Yehova Ndi Mbusa Wathu
Yehova Ndi Mbusa Wathu
“Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa [kanthu].”—SALMO 23:1.
1-3. N’chifukwa chiyani zili zosadabwitsa kuti Davide anafanizira Yehova ndi mbusa?
MUTAFUNSIDWA kuti mufotokoze mmene Yehova amasamalirira anthu ake, kodi munganene zotani? Kodi ndi fanizo lotani limene mungapereke losonyeza mmene iye amawasamalirira mwachikondi atumiki ake okhulupirika? Zaka zoposa 3,000 zapitazo, Mfumu Davide inam’fotokoza bwino kwambiri Yehova m’salmo limene inalemba. M’salmo limeneli Davide anapereka fanizo logwirizana ndi ntchito imene ankagwira ali mwana.
2 Ali mnyamata, Davide anali mbusa, motero ankadziwa za kasamaliridwe ka nkhosa. Ankadziwa bwino kuti, ngati nkhosa zilibe woziyang’anira, zimasochera, kubedwa, kapena kugwidwa ndi zilombo mosavuta. (1 Samueli 17:34-36) Popanda mbusa wachikondi, nkhosa sizingapeze busa la chakudya chokwanira. N’zosakayikitsa kuti Davide atakula, ankakumbukira bwino zomwe zinachitika nthawi zambiri pamene iye anali kutsogolera, kuteteza, ndiponso kudyetsa nkhosa.
3 Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti Davide anaganizira ntchito ya mbusa atauziridwa kufotokoza mmene Yehova amasamalirira anthu ake. Salmo la 23 limene linalembedwa ndi Davide, limayamba motere: “Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa [kanthu].” Tiyeni tione chifukwa chimene mawu amenewa alili oyenerera. Kenako, tigwiritsa ntchito Salmo 23, kuona kuti Yehova amasamalira motani anthu omulambira ngati mmene mbusa amasamalirira nkhosa zake.—1 Petro 2:25.
Fanizo Loyenerera
4, 5. Kodi Baibulo limafotokoza motani makhalidwe a nkhosa?
4 M’Baibulo muli mayina ambiri aulemu a Yehova, koma dzina lakuti “Mbusa” ndi limodzi mwa mayina amene amasonyeza bwino chikondi ndi chisamaliro chake chachikulu. (Salmo 80:1) Kuti timvetse bwino chifukwa chake Yehova akuyenerera kutchedwa Mbusa, ndi bwino kuti tidziwe zinthu ziwiri. Choyamba, tidziwe chikhalidwe cha nkhosa ndipo chachiwiri, ntchito ndi makhalidwe a mbusa wabwino.
5 Baibulo limatchula kawirikawiri makhalidwe a nkhosa, ndipo limati zimakopeka mosavuta ndi chikondi cha mbusa wawo (2 Samueli 12:3), n’zofatsa (Yesaya 53:7), ndiponso sizitha kudziteteza. (Mika 5:8) Mwamuna wina wolemba mabuku amene anawetapo nkhosa kwa zaka zambiri anati: “N’zosatheka kuti nkhosa ‘zidzisamalire zokha’ ngati mmene ena angaganizire. Palibenso ziweto zina zimene zimafuna kuziyang’anira ndi kuzisamalira nthawi zonse ngati nkhosa.” Moyo wa ziweto zosatha kudzisamalirazi umadalira pa mbusa wachikondi.—Ezekieli 34:5.
6. Kodi buku lina la matanthauzo a mawu a m’Baibulo limafotokoza motani zimene abusa akale ankachita tsiku lililonse?
6 Kodi abusa akale ankafunika kutani tsiku *
lililonse? Buku lina la matanthauzo a mawu a m’Baibulo limati: “M’mawa kwambiri ankatsogolera nkhosa kutuluka m’khola, ulendo nazo ku busa. Kumeneko, ankaziyang’anira tsiku lonse, n’kumaonetsetsa kuti palibe yosochera, ndipo ngati ina yazemba kwa nthawi yochepa chabe n’kumakayenda kwayokha, ankaifunafuna mpaka ataipeza n’kubwera nayo pa zinzake. . . . Usiku amabwera nazo ku khola, ndipo zikamadutsa pakhomo amaziwerenga ndi ndodo pofuna kutsimikizira kuti palibe imene yasowa. . . . Nthawi zambiri ankafunika kulondera kholalo usiku, kuliteteza kwa zilombo kapena anthu akuba.”7. N’chifukwa chiyani nthawi zina mbusa ankafunika kuleza mtima ndiponso kukhala wachikondi kwambiri?
7 Nthawi zina nkhosa, makamaka zabere ndiponso zazing’ono, zinkafunika kuleza nazo mtima ndiponso kuzikonda kwambiri. (Genesis 33:13) Buku lina lofotokoza za m’Baibulo limati: “Nthawi zambiri nkhosa zimaberekera kutali ndi kumudzi, m’mbali mwa phiri. Mbusa amayang’anira bwino nkhosa ikamabereka ndipo amanyamula kamwanako kupita nako ku khola. Kwa masiku angapo, mpaka pamene kayamba kuyenda, iye amatha kukanyamulira m’manja kapena pachovala chake chakumtunda chomwe wachipinda.” (Yesaya 40:10, 11) N’zoonekeratu kuti mbusa wabwino amafunika kukhala wamphamvu ndiponso wachikondi.
