Kodi Chofunika Ndi Chiyani Kuti Tikhale Ndi Moyo Waphindu?
Kodi Chofunika Ndi Chiyani Kuti Tikhale Ndi Moyo Waphindu?
‘Opa Mulungu, nusunge malamulo ake.’—MLAL. 12:13.
1, 2. Kodi kukambirana buku la Mlaliki kungatipindulitse bwanji?
TAGANIZIRANI za munthu amene sasowa chilichonse. Iye ndi mtsogoleri wotchuka ndipo ndi mmodzi wa anthu olemera kwambiri padziko lapansi, komanso ndi wanzeru kuposa wina aliyense. Ngakhale kuti ali ndi zinthu zimenezi, iye akudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingachite chiyani kuti ndikhale ndi moyo waphindu?’
2 Sikuti munthu ameneyu ndi wongopeka chabe ayi. Iye anakhalakodi zaka pafupifupi 3,000 zapitazo. Dzina lake ndi Solomo ndipo m’buku la Mlaliki, iye anafotokoza kuti anachita zambiri kuti apeze chisangalalo pamoyo. (Mlal. 1:13) Nkhani ya Solomo imatiphunzitsa zambiri. Ndipo nzeru za m’buku la Mlaliki zingatithandize kukhala ndi zolinga zabwino zimene zingachititse moyo wathu kukhaladi waphindu.
“Kungosautsa Mtima”
3. Tchulani mfundo yoona koma yomvetsa chisoni yokhudza moyo wa munthu imene tonsefe sitingaizembe.
3 Solomo anafotokoza kuti Mulungu analenga zinthu zambirimbiri zokongola padziko lapansi. Zinthuzo ndi zodabwitsa komanso zochititsa chidwi kwambiri mwakuti sititopa nazo. Ndipo titati tiyambe kufufuza zonse zimene Mulungu analenga, sitingakwanitse chifukwa moyo wathu ndi waufupi kwambiri. (Mlal. 3:11; 8:17) Baibulo limati masiku a moyo wathu ndi owerengeka ndipo sachedwa kutha. (Yobu 14:1, 2; Mlal. 6:12) Mfundo imeneyi ndi yoona koma yomvetsa chisoni, ndipo iyenera kutilimbikitsa kugwiritsa ntchito moyo wathu mwanzeru. Kuchita zimenezi ndi kovuta chifukwa dziko la Satanali limafuna kuti tichite zinthu zoipa.
4. (a) Kodi mawu akuti “zachabechabe” amatanthauza chiyani? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene anthu amafuna pamoyo zimene tikambirane?
4 Pofuna kusonyeza kuti moyo wathu ungakhale wopanda phindu ngati sitisamala, Solomo anagwiritsa ntchito mawu akuti “zachabechabe” kapena kuti “chabe” nthawi 30 m’buku la Mlaliki. Mawu a Chiheberi omasuliridwa kuti “zachabechabe” amanena za chinthu chopanda kanthu, chopanda phindu, chopanda tanthauzo, ndi chopanda pake kapena chosakhalitsa. (Mlal. 1:2, 3) Nthawi zina Solomo anagwiritsa ntchito mawu akuti “zachabechabe” pamodzi ndi mawu akuti “kungosautsa mtima,” kapena kuti kuyesa kugwira mphepo. (Mlal. 1:14; 2:11) N’zodziwikiratu kuti kuyesa kugwira mphepo n’kopanda phindu. Munthu amene angayese kuchita zimenezi angangokhala chimanjamanja, osagwira kanthu. Mofanana ndi munthu wotere, anthu amene sakhala ndi zolinga zanzeru amagwira fuwa la moto ndipo saphula kanthu. Moyo m’dongosolo lino la zinthu ndi waufupi kwambiri ndipo sitifunika kuuwonongera pa zinthu zopanda kanthu. Chotero, kuti tithandizane kupewa vuto limeneli, tiyeni tikambirane zinthu zimene Solomo ananena kuti anthu ambiri amafuna pamoyo. Choyamba, tikambirana za zosangalatsa ndiponso chuma. Kenako, tikambirana za ntchito yabwino.
