Mfundo Zazikulu za M’makalata Opita kwa Tito, Filemoni ndi Aheberi
Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’makalata Opita kwa Tito, Filemoni ndi Aheberi
NTHAWI ina mtumwi Paulo atamasulidwa ku ndende paulendo wake woyamba kumangidwa ku Roma mu 61 C.E., anapita ku chilumba cha Kerete. Ataona mmene unalili moyo wauzimu wa Akhristu m’mipingo ya kumeneko, anamusiya Tito komweko kuti alimbikitse mipingoyo. Patapita nthawi, Paulo analembera Tito kalata yomuthandiza pantchito yake komanso yosonyeza kuti ntchito imene anali kuchitayo anatumidwa ndi mtumwiyu. Zikuoneka kuti nthawi imeneyi Paulo anali ku Makedoniya.
M’mbuyomo, atatsala pang’ono kumasulidwa ku ndende mu 61 C.E., Paulo analembera Filemoni kalata. Filemoni anali m’bale wachikhristu amene ankakhala ku Kolose. Kalatayi inali yomulimbikitsa Filemoni monga mnzake.
Cha m’ma 61 C.E. momwemu, Paulo analemberanso kalata anthu achiheberi okhulupirira amene anali kukhala ku Yudeya. Zimenezi zikusonyeza kuti Chikhristu chinali chofala ku Yuda. Makalata onsewa ali ndi malangizo othandiza kwa ife.—Aheb. 4:12.
KHALANIBE OLIMBA MWAUZIMU
Atamulangiza zinthu zofunika kuona ‘poika akulu mu mzinda ndi mzinda,’ Paulo analangiza Tito ‘kupitiriza kudzudzula mwamphamvu [osaweruzika], kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba.’ Iye analimbikitsa anthu onse m’mipingo ya ku Kerete ‘kukana moyo wosaopa Mulungu ndi kukhala a maganizo abwino.’—Tito 1:5, 10-13; 2:12; Tito 1:5, 10-13; 2:12.
Paulo anapereka malangizo ena othandiza abale a ku Kerete kukhalabe olimba mwauzimu. Iye analangiza Tito kuti ‘apewe mafunso opusa ndi mikangano ndi kulimbana pa za Chilamulo.’—Tito 3:9.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:15—Kodi “zinthu zonse” zimakhala bwanji ‘zoyera kwa anthu oyera,’ koma zodetsedwa “kwa anthu oipitsidwa ndi opanda chikhulupiriro”? Yankho lagona pa kumvetsa zimene Paulo anali kunena ndi mawu akuti “zinthu zonse.” Iye ankanena za zinthu zimene munthu angasankhe yekha chochita malinga ndi chikumbumtima chake, osati zinthu zimene zimaletsedwa mwachindunji m’Malemba. Kwa anthu amene maganizo awo ndi ogwirizana ndi mfundo za Mulungu, zinthu zimenezi zimakhala zoyera. Koma si mmene zimakhalira kwa munthu amene maganizo ake ndi oipa ndiponso amene chikumbumtima chake n’choipitsidwa. *
3:5—Kodi Akhristu odzozedwa ‘amapulumutsidwa bwanji mwa kusambitsidwa’ ndipo ‘amasandutsidwa bwanji atsopano mwa mzimu woyera’? Iwo ‘amapulumutsidwa mwa kusambitsidwa’ chifukwa Mulungu amawasambitsa, kapena kuti kuwayeretsa, m’magazi a Yesu a nsembe ya dipo. Iwo ‘amasandutsidwa atsopano mwa mzimu woyera’ chifukwa amakhala ‘zolengedwa zatsopano’ monga ana a Mulungu obadwa ndi mzimu.—2 Akor. 5:17.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:10-13; 2:15. Oyang’anira achikhristu ayenera kukhala olimba mtima kuti akonze zinthu zolakwika mumpingo.
2:3-5. Monga zinalili m’nthawi za atumwi, masiku anonso alongo achikhristu okhwima mwauzimu ayenera kukhala ndi “khalidwe loyenera anthu opembedza, osati a miseche, kapena akapolo a vinyo wambiri, koma aphunzitsi a zinthu zabwino.” Mwakuchita zimenezi, angathe kulangiza bwino mwamseri “akazi ocheperapo msinkhu” mumpingo.
3:8, 14. Kuika ‘maganizo athu pa kuchitabe ntchito zabwino’ ndi ‘kwabwino ndiponso kopindulitsa’ chifukwa kumatithandiza kuti tizibala zipatso potumikira Mulungu komanso kukhala osiyana ndi dziko loipali.
APEMPHENI “MWACHIKONDI”
Filemoni anayamikiridwa chifukwa anali chitsanzo chabwino pankhani yosonyeza “chikondi ndi chikhulupiriro.” Iye ankatsitsimula Akhristu anzake, ndipo zimenezi ‘zinamusangalatsa ndi kumulimbikitsa kwambiri’ Paulo.—Filem. 4, 5, 7.
