Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala ndi Umbeta
Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala ndi Umbeta
PALI nthano zambiri zimene zimatha ndi mawu akuti, “Kenako anakwatirana n’kumakhala mosangalala moyo wawo wonse.” Mawu amenewa amasonyeza kuti munthu amasangalala akakwatiwa kapena kukwatira. Mfundo imeneyi imaonekanso m’mafilimu ndi m’mabuku achikondi ambiri. Ndiponso m’zikhalidwe zina achinyamata amakakamizidwa kuti akwatire kapena kukwatiwa. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Debby, ananena mawu otsatirawa ali ndi zaka zopitirira 20: “Anthu amakuchititsa kuganiza kuti cholinga chimene mtsikana aliyense ayenera kukhala nacho ndicho kukwatiwa basi. Iwo amati munthu ukalowa m’banja m’pamene umayamba kulemekezedwa komanso kusangalala.”
Koma munthu amene amadziwa mmene Yehova amaionera nkhaniyi saganiza choncho. Ngakhale kuti ukwati unali nkhani yaikulu kwa Aisiraeli, Baibulo limatchula amuna ndi akazi ena amene ankasangalala ndi umbeta. Masiku ano pali Akhristu ena amene asankha kukhala mbeta ndipo pali enanso amene ndi mbeta pa zifukwa zosiyanasiyana. Kaya munthu ndi mbeta pa zifukwa zotani, funso lofunika ndi lakuti: Kodi Mkhristu angatani kuti azisangalala ndi umbeta?
Yesu sanakwatire, ndipotu izi n’zomveka tikaganizira ntchito imene anapatsidwa. Iye anauza ophunzira ake kuti Akhristu ena “angathe” kukhala mbeta. (Mat. 19:10-12) Mawu amenewa akusonyeza kuti munthu angasangalale ndi umbeta ngati wavomereza mumtima mwake kukhala mbeta.
Kodi malangizo amenewa amakhudza anthu okhawo amene asankha kukhala mbeta n’cholinga choti akwanitse kutumikira Mulungu m’njira inayake? (1 Akor. 7:34, 35) Ayi. Taganizirani za Mkhristu amene akufuna kukwatira kapena kukwatiwa koma sakupeza munthu woyenerera. Mlongo wina dzina lake Ana, amene ali ndi zaka zoposa 30, ananena kuti: “Posachedwapa munthu wina kuntchito anandifunsira. Koma munthuyo si wa Mboni. Pang’ono pokha zinandisangalatsa ndithu koma sindinafune kukomedwa ndi maganizo amenewa chifukwa cholinga changa ndi choti ndidzakwatiwe ndi munthu amene adzandithandiza kukhalabe ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova.”
Mofanana ndi Ana, kukhala ndi cholinga chokwatiwa “mwa Ambuye” kumathandiza alongo ambiri kuti asakwatiwe ndi anthu osakhulupirira. * (1 Akor. 7:39; 2 Akor. 6:14) Chifukwa chotsatira malangizo a Mulungu iwo amalolera kukhalabe mbeta, mpaka pa nthawi imene adzapeze munthu woyenera. Ndiyeno kodi angatani kuti azikhala osangalala pa nthawi imeneyi?
Muziona Ubwino Wake
Umbeta ungakhale wosangalatsa ngati munthuyo akuuona moyenera. Mlongo wina wosakwatiwa wa zaka 40, dzina lake Carmen anati: “Ndimasangalala chifukwa choti panopa ndimangoganizira za mmene moyo wanga ulili ndipo sindiganizira kwambiri za mmene ukanakhalira ndikanakhala ndi mwamuna.” N’zoona kuti nthawi zina anthufe timasungulumwa 1 Pet. 5:9, 10.
kapena kukhumudwa. Koma kudziwa kuti pali abale ndi alongo ambiri amene akukumananso ndi mavuto oterewa padziko lonse, kungatilimbikitse kuti tisabwerere m’mbuyo. Yehova wathandiza anthu ambiri kusangalala ndi umbeta komanso kuthana ndi mavuto ena.—Abale ndi alongo ambiri azindikira kuti umbeta uli ndi ubwino wake. Mlongo wina wa zaka 30, dzina lake Ester anati: “Ndazindikira kuti chinsinsi cha kusangalala ndicho kuona ubwino wa chilichonse chimene chikukuchitikira pa moyo. Ndimadziwa kuti kaya ndikwatiwe kaya ndisakwatiwe, ndikamaika zinthu za Ufumu patsogolo Yehova adzandidalitsa.” (Sal. 84:11) Iye anatinso: “N’zoona kuti zimene zandichitikira si zimene ndinkayembekera, koma ndimasangalala ndipo ndizisangalalabe.”
Zitsanzo za M’Baibulo za Anthu Omwe Anali Mbeta
Mwana wamkazi wa Yefita sanali ndi cholinga choti akhale mbeta. Koma lumbiro la bambo ake linachititsa kuti akatumikire kukachisi kwa moyo wake wonse. N’zosachita kufunsa kuti utumiki umenewu unasokoneza zolinga zake zina chifukwa nayenso mwachibadwa ankafuna kukwatiwa. Atazindikira kuti sadzakwatiwa n’kukhala ndi banja lakelake analira kwa miyezi iwiri. Komabe, iye anavomereza zimenezi ndipo kwa moyo wake wonse anatumikira mokhulupirika. Akazi ena a ku Isiraeli ankapita kukamuyamikira chaka chilichonse chifukwa cha mtima wake wodzipereka.—Ower. 11:36-40.
