Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yobu Analemekeza Dzina la Yehova

Yobu Analemekeza Dzina la Yehova

Yobu Analemekeza Dzina la Yehova

“Lidalitsike dzina la Yehova.”​—YOBU 1:21.

1. Kodi ndani amene ayenera kuti analemba buku la Yobu, ndipo analilemba liti?

MOSE ali ndi zaka pafupifupi 40, anathawa ku Iguputo poopa Farao ndipo anakakhala ku Midyani. (Mac. 7:23) Ali kumeneko, iye ayenera kuti anamva za mayesero a Yobu, yemwe ankakhala m’dera lapafupi la Uzi. N’kutheka kuti Mose anamvanso zimene zinachitika m’zaka zakumapeto kwa moyo wa Yobu, pamene iye ndi mtundu wa Isiraeli anali pafupi ndi dera la Uzi, kumapeto kwa ulendo wawo wa m’chipululu. Ayuda amakhulupirira kuti Mose ndiye analemba buku la Yobu pambuyo pa imfa ya Yobuyo.

2. Kodi n’chifukwa chiyani buku la Yobu lili lolimbikitsa kwa atumiki a Yehova masiku ano?

2 Buku la Yobu limalimbitsa chikhulupiriro cha atumiki a Mulungu masiku ano. Tikutero chifukwa chakuti nkhani yake imatithandiza kudziwa zinthu zofunika kwambiri zimene zinachitika kumwamba, zimene zotsatira zake zimakhudza zambiri. Zimenezi zimatithandizanso kumvetsa nkhani yaikulu yokhudza ulamuliro wa Mulungu m’chilengedwe chonse. Nkhani ya Yobu imatithandizanso kumvetsa zimene kusunga umphumphu kumatanthauza ndiponso kumvetsa chifukwa chake nthawi zina Yehova amalola kuti atumiki ake avutike. Kuwonjezera pamenepo, buku la Yobu limasonyeza kuti Satana Mdyerekezi ndi Mdani wamkulu wa Yehova komanso anthu onse. Bukuli limasonyezanso kuti anthu opanda ungwiro monga Yobu angakhalebe okhulupirika kwa Yehova ngakhale atakumana ndi mayesero oopsa. Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene zafotokozedwa m’buku la Yobu.

Yobu Anayesedwa ndi Satana

3. Kodi Yobu anali munthu wotani, ndipo n’chifukwa chiyani Satana anamuukira?

3 Yobu anali munthu wolemera ndi wotchuka kwambiri ndiponso kholo la makhalidwe abwino. Zikuoneka kuti iye anali phungu wolemekezeka kwambiri ndipo ankathandiza anthu osowa. Koma koposa zonse, Yobu anali woopa Mulungu. Baibulo limanena kuti Yobu anali munthu “wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.” Inde, chifukwa chimene Satana Mdyerekezi anaukira Yobu chinali kudzipereka kwake kwa Mulungu, osati chuma kapena kutchuka kwake.​—Yobu 1:1; 29:7-16; 31:1.

4. Kodi umphumphu umatanthauza chiyani?

4 Nkhani yoyambirira m’buku la Yobu imafotokoza za msonkhano umene unachitika kumwamba, pamene angelo anaonekera kwa Yehova. Nayenso Satana anali pomwepo ndipo ananeneza Yobu. (Werengani Yobu 1:6-11.) Ngakhale kuti Satana anatchula chuma cha Yobu, cholinga chake chenicheni chinali kutsutsa umphumphu wa Yobu. Mawu akuti “umphumphu” amanena za kukhala woongoka mtima, wopanda cholakwa, wolungama ndi wopanda mlandu. M’Baibulo, umphumphu wa munthu umatanthauza kudzipereka kwake kwa Yehova ndi mtima wonse.

5. Kodi Satana ananena chiyani za Yobu?

5 Satana ananena kuti Yobu ankalambira Mulungu chifukwa cha dyera osati umphumphu wake. Iye ananena kuti Yobu sakanakhala wokhulupirika kwa Yehova ngati Mulungu akanasiya kumudalitsa ndi kumuteteza. Kuti atsutse bodza la Satanali, Yehova analola kuti Satana aukire munthu wokhulupirikayu. Kenako m’tsiku limodzi lokha, Yobu anamva kuti ziweto zake zabedwa ndipo zina zaphedwa, antchito akenso aphedwa ndiponso ana ake 10 afa nthawi imodzi. (Yobu 1:13-19) Kodi Yobu anagonja kwa Satana? Malemba amafotokoza kuti Yobu atagweredwa tsokali, anati: “Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.”​—Yobu 1:21.

6. (a) Kodi n’chiyani chinachitika pamsonkhano winanso kumwamba? (b) Kodi Satana ankaganizanso za ndani pamene anakayikira umphumphu wa Yobu?

