolinga zawo. Komanso iye sanawonjezere chisoni chawo mwa kuwakumbutsa za kufooka kwa chikhulupiriro chawo. M’malomwake, Yesu anawatsimikizira kuti iye pamodzi ndi Atate wake amawakonda mwa kuwapatsa udindo waukulu. Kodi zimenezi zinawakhudza bwanji atumwiwo? Iwo analimbikitsidwa, kuthandizidwa ndiponso kutonthozedwa kwambiri moti patapita kanthawi, iwo anayambiranso “kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino.”​—Mac. 5:42.

16. Popeza Yesu anachititsa msonkhano wotsitsimula, kodi akulu masiku ano amamutsanzira bwanji pa nkhaniyi?

16 Potsanzira Yesu, akulu masiku ano amaona kuti nthawi ya misonkhano imawapatsa mpata wotsimikizira okhulupirira anzawo kuti Yehova amakonda kwambiri anthu ake. (Aroma 8:38, 39) Choncho akamakamba nkhani zawo pa misonkhano, akulu amanena kwambiri zabwino zimene abale awo amachita osati zimene amalephera. Iwo sakayikira zolinga za abale awo. M’malomwake, iwo amasonyeza kuti amaona Akhristu anzawo kuti ndi anthu okonda Yehova ndiponso amafuna kuchita zinthu zabwino. (1 Ates. 4:1, 9-12) N’zoona kuti akuluwo nthawi zina amafunika kupereka malangizo okhudza mpingo wonse. Koma ngati ndi anthu ochepa chabe amene akufunika kulangizidwa, ndi bwino kupereka malangizowo mwachindunji kwa anthu amene akuwafunikira. (Agal. 6:1; 2 Tim. 2:24-26) Polankhula ndi mpingo wonse, akulu ayenera kukhala ndi cholinga choyamikira mpingowo ngati pakufunika kutero. (Yes. 32:2) Iwo amayesetsa kulankhula m’njira imene ingachititse kuti pamapeto pa misonkhano, aliyense azimva kuti watsitsimulidwa ndiponso walimbikitsidwa.​—Mat. 11:28; Mac. 15:32.

Timalimbikitsidwa ku Misonkhano Yathu

17. (a) N’chifukwa chiyani zili zofunika kwambiri kuti misonkhano yathu izikhala yolimbikitsa masiku ano? (b) Kodi inuyo mungatani kuti misonkhano izikhala yolimbikitsa? (Onani bokosi lakuti, “Mfundo 10 Zothandiza Kuti Misonkhano Izikhala Yolimbikitsa.”)

17 Dziko la Satanali likuipiraipira choncho tiyenera kuyesetsa kuti misonkhano yathu izikhala yolimbikitsa ndiponso yotonthoza. (1 Ates. 5:11) Mlongo wina amene anapirira vuto lalikulu pamodzi ndi mwamuna wake zaka zingapo zapitazo anati: “Tikakhala ku Nyumba ya Ufumu tinkamva ngati kuti tili m’manja mwa Yehova ndipo akutisamalira. Maola amene tinkakhala kumeneko limodzi ndi abale ndi alongo, tinkaona kuti ndi nthawi imene tinkatulira Yehova nkhawa zathu ndipo tinkapeza mtendere wa mumtima.” (Sal. 55:22) Zingakhale bwino kuti onse amene amafika pa misonkhano yathu azilimbikitsidwa ndiponso kutonthozedwa ngati mmene zinalili ndi banjali. Kuti izi zitheke tiyeni tonse tizichita mbali yathu kuti misonkhano izikhala yolimbikitsa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Ulosi unaneneratu kuti zinthu zina zimene zinkachitika pa misonkhano yachikhristu m’nthawi ya atumwi zidzatha. Mwachitsanzo, panopa ‘sitilankhula malilime’ kapena “kunenera.” (1 Akor. 13:8; 14:5) Ngakhale zili choncho, malangizo a Paulo akutithandiza kumvetsa mmene tiyenera kuchitira misonkhano yachikhristu masiku ano.

^ ndime 11 Kuti mudziwe mfundo zimene zingatithandize kupereka ndemanga zabwino, onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 2003, tsamba 19 mpaka 22.

^ ndime 13 Buku lina limafotokoza kusiyana pakati pa “kulimbikitsa” ndi “kutonthoza.” Bukuli limanena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kutonthoza” ndi mawu “achikondi kwambiri kuposa mawu amene anawamasulira kuti [kulimbikitsa].”​—Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words; Yerekezerani ndi Yohane 11:19.

^ ndime 14 N’kutheka kuti msonkhano umenewu ndi umene Paulo ankanena pamene analemba kuti Yesu “anaonekeranso kwa abale oposa 500.”​—1 Akor. 15:6.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi misonkhano yachikhristu ndi yofunika bwanji?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti ndemanga zimene zimaperekedwa pa misonkhano zimathandiza ‘kumanga mpingo’?

• Kodi tikuphunzira chiyani pa msonkhano umene Yesu anachita ndi otsatira ake?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi pamasamba 22, 23]

MFUNDO 10 ZOTHANDIZA KUTI MISONKHANO IZIKHALA YOLIMBIKITSA

Muzikonzekera. Mukakonzekera nkhani zimene mukaphunzire ku Nyumba ya Ufumu, mumakhala ndi chidwi kwambiri pa misonkhano ndipo zimene mwaphunzira zimakhazikika m’maganizo mwanu.

Muzipezekapo nthawi zonse. Munthu aliyense amalimbikitsidwa ngati anthu ambiri afika pa misonkhano, choncho muziyesetsa kupezekapo nthawi zonse.

Muzifika pa nthawi yabwino. Ngati mungamafike misonkhano isanayambe, muziimba nawo nyimbo yoyamba ndiponso kukhalapo pa nthawi ya pemphero loyamba, zomwe ndi mbali ya kulambira kwathu Yehova.

Muzitenga zonse zofunika. Pobwera ku misonkhano muzitenga Baibulo lanu ndi mabuku amene agwiritsidwe ntchito pa misonkhanopo n’cholinga choti muzitsatira ndiponso kuti mumvetse bwino zimene zikuphunziridwa.

Muzipewa zododometsa. Mwachitsanzo, musamawerenge uthenga pa foni yanu ya m’manja misonkhano ili mkati. Muyenera kuchita zimenezi misonkhano ikatha. Mukamatero mumasonyeza kuti mumachita zinthu zoyenera pa nthawi yake.

Muziyankha pa misonkhano. Abale ndi alongo ochuluka akamapereka ndemanga, anthu ambiri amalimbikitsidwa ndi ndemanga zosiyanasiyana zofotokoza chikhulupiriro chawo.

Ndemanga zanu zizikhala zazifupi. Kuchita zimenezi kumapereka mpata woti anthu ambiri apereke ndemanga.

Muzikwaniritsa mbali imene mwapatsidwa. Ngati mwapatsidwa nkhani mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, kapena ngati muli ndi mbali mu Msonkhano wa Utumiki, muyenera kukonzekera bwino, kuyeseza ndiponso kukwaniritsa mbali yanu.

Muziyamikira anthu amene atenga nawo mbali. Muziyamikira anthu amene akamba nkhani kapena kuyankha pa misonkhano, n’kuwauza kuti mumayamikira zimene amachita.

Muzicheza ndi anthu amene afika pa misonkhano. Kupereka moni mokoma mtima ndiponso kukambirana nkhani zolimbikitsa, misonkhano isanayambe kapena itatha, kumathandiza kuti anthu amene abwera asangalale komanso kuti apindule.