Kuyamba N’kuthamangitsidwa, Kenako Kukondedwa
Kuyamba N’kuthamangitsidwa, Kenako Kukondedwa
ZAKA zingapo zapitazo, Santiago ndi mkazi wake Lourdes anasamukira ku tawuni yokongola ya Huillcapata, m’dziko la Peru, kuti akauzeko anthu a kumeneko uthenga wa m’Baibulo wopatsa chiyembekezo. Koma pasanapite nthawi yaitali, wansembe wina anabwera kuchokera ku mzinda wa Cuzco ndipo anaitanitsa anthu a m’tawuniyo. Wansembeyo anachenjeza anthuwo kuti chifukwa choti a Mboni za Yehova abwera m’tawuniyo, mubwera mlili wakupha ndiponso mugwa chipale chofewa chambiri chomwe chidzaphe ng’ombe zawo ndi kuwononga zomera zawo.
Anthu ambiri anamvera mawu amenewa, ndipo koposa theka la chaka, palibe aliyense m’tawuniyo amene anavomera kuphunzira Baibulo ndi Santiago ndi Lourdes. Mkulu wina woyang’anira tawuniyo, dzina lake Miguel, anathamangitsa Santiago ndi Lourdes mumsewu, uku akuwaponya miyala. Koma iwo nthawi zonse ankachita zinthu mwamtendere monga Akristu.
Patapita nthawi, anthu ena m’tawuniyo anavomera kuphunzira Baibulo. Ngakhale Miguel anasintha maganizo ake. Anayamba kuphunzira ndi Santiago, anasiya kumwa mowa mopitirira muyeso, ndipo anakhala munthu wamtendere. Kenaka Miguel, mkazi wake, ndi ana ake awiri aakazi anayamba kutsatira choonadi cha m’Baibulo.
Panopa, m’tawuni imeneyi muli mpingo wa Mboni za Yehova umene ukuchita bwino. Miguel ndi wosangalala kuti miyala yambiri imene anaponyera Santiago ndi Lourdes inkaphonya, ndipo amathokoza kwambiri banja limeneli chifukwa cha chitsanzo chawo chabwino chochita zinthu mwamtendere.
[Zithunzi patsamba 32]
Chifukwa choti Santiago ndi Lourdes (pamwambapa) ankachita zinthu mwamtendere, Miguel (kumanja) anasintha maganizo ake