Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku la Chivumbulutso—Gawo 1

Mfundo Zazikulu za M’buku la Chivumbulutso—Gawo 1

Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Chivumbulutso​—Gawo 1

MTUMWI Yohane atakalamba anaona masomphenya 16. Panthawiyi n’kuti ali m’ndende pachilumba cha Patimo. M’masomphenya amenewa, iye anaona zimene Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu adzakwaniritse m’tsiku la Ambuye, lomwe ndi nthawi yoyambira pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914 mpaka mapeto aulamuliro wa Khristu wa zaka 1,000. Masomphenya ochititsa chidwi kwambiri amenewa ali m’buku la Chivumbulutso lomwe linalembedwa ndi Yohane cha m’ma 96 C.E.

Tsopano tiyeni tione mfundo zazikulu za Chivumbulutso 1:1–12:17, amene ndi masomphenya asanu ndi awiri oyambirira amene Yohane anaona. Masomphenya amenewa akutikhudza kwambiri chifukwa amafotokoza za zinthu zimene zikuchitika masiku ano komanso amafotokoza zimene Yehova akufuna kuchita posachedwa. Anthu amene amawerenga nkhani zimenezi ndi chikhulupiriro amalimbikitsidwa.​—Aheb. 4:12.

“MWANAWANKHOSA” AMATULA ZISINDIKIZO ZISANU NDI CHIMODZI PA ZISANU NDI ZIWIRI

(Chiv. 1:1–7:17)

Choyamba, Yohane anaona Yesu Khristu mu ulemerero wake ndipo anamuuza mauthenga ofunika kuti ‘alembe mu mpukutu ndi kuutumiza ku mipingo isanu ndi iwiri.’ (Chiv. 1:10, 11) Kenako anaona mpando wachifumu uli pamalo pake kumwamba. Amene anakhala pampandowo ananyamula mpukutu womatidwa zisindikizo zisanu ndi ziwiri m’dzanja lake la manja. Munthu amene anali “woyenerera kumatula zisindikizo za mpukutuwu,” ndi “Mkango wa fuko la Yuda” basi, kapena kuti “mwanawankhosa . . . wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri.”​—Chiv. 4:2; 5:1, 2, 5, 6.

Masomphenya achitatu akutchula zimene zinachitika “Mwanawankhosa” atamatula zisindikizo zisanu ndi chimodzi zoyambirira, chimodzi ndi chimodzi. Atamatula chisindikizo cha chisanu ndi chimodzi, kunachitika chivomezi chachikulu ndipo tsiku lalikulu la mkwiyo linafika. (Chiv. 6:1, 12, 17) Kenako Yohane anaona ‘angelo anayi atagwira zolimba mphepo zinayi za dziko lapansi,’ kufikira atamaliza kusindikiza a 144,000. Anaonanso “khamu lalikulu” la anthu amene alibe chisindikizo “ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pa Mwanawankhosa.”​—Chiv. 7:1, 9.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:4; 3:1; 4:5; 5:6—Kodi mawu akuti “mizimu isanu ndi iwiri” akutanthauza chiyani? Kwa Mulungu, 7 amatanthauza kukwanira. Choncho, uthenga wopita ku “mipingo isanu ndi iwiri” ukukhudza anthu onse a Mulungu omwe ali m’mipingo yoposa 100,000 ya padziko lonse. (Chiv. 1:11, 20) Popeza kuti Yehova amapereka mzimu woyera malinga ndi zimene zikufunika kukwaniritsidwa, mawu akuti “mizimu isanu ndi iwiri” akutanthauza kuti umagwira ntchito mokwanira pothandiza anthu kumvetsa maulosi ndi kudalitsa anthu amene amatsatira maulosiwo. Zikuoneka kuti buku la Chivumbulutso limafotokoza zinthu m’magulu a zinthu zisanu ndi ziwiri. Pa malembawa, 7 akutanthauza kukwanira. Ndipotu bukuli limafotokoza za ‘kuthetsedwa’ kapena kukwaniritsidwa kwa “chinsinsi chopatulika cha Mulungu.”​—Chiv. 10:7.

