Kodi Mwapatula Nthawi Yophunzirira Baibulo?
Kodi Mwapatula Nthawi Yophunzirira Baibulo?
CHAKA chatha, Bungwe Lolamulira linalengeza za kusintha kwa ndandanda yochitira misonkhano, kumene kunachititsa kuti mabanja akhale ndi nthawi yochulukirapo yophunzira ndi kukambirana Baibulo. Ngati ndinu mutu wa banja, onetsetsani kuti mukuchita phunziro la Baibulo la banja nthawi zonse ndi mkazi wanu ndi ana anu. Ngakhale mabanja amene alibe ana azigwiritsa ntchito nthawi imeneyi pophunzira Baibulo limodzi. Abale ndi alongo amene sali pabanja azigwiritsa ntchito bwino nthawi imeneyi pochita phunziro la Baibulo laumwini.
Anthu ambiri anena kuti akuyamikira kwambiri dongosolo lokhala ndi Kulambira kwa Pabanja. Mwachitsanzo, Kevin, yemwe ndi mkulu, analemba kuti: “Mumpingo mwathu tikuchita kusowa mawu oti tikuthokozereni. Akulufe takambirana kuti tionetsetse kuti tikugwiritsa ntchito tsiku lopanda misonkhano limeneli kuphunzira ndi mabanja athu, monga mmene Bungwe Lolamulira latiuzira.”
Jodi, amene mwamuna wake ndi mkulu, analemba kuti: “Tili ndi ana aakazi atatu. Wina ali ndi zaka 15, wina 11, ndipo wina ali ndi zaka ziwiri. Posachedwapa tinasamukira kumpingo wa chinenero chamanja. Timafunika nthawi yaitali ndiponso khama kuti tikonzekere misonkhano yonse. Koma tsopano ndi kusintha kumeneku, tili ndi tsiku lina lowonjezera loti tizingoganizira za kulambira kwa pabanja basi!”
John ndi JoAnn, omwe ndi banja limene likutumikira monga apainiya okhazikika, analemba kuti: “Phunziro lathu la banja linali kuchitika mwa apa ndi apo chifukwa zinali zovuta kupeza nthawi yochitira phunziroli, kuwonjezera pa zinthu zosiyanasiyana zakumpingo zimene timachita. Dongosolo latsopanoli ndi mphatso yochokera kwa Yehova imene ingatitsitsimule mwauzimu, ndipo ingatitsitsimule ngati titagwiritsadi ntchito nthawi yake m’njira yoyenerera.”
Tony, m’bale wosakwatira wa zaka pafupifupi 25, amapatula Lachiwiri madzulo kuti azichita phunziro lake laumwini. Amagwiritsa ntchito masiku ena pamlungu kukonzekera misonkhano yampingo. Tony anati: “Koma ndimasangalala kwambiri makamaka Lachiwiri.” Chifukwa chiyani? Tony akufotokoza kuti: “Limeneli ndi tsiku langa lapadera loti ndikhale ndi Yehova. Kwa maola pafupifupi awiri, ndimaphunzira zinthu zimene zimalimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova. Chifukwa ndili ndi nthawi yambiri yophunzirira, ndimathera nthawi yochulukirapo pa mavesi a m’Baibulo amene ndikuwerenga.” Kodi zotsatira zake zakhala zotani? Tony akuti: “Malangizo a Yehova ayamba kundifika pamtima kwambiri kuposa kale.” Mwachitsanzo, iye anati: “M’buku la Insight, ndinawerenga za ubwenzi wa Davide ndi Jonatani. Ndinaphunzira zambiri kwa Jonatani chifukwa cha mtima wake wodzimana. Chitsanzo chake chandithandiza kwambiri kumvetsa mmene ndingakhalire bwenzi lenileni. Masiku ano ndimangofuna kuti Lachiwiri lifike msanga kuti ndiphunzirenso mfundo zina zamtengo wapatali ngati zimenezi.”
Tili ndi chikhulupiriro kuti atumiki onse a Yehova angapindule kwambiri ngati atagwiritsa ntchito bwino nthawi yowonjezereka imene ali nayo tsopano yochitira phunziro la Baibulo ndi kulambira kwa pabanja kopindulitsadi.