Kutumikira pa Nthawi Imene Ntchito Yolalikira Yapita Patsogolo Kwambiri
Kutumikira pa Nthawi Imene Ntchito Yolalikira Yapita Patsogolo Kwambiri
Yosimbidwa ndi Harley Harris
Pa September 2, 1950, tinali pa msonkhano wa dera ku Kennett, Missouri, m’dziko la United States. Tinazunguliridwa ndi gulu la anthu olusa. Meya wa mzindawu anatumiza asilikali a boma kuti adzatiteteze. Asilikali okhala ndi mfuti komanso mipeni yoika kutsogolo kwa mfuti anaima mumsewu. Anthu ankatinena pamene tinkapita kukakwera magalimoto athu kupita ku Cape Girardeau ku Missouri kuti tikamalize msonkhanowu. Uku n’kumene ndinabatizidwa ndipo pa nthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 14. Mwina ndifotokoze kaye mmene ndinayambira kutumikira Yehova pa nthawi yovutayi.
CHA kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1930, agogo anga ndi ana awo 8 anamvetsera nkhani za M’bale Rutherford ndipo anakhulupirira kuti apezadi choonadi. Bambo anga a Bay Harris ndi mayi anga a Mildred Harris anabatizidwa mu 1935 pa msonkhano wachigawo umene unachitikira ku Washington, D.C. Pa msonkhano umenewu zinadziwika kuti pali “khamu lalikulu.” Iwo anasangalala kwambiri pozindikira kuti anali m’gulu la “khamu lalikulu” limeneli.—Chiv. 7:9,14.
Ine ndinabadwa chaka chotsatira. Patapita chaka chimodzi, makolo anga anasamukira kudera lina la kumidzi ku Mississippi. Pa nthawi imene tinkakhala kuderali, panalibe woyang’anira dera amene ankabwera kudzatichezera. Banja lathu linkalemberana makalata ndi abale a ku Beteli, komanso tinkapezeka pa misonkhano ya dera. Pa nthawiyi, ndi zinthu zokhazi zimene zinkatithandiza kuyanjana ndi abale.
Kupirira pa Nthawi ya Chizunzo
Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, Mboni za Yehova zinkazunzidwa kwambiri chifukwa chakuti sizinkapita nawo kunkhondo. Pamene zimenezi zinkachitika n’kuti titasamukira ku Mountain Home, mumzinda wa Arkansas. Tsiku lina ine ndi bambo anga tikulalikira mumsewu, munthu wina anangotulukira mwadzidzidzi n’kutsomphola magazini a bambo anga ndipo anawaotcha pomwepo. Iye ananena kuti ndife anthu amantha chifukwa chakuti sitipita ku nkhondo. Popeza pa nthawiyo ndinali ndi zaka zisanu zokha, ndinayamba kulira. Bambo anga ankangomuyang’ana munthu uja osalankhula chilichonse mpaka munthuyo anachoka.
Panalinso anthu abwino amene ankatikomera mtima. Tsiku lina gulu la anthu olusa litazungulira galimoto yathu, loya wina anafika pamalopo n’kufunsa kuti: “Chikuchitika n’chiyani?” Bambo wina anayankha kuti, “Amboni za Yehovawa samenyera nkhondo dziko lawo!” Kenako loyayo Mac. 27:3.
anaima pakhomo la galimoto yathu n’kunena kuti: “Ine ndinamenya nawo nkhondo yoyamba ya padziko lonse, ndipo ndimenya nawo yachiwiriyi. Asiyeni anthuwa azipita. Anthu amenewa savutitsa aliyense.” Gululo linanyamuka n’kumapita osayankha kalikonse. Tinayamikira kwambiri anthu abwinowa amene anatisonyeza kukoma mtima kwa umunthu.—Misonkhano ya Chigawo Inatilimbikitsa Kwambiri
Msonkhano wachigawo umene unachitika mu 1941 ku St. Louis, Missouri, unali wa pa nthawi yake. Zikuoneka kuti tinasonkhana anthu oposa 115,000. Gulu la anthu okwana 3,903 linabatizidwa pa msonkhanowu. Ndimakumbukira bwino nkhani imene M’bale Rutherford anakamba ya mutu wakuti, “Ana a Mfumu.” Iye ankalankhula kwa anafe ndipo aliyense analandira buku lokongola la buluu lakuti Ana. Msonkhanowu unandilimbikitsa kwambiri ndipo unandithandiza kukonzekera chaka chotsatira pamene ndinayamba sukulu. Ine ndi ana a achimwene a bambo anga tinachotsedwa sukulu chifukwa choti sitinkachitira sawatcha mbendera. Tinkapita kusukulu tsiku lililonse kuti tikaone ngati oyang’anira sukuluyi asintha maganizo. Nthawi zambiri tinkadutsa njira za m’nkhalango kupita kusukulu koma ankangotibweza. Komabe ndinkaona kuti imeneyi inali njira yosonyezera kuti ndife okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu.