8. Kodi Davide anapereka zifukwa zotani zomwe zinamuchititsa kukhala ndi chikhulupiriro mwa Yehova?
8 “Yehova ndiye mbusa wanga.” Kodi fanizo limeneli siloyenereradi Atate wathu wakumwamba? Pamene tikukambirana Salmo 23, tiona mmene Mulungu amatisamalirira mwamphamvu ndiponso mwachikondi ngati mbusa. M’vesi loyamba, Davide akufotokoza chikhulupiriro chake chakuti Mulungu adzapatsa nkhosa Zake zinthu zonse zofunikira moti ‘sizidzasowa’ kanthu kalikonse. M’mavesi otsatira, Davide akupereka zifukwa zitatu zomwe zinamuchititsa kukhala ndi chikhulupiriro choterocho. Nazi zifukwa zakezo: Yehova amatsogolera, amateteza, ndiponso amadyetsa nkhosa zake. Tiyeni tikambirane zifukwazi chimodzi ndi chimodzi.
“Anditsogolera”
9. Kodi Davide akupereka chithunzithunzi chotani chamtendere, ndipo nkhosa zingafike motani ku malo oterowo?
9 Choyamba, Yehova amatsogolera anthu ake. Davide analemba kuti: “Andigonetsa ku busa lamsipu: Anditsogolera ku madzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m’mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.” (Salmo 23:2, 3) Pofotokoza za nkhosa zitagona mwamtendere m’kati mwa msipu wochuluka, Davide akutipatsa chithunzithunzi cha kukhala wokhutira, wotsitsimulidwa, ndiponso wotetezeka. Mawu a Chihebri omwe anawamasulira kuti “busa” angatanthauze “malo abwino kwambiri.” N’zodziwikiratu kuti nkhosa sizingadzipezere zokha malo otsitsimula oti zigonepo mwamtendere. Mbusa wawo ayenera kuzitsogolera ku “malo abwino kwambiri” oterowo.
10. Kodi Mulungu amasonyeza motani kuti amatikhulupirira?
10 Kodi Yehova amatitsogolera motani masiku ano? Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndi mwa chitsanzo. Mawu ake amatilimbikitsa kuti ‘tikhale akutsanza a Mulungu.’ (Aefeso 5:1) M’nkhani imene mukupezeka mawu amenewa mukutchulidwa chifundo, kukhululuka, ndi chikondi. (Aefeso 4:32; 5:2) Kunena zoona, Yehova amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pankhani ya makhalidwe osangalatsa amenewa. Kodi pempho lakeli loti timutsanzire, ndi loti ife sitingalikwanitse? Ayi. Kwenikweni, malangizo ouziridwa amenewa ndi umboni woti iye amatikhulupirira. Motani? Tinapangidwa m’chifaniziro cha Mulungu, zomwe zikutanthauza kuti timatha kusonyeza makhalidwe abwino ndiponso timafuna kupembedza. (Genesis 1:26) Motero, Yehova amadziwa kuti ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, timabadwa ndi mtima woti tingathe kukhala ndi makhalidwe ofanana ndi ake. Tangoganizirani kuti Mulungu wathu wachikondi ali ndi chikhulupiriro choti tikhoza kukhala ngati iyeyo. Ngati titsatira chitsanzo chake, tingati iye adzatitsogolera ku malo abwino kwambiri kokapuma. M’dziko lachiwawali, ife ‘tidzakhala bwino’ kapena kuti motetezeka, ndi kukhala pamtendere chifukwa chodziwa kuti Mulungu amatiyanja.—Salmo 4:8; 29:11.
11. Potsogolera nkhosa zake, kodi Yehova amaganizira chiyani, ndipo kodi zimenezi zimaonekera motani pa zimene amafuna kuti tichite?
11 Pamene akutitsogolera, Yehova amachita zinthu mwachikondi ndiponso moleza mtima. Mbusa amaganizira zinthu zimene nkhosa zake sizingathe kuchita, motero amazitsogolera “monga mwa mayendedwe a” nkhosazo. (Genesis 33:14) N’chimodzimodzinso ndi Yehova. Iye amatsogolera “monga mwa mayendedwe a” nkhosa zake. Amaganizira zimene tingathe ndiponso mmene zinthu zilili pamoyo wathu. Akachita zimenezi, tingati amasintha mayendedwe ake, ndipo satiyembekezera kuchita zimene sitingakwanitse. Zomwe amafuna ndi kuti tichite zinthu mochokera mumtima. (Akolose 3:23) Komano bwanji ngati ndinu wachikulire ndipo simungathe kuchita zimene munkachita kale? Kapena bwanji ngati muli ndi matenda aakulu omwe akukulepheretsani kuchita zinthu zina? Pamenepo ndiye pokomera mfundo yakuti tichite zinthu ndi mtima wathu wonse. Palibe anthu awiri amene ali ofanana ndendende. Kutumikira ndi mtima wanu wonse kumatanthauza kuti muyesetse kuchita zonse zimene inuyo mungathe potumikira Mulungu. Ngakhale kuti pali mavuto amene angathe kusokoneza kayendedwe kathu, Yehova amayamikira tikamamupembedza ndi mtima wathu wonse.—Marko 12:29, 30.