1:8, 17—Kodi dzina lakuti “Alefa ndi Omega” komanso lakuti “Woyamba ndi Wotsiriza” ndi landani? Dzina lakuti “Alefa ndi Omega” ndi la Yehova, ndipo limatsindika mfundo yakuti Yehova ndiye Mulungu wamphamvuyonse ndipo sipadzakhalanso wina woposa iye. Iye ndi “chiyambi ndi mapeto.” (Chiv. 21:6; 22:13) Ngakhale kuti dzina lakuti “woyamba ndi wotsiriza” lopezeka pa Chivumbulutso 22:13 likunena za Yehova, zomwe zikusonyeza kuti palibe wina woposa iye ndipo sipadzakhalanso wina, tikawerenga chaputala choyamba cha Chivumbulutso, dzina lakuti “Woyamba ndi Wotsiriza,” likunena za Yesu Khristu. Iye anali munthu woyamba kuukitsidwira kumoyo wauzimu wosafa komanso anali womaliza kuukitsidwa ndi Yehova mwachindunji.​—Akol. 1:18.

2:7—Kodi “paradaiso wa Mulungu” n’chiyani? Popeza kuti mawu amenewa akuuza Akhristu odzozedwa, paradaiso wotchulidwa palembali akutanthauza moyo wabwino wakumwamba. Akhristu odzozedwa okhulupirika adzapatsidwa mwayi wodya “za mu mtengo wa moyo.” Iwo adzalandira moyo wosafa.​—1 Akor. 15:53.

3:7—Kodi Yesu analandira liti “kiyi ya Davide,” ndipo wakhala akuigwiritsa ntchito bwanji? Yesu atabatizidwa mu 29 C.E., anakhala Mfumu yosankhidwiratu ya m’mzera wa Davide. Komabe, Yesu analandira kiyi ya Davide mu 33 C.E. pamene anakwezedwa kumwamba kuti akhale kudzanja lamanja la Mulungu. Kumeneku analandira udindo wonse wa mu Ufumu wa Davide. Kuyambira nthawi imeneyi, Yesu wakhala akugwiritsa ntchito kiyi imeneyi kupatsa anthu mwayi wothandiza pantchito ya Ufumu. Mu 1919, Yesu anaika “mfungulo wa nyumba ya Davide” paphewa pa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” mwa kuika gulu la kapolo “kuyang’anira zinthu zake zonse.”​—Yes. 22:22; Mat. 24:45, 47.

3:12—Kodi ‘dzina latsopano’ la Yesu likutanthauza chiyani? Dzina limeneli likunena za udindo watsopano wa Yesu. (Afilipi 2:9-11) Ngakhale kuti palibe amene akulidziwa dzina limeneli monga mmene Yesu akulidziwira, Yesu amalilemba pa abale ake okhulupirika kumwamba, kuwathandiza kuti akhale naye paubwenzi wathithithi. (Chiv. 19:12) Iye amawapatsanso maudindo ena amene Yehova anam’patsa.

Zimene Tikuphunzirapo:

1:3. Popeza “nthawi yoikika [yakuti Mulungu aweruze dziko la Satanali] ili pafupi,” m’pofunika kwambiri kumvetsa uthenga wa m’buku la Chivumbulutso ndi kuchita mogwirizana ndi zimene umanena.