Koma pasanapite nthawi yaitali, Khothi Lalikulu la ku United States linalamula kuti anthu asamakakamizidwe kuchitira sawatcha mbendera. Kenako tinayambanso kupita kusukulu. Aphunzitsi athu anali munthu wabwino kwambiri moti anatiphunzitsa zinthu zonse zimene anzathu anaphunzira ife kulibe. Ana a sukulu anzathunso ankatilemekeza.
Ndimakumbukiranso bwino msonkhano wachigawo umene unachitika mu 1942 ku Cleveland, mumzinda wa Ohio. Pa msonkhanowu M’bale Nathan H. Knorr anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Peace—Can It Last?” (Kodi Padzikoli Padzakhala Mtendere?) Nkhani imeneyi, inafotokoza bwino Chivumbulutso chaputala 17 ndipo inasonyeza kuti pambuyo pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse padzakhala kamtendere ndithu. Chifukwa cha zimenezi anthu ankayembekezera kuti ntchito yolalikira idzapita patsogolo. Pokonzekera zimenezi, sukulu ya Gileadi inatsegulidwa mu 1943. Pa nthawi imeneyi sindinaganizire n’komwe mmene sukuluyi idzandithandizira. Nkhondoyi itatha panakhaladi mtendere ndipo chizunzo chinachepa. Koma nkhondo itayamba ku Korea mu 1950, anthu anayambanso kutsutsa ntchito yathu yolalikira ndipo izi n’zimene zinachititsa kuti zomwe ndafotokoza kumayambiriro kwa nkhani ino, zichitike.
Ndinathandiza Nawo Kuti Ntchito Yolalikira Ipite Patsogolo
Ndinamaliza sukulu ya sekondale m’chaka cha 1954 ndipo patatha mwezi umodzi ndinayamba kuchita upainiya. Nditatumikira ku Kennett, Missouri, kumene gulu la anthu olusa linatizungulira mu 1950, ndinaitanidwa kukatumikira ku Beteli m’mwezi wa March, 1955. Gawo la mpingo umene ndinkasonkhana linaphatikizapo dera la Times Square, lomwe linali m’katikati mwa mzinda wa New York City. Uku kunali kusintha kuchoka moyo wakumudzi kukayamba moyo wa m’tauni. Ndinkatha kulalikira anthu okhala mumzinda wa New York mwa kungowasonyeza mutu wochititsa chidwi wa m’maganizini n’kuwafunsa kuti: “Kodi munadzifunsapo funso ili?” Zimenezi zinkachititsa kuti anthu ambiri azilandira magazini.
Ndili pa Beteli ndinkasangalala kwambiri M’bale Knorr akamachititsa lemba la tsiku. M’baleyu ankafotokoza bwino mavesi a m’Baibulo ndiponso ankasonyeza mmene tingawagwiritsire ntchito bwino pa moyo wathu. Akamalankhula ndi abale osakwatirafe, ankalankhula ngati mmene bambo amalankhulira ndi mwana wake ndipo nthawi zambiri ankatipatsa malangizo a mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi alongo. M’chaka cha 1960, ndinaganiza zokwatira.
