Kulalikira Pamsika
Kulalikira Pamsika
ALI mu mzinda wa ku Atene, mtumwi Paulo ankapita tsiku lililonse ku msika kukalalikira uthenga wabwino wa Yesu. (Mac. 17:17) Iye ankakonda kulalikira ku msika chifukwa chakuti n’kumene kunkapezeka anthu ambiri.
Ngakhale kuti papita zaka 2,000 kuchokera nthawi imeneyi, anthu a Yehova akupitirizabe kulalikira uthenga wa Ufumu wa Mulungu m’misika. N’chifukwa chiyani amatero? Chifukwa kumsika n’kumene kumapezeka anthu ambiri. Masiku ano, msika ungathenso kukhala malo omwe amakhala ndi masitolo okhaokha. Zimene Mboni zina zinachita n’zakuti zinapempha woyang’anira sitolo kuti ziyale nawo mabuku ndi magazini ofotokoza Baibulo.
Mwachitsanzo, pasitolo ina yaikulu ku New Jersey, m’dziko la United States, Mboni zinayala mabuku ofotokoza nkhani zokhudza banja. Kodi zinthu zinayenda bwanji? Tsiku limodzi lokha anagawira mabuku a m’zinenero 6 okwana 153.
Mayi wina atapita pamene anayala mabukupo anamvetsera mwatcheru zimene Mbonizo zinkafotokoza. Mayiyo anavomereza kuti n’kofunikadi kuganizira Mulungu pamoyo wathu ndiponso m’banja mwathu. Ndipo analandira mabuku awa: Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja ndi Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.
Chakumadzulo a tsiku limeneli, mwamuna wina anadutsa cha pamene panayalidwa mabukuwo kuti alowe m’sitolo ina. Ataponya maso anachita chidwi ndi buku la Achichepere Akufunsa. Mlongo yemwe anali pamabukupo anaona kuti bamboyo wachita chidwi ndi bukulo. Ndipo anam’funsa kuti, “Kodi pali buku limene lakusangalatsani?” Bamboyo anavomera
n’kuloza buku la Achichepere Akufunsa. Ndipo mlongoyo anatenga bukulo ndi kum’patsa. Bamboyo anati ali ndi ana atatu ndipo awiri ndi achinyamata. Ananenanso kuti amakambirana ndi ana akewa kamodzi pamlungu. Akuvundukula bukulo, ananena kuti atha kukaligwiritsa ntchito pokambirana nkhani zina ndi banja lake. Mlongoyo anamuonetsanso buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, ndipo anam’tsimikizira kuti iye ndi mkazi wake akapezamo mfundo zothandiza kwambiri banja lawo. Bamboyu anathokoza kwambiri ndipo anapereka ndalama zothandiza ntchito imeneyi. Iwo anavomera kuti wa Mboni wina adzawayendere.Kodi amene anapita kukalalikira ku sitolo yaikulu ija anamva bwanji? Mlongo wina anati: “Ine ndinasangalala kulalikira mwa njira imeneyi ndipo ndinalimbikitsidwa kwambiri.” Mlongo winanso anati: “Yehova ananena kuti uthenga wabwino udzalalikidwa mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Masiku ano, ku Paramus, mu mzinda wa New Jersey, uthenga wabwino umenewu wakhudza mtima anthu azinenero zosiyanasiyana. Zinali zosangalatsa kwambiri kulalikira nawo ku dera limeneli. Aliyense amene anagwira nawo ntchito imeneyi anasangalala kwambiri. Ndipo tonse tinkafuna kumangopitirizabe kulalikira.”
Kodi mungawonjezere njira zanu zolalikirira? Njira yathu yeniyeni yolalikirira ndi yopita ku nyumba ndi nyumba. (Mac. 20:20) Komabe, kodi simungayese kulalikira pa msika ndi ku masitolo?