Popereka chitsanzo kwa oyang’anira onse, Paulo anakamba nkhani yovuta yokhudza Onesimo momupempha “mwachikondi” osati momulamula. Iye anauza Filemoni kuti: “Pokhulupirira kuti udzalabadira, ndikukulembera kalatayi. Ndikudziwa kuti udzachita ngakhale zoposa zimene ndanenazi.”—Filem. 8, 9, 21.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
10, 11, 18—Kodi Onesimo amene anali “wopanda thandizo” anakhala bwanji “wothandiza”? Onesimo anali kapolo wamwano amene anapita ku Roma atathawa kunyumba ya Filemoni ku Kolose. N’kutheka kuti, Onesimo anawaberanso Ambuye wake ndalama zimene anayendera paulendo wake wa makilomita 1,400. Iye analidi wopanda thandizo kwa Filemoni. Komabe, ku Roma, Paulo anathandiza Onesimo kukhala Mkhristu. Popeza anakhala Mkhristu, munthu amene anali “wopanda thandizo” tsopano anali “wothandiza.”
15, 16—Kodi n’chifukwa chiyani Paulo sanapemphe Filemoni kuti amasule Onesimo? Paulo ankafuna kungogwira ntchito yake ‘yolalikira za ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu’ basi. Motero, sanafune kulowerera m’nkhani zina, monga zokhudza ukapolo.—Mac. 28:31.
Zimene Tikuphunzirapo:
2. Filemoni anapereka nyumba yake kuti anthu azichitiramo misonkhano yachikhristu. Ndi mwayi zedi kuchitira msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda m’nyumba yathu.—Aroma 16:5; Akol. 4:15.
4-7. Tiziyamba ndife kuyamikira okhulupirira anzathu achitsanzo chabwino pankhani ya chikhulupiriro ndi chikondi.
15, 16. Ngati zinthu sizikuyenda bwino pamoyo wathu tisamade nkhawa kwambiri. Zinthu zingathe kusintha monga zinakhalira kwa Onesimo.
21. Paulo ankayembekezera kuti Filemoni amukhululukira Onesimo. Nafenso timafunika kuwakhululukira abale amene atilakwira.—Mat. 6:14.
‘YESETSANI MWAKHAMA KUFIKA PA UCHIKULIRE’
Posonyeza kuti kukhulupirira Yesu n’kofunika kwambiri kuposa ntchito za Chilamulo, Paulo anafotokoza ubwino wa munthu amene anayambitsa Chikhristu, utumiki wake monga wansembe, nsembe yake, ndiponso chipangano chatsopano. (Aheb. 3:1-3; 7:1-3, 22; 8:6; 9:11-14, 25, 26) Kudziwa zimenezi kuyenera kuti kunathandiza Akhristu achiheberi kupirira pamene ankazunzidwa ndi Ayuda. Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake achiheberi ‘kuyesetsa mwakhama kufika pa uchikulire.’—Aheb. 6:1.
Kodi chikhulupiriro n’chofunika bwanji pamoyo wachikhristu? Paulo analemba kuti: “Popanda chikhulupiriro n’kosatheka kum’kondweretsa Mulungu.” Ndipo iye analimbikitsanso Aheberi kuti: “Tithamange [mwachikhulupiriro ndiponso] mopirira mpikisano umene atiikirawu.”—Aheb. 11:6; 12:1.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
2:14, 15—Popeza kuti Satana “ali ndi njira yochititsa imfa,” kodi zimenezi zikusonyeza kuti angathe kupha aliyense amene akufuna? Ayi, sichoncho. Komabe, kuyambira nthawi imene anayamba kuchita zoipa m’munda wa Edeni, mabodza ake achititsa kuti anthu azifa chifukwa Adamu anachimwa ndipo anapatsira uchimo ndi imfa kwa anthu onse. (Aroma 5:12) Komanso, anthu amene amachita zofuna za Satana amazunza mpaka kupha atumiki a Mulungu, monga anachitira ndi Yesu. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti Satana ali ndi mphamvu zopanda malire zophera aliyense amene akufuna. Zikanakhala kuti ali ndi mphamvu zimenezi, bwenzi ataseseratu kalekale olambira a Yehova. Yehova amateteza anthu ake monga gulu ndipo sangalole kuti Satana awawonongeretu. Ngakhale Mulungu atalola kuti Satana atiukire ndi kutipha, tili ndi chikhulupiriro choti Mulungu adzatiukitsa.