6 Kenako, kumwamba kunachitika msonkhano wina. Apanso Satana ananeneza Yobu kuti: “Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake. Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.” Onani kuti apa Satana ananeneza anthu onse. Mwa kunena kuti ‘Munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake,’ Mdyerekezi anakayikira umphumphu wa Yobu komanso wa “munthu” wina aliyense amene amalambira Yehova. Atanena zimenezi, Mulungu analola kuti Satana akanthe Yobu ndi matenda osautsa. (Yobu 2:1-8) Koma mayesero a Yobu sanathere pamenepa.

Zimene Tikuphunzira kwa Yobu

7. Kodi anzake a Yobu ndi mkazi wake anawonjezera bwanji mavuto ake?

7 Poyamba, mkazi wa Yobu nayenso anavutika mofanana ndi mwamuna wake. Kufa kwa ana awo ndi kuwonongeka kwa chuma chawo kuyenera kuti kunamupweteka kwambiri. Ayeneranso kuti zinamuwawa kwambiri kuona mwamuna wake akudwala matenda osautsa. Podandaulira Yobu, iye anati: “Kodi uumiriranso kukhala wangwiro [“umphumphu wako,” NW]? Chitira Mulungu mwano, ufe.” Kenako, kunabwera amuna atatu, Elifazi, Bilidadi ndi Zofari, ati kudzamutonthoza Yobu. Koma iwo anayamba kumuuza mfundo zosocheretsa ndipo anali ‘otonthoza mtima olemetsa.’ Mwachitsanzo, Bilidadi ananena kuti ana a Yobu ayenera kuti anachita zoipa ndipo n’chifukwa chake anafa. Elifazi ananena zosonyeza kuti kuvutika kwa Yobu kunali kulangidwa chifukwa cha zolakwa zimene anachita m’mbuyomo. Iye anachita kufika pokayikira ngati Mulungu amawerengera n’komwe anthu okhulupirika. (Yobu 2:9, 11; 4:8; 8:4; 16:2; 22:2, 3) Ngakhale anakumana ndi mavuto onsewa, Yobu sanataye umphumphu wake. N’zoona kuti Yobu analakwitsa pamene “anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.” (Yobu 32:2) Koma iye anakhalabe wokhulupirika pamavuto onsewa.

8. Kodi Elihu anasonyeza bwanji chitsanzo chabwino kwa amene amapereka uphungu masiku ano?

8 Kenako timawerenga za Elihu, amene anabweranso kudzamuona Yobu. Poyamba Elihu ankangomvetsera pamene Yobu ndi anzake atatuwo ankatsutsana. Ngakhale kuti iye anali wamng’ono kwa amuna anayiwo, Elihu anali wanzeru kwambiri. Iye analankhula ndi Yobu mokoma mtima kusiyana ndi enawo, ndipo ankamutchula dzina lake. Elihu anamuyamikira Yobu chifukwa chakuti anali woongoka mtima. Koma ananenanso kuti Yobu ananyanyira polimbikira kukana kuti iye analibe mlandu. Kenako, Elihu anamutsimikizira Yobu kuti ndi bwino kutumikira Mulungu mokhulupirika nthawi zonse. (Werengani Yobu 36:1, 11.) Elihu ndi chitsanzo chabwino kwa anthu amene amapereka uphungu kwa anzawo masiku ano. Iye anali woleza mtima, anamvetsera bwinobwino, anayamikira zinthu zabwino ndipo anapereka uphungu wolimbikitsa.​—Yobu 32:6; 33:32.

9. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito chiyani pofuna kuthandiza Yobu?

9 Pomaliza, Yobu analandira mlendo wochititsa mantha. Malemba amati: “Pamenepo Yehova anayankha Yobu m’kavumvulu.” Pogwiritsa ntchito mafunso osiyanasiyana, Yehova mokoma mtima koma mosabisa mawu, anathandiza Yobu kuwongolera maganizo ake. Atadzudzulidwa moteremu, Yobu anavomereza kulakwa kwake ponena kuti: “Ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa m’fumbi ndi mapulusa.” Yehova atalankhula ndi Yobu, anadzudzula anzake atatu aja chifukwa sanalankhule “choyenera,” kapena kuti zoona. Choncho, Yobu anawapempherera. Kenako, “Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, pamene anapempherera mabwenzi ake; Yehova nachulukitsa zake zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza.”​—Yobu 38:1; 42:6-10.

Kodi Timakonda Yehova ndi Mtima Wathu Wonse?