Kodi Munthu Wokonda Zosangalatsa Amakhala ndi Moyo Waphindu?
5. Kodi Solomo anachita chiyani pofuna kukhala ndi moyo wachimwemwe?
5 Mofanana ndi anthu ambiri masiku ano, Solomo anali kukonda zosangalatsa pofuna Mlal. 2:10) Kodi anachita chiyani pofuna kusangalala? Malinga ndi Mlaliki chaputala 2, iye ‘anasangalatsa thupi lake ndi vinyo’ koma anali kumwa modziletsa. Anali kuchitanso zinthu zina monga kukongoletsa malo, kulemba mapulani a nyumba zachifumu, kumvetsera nyimbo ndi kudya zakudya zabwino.
kukhala ndi moyo wachimwemwe. Iye anati: “Sindinakaniza mtima wanga chimwemwe chilichonse.” (6. (a) Kodi n’chifukwa chiyani sikulakwa kusangalala ndi zinthu zabwino pamoyo? (b) Kodi zosangalatsa tiyenera kuziona bwanji?
6 Kodi Baibulo limaletsa kusangalala limodzi ndi mabwenzi? Sililetsa ngakhale pang’ono. Mwachitsanzo, Solomo ananena kuti kudya chakudya pamalo abata pambuyo pogwira ntchito kwambiri, ndi mtulo kapena kuti mphatso yochokera kwa Mulungu. (Werengani Mlaliki 2:24; 3:12, 13.) Ndiponso Yehova mwini wakeyo amauza achinyamata kuti ‘akondwere ndi kuti mtima wawo usangalale,’ koma kuti ayenera kusamala pochita zimenezi. (Mlal. 11:9) Anthufe timafunika kupumula komanso zosangalatsa zoyenera. (Yerekezerani ndi Maliko 6:31.) Komabe, kusangalalako kusakhale chinthu chachikulu pamoyo wathu. M’malo mwake zosangalatsa ziyenera kukhala ngati mchere mundiwo. Mungavomereze kuti kaya munthu amakonda ndiwo zochuluka mchere bwanji, kuthira mchere wambirimbiri mundiwo kumapangitsa ndiwozo kusakoma, ndipo munthu atadya ndiwo zoterozo angathe kudwala nazo. Mofanana ndi zimenezi, Solomo anazindikira kuti kukonda kwambiri zosangalatsa ndi “kungosautsa mtima.”—Mlal. 2:10, 11.
7. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala posankha zosangalatsa?
7 Ndiponso, sikuti zosangalatsa zonse ndi zabwino. Zambiri zimawononga moyo wauzimu wa munthu ndi makhalidwe ake. Palitu anthu ambirimbiri amene agwa m’mavuto aakulu chifukwa chogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa mwauchidakwa kapena kutchova juga, pofuna kusangalala. Mwachikondi, Yehova amatichenjeza kuti tikalola mtima ndi maso athu kutichititsa zinthu zoipa, tidzakumana ndi mavuto.—Agal. 6:7.
8. N’chifukwa chiyani ndi bwino kuganizira mofatsa za moyo wathu?
8 Komanso, kukonda kwambiri zosangalatsa kungatilepheretse kuika mtima wathu pa zinthu zofunika kwambiri. Musaiwale kuti moyo ndi waufupi kwambiri ndipo nthawi ina iliyonse tikhoza kudwala kapena kukumana ndi mavuto a mtundu uliwonse. N’chifukwa chake Solomo ananenso kuti tingapindule kwambiri kupita ku maliro, makamaka akakhala a m’bale kapena mlongo wokhulupirika, kuposa kupita ku “nyumba ya kuseka.” (Werengani Mlaliki 7:2, 4.) N’chifukwa chiyani anatero? Tikamamvetsera nkhani ya maliro ndi kuganizira zimene mtumiki wokhulupirika wa Yehova, yemwe wamwalirayo anali kuchita, zingatilimbikitse kuganiza mofatsa za moyo wathu. Mapeto ake, tingaone kuti ndi bwino kusintha zolinga zathu kuti tigwiritse ntchito mwanzeru nthawi yotsala ya moyo wathu.—Mlal. 12:1.