4:9-11—Kodi ‘timalowa bwanji mu mpumulo wa Mulungu’? Atatha masiku 6 akulenga zinthu, Mulungu anapuma pa ntchito yake yolenga akudziwa kuti cholinga chake chokhudza dziko lapansi ndi anthu chikwaniritsidwa. (Gen. 1:28; 2:2, 3) ‘Timalowa mu mpumulo umenewo’ tikamapewa kudzilungamitsa ndiponso tikamakhulupirira njira yotipulumutsira imene Mulungu wakonza. Tikamakhulupirira Yehova ndi kutsatira ndi mtima wonse Mwana wake, osati zofuna zathu, timatsitsimulidwa ndipo timapeza mpumulo wabwino tsiku lililonse.—Mat. 11:28-30.
9:16—M’chipangano chatsopano, kodi “wochita naye chipangano waumunthuyo” ndi ndani? Yehova ndi amene anayambitsa chipangano chatsopano ndipo Yesu ndiye “wochita naye chipangano waumunthuyo.” Yesu ndi amene ali Mkhalapakati wa pangano limeneli, ndipo mwa imfa yake anapereka nsembe imene inachititsa kuti chipangano chimenechi chiyambe kugwira ntchito.—Luka 22:20; Aheb. 9:15.
11:10, 13-16—Kodi Abulahamu ankayembekezera “mzinda” uti? Umenewu sunali mzinda weniweni koma wophiphiritsa. Abulahamu ankayembekezera Yerusalemu Wakumwamba yemwe amapangidwa ndi Khristu Yesu ndiponso anthu 144, 000 omwe adzalamulire naye pamodzi. Anthu omwe adzalamulire naye amenewa amatchedwa “mzinda woyera, Yerusalemu watsopano” akakhala mu ulemerero wawo kumwamba. (Aheb. 12:22; Chiv. 14:1; 21:2) Abulahamu ankayembekezera kudzakhala ndi moyo mu Ufumu wa Mulungu.
12:2—Kodi “chimwemwe chimene anamuikira [Yesu] patsogolo pake” chimenenso chinamuchititsa ‘kupirira mtengo wozunzikirapo’ chinali chiyani? Chinali chimwemwe chimene anachipeza poganizira zimene utumiki wake udzakwaniritse. Ndipo zimenezi zinaphatikizapo kuyeretsa dzina la Yehova, kusonyeza kuti Mulungu ndiye woyenera kulamulira ndiponso kupulumutsa anthu ku imfa mwa kupereka moyo wake dipo. Yesu ankayembekezeranso mwachidwi mwayi wodzalamulira monga Mfumu ndiponso wotumikira monga Mkulu wa Ansembe n’cholinga chothandiza anthu.
13:20—N’chifukwa chiyani chipangano chatsopano chimatchedwa kuti chipangano “chosatha”? Pali zifukwa zitatu: (1) chipanganochi sichidzalowedwa m’malo, (2) zimene chikukwaniritsa n’zosatha, ndipo (3) a “nkhosa zina” adzapitirizabe kupindula ndi chipangano chatsopano chimenechi Aramagedo itachitika.—Yoh. 10:16.
Zimene Tikuphunzirapo:
5:14. Tiyenera kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu, Baibulo ndiponso kugwiritsa ntchito zimene tikuphunzirazo. Ndipo ndi njira yokhayi imene tingaphunzitsire ‘luntha lathu la kuzindikira kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika.’—1 Akor. 2:10.
6:17-19. Kuyembekeza mwachidwi zimene Mulungu analonjeza komanso zimene analumbira kuti adzachita, kudzatithandiza kuyendabe m’njira ya choonadi.
12:3, 4. M’malo ‘motopa, ndi moyo wathu kulefuka’ chifukwa cha mayesero kapena chitsutso chilichonse chimene tingakumane nacho, tiyenera kupitirizabe kupita patsogolo mwauzimu ndiponso kukhala ndi mtima wopirira mayesero. Tiyenera kutsimikiza mtima kupirira “mpaka kutaya magazi,” kapena kuti mpaka imfa.—Aheb. 10:36-39.
12:13-15. Tisalole “muzu wa ululu” kapena kuti munthu wina aliyense mumpingo amene samasangalala ndi mmene zinthu zikuyendera, kutilepheretsa ‘kuwongolabe njira zoyendamo mapazi athu.’
12:26-28. “Zinthu zimene zinapangidwa” ndi anthu osati Mulungu, kutanthauza dongosolo lonse la zinthu lino kuphatikizapo “miyamba” yoipa, zidzawonongedwa. Zimenezi zikadzachitika, zinthu “zimene sizikugwedezedwa,” zomwe ndi Ufumu ndi anthu ake, zidzatsala. Motero, tifunika kulengeza mwakhama Ufumu ndiponso kutsatira malamulo ake.
13:7, 17. Kukumbukira malangizo amenewa, oti tizimvera ndi kugonjera oyang’anira mumpingo, kudzatithandiza kuti tizigwirizana nawo.
[Mawu a M’munsi]