Tsanzirani Mmishonale Woposa Amishonale Onse
Tsanzirani Mmishonale Woposa Amishonale Onse
“Khalani otsanzira ine, monga inenso ndili wotsanzira Khristu.”—1 AKOR. 11:1.
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira Yesu Khristu?
MTUMWI Paulo anatsanzira Yesu Khristu, Mmishonale woposa amishonale onse. Kenako, Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Khalani otsanzira ine, monga inenso ndili wotsanzira Khristu.” (1 Akor. 11:1) Yesu anapereka chitsanzo kwa atumwi ake pankhani ya kudzichepetsa. Iye modzichepetsa anasambitsa mapazi awo ndipo anawauza kuti: “Ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.” (Yoh. 13:12-15) Ifenso Akhristu a masiku ano, tili ndi udindo wotsanzira Yesu Khristu pazonena ndi zochita zathu ndiponso makhalidwe athu.—1 Pet. 2:21.
2. Ngakhale ngati Bungwe Lolamulira silinakusankheni kukhala mmishonale, kodi mungakhalebe ndi mtima wotani?
2 M’nkhani yapita, tinaphunzira kuti mmishonale ndi munthu amene amatumizidwa monga mlaliki ndipo amauza ena uthenga wabwino. Pankhani imeneyi, Paulo anapereka mafunso ochititsa chidwi. (Werengani Aroma 10:11-15.) Monga mwaonera, mtumwiyo anafunsa kuti: “Adzamva bwanji . . . popanda wina kulalikira?” Ndipo anagwira mawu a mneneri Yesaya akuti: “Ha, akongolatu . . . mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino.” (Yes. 52:7) Ngakhale ngati sindinu mmishonale kapena simunatumizidwe monga mmishonale kudziko lina, mungakhalebe ndi mtima wokonda kulalikira potsanzira Yesu mwa kukhala mlaliki wachangu wa uthenga wabwino. Chaka chatha, ofalitsa Ufumu 6,957,852 ‘anagwira ntchito ya alaliki’ m’mayiko 236.—2 Tim. 4:5.
“Ife Tasiya Zinthu Zonse ndi Kukutsatirani”
3, 4. Kodi Yesu anasiya chiyani kumwamba, ndipo tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale otsatira ake?
3 Kuti akwaniritse ntchito yake padziko lapansi, Yesu “anakhuthula zonse za mwa iye n’kukhala ngati kapolo,” ndipo anasiya moyo ndi ulemerero wake wakumwamba. (Afil. 2:7) Zilizonse zimene tingachite potsanzira Khristu, sizingafanane ndi zimene Yesu anachita pobwera padziko lapansi. Ngakhale zili choncho, titha kukhalabe otsatira ake olimba popanda kulakalaka zinthu zomwe tinali nazo m’dziko la Satana.—1 Yoh. 5:19.
4 Tsiku lina, mtumwi Petulo anauza Yesu kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatirani.” (Mat. 19:27) Petulo, Andireya, Yakobe ndi Yohane ataitanidwa kuti atsatire Yesu, anasiya makoka awo popanda kuzengereza. Anasiya ntchito ya usodzi ndi kuyamba utumiki monga ntchito yawo. Malinga ndi Uthenga Wabwino wa Luka, Petulo anati: “Taonani! Ife tasiya zinthu zathu ndi kukutsatirani.” (Luka 18:28) Ambirife sitinachite kusiya “zinthu zathu” zonse kuti titsatire Yesu. Komabe, tinachita ‘kudzikana tokha’ kuti tikhale otsatira a Khristu ndi atumiki a Yehova odzipereka ndi mtima wonse. (Mat. 16:24) Kuchita zimenezi kwatibweretsera madalitso ambiri. (Werengani Mateyo 19:29.) Timakhala osangalala chifukwa cha mtima wokonda kulalikira umene tili nawo potsanzira Khristu. Timatero makamaka ngati tathandizapo munthu ngakhale pang’ono pokha kuyandikira Mulungu ndi Mwana wake wokondedwa.
5. Fotokozani nkhani yosonyeza zimene munthu amene anachoka kwawo angachite ataphunzira choonadi cha m’Baibulo.
5 Valmir wa ku Brazil anali kukhala m’katikati mwa dziko la Suriname, ndipo anali ndi mgodi wa golide. Mwamuna ameneyu anali chidakwa ndipo anali wachiwerewere. Tsiku lina ali mu mzinda, Mboni za Yehova zinayamba kuphunzira naye Baibulo. Iye anali kuphunzira tsiku lililonse, anasintha moyo wake kwambiri ndipo posapita nthawi anabatizidwa. Ataona kuti zikuvuta kutsatira chipembedzo chake chatsopano chifukwa cha ntchito yakeyo, anagulitsa bizinesi yake yobweretsa ndalama zambiri ndi kubwerera ku Brazil kuti akathandize banja lake kupeza chuma chauzimu. Anthu ambiri ochoka kwawo
kupita ku mayiko olemera, amati akaphunzira choonadi cha m’Baibulo, amasiya ntchito ndi kubwerera kwawo kuti akathandize achibale ndi anthu ena mwauzimu. Anthu ofalitsa Ufumu amenewa amasonyezadi mtima wokonda kulalikira.6. Kodi tingachite chiyani ngati sitingathe kusamukira ku dera limene kukufunika alaliki a Ufumu ambiri?