Kodi Chuma Chingachititse Kuti Tikhale Wosangalala?
9. Kodi Solomo anazindikira chiyani pankhani yokhala ndi chuma?
9 Solomo anali mmodzi wa anthu olemera kwambiri padziko lapansi pamene anali kulemba buku la Mlaliki. (2 Mbiri 9:22) Akanatha kupeza chilichonse chimene anali kufuna. Iye analemba kuti: “Chilichonse maso anga anachifuna sindinawamana.” (Mlal. 2:10) Koma Solomo anazindikira kuti chuma pachokha sichibweretsa chisangalalo. Choncho anati: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu.”—Mlal. 5:10.
10. Kodi tingapeze bwanji chisangalalo ndi chuma chenicheni?
10 Ngakhale kuti chuma sichibweretsa chisangalalo, anthu ambiri amakopeka nachobe. Mwachitsanzo ku United States , ophunzira a chaka choyamba kuyunivesite atafunsidwa mafunso, 75 pa 100 alionse anati cholinga chawo chachikulu pamoyo ndi kukhala “olemera kwambiri.” Ngakhale atalemera, kodi angakhaledi osangalala? M’povuta kunena, chifukwa ofufuza anena kuti kusakasaka chuma ndi kumene kumalepheretsanso munthu kukhala ndi moyo wosangalala ndi waphindu. Kalelo, Solomo anali ataiona mfundo imeneyi. Iye analemba kuti: “Ndinakundikanso * (Mlal. 2:8, 11) Mosiyana ndi zimenezi, ngati ifeyo tigwiritsa ntchito moyo wathu kutumikira Yehova ndi mtima wonse ndipo iye akatidalitsa, timapeza chuma chenicheni.—Werengani Miyambo 10:22.
siliva ndi golidi ndi chuma cha mafumu . . . Ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima.”Kodi Ndi Ntchito Yotani Imene Imasangalatsadi?
11. Kodi Malemba amati chiyani za ntchito?
11 Yesu anati: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.” (Yoh. 5:17) Ndi zodziwikiratu kuti Yehova ndi Yesu amasangalala ndi ntchito yawo. Baibulo limasonyeza kuti Yehova anasangalala kwambiri atamaliza ntchito yake yolenga. Limati: “Anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.” (Gen. 1:31) Angelonso “anafuula ndi chimwemwe” ataona zonse zimene Mulungu analenga. (Yobu 38:4-7) Solomo nayenso anazindikira kuti ntchito yabwino imasangalatsa.—Mlal. 3:13.
12, 13. (a) Kodi anthu ena awiri anati chiyani za chisangalalo chimene amapeza chifukwa chogwira ntchito mwakhama? (b) Kodi n’chifukwa chiyani nthawi zina ntchito yolembedwa imakhumudwitsa?
12 Anthu ambiri amazindikiranso kuti munthu akamagwira ntchito mwakhama amasangalala. Mwachitsanzo, José, yemwe ndi katswiri wa zojambulajambula anati: “Ukamaliza kujambula chithunzi chimene unali kufuna, umamva ngati mtima wako uphulika ndi chisangalalo.” Miguel, * yemwe ndi wabizinesi, anati: “Ntchito imasangalatsa chifukwa imakuthandiza kudyetsa banja lako. Umamvanso kuti wachita zinazake zaphindu.”
