Kodi Tingatani ndi Mavuto Amene Timakumana Nawo Muutumiki wa ku Nyumba ndi Nyumba?
Kodi Tingatani ndi Mavuto Amene Timakumana Nawo Muutumiki wa ku Nyumba ndi Nyumba?
“Tinalimba mtima mwa Mulungu wathu kulankhula kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu movutikira kwambiri.”—1 ATES. 2:2.
1. Kodi Yeremiya anakumana ndi mavuto otani, ndipo anatha bwanji kuwagonjetsa?
YEREMIYA anali munthu ngati ife tomwe ndipo nthawi zina ankachita mantha. Yehova atamuuza kuti wamusankha kukhala “mneneri wa mitundu ya anthu,” iye anadandaula kuti: “Ha, Ambuye Mulungu! taonani, sindithai kunena pakuti ndili mwana.” Komabe chifukwa chodalira Yehova, iye anavomera ntchitoyo. (Yer. 1:4-10) Kwa zaka zoposa 40, Yeremiya analimbana ndi mavuto monga kupanda chidwi kwa anthu, kukanidwa, kunyozedwa, ngakhale kumenyedwa kumene. (Yer. 20:1, 2) Nthawi zina anafuna kungosiya ntchitoyo. Ngakhale kuti anthu ambiri anali osalabadira, iye anapitirizabe kulengeza uthenga umene anthuwo ankadana nawo. Ndi mphamvu ya Mulungu, Yeremiya anachita zimene sakanatha mwa iye yekha.—Werengani Yeremiya 20:7-9.
2, 3. Kodi atumiki a Mulungu masiku ano amakumana bwanji ndi mavuto ngati a Yeremiya?
2 Ambiri mwa atumiki a Mulungu a masiku anofe tinachitapo mantha ngati Yeremiya. Pamene tinaganizira zolalikira nyumba ndi nyumba, tinati, ‘Ee! Sindingakwanitse zimenezo.’ Koma titazindikira Mat. 24:13.
kuti chifuniro cha Yehova ndi chakuti tilengeze uthenga wabwino, tinasiya kuchita mantha n’kuyamba kulalikira kwambiri. Ngakhale zinali choncho, ambiri a ife tinakumana ndi zothetsa nzeru kwa kanthawi ndithu, ndipo zinali zovuta kuti tipitirize kulalikira. Kunena zoona, n’zovuta kuyamba kulalikira nyumba ndi nyumba ndi kupitirizabe kulalikira mpaka mapeto.—3 Nanga bwanji ngati mwakhala mukuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndiponso mwakhala mukupezeka pa misonkhano ya mpingo kwa nthawi ndithu, koma mukuzengereza kuyamba kulalikira nyumba ndi nyumba? Kapena, bwanji ngati ndinu Mboni yobatizidwa koma zimakuvutani kulalikira khomo ndi khomo, ngakhale kuti muli ndi moyo wathanzi? Musataye mtima. Anthu osiyanasiyana akugonjetsa mavuto a utumiki wa ku nyumba ndi nyumba. Inunso mungathe kutero ndi thandizo la Yehova.
Limbani Mtima
4. Kodi n’chiyani chinathandiza mtumwi Paulo kulankhula uthenga wabwino molimba mtima?
4 Mosakayikira, inu mukudziwa kuti ntchito yolalikira padziko lonse ikutheka ndi mzimu wa Mulungu, osati ndi mphamvu kapena nzeru za anthu. (Zek. 4:6) Ndi mmenenso zilili ndi utumiki wa Mkhristu aliyense payekha. (2 Akor. 4:7) Taganizirani za mtumwi Paulo. Atakumbukira nthawi imene iye ndi mmishonale mnzake anazunzidwa ndi otsutsa, analemba kuti: “Choyamba titavutika ndi kuchitidwa za chipongwe ku Filipi, tinalimba mtima mwa Mulungu wathu kulankhula kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu movutikira kwambiri.” (1 Ates. 2:2; Mac. 16:22-24) Mwina sitingakhulupirire kuti mlaliki wachangu ngati Paulo nthawi zina ankachita kuvutikira kulalikira. Komabe, mofanana ndi ife tonse, Paulo anafunika kudalira Yehova kuti alankhule uthenga wabwino molimba mtima. (Werengani Aefeso 6:18-20.) Kodi ife tingam’tsanzire bwanji Paulo?
5. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala olimba mtima kuti tilalikire?
5 Pemphero lingatithandize kukhala olimba mtima kuti tilalikire. Mpainiya wina anati: “Ndimapemphera kuti ndizilankhula molimba mtima, kuti ndiziwafika anthu pamtima ndiponso kuti ndizikhala wachimwemwe muutumiki. Pajatu ntchitoyi ndi ya Yehova, si yathu ayi. Choncho popanda thandizo lake, palibe chomwe tingachite.” (1 Ates. 5:17) Tonsefe tiyenera kupitiriza kupemphera kuti Mulungu atithandize ndi mzimu wake woyera, n’cholinga choti tizilalikira molimba mtima.—Luka 11:9-13.
6, 7. (a) Kodi Ezekieli anaona masomphenya otani, ndipo masomphenyawo anatanthauza chiyani? (b) Kodi atumiki a Mulungu masiku ano akupeza phunziro lotani m’masomphenya a Ezekieli?
6 Buku la Ezekieli limasonyeza chinthu chinanso chomwe chingatithandize kuti tizilankhula molimba mtima. M’masomphenya, Yehova anapatsa Ezekieli mpukutu umene mkati ndi kunja analemba “nyimbo za maliro, ndi chisoni, ndi tsoka,” ndipo anamuuza kuti adye. Anati: “Wobadwa ndi munthu iwe, dyetsa m’mimba mwako, nudzaze matumbo ako ndi mpukutu uwu ndakupatsawu.” Kodi masomphenya amenewa anatanthauza chiyani? Uthenga umene Ezekieli anafunika kupereka, unayenera kulowerera mwa iye mpaka kukhudza mtima wake wonse. Mneneriyu anapitiriza kuti: “M’mwemo ndinaudya, ndi m’kamwa mwanga munazuna ngati uchi.” Kwa Ezekieli, kulengeza uthenga wa Mulungu kwa anthu kunali kokoma ngati kudya uchi. Iye anaona kuti unali mwayi waukulu kuimira Yehova ndi kuchita ntchito imene Mulungu anam’patsa, ngakhale kuti anafunika kupereka uthenga wowawa kwa anthu osalabadira.—Werengani Ezekieli 2:8–3:4, 7-9.
7 Masomphenya amenewa ali ndi phunziro lofunika kwambiri kwa atumiki a Mulungu masiku ano. Ifenso tili ndi uthenga wowawa woti tiupereke kwa anthu amene nthawi zambiri sayamikira zimene timachita. Kuti tipitirizebe kuona utumiki wachikhristu monga dalitso lochokera kwa Mulungu, tiyenera kudya bwino mwauzimu. Chizolowezi chophunzira mongodutsa pamwamba ndiponso mosakhazikika, sichingathandize kuti Mawu a Mulungu alowerere bwinobwino mwa ife. Kodi mukufunika kumawerenga Baibulo ndi kuchita phunziro laumwini mozamirapo kapena mokhazikika? Kodi mukufunika kumasinkhasinkha pafupipafupi zimene mwawerenga?—Sal. 1:2, 3.
Kodi Mungayambe Bwanji Kukambirana za Baibulo?
8. Kodi ndi njira iti yomwe yathandiza ofalitsa Ufumu ena kuyamba kukambirana ndi anthu za Baibulo mu utumiki wa ku nyumba ndi nyumba?
8 Kwa ofalitsa ambiri, mbali ya utumiki wa ku nyumba ndi nyumba yovuta kwambiri ndiyo kuyamba kukambirana ndi mwininyumba. Zoonadi, m’madera ena n’zovuta kuyamba kukambirana ndi munthu. Ofalitsa ena akamalankhula ndi anthu pakhomo, amaona kuti mtima wawo umakhala m’malo ngati ayamba ulaliki wawo ndi mawu ochepa osankhidwa bwino ndipo kenako kupatsa mwininyumba thirakiti, kapena kuti kapepala, ngati mmene bokosili pamunsipa likusonyezera. Mutu wa kapepalako kapena chithunzi chake chokongola chingachititse chidwi mwininyumbayo, ndipo zimenezi zingatipatse mpata womuuza mwachidule chomwe tabwerera komanso kumufunsa funso. Njira inanso ndiyo kumuonetsa mwininyumbayo timapepala titatu kapena tinayi tosiyanasiyana ndi kumuuza kuti asankhe kamene kamusangalatsa. Komabe cholinga chathu sikungogawira timapepala kapena kutigwiritsa ntchito pakhomo lililonse, koma kuyamba kukambirana za Baibulo ndi kuyambitsa maphunziro.
