Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito Yapadera ku Bulgaria Inali ndi Zotsatira Zabwino

Ntchito Yapadera ku Bulgaria Inali ndi Zotsatira Zabwino

Ntchito Yapadera ku Bulgaria Inali ndi Zotsatira Zabwino

“Zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.”​—MAT. 9:37, 38.

MAWU a Yesu amenewa akufotokoza bwino mmene zinthu zilili ku Bulgaria, dziko lokongola limene lili m’chigawo chotchedwa Balkan, kum’mwera chakum’mawa kwa Ulaya. Pakufunikadi antchito ambiri kuti alalikire uthenga wabwino kwa anthu oposa 7 miliyoni amene amakhala m’dzikoli. Ku Bulgaria kuli ofalitsa okwana 1,700 koma sangakwanitse kulalikira m’madera onse a dzikoli. Chifukwa cha zimenezi, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti Mboni zochokera m’mayiko osiyanasiyana ku Ulaya, zolankhula Chibugariya zipite kudzikoli kukagwira nawo ntchito yapadera m’chaka cha 2009. Anakonza zoti ntchito yapaderayi ichitike m’chilimwe, kutatsala masabata 7 kuti Msonkhano Wachigawo wakuti “Khalani Maso” uchitike, ku Sofia pa August 14 mpaka 16, 2009.

Abale ndi Alongo Ambiri Anadzipereka

Abale a ku ofesi ya nthambi ku Sofia sankadziwa kuti ndi anthu angati amene angadzipereke kuchokera ku France, Germany, Greece, Italy, Poland, ndi Spain. Abale amene anadzipereka kukagwira nawo ntchito imeneyi, anafunika kugwiritsa ntchito ndalama zawo ndiponso masiku awo a tchuthi. Zinalitu zosangalatsa kwambiri kuona kuti mlungu uliwonse anthu amene ankadzipereka kuti akagwire nawo ntchito imeneyi ankawonjezeka mpaka kufika 292. Izi zinachititsa kuti abale ndi alongowa atumizidwe m’mizinda itatu ya ku Bulgaria yomwe ndi Kazanlak, Sandanski, ndi Silistra. Ndiponso oyang’anira madera anapempha apainiya ndi ofalitsa a ku Bulgaria kuti athandize pa ntchitoyi. Pamapeto pake anthu odzipereka okwana 382 ankalalikira mwakhama m’madera amene uthenga wabwino sunkalalikidwa kawirikawiri.

Nthawiyi isanakwane, abale a m’mipingo yapafupi anatumizidwa kuti akakonze malo ogona. Iwo anachita lendi nyumba ndiponso mahotela otsika mtengo. Abalewa anagwira ntchito mwakhama kwambiri pofuna kuthandiza amene anadzipereka kudzagwira ntchitoyi kuti apeze pofikira ndiponso zinthu zina zofunika. M’mizinda yonse itatu imene tatchula ija, anachita lendi malo oti azichitira misonkhano. Anakonzanso zoti abale amene anatumizidwa kuderali azichititsa misonkhano ya mpingo. Zinali zosangalatsa kwambiri kuona kuti m’madera amene kunalibe ngakhale Mboni ndi imodzi yomwe, ofalitsa okwana 50 ankasonkhana kuti atamande Yehova.

Anthu amene anabwera kudzagwira nawo ntchito yapaderayi anasonyeza khama kwambiri. Nthawi ya chilimwe ku Bulgaria kumatentha kwambiri kufika pa 40°C. Koma palibe chikanaletsa abale ndi alongo akhamawa kugwira ntchito imeneyi. Mumzinda wa Silistra, womwe uli mphepete mwa mtsinje wa Danube, mumakhala anthu oposa 50,000. Abale ndi alongo analalikira mumzinda wonsewu m’milungu itatu yoyambirira. Kenako abale analalikiranso midzi yoyandikana ndi mzinda wa Silistra mpaka anakafika ku Tutrakan, mudzi womwe uli pa mtunda wa makilomita 55, kumadzulo kwa mzindawu. Nthawi zambiri ankayamba kulalikira 9:30 m’mawa. Akamaliza kudya masana, ankapitiriza kulalikira mpaka 7:00 madzulo kapena kupitirira. Chifukwa cha khama lawo, abale ndi alongowa analalikiranso m’midzi ndi m’mizinda yapafupi ndi Kazanlak ndi Sandanski.