10. N’chifukwa chiyani Yehova sanangomusiya kapenanso kungomuwononga Satana?

10 Yehova ndi Mlengi komanso Mfumu ya chilengedwe chonse. Nanga n’chifukwa chiyani iye sanangonyalanyaza mabodza a Mdyerekezi? Mulungu anadziwa kuti kungomusiya Satana kapena kumuwononga sikukanathetsa nkhani imene Satanayo anabutsa. Mdyerekezi anali atanena kuti Yobu, mtumiki wokhulupirika wa Yehova, sakanakhalabe wokhulupirika ngati akanataya chuma chake chonse. Koma Yobu anakhalabe wokhulupirika pamene anayesedwa. Kenako, Satana ananenanso kuti munthu wina aliyense angasiye kutumikira Mulungu moyo wake utakhala pa chiswe. Yobu anavutika, koma sanataye umphumphu wake. Choncho, nkhani ya munthu wokhulupirika koma wopanda ungwiro ameneyu inasonyeza kuti Satana ndi wabodza. Nanga bwanji za anthu ena olambira Mulungu?

11. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti Satana ndi wabodza?

11 Ngati mtumiki wina aliyense wa Mulungu akhalabe wokhulupirika ngakhale atakumana ndi mayesero aakulu amene Satana angabweretse, ndiye kuti iyeyo payekha akusonyeza kuti zimene mdani wankhanza ameneyu amamuneneza ndi zabodza. Mwachitsanzo, Yesu atabwera padziko lapansi anasonyeza kuti Satana ndi wabodza. Inde, iye anali munthu wangwiro ngati kholo lathu loyamba, Adamu. Komabe kukhulupirika kwa Yesu kufikira imfa kunasonyeza kuti Satana ndi wabodza ndipo zimene amaneneza anthu ndi zabodza.​—Chiv. 12:10.

12. Kodi mtumiki aliyense wa Yehova ali ndi mpata komanso udindo wotani?

12 Ngakhale zili choncho, Satana akupitirizabe kuyesa anthu amene amalambira Yehova. Aliyense wa ife ali ndi udindo wosonyeza kuti amatumikira Yehova chifukwa chomukonda osati chifukwa cha dyera. Choncho, kusunga umphumphu kumapatsa aliyense wa ife mpata wosonyeza zimenezi. Kodi timauona bwanji udindo umenewo? Timaona kuti ndi mwayi waukulu kupatsidwa udindo wosonyeza kukhulupirika kwathu kwa Yehova. Komanso n’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira, ndiponso monga mmene zinalili ndi Yobu, Iye salola kuti tikumane ndi mayesero amene sitingathe kuwapirira.​—1 Akor. 10:13.

Satana Ndi Mdani Wankhanza Ndiponso Wampatuko

13. Kodi buku la Yobu limatithandiza kudziwa zotani zokhudza Satana?

13 Malemba Achiheberi amafotokoza zinthu zochititsa manyazi zimene Satana anachita potsutsa Yehova ndiponso powasocheretsa anthu. Ndipo Malemba Achigiriki Achikhristu, amatifotokozera zowonjezereka pa zimene Satana amachita potsutsa Yehova. M’buku la Chivumbulutso timawerenganso kuti posachedwapa Yehova adzasonyeza kuti ndiye woyenera kulamulira ndipo Satana adzawonongedwa kotheratu. Buku la Yobu limatithandiza kudziwa bwino zochita za Satana zachipanduko. Pa nthawi imene kumwamba kunkachitika misonkhano, Satana ankapezekapo. Koma iye sanali ndi cholinga chotamanda Yehova. Mdyerekezi anali ndi zolinga zoipa ndipo ankangofuna kuipitsa mbiri ya ena. Ndipo iye atamuneneza Yobu, analoledwa kuti amuyese, kenako ‘anatuluka Satana pamaso pa Yehova.’​—Yobu 1:12; 2:7.

14. Kodi Satana anasonyeza mtima wotani kwa Yobu?

14 Choncho, buku la Yobu limasonyeza kuti Satana ndi mdani wopanda chifundo wa anthu. Msonkhano umene watchulidwa pa Yobu 1:6 utachitika kumwamba, panadutsa nthawi yosadziwika kufika pamene msonkhano wina umene watchulidwa pa Yobu 2:1 unachitika. Pa nthawiyi, Yobu anayesedwa mwankhanza kwambiri. Ndipo chifukwa cha kukhulupirika kwa Yobu, Yehova ananena kwa Satana kuti: ‘[Yobu] aumirirabe kukhala wangwiro [“umphumphu wake,” NW], chinkana undisonkhezera ndimuwononge kopanda chifukwa.’ Koma Satana sanavomereze kuti zimene ananena zokhudza Yobu zinali zabodza. M’malomwake, iye anapempha kuti Yobu ayesedwenso. Choncho Mdyerekezi anamuyesa Yobu pamene zinthu zinkamuyendera bwino komanso pamene analibe kalikonse. Mwachionekere Satana alibe chisoni kwa anthu osauka kapenanso amene amagweredwa masoka. Iye amadana ndi anthu okhulupirika. (Yobu 2:3-5) Komabe kukhulupirika kwa Yobu kunasonyeza kuti Satana ndi wabodza.

