Kodi Woweruza Angalangizidwe?
Kodi Woweruza Angalangizidwe?
SLADJANA, yemwe ndi wa Mboni za Yehova ku Croatia, ankayembekeza kuonekera kukhoti pa nkhani inayake ya zachuma. Iye anafika kwa woweruza pa nthawi yake. Komano mkulu wa khotiyo anachedwa. Sladjana ankafunitsitsa atalankhula za Mawu a Mulungu, motero aliyense akudikirira, iye analimba mtima kuti alankhule ndi woweruzayo.
Ndiye anam’funsa kuti: “Kodi bwana, mukudziwa kuti posachedwapa sikudzakhalanso oweruza ndi makhoti padziko lapansi pano?” Iye ankatanthauza oweruza a masiku anowa.
Podabwa, woweruzayo anangomuyang’ana, osanena kanthu. Posakhalitsa khoti linayamba kugamula nkhaniyo. Atamaliza, Sladjana anaimirira kuti asayine chikalata, ndipo woweruzayo anawerama n’kumufunsa monong’ona kuti: “Kodi umanena zoonadi kuti posachedwapa sikudzakhalanso oweruza ndiponso makhoti padziko lonse?”
Sladjana anayankha kuti: “Inde, bwana. Sindikukayikira ngakhale pang’ono.”
Woweruzayo anafunsa kuti: “Uli ndi umboni wanji?”
Sladjana anayankha kuti: “Ulipo m’Baibulo.”
Ndiye woweruzayo anati angakonde kuwerenga umboni umenewu, koma alibe Baibulo. Motero Sladjana anati akamupezera Baibulo. Wamboniyo anadzapitanso kwa woweruzayo n’kukamupatsa Baibulo, n’kumulimbikitsa kuti azichita phunziro la Baibulo mlungu ndi mlungu. Woweruzayo anavomereza zimenezi ndipo posakhalitsa anakhala wa Mboni za Yehova.
Mwaulosi, lemba la Salmo 2:10 limati: “Tsono Mafumu inu, chitani mwanzeru: langikani [kapena kuti langizikani], oweruza inu a dziko lapansi.” N’zolimbikitsa kwambiri anthu oterewa akavomereza malangizo achikondi a Yehova.
[Chithunzi patsamba 32]
Sladjana ali ndi woweruzayo