Ndinalemba kalata yowadziwitsa abale kuti ndichoka pa Beteli pakatha masiku 30, koma panapita nthawi asanandiyankhe. Ngakhale kuti ndine wamanyazi, patatha masiku 30 ndinalimba mtima n’kuimba foni kufunsa za tsiku limene ndidzanyamuke. M’bale Robert Wallen ndi amene anayankha foniyi ndipo anabwera kumene ndinkagwira ntchito. Iye anandifunsa ngati ndingakonde kuchita upainiya wapadera kapena kuyendera dera. Ndinayankha kuti: “Bob, komatu
ndili ndi zaka 24 zokha ndipo sindidziwa zambiri pa nkhani ya upainiya wapadera kapena kuyang’anira dera.”Kutumikira Monga Woyang’anira Dera
Tsiku lomweli nditafika m’chipinda chomwe ndinkagona ndinapeza enivelopu yaikulu. Munali mafomu awiri oti ndilembepo. Ina inali ya upainiya wapadera, ina ya ntchito yoyang’anira dera. Ndinadabwa kwambiri. Ndinapeza mwayi wamtengo wapatali wotumikira abale ndi alongo m’dera la kumwera cha kumadzulo kwa Missouri ndi kum’mawa kwa Kansas. Ndisanachoke pa Beteli, ndinakhala nawo pa msonkhano wa oyang’anira madera. Kumapeto kwa nkhani yake, m’bale Knorr anati: “Ngakhale kuti ndinu oyang’anira dera kapena chigawo, sikuti mukudziwa zambiri kuposa abale m’dera limene mukukatumikira. Ena akudziwa zambiri kuposa inuyo, kungoti chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wawo sangathe kuchita utumiki umenewu. Mungaphunzire zambiri kwa abale amenewa.”
Mawu amenewa analidi oona. M’bale Fred Molohan ndi mkazi wake komanso mchimwene wake, Charley wa ku Parsons mumzinda wa Kansas, anali zitsanzo zabwino pa nkhaniyi. Iwo anaphunzira choonadi m’zaka za m’ma 1900. Ndinasangalala kwambiri kumva zinthu zambiri zimene zinawachitikira ine ndisanabadwe. Panalinso m’bale wina wachikulire komanso wokoma mtima dzina lake John Wristen wa ku Joplin, mumzinda wa Missouri, yemwe anali atachita upainiya kwa zaka zambiri. Abale amenewa ankalemekeza kwambiri dongosolo la gulu la Mulungu. Ngakhale kuti ndinali wamng’ono kuposa iwowo, ndinkaona kuti ankandilemekeza monga woyang’anira dera wawo.
Mu 1962 ndinakwatira Cloris Knoche, mpainiya wansangala ndiponso watsitsi lofiirira. Titakwatirana, tinapitiriza ntchito yoyang’anira dera. Kukhala ndi abale, kunatithandiza kuti tiwadziwe bwino. Tinalimbikitsa achinyamata kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Jay Kosinski ndiponso JoAnn Kresyman, ndi ena mwa achinyamata a m’dera lathu amene tinawalimbikitsa ndipo izi zinali za pa nthawi yake. Kuyenda nawo limodzi mu utumiki ndiponso kukambirana madalitso amene amabwera chifukwa chokhala moyo wodzimana, kunawalimbikitsa kukhala ndi zolinga zauzimu pa moyo wawo. JoAnn anakhala mpainiya wapadera ndipo Jay anayamba kutumikira pa Beteli. Kenako awiriwa anakwatirana ndipo akhala akugwira ntchito yoyang’anira dera kwa zaka pafupifupi 30.
Kutumikira Monga Amishonale
M’chaka cha 1966, M’bale Knorr anatifunsa ngati tingakonde kukatumikira kudziko lina. Tinayankha kuti: “Tikusangalala kutumikira kunoko, koma ngati pangafunikire thandizo kwina kulikonse, ndife okonzeka kupita.” Mlungu wotsatira, tinaitanidwa kusukulu ya Gileadi. Zinali zosangalatsa kukhalanso pa Beteli pa nthawi imene tinali pa sukulu ya Gileadi limodzi ndi anthu amene ndinkawakonda ndiponso kuwalemekeza. Tinapezanso mabwenzi pakati pa anthu amene tinali nawo kusukuluyi omwe akutumikirabe mokhulupirika mpaka pano.