13 Komabe, ntchito zambiri ndi zotopetsa ndipo sizipereka mpata wakuti munthu agwiritse ntchito luso lake lonse bwinobwino. Nthawi zina kuntchito kwenikweniko, munthu amakumana ndi mavuto ngakhale kupanda chilungamo kumene. Malinga ndi zimene Solomo ananena, munthu waulesi angalandire mphoto ya munthu amene amagwira ntchito mwakhama, chabe chifukwa chakuti waulesiyo amadziwana ndi mabwana. (Mlal. 2:21) Zinthu zinanso zingakhumudwitse munthu. Mwachitsanzo, munthu angayambe bizinesi imene akuona kuti apindula nayo kwambiri, koma kenako ingalowe pansi chifukwa cha kugwa kwa chuma kapena zinthu zina zogwa mwadzidzidzi. (Werengani Mlaliki 9:11.) Nthawi zambiri, munthu amene amayesetsa kwambiri kuti atukule moyo wake, mapeto ake amakhumudwa atazindikira kuti wakhala ‘akungodzisautsa chabe.’—Mlal. 5:16.
14. Kodi ndi ntchito iti imene nthawi zonse imapatsa chisangalalo chenicheni?
14 Nanga kodi pali ntchito ina imene sikhumudwitsa ngakhale pang’ono? José, wa zojambulajambula uja, anati: “Vuto la zojambulajambula ndi lakuti zaka zikamadutsa, zojambulazo zingasowe kapena kuwonongeka. Koma zinthu zauzimu sizitero. Chifukwa chomvera Yehova mwa kulalikira uthenga wabwino, ndathandiza anthu ena kukhala Akhristu oopa Mulungu, ndipo phindu lake ndi 1 Akor. 3:9-11) Miguel nayenso anati kulalikira uthenga wa Ufumu kumamubweretsera chisangalalo chachikulu kuposa ntchito yake yolembedwa. Iye anati: “Munthu umasangalala kwambiri ukakambirana ndi munthu wina mfundo ya m’Malemba ndi kuona kuti mfundoyo yamukhudza mtima.”
losatha. Palibe chimene chingapose zimenezi.” (“Ponya Zakudya Zako”
15. Kodi chofunika ndi chiyani kuti tikhaledi ndi moyo waphindu?
15 Pomaliza, kodi chofunika ndi chiyani kuti tikhale ndi moyo waphindu? Kuti tikhaledi ndi moyo wosangalala, tiyenera kugwiritsa ntchito zaka zathu zochepa m’dongosolo la zinthu lino kuchita zabwino ndi kusangalatsa Yehova. Tiyenera kukhala pa ubale weniweni ndi Yehova, kuphunzitsa ana athu zinthu zauzimu, kuthandiza ena kudziwa Yehova ndiponso tiyenera kupanga ubwenzi wokhalitsa ndi abale ndi alongo athu. (Agal. 6:10) Zinthu zimenezi phindu lake silitha ndipo amene amazichita amadalitsidwa. Solomo anagwiritsa ntchito fanizo lochititsa chidwi pofotokoza phindu lochita zabwino. Iye anati: “Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri.” (Mlal. 11:1) Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti: “Khalani opatsa, inunso anthu adzakupatsani.” (Luka 6:38) Ndiponso Yehova mwini wakeyo walonjeza kuti adzapereka mphoto kwa anthu amene amachitira anzawo zabwino.—Miy. 19:17; werengani Aheberi 6:10.
16. Kodi nthawi yabwino kwambiri yosankha zochita pamoyo wathu ndi iti?
16 Baibulo limatilimbikitsa kuti pamene tili achinyamata, tisankhe mwanzeru zimene tidzachita pamoyo wathu. Tikatero, sitidzakhumudwa tikadzakalamba. (Mlal. 12:1) Zingakhale zomvetsa chisoni ngati tingawonongere zaka zofunika kwambiri za moyo wathu tikufunafuna zinthu zokopa za dzikoli, kenako n’kuzindikira kuti tinali kuyesa kugwira mphepo.