6 Mboni zambiri zasamukira ku madera amene kukufunika alaliki a Ufumu ambiri. Mboni zina mpaka zikutumikira ku mayiko ena. Mwina sizingatheke kuti ifeyo tichite zimenezi, koma tingatsanzirebe Yesu mwa kuchita zimene tingathe muutumiki nthawi zonse.
Yehova Akuphunzitsa Anthu Ake
7. Kodi ndi sukulu ziti zomwe zimaphunzitsa anthu ofuna kukhala aluso polengeza Ufumu?
7 Mofanana ndi Yesu amene analandira maphunziro kwa Atate ake, ifenso tingalandire maphunziro amene Yehova akupereka masiku ano. Yesu anati: “Zinalembedwa m’mabuku a aneneri kuti, ‘Ndipo onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.’” (Yoh. 6:45; Yes. 54:13) Masiku ano, pali sukulu zimene cholinga chake ndi kutithandiza kukhala olengeza Ufumu odziwa bwino ntchito. Mosakayikira, tonsefe tapindula ndithu ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu m’mipingo mwathu. Apainiya ali ndi mwayi wopita ku Sukulu ya Utumiki Waupainiya. Ndipo apainiya ambiri amene anayamba kale ntchito yawoyo, akhala ndi mwayi wopita ku sukuluyi kachiwiri. Akulu ndi atumiki othandiza amapita ku Sukulu ya Utumiki wa Ufumu kuti luso lawo la kuphunzitsa lipite patsogolo ndi kuti azitha kuthandiza bwino okhulupirira anzawo. Akulu ndi atumiki othandiza ambiri osakwatira amapita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki, kumene amaphunzira mmene angathandizire anthu ena pantchito yolalikira. Ndipo abale ndi alongo ambiri amene ndi amishonale m’mayiko ena, anaphunzitsidwa ku Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo.
8. Kodi abale ena amachita chiyani poona kuti maphunziro amene Yehova akupereka ndi ofunika kwambiri?
8 Mboni za Yehova zambiri zasintha moyo ndi zochita zawo kuti zipite ku sukuluzi. Yugu wa ku Canada anasiya ntchito chifukwa chakuti bwana ake anamukaniza kupita pa tchuthi. Iye anafuna kukhala pa tchuthi kuti apite ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Yugu anati: “Sindikudandaula. Mwina akanandipatsa tchuthi, akanafuna kuti ndizigwirabe ntchito pakampanipo posonyeza kuyamikira. Koma tsopano ndine womasuka kuchita utumiki uliwonse umene Yehova angandipatse.” Pofuna kupindula ndi maphunziro amene Mulungu akupereka, ambiri adzipereka ndi kusiya zinthu zimene kale zinali zofunika kwa iwo.—Luka 5:28.
9. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kuphunzira Malemba ndiponso khama zimathandiza.
9 Kuphunzira Malemba ndiponso khama zimathandiza kwambiri. (2 Tim. 3:16, 17) Taganizirani zimene zinachitikira Saulo ku Guatemala. Iye anabadwa ndi nzeru zochepa, ndipo mphunzitsi wake wina anauza mayi ake kuti asamamukakamize kuphunzira kuwerenga, chifukwa mnyamatayo azingokhumudwa. Saulo anasiya sukulu wosadziwa kuwerenga. Komabe, Mboni ina inaphunzitsa Saulo kuwerenga pogwiritsa ntchito kabuku ka Dziperekeni pa Kuwerenga ndi Kulemba. Patapita nthawi, Saulo anapita patsogolo mpaka anayamba kukamba nkhani m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Tsiku lina ali mu utumiki wa nyumba ndi nyumba, mayi a Saulo anakumana ndi aphunzitsi ake aja. Atamva kuti Saulo amadziwa kuwerenga, aphunzitsiwo anauza mayi ake kuti akabwere naye mlungu wotsatira. Atabwera naye, aphunzitsiwo anamufunsa Saulo kuti, “Kodi undiphunzitsa chiyani lero?” Saulo anangoyamba kuwerenga ndime m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Aphunzitsiwo anati: “Sindikukhulupirira kuti ndiwe ukundiphunzitsa.” Atalephera kuugwira mtima, mphunzitsiyo anayamba kugwetsa misozi ndipo anakumbatira Saulo.