M’masiku a Yesaya, panali amuna ofulika omwe ankakhala osakwatira. N’kutheka kuti zimenezi zinkawapweteka mumtima. Baibulo silitchula chimene chinachititsa kuti akhale otero. Chifukwa cha zimenezi sankapatsidwa udindo pakati pa Aisiraeli ndipo sakanatha kukwatira kapena kukhala ndi ana. (Deut. 23:1) Komatu Yehova ankadziwa mmene ankamvera mumtima mwawo ndipo ankawayamikira chifukwa chomvera mokhulupirika malamulo a m’pangano lake. Iye anawauza kuti adzakhala ndi “malo,” ndiponso “dzina lachikhalire” m’nyumba yake. Izi zikutanthauza kuti anthu oterewa amene anakhalabe okhulupirika adzalandira moyo wosatha mu ulamuliro wa Yesu, yemwe ndi Mesiya. Yehova sadzawaiwala.—Yes. 56:3-5.
Yeremiya naye sanakwatire, koma pa zifukwa zina. Mulungu atamuuza kuti akhale mneneri, anamulangiza kuti asakwatire. Anachita zimenezi chifukwa chakuti inali nthawi yovuta kwambiri komanso chifukwa cha ntchito imene anamupatsa. Iye anati: “Usatenge mkazi, usakhale ndi ana amuna ndi akazi, m’malo muno.” (Yer. 16:1-4) Baibulo silinena mmene Yeremiya anamvera atauzidwa zimenezi, koma limasonyeza kuti iye anali munthu wokonda mawu a Yehova. (Yer. 15:16) Patapita zaka, Yerusalemu anazingidwa kwa miyezi 18, ndipo Yeremiya anapulumuka pa nthawi yoopsa kwambiri imeneyi. N’zosakayikitsa kuti iye sananong’oneze bondo chifukwa anaona ubwino womvera malangizo anzeru amene Yehova anamupatsa oti asakwatire.—Maliro 4:4, 10.
Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala
Anthu otchulidwa m’Baibulo amenewa anali osakwatira koma Yehova anawathandiza ndipo anam’tumikira ndi mtima wonse. Masiku anonso timakhala osangalala tikamachita zambiri potumikira Yehova komanso kuthandiza ena. Baibulo linalosera kuti padzakhala khamu la akazi olalikira uthenga wabwino. (Sal. 68:11) M’khamu limeneli muli alongo osakwatiwa ambirimbiri. Utumiki wawo umabala zipatso ndipo ambiri ali ndi ana auzimu.—Maliko 10:29, 30; 1 Ates. 2:7, 8.
Mlongo wina dzina lake Loli atachita upainiya kwa zaka 14, anati: “Upainiya umandithandiza kugwiritsira ntchito moyo wanga m’njira yopindulitsa. Ndine mbeta koma ndili ndi zochita zambiri pa moyo wanga. Zimenezi zimandithandiza kuti ndisamasungulumwe. Dzuwa likamakalowa ndimakhutira ndi zimene ndachita chifukwa ndimaona kuti utumiki wanga umathandiza kwambiri anthu. Zimenezi zimandipatsa chimwemwe kwambiri.”
Pali alongo ambiri amene aphunzira chinenero chatsopano ndipo amalalikira kwa anthu a chinenero china. Mlongo wotchedwa Ana, amene tam’tchula poyamba uja, anati: “Mumzinda umene timakhala muli anthu ambiri ochokera kumayiko ena.” Iye amakonda kulalikira anthu olankhula Chifalansa. Ana anapitiriza kunena kuti: “Ndaphunzira chinenero chimene chimandithandiza kulankhulana ndi anthu ambiri. Izi zachititsa kuti ndikhale ndi gawo latsopano ndipo ndimasangalala kwambiri ndi ntchito yolalikira.”
Anthu ambiri amene ali mbeta sakhala ndi maudindo ochuluka. Motero ena amakatumikira kudera limene kulibe ofalitsa ambiri. Mlongo wina wosakwatiwa, dzina lake Lidiana, yemwe ali ndi zaka zoposa 30, anatumikirapo kumayiko amene kulibe ofalitsa ambiri. Iye anati: “Ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti munthu ukamachita zambiri potumikira Yehova umapezanso mabwenzi ambiri amene amakukonda. Panopa ndili ndi anzanga apamtima ochokera m’mayiko osiyanasiyana komanso a zikhalidwe zosiyanasiyana. Moyo wanga ndi wosangalatsa kwambiri chifukwa cha anzanga amenewa.”