9. Kodi n’chifukwa chiyani kukonzekera bwino n’kofunika?
9 Njira iliyonse imene mungatsatire, kukonzekera bwino kungakuthandizeni kuchotsa mantha ndi kulankhula mwaumoyo pamene muli Akol. 3:23; 2 Tim. 2:15.
mu utumiki wa ku nyumba ndi nyumba. Mpainiya wina anati: “Ndimakhala wachimwemwe ngati ndakonzekera bwino. Ndipo ndimalakalaka nditapereka ulaliki umene ndakonzekerawo.” Mpainiya winanso anati: “Ndikadziwa mfundo za m’mabuku amene ndikukagawira, mtima wanga umafunitsitsa kuti ndiwagawire.” Ngakhale kuti kukonzekera chamumtima ulaliki wanu kuli ndi ubwino wake, ambiri amaona kuti n’zothandiza kuyeseza ulalikiwo mokweza mawu. Kuchita zimenezi kumawathandiza kutumikira Yehova ndi moyo wawo wonse.—10. Kodi chofunika n’chiyani kuti misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda izikhala yoyenera ndi yothandiza?
10 Misonkhano yokonzekera utumiki yokhala ndi mfundo zothandiza, ingachititse kuti tizikhala ogwira mtima ndi achimwemwe muutumiki wa ku nyumba ndi nyumba. Ngati lemba la tsiku likunena za ntchito yolalikira, mungaliwerenge ndi kukambirana mwachidule. Komabe, m’bale wochititsa msonkhanowo ayenera kukhala ndi nthawi yokwanira yokambirana ulaliki kapena yochita chitsanzo cha ulaliki wogwirizana ndi gawo lawo. Kapenanso angakambirane mfundo zina zothandiza zimene abale angagwiritse ntchito muutumiki tsiku limenelo. Zimenezi zidzathandiza amene apezekapo kukhala okonzeka kulalikira mogwira mtima. Akamakonzekera bwino pasadakhale, akulu ndi ena amene amachititsa misonkhano imeneyi angakwanitse kuchita zonsezi ndi kumaliza msonkhanowo panthawi yake.—Aroma 12:8.
Ubwino Womvetsera
11, 12. Kodi kumvetsera ndi mtima wachifundo kungatithandize bwanji kuuza anthu uthenga wabwino? Perekani zitsanzo.
11 Sikukonzekera bwino kokha kumene kumathandiza kuti tiyambe kukambirana ndi anthu za Baibulo muutumiki ndi kuwafika pa mtima. Tiyeneranso kuwasonyeza chidwi chachikulu. Tingasonyeze chidwicho malinga ndi mmene timamvetserera. Woyang’anira woyendayenda wina anati: “Kuleza mtima kwathu ndiponso kufunitsitsa kumva zimene anthu akulankhula, kumakopa anthuwo ndipo ndi njira yabwino kwambiri yosonyezera kuti tili ndi chidwi.” Tikamamvetsera ndi mtima wachifundo, mwininyumba amamasuka n’kuyamba kukambirana nafe, ngati mmene nkhani yotsatirayi ikusonyezera.
12 Mayi wina analemba kalata m’nyuzipepala yakuti Le Progrès, ya ku Saint-Étienne, ku France kuti anthu onse aiwerenge. M’kalatayo, anafotokoza za anthu awiri amene anafika pakhomo pake iye ali pachisoni chachikulu, chifukwa panali patangopita nthawi yochepa kuchokera pamene mwana wake wamkazi wamiyezi itatu anamwalira. Mayiyu analemba kuti: “Nditangowaona, ndinazindikira kuti iwo ndi Mboni za Yehova. Ndinafuna kuwabweza mwaulemu, koma kenako ndinaona kabuku kamene anali kugawira. Kanali kofotokoza chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti anthu azivutika. Choncho, ndinawauza kuti alowe ndi cholinga chakuti ndiwathetse makani. . . . Mbonizo zinacheza nane kupitirira ola limodzi. Ine ndikamalankhula, iwo anali kumvetsera ndi mtima wachifundo motero kuti atanyamuka kumapita, ndinatsitsimulidwa kwambiri mpaka ndinavomera kuti adzabwerenso.” (Aroma 12:15) Patapita nthawi, mayiyu anayamba kuphunzira Baibulo. Choncho, mukhoza kuona kuti zimene mayiyo anakumbukira zokhudza ulendo woyamba uja, si zimene Mbonizo zinanena, koma kumvetsera kwawo.