3:17, 18. Kuti tikhale olemera mwauzimu, tifunika kugula kwa Yesu “golide woyengedwa ndi moto.” Zimenezi zikutanthauza kuti tifunika kuyesetsa kukhala akhama pantchito zabwino. (1 Tim. 6:17-19) Tifunikanso kuvala “malaya akunja oyera,” zimene zimatidziwikitsa kuti ndife otsatira Khristu, ndipo tizigwiritsa ntchito “mankhwala opaka m’maso,” monga malangizo a m’magazini a Nsanja ya Olonda, kuti tikhale ozindikira mwauzimu.​—Chiv. 19:8

7:13, 14. Akulu 24 akuimira a 144,000 mu ulemerero wawo wakumwamba, kumene amatumikira monga mafumu komanso ansembe. Mu Isiraeli wakale, ansembe amene mfumu Davide ankawaika m’magulu 24, ankaimira anthu a 144,000. Mmodzi wa akulu amenewa anam’fotokozera Yohane chizindikiro cha khamu lalikulu. Choncho, Akhristu odzozedwa anayamba kuukitsidwa chaka cha 1935 chisanafike. Tikutero chifukwa m’chaka chimenechi atumiki odzozedwa a Mulungu padziko lapanso anathandizidwa kulidziwa bwino khamu lalikulu.​—Luka 22:28-30; Chiv. 4:4; 7:9.

CHISINDIKIZO CHA CHISANU NDI CHIWIRI CHITAMATULIDWA KUNAMVEKA MALIPENGA ASANU NDI AWIRI

(Chiv. 8:1–12:17)

Mwanawankhosa anamatula chisindikizo chachisanu ndi chiwiri. Angelo asanu ndi awiri analandira malipenga asanu ndi awiri. Ndipo angelo asanu ndi mmodzi pa angelowa anaimba malipenga awo, kulalikira zoweruza “magawo atatu” a anthu a m’Matchalitchi Achikhristu. (Chiv. 8:1, 2, 7-12; 9:15, 18) Zimenezi n’zimene Yohane anaona m’masomphenya ake a chisanu. M’masomphenya otsatira, Yohane anadya mpukutu waung’ono ndiponso anayeza kachisi. Atawomba lipenga la chisanu ndi chiwiri, kunamveka mawu okweza akuti: “Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake.”​—Chiv. 10:10; 11:1, 15.

Masomphenya a chisanu ndi chiwiri akuwonjezera pa zimene zafotokozedwa pa Chivumbulutso 11:15, 17. M’masomphenyawa, kumwamba kunaoneka chizindikiro chachikulu. Mkazi wakumwamba anabala mwana wamwamuna. Kenako Mdyerekezi anachotsedwa kumwamba. Ndipo pokwiya ndi mkaziyo, Mdyerekezi anapita “kukachita nkhondo ndi otsala a mbewu yake.”​—Chiv. 12:1, 5, 9, 17.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

8:1-5—N’chifukwa chiyani kumwamba kunangoti chete, ndipo kenako n’chiyani chinaponyedwa ku dziko lapansi? Kumwamba kunakhala chete mophiphiritsira kuti “mapemphero a oyera” padziko lapansi amveke. Zimenezi zinachitika pamapeto a nkhondo yoyamba yapadziko lonse. Akhristu odzozedwa sanapite kumwamba Nthawi za Akunja zitatha monga mmene anthu ambiri ankaganizira. Iwo anakumana ndi mavuto aakulu panthawi ya nkhondoyo. Choncho anapemphera mochokera pansi pamtima kuti Mulungu awathandize. Poyankha mapempherowo, mngelo anaponya padziko lapansi moto wophiphiritsira umene unachititsa Akhristu odzozedwawo kukhala achangu mwauzimu. Ngakhale kuti iwo anali ochepa, anayamba ntchito yolalikira padziko lonse imene inapangitsa Ufumu wa Mulungu kukhala nkhani yofunika. Ndipo zimenezi zinabweretsa mavuto aakulu m’Matchalitchi Achikhristu. Mawu ochenjeza ndiponso amphamvu ochokera m’Baibulo analengezedwa, malemba ena anadziwidwa molondola ndipo maziko a zipembedzo zonyenga anagwedezeka monga mmene nyumba zimagwederera ndi chivomezi.