Baibulo limanena za mlaliki wina dzina lake Filipo, amene anali ndi ana aakazi anayi osakwatiwa omwe ankanenera. (Mac. 21:8, 9) Iwo ayenera kuti anali a changu potengera chitsanzo cha bambo awo. N’kutheka kuti iwo ankagwiritsa ntchito mphatso ya kunenerayi kuti alimbikitse Akhristu a ku Kaisareya. (1 Akor. 14:1, 3) Masiku anonso alongo ambiri osakwatiwa amalimbikitsa ena. Iwo sajomba ku misonkhano komanso amapereka ndemanga zabwino.
Komanso panali Lidiya, Mkhristu wa ku Filipi m’nthawi ya atumwi. Baibulo limati iyeyo ankachereza alendo. (Mac. 16:14, 15, 40) Iye ayenera kuti anali asanakwatiwepo kapena anali wamasiye, koma anali wowolowa manja. Izi zinachititsa kuti azichereza oyang’anira madera monga Paulo, Sila ndi Luka. Masiku anonso anthu amene amachita zimenezi amasangalala.
Zimene Mungachite Kuti Anthu Azikukondani
N’zoona kuti kukhala ndi zochita zambiri n’kofunika, komabe tonsefe timafunanso kuti tizikondedwa. Kodi anthu osakwatira kapena kukwatiwa angatani kuti azidzimva kuti amakondedwa? Choyamba dziwani kuti Yehova amatikonda, kutilimbikitsa komanso kutimvetsera. Pa nthawi zina Mfumu Davide ankakhala wosungulumwa ndiponso ankasowa mtendere koma ankadziwa kuti akapemphera, Yehova amuthandiza. (Sal. 25:16; 55:22) Iye analemba kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Sal. 27:10) Mulungu amauza atumiki ake kuti amuyandikire n’kukhala mabwenzi ake a pamtima.—Sal. 25:14; Yak. 2:23; 4:8.
Komanso tili ndi abale padziko lonse amene amatikonda. Pakati pa abale amenewa tingathe kupeza abambo, amayi, azing’ono ndi azikulu athu. (Mat. 19:29; 1 Pet. 2:17) Akhristu ambiri omwe ndi mbeta amasangalala pochita zinthu zofanana ndi zimene Dorika ankachita. Iye “anali kuchita ntchito zabwino zambiri, ndi kupereka mphatso za chifundo zochuluka.” (Mac. 9:36, 39) Loli uja ananenanso kuti: “Kulikonse kumene ndimapita, ndimayesetsa kupeza mabwenzi mumpingo. Iwo amandikonda komanso kundithandiza ndikalefuka. Kuti anthu amenewa apitirizebe kukhala mabwenzi anga, ndimayesetsa kuwakonda komanso kuwasonyeza chidwi. M’mipingo 8 yomwe ndatumikira ndapeza mabwenzi enieni. Ambiri mwa iwo si amsinkhu wanga chifukwa ena ndi okalamba pomwe ena ndi ocheperapo.” Mumpingo uliwonse mumakhala anthu amene amafuna kukondedwa ndi anzawo. Tikamakhala ndi chidwi ndi anthu amenewa, ndiye kuti tidzawathandiza komanso nawo adzayamba kutikonda.—Luka 6:38.
Mulungu Sadzaiwala
Baibulo limasonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza. Chifukwa cha zimenezi Mkhristu aliyense ayenera kulolera kudzimana zinthu zina ndi zina. (1 Akor. 7:29-31) Anthu amene ndi mbeta chifukwa chofuna kumvera lamulo lakuti akwatire kapena kukwatiwa mwa Ambuye ndi oyenera kulemekezedwa komanso kukondedwa kwambiri. (Mat. 19:12) Koma ngakhale kuti iwo amafunika kudzimana kuti achite zimenezi, anthu oterewa akhoza kukhala osangalala kwambiri.
Lidiana amene tam’tchula kale uja anati: “Ndimasangalala kwambiri chifukwa chakuti ndili pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso ndimamutumikira. Ndaonapo anthu a pa banja amene akusangalala komanso amene sakusangalala. Izi zandithandiza kudziwa kuti ukwati si umene ungadzachititse kuti ndikhale wosangalala.” Yesu ananena kuti munthu amakhala wosangalala ngati ali wopatsa komanso ngati amatumikira ena. Ndipotu Mkhristu aliyense angathe kuchita zimenezi.—Yoh. 13:14-17; Mac. 20:35.
Sitikayika kuti Yehova adzatidalitsa chifukwa cha utumiki uliwonse umene timachita mogwirizana ndi chifuniro chake. Izi zimachititsa kuti tizikhala osangalala. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.”—Aheb. 6:10.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Nkhaniyi sikukhudza alongo okha chifukwa mfundo zake n’zothandizanso kwa abale.
[Mawu Otsindika patsamba 25]
“Ndimasangalala chifukwa choti panopa ndimangoganizira za mmene moyo wanga ulili ndipo sindiganizira kwambiri za mmene ukanakhalira ndikanakhala ndi mwamuna.”—Anatero Carmen
[Chithunzi patsamba 26]
Loli ndi Lidiana amasangalala kutumikira kumene kulibe ofalitsa ambiri
[Chithunzi patsamba 27]
Mulungu amauza atumiki ake kuti amuyandikire