13. Kodi tingasinthe bwanji ulaliki wathu wa uthenga wabwino malinga ndi anthu amene takumana nawo?
13 Tikamamvetsera ndi mtima wachifundo, timakhala ngati tikupatsa anthu mpata wakuti atiuze chifukwa chimene iwo akufunikira Ufumu, ndipo timakhala m’malo abwino owauza uthenga wabwino. Inu muyenera kuti mwaona kuti alaliki amene amakhala ogwira mtima, ndi anthu amene ali ndi luso la kumvetsera. (Miy. 20:5) Amasonyeza chidwi chenicheni kwa anthu amene amakumana nawo muutumiki. Sikuti amangofuna kudziwa mayina ndi maadiresi a anthuwo, koma amaonanso zinthu zimene anthuwo amachita nazo chidwi ndi zimene akufunikira. Munthu akawafotokozera za vuto lina lake, iwo amakafufuza ndi kubwereranso mwamsanga kwa munthuyo kukamuuza zimene apeza. Mofanana ndi mtumwi Paulo, iwo amasintha ulaliki wawo wa uthenga wa Ufumu malinga ndi anthu amene akumana nawo. (Werengani 1 Akorinto 9:19-23.) Chidwi chenicheni chimenecho chimakopa anthu kuti amve uthenga wabwino ndipo chimasonyeza bwino “chifundo chachikulu cha Mulungu wathu.”—Luka 1:78.
Khalani ndi Maganizo Oyenera
14. Kodi tingaonetse bwanji makhalidwe a Yehova pochita utumiki wathu?
14 Yehova watilemekeza kwambiri potipatsa ufulu wosankha. Iye ndi Mulungu Wamphamvuyonse, komabe sakakamiza munthu aliyense kuti amutumikire. M’malomwake, amachita kupempha anthu kuti amutumikire chifukwa cha chikondi chake, ndipo amadalitsa amene ndi mtima woyamikira amalabadira iye akamawachitira chifundo. (Aroma 2:4) Popeza ndife atumiki ake, tizikhala okonzeka kupereka uthenga wabwino m’njira yogwirizana ndi Mulungu wathu wachifundo nthawi iliyonse imene tikuchitira umboni. (2 Akor. 5:20, 21; 6:3-6) Kuti zimenezi zitheke, tifunika kukhala ndi maganizo oyenera kwa anthu a m’gawo lathu. Kodi chingatithandize n’chiyani?
15. (a) Kodi Yesu analangiza atumwi ake kuchita chiyani anthu akakana uthenga wawo? (b) Kodi chingatithandize n’chiyani kuika maganizo athu onse pa kufunafuna anthu oyenerera?
15 Yesu analangiza otsatira ake kuti asamade nkhawa kwambiri ngati anthu ena akana uthenga wawo. M’malomwake, anawauza kuti aziika maganizo awo onse pa kufunafuna anthu oyenerera. (Werengani Mateyo 10:11-15.) Chimene chingatithandize kuchita zimenezi ndicho kukhala ndi zolinga zazing’ono zimene tingakwanitse. M’bale wina amadziyerekezera ndi munthu wofunafuna golide. Iye amayendera mfundo yakuti, “Lero, ndipeza golide penapake,” kunena munthu wachidwi. M’bale winanso, cholinga chake ndi “kukumana ndi munthu mmodzi wachidwi mlungu uliwonse, ndi kubwerera kwa munthuyo pakapita masiku ochepa kuti akakolezere chidwicho.” Ofalitsa ena amayesetsa kuwerengera mwininyumba ngakhale lemba limodzi ngati n’kotheka. Nanga ndi zolinga zotani zimene inu mungakwanitse?