Zotsatira za Ntchito Yapaderayi

M’milungu 7 imeneyi, abale ndi alongo anachitira umboni kwa anthu ambiri. Mofanana ndi m’nthawi ya atumwi, anthu okhala m’mizinda imeneyi akanatha kunena kuti: ‘Mwadzaza mzinda wathu wonse ndi chiphunzitso chanuchi.’ (Mac. 5:28) Abale ndi alongo amene anagwira ntchito yapaderayi, anagawira magazini pafupifupi 50,000 ndipo anayambitsa maphunziro a Baibulo 482. Chosangalatsa n’chakuti, pofika pa September 1, 2009, mpingo unakhazikitsidwa ku Silistra ndipo tsopano pali magulu akutali ku Kazanlak ndi ku Sandanski. N’zosangalatsa kwambiri kuona kuti anthu amene anayamba kumva choonadi pa nthawi ya ntchito yapaderayi akupita patsogolo mwauzimu.

Pa mlungu woyambirira wa ntchito yapaderayi mlongo wina wa ku Spain, yemwe amalankhula Chibugariya, analalikira kwa mayi wina dzina lake Karina mumzinda wa Silistra, yemwe ankagulitsa nyuzipepala mumsewu. Karina anasonyeza chidwi ndipo anapita ku misonkhano. Iye anavomera kuti aziphunzira Baibulo koma chifukwa chakuti mwamuna wake sakhulupirira zoti kuli Mulungu, Karina anasankha zoti azikaphunzirira ku paki. Ana ake aakazi awiri ankakhala nawo pa phunziro la Baibuloli. Pa ana ake awiriwa, wamkulu dzina lake ndi Daniela ndipo anasonyeza chidwi kwambiri. Pakutha kwa mlungu umodzi, Daniela anali atamaliza kuwerenga buku lonse la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo anayamba kutsatira zimene Baibulo limanena kuti sitiyenera kugwiritsa ntchito zifanizo polambira. Kenako anayamba kuuza anzake choonadi. Patangotha milungu itatu yokha kuchokera pa tsiku limene anayamba kupezeka pa misonkhano, Daniela anauza mlongo amene ankamuphunzitsa Baibulo uja kuti: “Ndikungomva ngati inenso ndine wa Mboni za Yehova. Kodi ndingatani kuti inenso ndizilalikira?” Panopa Daniela, mayi ake ndiponso mng’ono wake akupitabe patsogolo.

Ku Kazanlak, kunali m’bale wina wolankhula Chibugariya dzina lake Orlin amene anachokera ku Italy kudzagwira nawo ntchitoyi. Tsiku lina akuchokera mu utumiki analalikira anyamata awiri amene anakhala pa benchi m’paki ina. Anawagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo anagwirizana zokumananso tsiku lotsatira. Pa ulendo wotsatirawo, Orlin anayambitsa phunziro la Baibulo ndi Svetomir ndipo anapangana kuti akumanenso tsiku lotsatira. Pa masiku 9 okha, Orlin anaphunzira ndi Svetomir maulendo 8. Kenako Svetomir ananena kuti: “Nthawi imene tinkakumana ija, n’kuti patangopita masiku awiri kuchokera pamene ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kumudziwa bwino. Ndinalonjezanso kuti akandithandiza ndidzadzipereka kwa iye.” Orlin atabwerera ku Italy, abale a ku Bulgaria anapitiriza kuphunzira Baibulo ndi Svetomir ndipo iye akukonda kwambiri choonadi.

Anthu Amene Anadzipereka Anadalitsidwa Kwambiri

Kodi anthu amene anadzipereka kugwiritsa ntchito ndalama zawo ndiponso masiku awo a tchuthi kuti akalalikire uthenga wabwino m’dzikoli anamva bwanji? M’bale wina amene ndi mkulu ku Spain analemba kuti: “Ntchito yapaderayi yagwirizanitsa abale a ku Spain olankhula Chibugariya. Yathandiza kwambiri abale amene anagwira nawo ntchitoyi.” Banja lina la ku Italy linalemba kuti: “Pa moyo wathu wonse, mwezi umenewu ndi umene unali wosangalatsa kwambiri.” Ananenanso kuti: “Ntchito imeneyi yasintha kwambiri moyo wathu. Panopa tasinthiratu.” Banja limeneli linayamba kuganizira zosamuka n’kukakhala ku Bulgaria kuti lizikatumikira kudera limene kulibe ofalitsa ambiri. Carina ndi mlongo wosakwatiwa wa ku Spain ndipo akuchita upainiya wokhazikika. Iye anagwira nawo ntchito yapadera ku Silistra. Kenako mlongoyu anasiya ntchito ku Spain n’kusamukira ku Bulgaria kukatumikira mu mpingo watsopano umene unakhazikitsidwa mumzinda umenewu. Iye anali atasunga ndalama zoti akagwiritse ntchito ku Bulgaria kwa chaka chimodzi. Pofotokoza zimene anasankhazi Carina anati: “Ndine wosangalala kwambiri kuti Yehova wandilola kutumikira ku Bulgaria kuno ndipo ndikukhulupirira kuti ndikhala kuno kwa nthawi yaitali ndithu. Panopa ndili ndi maphunziro a Baibulo asanu ndipo atatu mwa ophunzirawa amapezeka pa misonkhano ya mpingo.”