15. Kodi anthu ampatuko amasiku ano amafanana bwanji ndi Satana?

15 Satana anali woyamba kukhala wampatuko. Anthu ampatuko masiku ano amasonyeza makhalidwe ofanana ndi a Mdyerekezi. Maganizo awo ndi oipa ndipo amangokhalira kupezera zifukwa anthu mumpingo, akulu achikhristu komanso Bungwe Lolamulira. Ampatuko ena amaletsa kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova. Iwo safuna kuphunzira za Yehova kapena kumutumikira. Mofanana ndi atate wawo Satana, iwo amafuna kusocheretsa anthu okhulupirika. (Yoh. 8:44) N’chifukwa chake atumiki a Yehova amapeweratu anthu amenewa.​—2 Yoh. 10, 11.

Yobu Analemekeza Dzina la Yehova

16. Kodi Yobu anasonyeza mtima wotani kwa Yehova?

16 Yobu ankagwiritsa ntchito komanso ankalemekeza dzina la Yehova. Ngakhale pamene anauzidwa za imfa ya ana ake, Yobu sananyoze Mulungu. N’zoona kuti Yobu anaganiza molakwika kuti Mulungu ndi amene wamubweretsera mavuto, komabe iye analemekeza dzina la Yehova. Ndipo patsogolo pake Yobu anadzanena kuti: “Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.”​—Yobu 28:28.

17. Kodi n’chiyani chinamuthandiza Yobu kusungabe umphumphu wake?

17 Kodi n’chiyani chinamuthandiza Yobu kusungabe umphumphu wake? N’zodziwikiratu kuti iye anali atalimbitsa kale ubwenzi wake ndi Yehova masoka asanamugwere. Ngakhale kuti tilibe umboni wosonyeza kuti Yobu ankadziwa kuti Satana anali atatsutsa Yehova, iye anatsimikiza mtima kukhalabe wokhulupirika. Iye anati: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro [“umphumphu,” NW] wanga.” (Yobu 27:5) Kodi Yobu anachita chiyani kuti akhale pa ubwenzi wolimba choncho ndi Mulungu? Mosakayikira, iye anamva zimene Mulungu anachitira Abulahamu, Isake ndi Yakobo omwe anali abale ake ndipo ankazikhulupirira. Ndiponso iye anaphunzira za makhalidwe ambiri a Yehova poona chilengedwe.​—Werengani Yobu 12:7-9, 13, 16.

18. (a) Kodi Yobu anasonyeza bwanji kuti anali wodzipereka kwa Yehova? (b) Kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo cha Yobu?

18 Zimene Yobu anaphunzira zinamupatsa chikhumbo chofuna kukondweretsa Yehova. Nthawi zonse Yobu ankapereka nsembe poganiza kuti mwina ana ake anachita chinachake chosakondweretsa Mulungu kapena ‘anachitira Mulungu mwano m’mtima mwawo.’ (Yobu 1:5) Ngakhale pamene ankayesedwa, iye ankanenabe zinthu zabwino zokhudza Yehova. (Yobu 10:12) Yobu ndi chitsanzo chabwino kwambiri. Ifenso nthawi zonse tiyenera kuphunzira kuti tidziwe Yehova komanso zolinga zake molondola. Nthawi zonse tifunika kuchita zinthu zauzimu monga kuphunzira Mawu ake, kupezeka pamisonkhano, kupemphera komanso kulalikira uthenga wabwino. Kuwonjezera pamenepa, tiyenera kuchita chilichonse chimene tingathe kuti tidziwikitse dzina la Yehova. Umphumphu wa Yobu unakondweretsa Yehova. Mofananamo umphumphu wa atumiki a Mulungu masiku ano umakondweretsa mtima wa Yehova. Tidzakambirana nkhani imeneyi m’mutu wotsatira.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani Satana Mdyerekezi ananeneza Yobu?

• Kodi Yobu anakumana ndi mayesero otani, ndipo iye anatani?

• Kodi n’chiyani chingatithandize kusunga umphumphu monga mmene Yobu anachitira?

• Kodi buku la Yobu likutiphunzitsa chiyani za Satana?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 4]

Nkhani ya Yobu imatidziwitsa za nkhani yaikulu yokhudza ulamuliro wa Mulungu m’chilengedwe chonse

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi umphumphu wanu ungayesedwe pa zinthu ziti?