Kuphunzitsa Mogwira Mtima
10. Kodi ndi buku labwino liti limene lafalitsidwa kuti tiziphunzitsira anthu choonadi cha m’Baibulo?
10 Yesu anali kuphunzitsa zinthu zimene Yehova anamuphunzitsa mwachindunji ndiponso malangizo olembedwa m’Mawu a Mulungu. (Luka 4:16-21; Yoh. 8:28) Timatsanzira Yesu mwa kugwiritsa ntchito uphungu wake ndi kuphunzitsa za m’Malemba. Tikamachita zimenezi, tonsefe timalankhula ndi kuganiza chimodzimodzi, ndipo zimenezi zimalimbikitsa umodzi wathu. (1 Akor. 1:10) Tikuthokoza kwambiri kuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akufalitsa mabuku ofotokoza Baibulo amene amatithandiza kukhalabe ogwirizana paziphunzitso zathu ndi kukwaniritsa ntchito yathu yolalikira. (Mat. 24:45; 28:19, 20) Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndi limodzi mwa mabuku amenewa, ndipo lili m’zinenero 179.
11. Kodi mlongo wina wa ku Ethiopia anagwiritsa ntchito motani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani atakumana ndi wotsutsa?
11 Kugwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pophunzira Malemba kungasinthe mtima ngakhale wa otsutsa. Tsiku lina Lula, mpainiya wa ku Ethiopia, anali kuchititsa phunziro la Baibulo pamene wachibale wa wophunzirayo anangolowa mwamwano ndi kuwauza kuti asiye kuphunzira. Koma mlongo wathu Lula anakambirana mwaulemu ndi wachibaleyo pogwiritsa ntchito fanizo la ndalama zachinyengo, lomwe lili m’mutu 15 wa buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Mtima wa mayiyo unakhala pansi ndipo anawalola kuti apitirize kuphunzira. Ndipotu anakhala nawo paphunziro lotsatira komanso anapempha kuti nayenso aziphunzira Baibulo, mpaka ananena kuti azilipira. Posapita nthawi, anayamba kuphunzira katatu pamlungu ndipo anapita patsogolo mwauzimu.
12. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene achinyamata angaphunzitsire anzawo choonadi cha m’Baibulo mogwira mtima.
12 Achinyamata angathandize anzawo pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Keanu ali ndi zaka 11 ndipo amakhala ku Hawaii. Iye anali kuwerenga bukuli kusukulu ndipo mnzake wa m’kalasi anamufunsa kuti, “Bwanji suchita zikondwerero zokhudza maholide?” Poyankha, Keanu anawerenga zakumapeto pamutu wakuti “Kodi Tiyenera Kuchita Zikondwerero Zokhudzana ndi Maholide?” Kenako anasonyeza mnzakeyo mitu ya bukuli ndi kumupempha kuti asankhe mutu umene wamusangalatsa kwambiri. Phunziro la Baibulo linayambika. Chaka chautumiki chathachi, Mboni za Yehova zinachititsa maphunziro a Baibulo 6,561,426, ndipo maphunziro ambiri anali kugwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kodi inu mukugwiritsa ntchito buku limeneli pamaphunziro a Baibulo?
13. Kodi kuphunzira Baibulo kumasintha kwambiri maganizo a anthu m’njira yotani?
13 Kuphunzira Malemba pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, kumasintha kwambiri maganizo a anthu amene akufuna kuchita chifuniro cha Mulungu. M’bale wina ndi mkazi wake amene ndi apainiya apadera ku Norway, anayamba kuphunzira Baibulo ndi banja lina lochokera ku Zambia. M’banjali munali ana atatu ndipo sanali kufuna mwana wina. Choncho mkaziyo atakhala ndi pathupi, anagwirizana zochotsa mimbayo. Patangotsala masiku ochepa kuti akaonane ndi dokotala, anaphunzira mutu wakuti “Onani Moyo Mmene Mulungu Amauonera.” Ataona chithunzi cha mwana wosabadwa m’mutuwo, zinawakhudza kwambiri motero kuti anasintha maganizo ochotsa mimba aja. Iwo anapitabe patsogolo mwauzimu ndipo mwanayo atabadwa, anamupatsa dzina la m’bale amene anali kuwaphunzitsa.
14. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kutsatira zimene timaphunzitsa kuli ndi ubwino wake.