Ine ndi Cloris tinatumizidwa ku Ecuador ku South America, limodzi ndi Dennis ndi Edwina Crist, Ana Rodríguez ndi Delia Sánchez. Dennis ndi Edwina anapita ku Quito komwe ndi likulu la dziko la Ecuador. Ifeyo ndiponso Ana ndi Delia,
anatitumiza ku Cuenca womwenso ndi mzinda waukulu m’dzikoli. Dera limeneli linali ndi zigawo ziwiri. Mpingo woyambirira wa ku Cuenca unkasonkhana m’nyumba yathu. Tinkasonkhana anthu anayife ndi anthu ena owerengeka. Sitinkadziwa kuti tizigwira bwanji ntchito yolalikira.Ku Cuenca kunali matchalitchi ambiri ndipo masiku a holide anthu ankakhala balalabalala. Anthu a kumeneko anali ndi mafunso ambiri. Mwachitsanzo, nditakumana ndi Mario Polo, katswiri wopalasa njinga ku Cuenca ndinadabwa kwambiri atandifunsa kuti, “Kodi mkazi wachiwerewere wotchulidwa m’buku la Chivumbulutso ndi ndani?”
Tsiku lina Mario anabwera kwathu usiku akuoneka kuti ali ndi nkhawa. M’busa wina wa Evanjeliko anali atam’patsa buku lotsutsa kwambiri Mboni za Yehova. Ndinamuuza Mario kuti ndi bwino kuti atatufe tikumane n’kukambirana. Choncho, tsiku lotsatira Mario anaitana m’busayo ndi ineyo kunyumba kwake. Titakumana, ndinawapempha kuti pa tsikuli tingokambirana za Utatu. M’busayo atawerenga lemba la Yohane 1:1, Mario anafotokoza bwinobwino tanthauzo la lembali. Ndipo izi n’zimene zinkachitika akawerenga lemba lililonse. Zinali zosadabwitsa kuona m’busayo akunyamuka atalephera kupereka umboni wa m’Malemba wosonyeza kuti tiyenera kukhulupirira Utatu. Izi zinachititsa kuti Mario ndi mkazi wake akhulupirire kuti timaphunzitsa choonadi ndipo anayamba kuikira kumbuyo zimene Baibulo limaphunzitsa. Zinali zosangalatsa kuona mipingo ya mumzinda wa Cuenca ikuwonjezeka kufika pa 33. M’dera lonse limene tinkayendera munali mipingo yokwana 63 ndipo uku kunalidi kupita patsogolo kwa ntchito yolalikira.
Ndinaona Kupita Patsogolo kwa Ntchito Yolalikira Ndili pa Nthambi
Mu 1970 ndinauzidwa kuti ndikatumikire ku nthambi ya ku Guayaquil limodzi ndi Al Schullo. Awirife tinkagwira ntchito panthambi. Mabuku akabwera, Joe Sekerak ankagwira ntchito yolongedza mabuku opita ku mipingo yonse 46 ya m’dzikoli. Kwa nthawi ndithu, Cloris ankagwira ntchito yolalikira monga mmishonale, pamene ineyo ndinkagwira ntchito pa Beteli. Iye anathandiza anthu 55 mpaka anabatizidwa ndipo nthawi zambiri anthu atatu kapena asanu amene ankaphunzira nawo, ankabatizidwa pa msonkhano uliwonse.
Mwachitsanzo, Cloris anaphunzirapo ndi mayi wina dzina lake Lucresia amene mwamuna wake anali wotsutsa. Komabe patapita nthawi Lucresia anabatizidwa ndipo anayamba kuchita upainiya wokhazikika. Iye anaphunzitsanso ana ake njira za Yehova. Panopa, ana ake aamuna awiri ndi akulu, wina ndi mpainiya wapadera ndipo mwana wake wamkazi ndi mpainiya wokhazikika. M’dzukulu wake anakwatiwa ndi m’bale wokonda zinthu zauzimu kwambiri ndipo onse akuchita upainiya wapadera. Banja limeneli lathandiza anthu ambiri kuphunzira choonadi.