17. Kodi chingakuthandizeni ndi chiyani kusankha njira ya moyo yabwino koposa?
17 Mofanana ndi tate aliyense wachikondi, Yehova amafuna kuti musangalale ndi moyo, muchite zabwino ndiponso mupewe mavuto. (Mlal. 11:9, 10) Kodi chingakuthandizeni kuchita zimenezi ndi chiyani? Khalani ndi zolinga zauzimu ndipo yesetsani kuzikwaniritsa. Pafupifupi zaka 20 zapitazo, Javier anafunika kusankha pakati pa ntchito yaudokotala ya ndalama zambiri ndi utumiki wa nthawi zonse. Iye anati: “Ngakhale kuti ntchito yaudokotala ingakhale yosangalatsa, singafanane ndi chisangalalo chimene ndinali nacho nditathandiza anthu angapo kudziwa choonadi. Utumiki wa nthawi zonse wandithandiza kusangalaladi ndi moyo. Ndimangodandaula kuti ndinauyamba mochedwa.”
18. Kodi n’chifukwa chiyani moyo wa Yesu padziko lapansi unalidi waphindu?
Mlal. 7:1) Mfundo imeneyi ndi yoona, makamaka tikaganizira moyo wa Yesu. Kunena zoona, iye anadzipangira mbiri yabwino koposa kwa Yehova. Atamwalira mokhulupirika, Yesu anasonyeza kuti Atate wake ndiye woyenera kulamulira ndipo anapereka nsembe ya dipo yomwe inatsegula njira ya chipulumutso. (Mat. 20:28) Pazaka zochepa zimene Yesu anakhala pa dziko lapansi, anapereka chitsanzo changwiro cha mmene munthu amakhalira ndi moyo waphindu, chimene timayesetsa kutsatira.—1 Akor. 11:1; 1 Pet. 2:21.
18 Motero, kodi chinthu chofunika kwambiri chimene tiyenera kuyesetsa kukhala nacho ndi chiyani? Buku la Mlaliki limati: “Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.” (19. Kodi Solomo anapereka uphungu wanzeru wotani?
19 Ifenso tingadzipangire mbiri yabwino kwa Mulungu. Kukhala ndi mbiri yabwino kwa Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri kwa ife kuposa chuma. (Werengani Mateyo 6:19-21.) Tsiku ndi tsiku, tingayesetse kuchita zinthu zabwino kwa Yehova zimene zingapindulitse moyo wathu. Mwachitsanzo, tingauze ena uthenga wabwino ndiponso kulimbitsa ukwati ndi banja lathu lonse. Komanso tingalimbitse moyo wathu wauzimu mwa kuchita phunziro laumwini ndi kupezeka pa misonkhano. (Mlal. 11:6; Aheb. 13:16) Ndiyeno kodi mukufunadi kukhala ndi moyo waphindu? Ngati mukufuna moyo umenewu, pitirizani kutsatira uphungu wa Solomo wakuti: ‘Opa Mulungu, nusunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.’—Mlal. 12:13.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 10 Solomo anali kupeza ndalama zokwana matalente 666 (zoposa makilogalamu 22,000) a golidi pachaka.—2 Mbiri 9:13.
^ ndime 12 Dzina lasinthidwa.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• N’chifukwa chiyani tifunika kuganizira mofatsa zolinga zathu pamoyo?
• Kodi zosangalatsa ndiponso chuma tiyenera kuziona motani?
• Kodi ndi ntchito yotani imene imabweretsa chisangalalo chosatha?
• Kodi chinthu chofunika kwambiri chimene tiyenera kuyesetsa kukhala nacho ndi chiyani?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 23]
Kodi zosangalatsa tiyenera kuziona bwanji?
[Chithunzi patsamba 24]
N’chifukwa chiyani ntchito yolalikira ili yosangalatsa kwambiri?