Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Umboni wa Chikondi, Chikhulupiriro, ndi Kumvera

Umboni wa Chikondi, Chikhulupiriro, ndi Kumvera

Umboni wa Chikondi, Chikhulupiriro, ndi Kumvera

PA May 16, 2005, ku Watchtower Farms ku Wallkill, New York, kunacha kozizira bwino ndipo dzuwa linawala bwino. Udzu ndi maluwa zotchetchedwa bwino zinali kuoneka bwino kwambiri chifukwa cha mvula yomwe inagwa mbandakucha wa tsikuli. Bakha ndi anapiye ake asanu ndi atatu anali kusambira m’madzi abata m’mphepete mwa dziwe. Alendo anadabwa kwambiri ndi kukongolaku ndipo amalankhula chapansipansi, monga ngati sanali kufuna kusokoneza bata limene linapo m’mawawo.

Alendowo anali Mboni za Yehova zomwe zinachokera ku mayiko 48 padziko lonse lapansi. Koma sanabwere kudzaona chilengedwe. Iwo anali ndi chidwi ndi zimene zinali kuchitika m’nyumba yaikulu ya njerwa zofiira, yomwe inawonjezedwa posachedwa ku nyumba za ku Wallkill, zomwe ndi mbali ya Beteli ya ku United States. Atalowa m’nyumbayo, anadabwanso ngakhale kuti zimene zinali kuchitika m’kati sizinali za bata.

Atakwera pamwamba, alendowo anali kuyang’ana pansi n’kuona makina amphamvu kwambiri. Makina osindikizira asanu aakulu anali pa konkiri yong’azimira yaikulu kuposa mabwalo asanu ndi anayi osewererapo mpira wamiyendo atawaphatikiza pamodzi. M’malo amenewa ndi mmene Mabaibulo, mabuku ndi magazini amawasindikizira. Mipukutu ikuluikulu ya mapepala, uliwonse wolemera makilogalamu 1,700, imazungulira monga mawiro a lole yaikulu yothamanga kwambiri. Mpukutu uliwonse wa mapepala wotalika makilomita 23, umatambasuka ndi kudutsa m’makina m’mphindi 25 zokha. Panthawi imeneyi, makina amathira inki ndi kuiumitsa ndiponso kuziziritsa mapepala kotero kuti apangidwe kukhala magazini. Magaziniwa amayenda mothamanga kwambiri kudutsa pamalamba m’mwamba kuti akaikidwe m’mabokosi ndi kutumizidwa ku mipingo. Makina ena ali m’kati mosindikiza zigawo za mabuku, zimene mwamsanga amakaziika ku malo osungirako aakulu kufikira nthawi yozitumiza kumene amapangira mabuku. Zonsezi amachita mogwiritsa ntchito kompyuta.

Alendowa atachoka ku malo osindikizira anakaona malo opangira mabuku. Kumalo amenewa, makina amapanga mabuku a zikuto zolimba ndi Mabaibulo a zikuto zofewa. Tsiku lililonse amapanga mabuku okwana 50,000. Zigawo za mabuku zimasanjidwa bwinobwino, kumatidwa kapena kusokedwa ndi kudulidwa bwinobwino. Ndiyeno amaikako zikuto. Mabuku omalizidwa amaikidwa m’makatoni. Makatoni amamatidwa, kulembedwa ndiponso kuikidwa pamodzi pogwiritsa ntchito makina. Komanso, makina opanga mabuku a zikuto zofewa amapanga ndi kupakira mabuku okwana 100,000 tsiku lililonse. Makina awanso ndi aakulu kwambiri ndipo ali ndi mbali zosiyanasiyana zimene zimathamanga kwambiri popanga mabuku ofotokoza za m’Baibulo.