8:6-12; 9:1, 13; 11:15—Kodi angelo asanu ndi awiri anakonzekera liti kuwomba malipenga awo, nanga malipengawo anawombedwa liti ndipo anamveka motani? Kukonzekera kuwomba malipenga asanu ndi awiriwo kunaphatikizapo kupereka malangizo kwa anthu a m’gulu la Yohane lapadziko lapansi kuyambira mu 1919 mpaka mu 1922. Abale odzozedwa amenewa anali otanganidwa kwambiri pantchito yolalikira ndiponso kumanga malo osindikizira mabuku. (Chiv. 12:13, 14) Kuwomba malipengawo kunaimira kulengeza mopanda mantha chiweruzo cha Yehova padziko la Satana, kumene anthu a Mulungu akuchita mogwirizana ndi angelo. Ndipo kulengeza kumeneku kunayambira pamsonkhano umene unachitika mu 1922 ku Cedar Point, Ohio ndipo kudzapitirirabe mpaka pachisautso chachikulu.

8:13; 9:12; 11:14—Kodi kuwomba malipenga atatu omaliza ndi “tsoka” chifukwa chiyani? Popeza kuti kuwomba malipenga anayi oyambirira ndi mauthenga osonyeza kuti Matchalitchi Achikhristu ndi akufa mwauzimu, kuwomba malipenga atatu omalizawo ndi tsoka chifukwa kukukhudza zochitika zapadera. Kuwomba lipenga la chisanu kunachititsa kuti mu 1919 anthu a Mulungu atuluke “kuphompho” limene limatanthauza nthawi imene sanathe kuchita chilichonse. Ndipo anayamba kugwira ntchito yolalikira mwakhama imene inali ngati mlili wozunza ku Matchalitchi Achikhristu. (Chiv. 9:1) Lipenga la chisanu ndi chimodzi likunena za nkhondo yaikulu ya okwera pa akavalo ndiponso ntchito yolalikira ya padziko lonse imene inayamba mu 1922. Lipenga lomaliza likukhudza kubadwa kwa Ufumu wa Mesiya.

Zimene Tikuphunzirapo:

9:10, 19. Uthenga wodalirika wa m’Baibulo wopezeka m’mabuku a kapolo “wokhulupirika ndi wanzeru” umakhala wamphamvu. (Mat. 24:45) Uthenga umenewu umafanana ndi michira ya dzombe yokhala ndi “mbola ngati zinkhanira” ndi akavalo ankhondo amene ‘michira yawo ili ngati njoka.’ N’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa chakuti mabuku amenewa amachenjeza za “tsiku la [Yehova] lakubwezera.” (Yes. 61:2) Tiyeni tikhale olimba mtima ndi achangu pogawira mabuku amenewa.

9:20, 21. Anthu oona mtima ambiri amene amakhala m’madera amene anthu amati kulibe Akhristu, amamvetsera uthenga umene timalalikira. Komabe, sitikuyembekezera kuti anthu onse amene si Akhristu, amene akutchedwa kuti “anthu ena onse,” angatembenuke. Ngakhale zili choncho timalimbikirabe kulalikira.

12:15, 16. “Dziko lapansi,” lomwe ndi dongosolo la Satana, kapena kuti olamulira a m’mayiko osiyanasiyana, lalimbikitsa ufulu wolambira. Kuyambira cha m’ma 1940, olamulira amenewa ‘anameza mtsinje [wa chizunzo] umene chinjoka chinalavula kuchokera m’kamwa mwake.’ Ndithudi, Yehova akhoza kugwiritsa ntchito olamulira aboma kuchita chifuniro chake. N’chifukwa chake lemba la Miyambo 21:1 limanena kuti: “Mtima wa mfumu uli m’dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi; aulozetsa komwe afuna.” Zimenezi zitilimbikitse kukhulupirira Mulungu.