Mlongo wina wa ku Italy ankafuna kugwira nawo ntchito yapaderayi, koma anali atangoyamba kumene ntchito choncho analibe masiku a tchuthi. Komabe zimenezi sizinamulepheretse cholinga chakechi. Iye anapempha kuti akhale patchuthi kwa mwezi umodzi popanda kumupatsa malipiro. Mlongoyu anali wokonzeka kusiya ntchito ngati sakanamulola kutenga tchuthi. Iye anadabwa pamene bwana wake anamuuza kuti: “Ukhoza kupita ngati ukudziwa kuti ukapita ku Bulgariako ukanditumizira khadi.” Mlongoyu anaona kuti Yehova wayankha mapemphero ake.

Mlongo wina wachitsikana dzina lake Stanislava, yemwe ankakhala mumzinda wa Varna ku Bulgaria ankagwira ntchito ya ndalama zambiri yomwe inkamutengera nthawi yambiri. Iye anatenga tchuthi kuti akagwire nawo ntchito yapaderayi ku Silistra. Iye analira ataona mmene apainiya ambiri amene anachokera kumayiko ena kudzagwira nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino m’dziko lawo ankasangalalira. Iye anayamba kuona kuti sakugwiritsa ntchito bwino moyo wake chifukwa ankangogwira ntchito yolembedwa. Patatha milungu iwiri anabwerera kwawo ndipo anasiya ntchito n’kuyamba upainiya wokhazikika. Panopa iye amaona kuti ndi wosangalaladi chifukwa akukumbukira Mlengi wake pamene ali wachinyamata.​—Mlal. 12:1.

Ndi madalitso aakulu kutumikira Yehova mwakhama. Palibenso chinthu china chofunika kwambiri kuposa kupereka nthawi ndi mphamvu zanu pa ntchito yofunika kwambiri yomwe ndi yophunzitsa ndiponso kulalikira uthenga wabwino. Kodi pali zimene mungachite kuti muzichita zambiri pa ntchito yopulumutsa moyo imeneyi? N’kutheka kuti ngakhale m’dziko lanu muli madera ena amene kukufunika ofalitsa ambiri. Kodi mungasamukire kumadera amenewa? Apo ayi, mukhoza kuphunzira chinenero china kuti muthandize anthu amene ali ndi ludzu la choonadi cha m’Baibulo m’dziko lanu lomwelo. Dziwani kuti Yehova adzakudalitsani kwambiri chifukwa cha zilizonse zimene mungachite pofuna kuchita zambiri mu utumiki.​—Miy. 10:22.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 32]

Tsiku Losaiwalika

Ambiri mwa anthu amene anachokera m’mayiko ena ku Ulaya, kudzagwira nawo ntchito yapaderayi ku Bulgaria, anakonza zopezeka nawo pa Msonkhano Wachigawo wakuti, “Khalani Maso” ku Sofia. Abale ndi alongo a kumeneku analimbikitsidwa kwambiri pamene anakumana ndi alendo ambiri ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Anthu 2,039 amene anali pa msonkhanowu anasangalala kwambiri pamene M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira anatulutsa Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures m’chinenero cha Chibugariya. Anthu onse amene anasonkhana Lachisanu anasonyeza chisangalalo chawo mwa kuwomba m’manja kwambiri ndiponso kwa nthawi yaitali. Ena mpaka anayamba kulira chifukwa cha chisangalalo. Baibulo limeneli lomwe linamasuliridwa molondola ndiponso m’njira yosavuta kumva, lithandiza anthu a maganizo abwino ku Bulgaria kuti adziwe Yehova.

[Mapu pamasamba 30, 31]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

BULGARIA

SOFIA

Sandanski

Silistra

Kazanlak

[Zithunzi patsamba 31]

Abale ndi alongo anachitira umboni mogwira mtima kwa milungu 7