Makina amenewa amene amagwira ntchito bwinobwino amathamanga kwambiri ndipo ndi opangidwa ndi luso lamakono, lapamwamba kwambiri. Monga momwe tidzaonera, uwu ndi umboninso wa chikondi, chikhulupiriro, ndi kumvera kwa anthu a Mulungu. Koma, n’chifukwa chiyani ntchito yosindikiza inasamutsidwa kuchoka ku Brooklyn, mumzinda wa New York, kupita ku Wallkill?

Chifukwa chachikulu chinali kupepukitsa ntchito yosindikiza ndi kutumiza mabuku mwa kuchitira zonse pamalo amodzi. Kwa zaka zambiri, mabuku anali kuwasindikiza ku Brooklyn ndi kuwatumizira kumeneku, ndipo magazini anali kuwasindikiza ku Wallkill ndi kuwatumizira kumeneku. Kuchita ntchito yonseyi pamalo amodzi kungachepetse anthu ogwira ntchito ndipo ndalama zoperekedwa kwa Yehova zingagwiritsidwe ntchito bwino. Ndiponso, popeza makina osindikizira ku Brooklyn anali akale, makina osindikizira awiri atsopano otchedwa MAN Roland Lithoman anagulidwa kuchokera ku Germany. Makina amenewa anali aakulu kwambiri moti sakanatha kulowa m’nyumba yosindikizira ya ku Brooklyn.

Yehova Akuthandiza pa Ntchitoyi

Nthawi zonse cholinga chosindikiza ndicho kupititsa patsogolo uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Zakhala zoonekeratu kuti kungoyambira pachiyambi Yehova wakhala akudalitsa ntchitoyi. Kuyambira mu 1879 mpaka 1922, mabuku anali kusindikizidwa ndi makampani. Mu 1922, tinachita lendi nyumba ya nsanjika zisanu mu msewu wa 18 Concord Street ku Brooklyn ndipo makina osindikizira mabuku anagulidwa. Panthawi imeneyo, anthu ena anakayikira ngati abale akanatha kugwira ntchitoyo.

Mmodzi wa anthu okayikirawo anali mkulu wa kampani ina yomwe inasindikiza mabuku athu ambiri. Pamene anakacheza ku Concord Street, anati: “Muli ndi makina osindikizira apamwamba kwambiri, koma mulibe munthu amene amadziwa kuwagwiritsa ntchito. Pakangotha miyezi sikisi makinawa sadzatha kugwiranso ntchito. Ndipo mudzazindikira kuti anthu oyenera kusindikiza mabuku anu ndi aja amene akhala akuchita ntchitoyi nthawi yonseyi ndipo amaidziwa bwino kwambiri.”

Panthawi imeneyo woyang’anira nyumba yosindikizira, Robert J. Martin anati: “Mawu amenewa anali omveka ndithu, koma sanaganizire Ambuye ndipo Ambuye yemweyu wakhala nafe nthawi yonseyi. . . . Sipanapite nthawi yaitali chichitikireni zimenezi, tinayamba kupanga mabuku.” Pa zaka 80 zotsatira, Mboni za Yehova zasindikiza mabuku miyandamiyanda pa makina awoawo osindikizira.

Ndiyeno pa October 5, 2002, pamsonkhano wa pachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, chilengezo chinaperekedwa chakuti Bungwe Lolamulira lavomereza kusamutsa ntchito yosindikiza ku United States kupita ku Wallkill. Makina atsopano awiri osindikizira anagulidwa, ndipo anafunika kufika mu February 2004. Abale anafunika kulemba mapulani ndi kukuza nyumba yosindikizira ndi kuimaliza m’chaka chimodzi ndi miyezi itatu kotero kuti mudzalowe makina atsopanowo. Ndiyeno ntchito yolumikiza makina ndi yokonza dongosolo lotumiza mabuku inafunika kutha m’miyezi isanu ndi inayi yotsatira. Ena ayenera kuti anakayikira atamva ndondomeko imeneyi ya kagwiridwe ka ntchito chifukwa ntchitoyi inaoneka yaikulu kwambiri. Koma abale anadziwa kuti chifukwa cha dalitso la Yehova, ntchitoyo itheka.