Pofika mu 1980 panali ofalitsa okwana 5,000 ku Ecuador. Chiwerengerochi chinali chachikulu kwambiri moti sizikanatheka kugwira bwino ntchito yochirikiza ofalitsawa pakaofesi kamene tinali nako. Kenako m’bale wina anapereka malo okwana mahekitala 32 kunja kwa tawuni ya Guayaquil kuti timangepo maofesi a nthambi. Mu 1984 tinayamba kumanga maofesi a nthambi ndiponso Malo a Msonkhano pamalo amenewa ndipo zonsezi zinaperekedwa kwa Yehova mu 1987.
Anthu Ambiri Anadzipereka Kuthandiza
Kwa zaka zambiri, zakhala zolimbikitsa kuona ofalitsa ndi apainiya ochokera kumayiko ena akubwera ku Ecuador kumadera amene kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Mmodzi mwa anthu amenewa yemwe sindimuiwala ndi m’bale Andy Kidd, amene anapuma pa ntchito ya uphunzitsi ku Canada. Iye anasamukira ku Ecuador mu 1985 ali ndi zaka 70 ndipo anatumikira mokhulupirika mpaka mu 2008 pamene anamwalira ali ndi zaka 93. Pa nthawi yoyamba pamene ndinakumana naye, n’kuti ali mkulu yekhayo mu mpingo winawake waung’ono. Ngakhale kuti sankadziwa bwino Chisipanishi, iye anakamba nkhani ya onse ndiponso kuchititsa phunziro la Nsanja ya Olonda. Iye ankachititsanso Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndiponso kukamba nkhani zina mu Msonkhano wa Utumiki. M’dera limeneli, tsopano muli mipingo iwiri ikuluikulu yokhala ndi ofalitsa pafupifupi 200 ndipo muli akulu a komweko ambiri.
Patapita miyezi 8, m’bale Ernesto Diaz amene anasamuka ndi banja lake ku United States kupita ku Ecuador ananena kuti: “Ana athu atatu aphunzira kale chilankhulo cha kuno ndipo amaphunzitsa mogwira mtima. Ndakwaniritsa cholinga changa chimene ndinkaona kuti ndi chovuta kwambiri m’dongosolo lino. Ndine mpainiya, ndipo ndikuchita utumiki wa nthawi zonse ndi banja langa. Tikaphatikiza maphunziro anthu onse a Baibulo, akukwana 25. Zimenezi zathandiza kuti banja lathu likhale logwirizana ndipo koposa zonse ubwenzi wathu ndi Yehova walimba kwambiri kuposa kale.” Timayamikira abale ndi alongo athu okondedwa amenewa.
Mu 1994, maofesi a nthambi anawaonjezera kuwirikiza kawiri. Pofika mu 2005 panali ofalitsa oposa 50,000 ndipo maofesi a nthambi anafunika kuonjezeredwanso. Choncho anaonjezera Nyumba ya Misonkhano, nyumba yogona ndiponso maofesi a omasulira mabuku. Nyumba zatsopano zimenezi anazipereka kwa Yehova pa October 31, 2009.
Pamene ankandichotsa sukulu mu 1942, ku United States kunali Mboni pafupifupi 60,000. Tsopano kuli Mboni zoposa 1 miliyoni. Pamene tinkafika ku Ecuador m’chaka cha 1966, kunali ofalitsa Ufumu pafupifupi 1,400. Koma tsopano kuli ofalitsa oposa 68,000. Ndipo ofalitsawa akhoza kuonjezeka chifukwa pali anthu okwana 120,000 amene akuphunzira Baibulo ndi enanso 232,000 amene anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Khristu, m’chaka cha 2009. Ndithudi, Yehova wadalitsa anthu ake m’njira yodabwitsa kwambiri. N’zosangalatsatu kukhala m’nthawi ndiponso malo amene ntchito yolalikira ikupita patsogolo kwambiri. *
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 34 M’bale Harley Harris anamwalira ali wokhulupirika kwa Yehova pamene nkhani ino inkakonzedwa kuti ifalitsidwe.
[Zithunzi patsamba 5]
Malo a msonkhano pamtetete (mu 1981) ku Guayaquil ndi Nyumba ya Msonkhano (mu 2009) imene yamangidwa pamalo omwewo