14 Mbali ina yofunika kwambiri pa kaphunzitsidwe ka Yesu ndi yakuti iye anali kuchita zimene anaphunzitsa. Anthu ambiri amachita chidwi ndi khalidwe labwino la Mboni za Yehova, zimene zimatsanzira Yesu pankhani imeneyi. Ku New Zealand, akuba anathyola galimoto ya munthu wabizinesi ndi kutenga chikwama chake. Atakanena ku polisi, wapolisi anati: “Chikwama chakocho udzachipeza ngati amene watola ndi wa Mboni za Yehova.” Wa Mboni wina amene anali kuperekera nyuzipepala anatola chikwamacho. Mwini wake atadziwitsidwa, anapita ku nyumba ya mlongoyo. Anasangalala kwambiri atapeza kuti chikalata chofunika kwambiri chinali momwemo. Mlongoyo anauza munthuyo kuti, “Ndinaona kuti ndi bwino kubweza chikwamachi, makamaka chifukwa chakuti ndine wa Mboni za Yehova.” Munthuyo anadabwa kwambiri chifukwa chakuti anakumbukira zimene wapolisi uja anamuuza m’mawa. Zoonadi, Akhristu oona amatsatira zimene amaphunzira m’Baibulo ndipo amatsanzira Yesu.—Aheb. 13:18.
Khalani ndi Mtima Umene Yesu Anali Nawo kwa Anthu
15, 16. Kodi tingachite chiyani kuti anthu akopeke ndi uthenga umene timalalikira?
15 Anthu anakopeka ndi uthenga wa Yesu chifukwa cha mtima umene iye anali nawo. Mwachitsanzo, anthu ovutika anali kupita kwa iye poona kuti anali wachikondi ndi wodzichepetsa. Anthu akafika kwa iye, anali kuwasonyeza chifundo ndi kuwatonthoza ndi mawu olimbikitsa, ndipo anachiritsa matenda a anthu ambiri. (Werengani Maliko 2:1-5.) Ife sitingachite zozizwitsa koma tikhoza kukhala achikondi, odzichepetsa ndi achifundo, ndipo anthu akaona makhalidwe amenewa, amayamba kuphunzira choonadi.
16 Chifundo chinathandiza kwambiri pamene Tariua, mpainiya wapadera, anafika pa khomo la mwamuna wokalamba dzina lake Beere. Mwamunayu amakhala pa chimodzi cha zilumba zakutali za Kiribati ku South Pacific. Ngakhale kuti munthu ameneyu sanafune kumvetsera, Tariua anaona kuti ndi wolemala ndipo chifundo chinamugwira. Mlongoyo anafunsa kuti: “Kodi mukudziwa zimene Mulungu walonjeza kuchitira anthu odwala ndi okalamba?” Kenako anawerenga mavesi mu ulosi wa Yesaya. (Werengani Yesaya 35:5, 6.) Mwamunayo anadabwa ndipo anati, “Ndakhala ndikuwerenga Baibulo kwa zaka zambiri ndipo amishonale a kumpingo kwathu akhala akubwera kwa zaka zambiri, koma sindinaonepo zimenezi m’Baibulo.” Phunziro la Baibulo linayambika ndi Beere, ndipo anapita patsogolo mwauzimu. Ngakhale kuti ndi wolemala, anabatizidwa ndipo tsopano amasamalira kagulu kakutali, ndiponso amayenda pansi kupita kulikonse pachilumbacho kulalikira uthenga wabwino.
Musasiye Kutsanzira Khristu
17, 18. (a) Kodi muyenera kuchita chiyani kuti mukhale mlaliki wogwira mtima? (b) Kodi amene akuchita utumiki wawo mwakhama adzapeza chiyani?
17 Mogwirizana ndi zokumana nazo zosangalatsa zimene zimachitika kawirikawiri mu utumiki, ifenso tingakhale alaliki ogwira mtima ngati tili ndi makhalidwe amene Yesu anali nawo. Choncho, n’koyenera kuti titsanzire Khristu mwa kukhala alaliki achangu.
18 Ena atakhala ophunzira a Yesu, Petulo anafunsa kuti: “N’chiyani chimene ife tidzapezapo?” Yesu anayankha kuti: “Aliyense amene wasiya nyumba kapena abale kapena alongo kapena atate kapena amayi kapena ana kapena minda chifukwa cha dzina langa adzalandira zochuluka koposa ndipo adzapeza moyo wosatha.” (Mat. 19:27-29) Ifenso tikapanda kusiya kutsanzira Yesu Khristu, Mmishonale woposa amishonale onse, mawuwa adzakwaniritsidwa pa ife.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi Yehova akutiphunzitsa m’njira zotani kuti tikhale alaliki?
• N’chifukwa chiyani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndi lothandiza muutumiki?
• Kodi tingakhale bwanji ndi mtima umene Yesu anali nawo kwa anthu?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 17]
Petulo, Andireya, Yakobe ndi Yohane ataitanidwa kuti atsatire Yesu, sanazengereze
[Chithunzi patsamba 19]
Mabuku monga “Baibulo Limaphunzitsa Chiyani,” amatithandiza kukhalabe ogwirizana paziphunzitso zathu