“Mtima Wogwirizana ndi Wachimwemwe”

Podziwa kuti anthu a Yehova adzazipereka eni ake, abale anayamba ntchitoyo. (Salmo 110:3) Kukula kwa ntchito kunafuna anthu ambiri kuposa amene analipo omwe amagwira ntchito m’madipatimenti omanga a pa Beteli. Abale ndi alongo oposa 1,000 a ku United States ndi Canada, aluso la ntchito yomanga, anadzipereka kuti atumikire kwa kanthawi kuyambira pa mlungu umodzi mpaka miyezi itatu. Ena omwe anali atumiki a m’mayiko ena ndi antchito odzipereka anaitanidwa kuti atenge nawo mbali pa ntchitoyi. Makomiti Omanga Achigawo nawonso anathandiza kwambiri.

Kwa anthu ambiri, kudzipereka kukagwira ntchito ya ku Wallkill kunafuna ndalama zambiri zoyendera ndiponso kupempha nthawi yoti asagwire ntchito yolembedwa. Koma anachita zimenezi mosangalala. Kupeza malo ogona ndi chakudya cha anthu owonjezereka odzipereka amenewa kunapatsa mwayi a banja la Beteli woyesetsa kuchirikiza ntchitoyi. A banja la Beteli oposa 535 ochokera ku Brooklyn, Patterson ndi Wallkill anadzipereka kugwira ntchito Loweruka, kuwonjezera pantchito yawo ya masiku onse ya m’kati mwa mlungu. Chithandizo chachikulu chimene anthu a Mulungu anapereka pantchito yofunikayi chinatheka kokha chifukwa choti Yehova anali kuichirikiza.

Ena anapereka ndalama. Mwachitsanzo, abale analandira kalata yochokera kwa Abby, mtsikana wa zaka zisanu ndi zinayi. Iye analemba kuti: “Ndikuyamikira kwambiri ntchito yonse imene mumagwira, kupanga mabuku onse abwino kwambiri. Mwina ndidzakuchezerani posachedwapa. Bambo anga anati chaka chamawa. Ndidzavala baji kuti mudzandidziwe. Ndikutumiza ndalama zokwana madola 20 zochirikizira makina osindikizira atsopano. Ndi ndalama yanga yodyera imeneyi, koma ndifuna kukupatsani inu abale.”

Mlongo wina analemba kuti: “Landirani zipewa za kolosheni zimene ndinaluka ndekha. Ndikufuna kuti zipewazi ziperekedwe kwa anthu omwe akugwira ntchito ya ku Wallkill. Buku lina lofotokoza za nyengo linanena kuti kudzazizira kwambiri. Sindikudziwa kaya n’zoona kapena ayi. Koma ndikudziwa kuti ntchito yambiri ku Wallkill idzagwiridwa panja, ndipo sindifuna kuti mitu ya abale ndi alongo anga idzazizidwe. Ndilibe luso lililonse limene abale akufuna, koma ndimatha kuluka, chotero ndinafuna kugwiritsa ntchito luso limeneli kuti ndithandize mmene ndingathere.” Anatumiza zipewa za kolosheni zokwana 106.

Nyumba yosindikizira inamalizidwa panthawi yake. Woyang’anira ntchito yosindikiza, John Larson, anati: “Anthu anasonyeza mtima wogwirizana ndi wachimwemwe. Ndani akanakayikira zoti Yehova anali kudalitsa ntchitoyi? Ntchito inayenda mofulumira kwambiri. Ndikukumbukira nditaimirira m’matope mu May 2003 ndikuyang’ana abale akuika maziko a nyumbayi. Chaka chimodzi chisanathe, ndinaimirira pamalo amodzimodziwo ndikuyang’ana makina osindikizira akugwira ntchito.”