16. Kodi tili ndi zifukwa zotani zopitirizira kulalikira?
16 Kuti tinene kuti utumiki wa ku nyumba ndi nyumba ukuyenda bwino, sizidalira chabe mmene anthu a m’gawo lathu akulabadirira uthengawo. N’zoona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri kuti anthu a maganizo oyenerera apulumuke. Komanso ndi yofunika pazifukwa zina. Utumiki wachikhristu umatipatsa mwayi wosonyeza chikondi chathu kwa Yehova. (1 Yoh. 5:3) Umatithandiza kupewa mlandu wa magazi. (Mac. 20:26, 27) Umachenjeza anthu oipa kuti “ola lakuti [Mulungu] apereke chiweruzo lafika.” (Chiv. 14:6, 7) Kuposa zonsezi, dzina la Yehova limalemekezedwa padziko lonse lapansi kudzera m’ntchito yolalikira uthenga wabwino. (Sal. 113:3) Choncho, kaya anthu amve kapena ayi, tiyeni tipitirizebe kulengeza uthenga wa Ufumu. Indedi, zonse zimene timayesetsa kuchita polalikira uthenga wabwino n’zokongola m’maso mwa Yehova.—Aroma 10:13-15.
17. Kodi anthu posachedwapa adzakakamizika kuzindikira chiyani?
17 Ngakhale kuti anthu ambiri masiku ano amanyoza ntchito yathu yolalikira, posachedwapa iwo adzaionera mwina. (Mat. 24:37-39) Yehova anatsimikizira Ezekieli kuti mauthenga achiweruzo amene analengeza akadzakwaniritsidwa, nyumba yopanduka ya Isiraeli ‘idzadziwa kuti panali mneneri pakati pawo.’ (Ezek. 2:5) Mofanana ndi zimenezi, Mulungu akadzapereka chiweruzo chake pa dongosolo la zinthu lilipoli, anthu adzakakamizika kuzindikira kuti uthenga umene Mboni za Yehova zinali kulalikira kulikonse ndi ku nyumba ndi nyumba unachokeradi kwa Mulungu woona yekha, Yehova, ndi kuti Mbonizo zinalidi kutumikira ngati omuimira. Tilitu ndi mwayi waukulu wonyamula dzina lake ndi kulengeza uthenga wake m’nthawi ino imene kukuchitika zinthu zazikulu! Mwa mphamvu yake, tiyeni tipitirizebe kugonjetsa mavuto a utumiki wa ku nyumba ndi nyumba.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi tingalimbe bwanji mtima kuti tilalikire?
• Kodi chingatithandize kuyamba kukambirana za Baibulo ndi anthu muutumiki wa ku nyumba ndi nyumba n’chiyani?
• Kodi tingasonyeze bwanji anthu ena chidwi chenicheni?
• Kodi chingatithandize kukhala ndi maganizo oyenera kwa anthu a m’gawo lathu n’chiyani?
[Mafunso]
[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]
Njira Ina Yoyambira Kukambirana za Baibulo
Kuyamba:
▪ Mutapereka moni kwa mwininyumba, mungamupatse kapepala ndi kunena kuti, “Ndabwera kuti ndikambirane nanu mfundo yolimbikitsa pankhani yofunika iyi.”
▪ Kapena mungamupatse kapepala ndi kunena kuti, “Lero ulendo wanga ndi wosachedwa. Ndabwera kuti ndidziwe maganizo anu pankhani iyi.”
Akalandira kapepalako:
▪ Mosataya nthawi, m’funseni maganizo ake pamutu wa kapepalako.
▪ Mvetserani bwinobwino, kuti mumvetse maganizo a mwininyumbayo. Yamikirani ndemanga zake mochokera pansi pa mtima.
Kuti mupitirize kukambirana:
▪ Werengani ndi kukambirana lemba limodzi kapena angapo, ndipo sinthani ulaliki wanu malinga ndi zinthu zimene munthuyo wachita nazo chidwi ndi zimene akufunikira.
▪ Ngati ali ndi chidwi, m’gawireni buku ndi kumusonyeza mmene mumachitira phunziro la Baibulo ngati zingatheke. Konzani zodzabweranso.