Mwambo Wopereka Nyumbazi

Mwambo wopereka nyumba yatsopano yosindikizirayi, limodzi ndi nyumba zitatu zogonamo, unachitika Lolemba, pa May 16, 2005, ku Wallkill. Anthu ku nyumba za Beteli ku Patterson ndi Brooklyn ndiponso ku Canada, anaonerera mwambowu pa vidiyo pamene unali kuchitika. Onse omwe anapezeka pa mwambowu anali okwana 6,049. Theodore Jaracz wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anali tcheyamani ndipo anafotokoza mwachidule mbiri ya ntchito yosindikiza. Mwa kufunsa ndi kusonyeza vidiyo, a John Larson ndi a John Kikot a m’Komiti ya Nthambi, anapenda mbiri ya ntchito yomanga ndiponso ntchito yosindikiza ku United States. John Barr wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yomaliza, ndipo anapereka nyumba yosindikizira ndi nyumba zitatu zatsopano zogonamo kwa Yehova Mulungu.

Mu mlungu wotsatira, ogwira ntchito pa Beteli ochokera ku Patterson ndi Brooklyn anapatsidwa mwayi woona nyumba zatsopanozi. Onse amene anabwera kudzaona malowa panthawiyi anali okwana 5,920.

Kodi Nyumba Yosindikizira Mabukuyi Timaiona Bwanji?

M’nkhani yoperekera nyumbazi, Mbale Barr anakumbutsa omvera ake kuti, nyumba yosindikizikirayi sikukhala yofunika chifukwa cha makinawa. Koma ndi yofunika chifukwa cha anthu. Mabuku amene timasindikiza amakhudza kwambiri moyo wa anthu.

Makina amodzi osindikizira atsopanowa angasindikize mathirakiti okwana miliyoni imodzi mu ola limodzi lokha. Koma thirakiti imodzi ingakhudze kwambiri moyo wa munthu. Mwachitsanzo, mu 1921 anthu okonza njanji ku South Africa anali kugwira ntchito pa njanji ina yaitali kwambiri. Mmodzi wa ogwira ntchitowo, dzina lake Christiaan, anaona kapepala kunsi kwa njanji. Pepalalo linali limodzi la mathirakiti athu. Christiaan anakawerenga mwachidwi kwambiri. Iye anathamangira kwa mpongozi wake ndi kumuuza mosangalala kuti: “Lero ndapeza choonadi!” Patapita nthawi yochepa, iwo anafunsira kudziwa zambiri. Nthambi ya ku South Africa inawatumizira mabuku ena ofotokoza za m’Baibulo. Amuna awiriwa anayamba kuphunzira, anabatizidwa ndipo anali kulalikira kwa ena choonadi cha Baibulo. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri analandira choonadi. Ndipotu, kumayambiriro kwa m’ma 1990, anthu oposa 100 a m’banja lawo anali atakhala Mboni za Yehova. Zonsezi zinatheka chifukwa choti munthu mmodzi anapeza thirakiti imodzi pa njanji.

Mbale Barr anati, mabuku amene timasindikiza, amabweretsa anthu m’choonadi, amawasunga m’choonadi, amawalimbikitsa kukhala achangu kwambiri ndipo amalimbitsa ubale wathu. Ndipo koposa zonse, mabuku amene ife tonse timatenga nawo mbali kugawira ena, amalemekeza Yehova, Mulungu wathu.

Kodi Yehova Amaiona Bwanji Nyumba Yosindikizirayi?

Mbale Barr anafunsanso omvera kuti aganizire mmene Yehova amaionera nyumba yosindikizirayi. Ndithudi, iye sadalira nyumbayi. Iye angathe kupangitsa miyala kulalikira uthenga wabwino. (Luka 19:40) Iye samachita chidwi ndi mphamvu za makinawa, kukula kwake, kuthamanga kwake, kapena zimene angachite. Iye ndi amene anapanga chilengedwe chonsechi. (Salmo 147:10, 11) Yehova amadziwa njira zapamwamba kwambiri zopangira mabuku zimene munthu sanazitulukirepo ngakhale kuziganizira n’komwe. Chotero, n’chiyani chimene Yehova amaona kukhala chofunika kwambiri? Zoonadi, m’nyumbayi amaonamo makhalidwe ofunika kwambiri a anthu ake monga chikondi, chikhulupiriro ndi kumvera.

Iye anafotokoza chikondi mogwiritsa ntchito fanizo. Mtsikana anaphikira makolo ake keke. N’kutheka kuti makolowo anasangalala. Mulimonse mmene kekeyo inaphikidwira, chimene chinasangalatsa kwambiri makolowa ndi chikondi cha mwanayo, chimene anasonyeza mwa kuwapatsa keke. Mofananamo, pamene Yehova ayang’ana nyumba yosindikizira yatsopanoyi, iye samangoona nyumba ndi makinawa. Choyamba, amaona chikondi chimene tam’sonyeza.​—Ahebri 6:10.

Ndiponso, monga momwe Yehova anaonera chingalawa kukhala njira imene Nowa anasonyezera chikhulupiriro, nyumba yosindikizirayi amaionanso kukhala umboni wa chikhulupiriro chathu. Kukhulupirira chiyani? Nowa anakhulupirira kuti zimene Yehova analosera zidzachitika. Tili ndi chikhulupiriro choti tikukhala m’masiku otsiriza, kuti uthenga wabwino ndiwo uthenga wofunika kwambiri umene ukulalikidwa padziko lapansi, ndiponso kuti n’kofunika kuti anthu aumve. Timadziwa kuti uthenga wa m’Baibulo ungapulumutse anthu.​—Aroma 10:13, 14.

Mosakayikira, Yehova amaonanso nyumbayi, kukhala umboni wa kumvera kwathu. Monga momwe tikudziwira, ndi chifuniro chake kuti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse mapeto asanafike. (Mateyu 24:14) Nyumba yosindikizirayi, kuphatikizapo nyumba zinanso zosindikizira zomwe zili m’madera ena padziko lapansi, idzathandiza pokwaniritsa ntchitoyi.

Ndithudi, chikondi, chikhulupiriro ndi kumvera zimene zasonyezedwa posonkhanitsa ndalama zomangira ndi zoyendetsera ntchitoyi, zikusonyezedwanso ndi ntchito imene anthu a Yehova kulikonse akuchita mwachangu pamene akupitiriza kulengeza choonadi kwa anthu onse ofuna kumvera.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 11]

KUWONJEZEKA KWA NTCHITO YOSINDIKIZA MABUKU KU UNITED STATES

1920: Kusindikiza magazini ndi makina oyenda okha, ku 35 Myrtle Avenue, Brooklyn.

1922: Nyumba yosindikizira isamutsidwa kupita ku 18 Concord Street m’nyumba ya nsanjika zisanu. M’chaka chimenechi mabuku anayamba kusindikizidwa.

1927: Nyumba yosindikizira inasamutsidwa kupita ku nyumba yatsopano yomwe inamangidwa ku 117 Adams Street.

1949: Nyumba ya nsanjika zisanu ndi zitatu inawonjezera kukula kwa nyumba yosindikizira inayo kuwirikiza kawiri.

1956: Nyumba yosindikizira ya ku Adams Street inawonjezedwanso kuwirikiza kawiri pamene nyumba yatsopano inamangidwa ku 77 Sands Street.

1967: Nyumba ya nsanjika zisanu ndi zinayi inamangidwa, ndipo anaiphatikiza ndi yakale, inakula kuwirikiza kakhumi kuposa yakale.

1973: Nyumba yothandizana ndi imene inalipo inamangidwa ku Wallkill, makamaka kuti azisindikiziramo magazini.

2004: Ntchito yonse yosindikiza, kupanga mabuku ndi kuwatumiza ya ku United States anaisamutsa kuti yonse izichitikira pamodzi ku Wallkill.