12. Kodi m’Chilamulo cha Mose muli chitsanzo chotani chosonyeza kuti Yehova amatsogolera “monga mwa mayendedwe a” nkhosa zake?
12 Kuti mumvetse bwino momwe Yehova amatsogolera “monga mwa mayendedwe a” nkhosa zake, taonani chitsanzo ichi chokhudza zina mwa nsembe zopalamula zotchulidwa m’Chilamulo cha Mose. Yehova ankafuna nsembe zabwino zoperekedwa ndi munthu woyamikira. Komanso, nsembezo zinali m’magulumagulu malinga ndi zimene munthu woperekayo angakwanitse. Chilamulo chinati: ‘Chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nazo . . . njiwa ziwiri, kapena maunda awiri.’ Nanga bwanji ngati sakanatha kupereka maunda awiri? Ankatha kubwera ndi “ufa wosalala.” (Levitiko 5:7, 11) Izi zikusonyeza kuti Mulungu sanalamule zinthu zimene woperekayo sangazikwanitse. Poti Mulungu sasintha, n’zolimbikitsa kudziwa kuti iye safuna kuti tim’patse zimene sitingakwanitse. M’malo mwake iye amasangalala kulandira zomwe tingakwanitse. (Malaki 3:6) Ndi zosangalatsa kwambiri kutsogoleredwa ndi Mbusa womvetsa zinthu ngati ameneyu!
“Sindidzawopa Choipa; Pakuti Inu Muli ndi Ine”
13. Pa Salmo 23:4, kodi Davide akulankhula motani mosonyeza ubwenzi wolimba kwambiri, ndipo n’chifukwa chiyani izi sizodabwitsa?
13 Davide akupereka chifukwa chachiwiri cha chikhulupiriro chake: Yehova amateteza nkhosa zake. Timawerenga kuti: “Inde, ndingakhale ndiyenda m’chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzawopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine: Chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.” (Salmo 23:4) Pano tsopano Davide akulankhula mosonyeza ubwenzi wolimba kwambiri, ndipo akutchula Yehova ndi m’lowam’malo wa dzina wakuti “inu.” Izi sizodabwitsa, chifukwa Davide akunena za mmene Mulungu anam’thandizira kupirira mavuto. Davide anakhalapo m’zigwa zambiri zoopsa. Izi ndi nthawi zimene moyo wake unali pangozi. Komatu sanalefulidwe ndi mantha, chifukwa ankadziwa kuti Mulungu anali naye limodzi ndi “chibonga” ndiponso “ndodo” Yake. Kudziwa zimenezi kunam’limbikitsa Davide ndipo mosakayikira kunalimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova. *
14. Kodi Baibulo limatitsimikizira zotani pankhani ya chitetezo cha Yehova, koma kodi zimenezi sizikutanthauza chiyani?
14 Kodi Yehova amaziteteza motani nkhosa zake masiku ano? Baibulo limatitsimikizira kuti palibe mdani aliyense, kaya chiwanda kapena munthu, amene adzathe kufafaniza nkhosa zake padziko pano. Yehova sangalole zimenezo kuchitika. (Yesaya 54:17; 2 Petro 2:9) Komano izi sizikutanthauza kuti Mbusa wathuyu adzatitchinjiriza ku mavuto onse. Timakumana ndi mayesero ofanana ndi a anthu ena onse, ndiponso timatsutsidwa monganso mmene zimachitikira kwa Akristu ena onse oona. (2 Timoteo 3:12; Yakobo 1:2) Nthawi zina tinganene kuti ‘timayenda m’chigwa cha mthunzi wa imfa.’ Mwachitsanzo, tingafike potsala pang’ono kufa chifukwa cha kuzunzidwa kapena matenda. Kapena n’kutheka kuti munthu amene timam’konda kwambiri wangotsala pang’onong’ono kufa kapena wamwalira kumene. Panthawi imene imaoneka yovuta kwambiri imeneyi, Mbusa wathu amakhala nafe, ndiponso amatiyang’anira. Kodi amatero motani?
15, 16. (a) Kodi Yehova amatithandiza motani kuthana ndi mavuto amene tingakumane nawo? (b) Fotokozani nkhani imene ikusonyeza mmene Yehova amatithandizira pamavuto.
15 Yehova salonjeza kuti adzachita zozizwitsa potithandiza. * Koma izi zikutsimikizira kuti: Yehova adzatithandiza kuthana ndi vuto lililonse limene tingakumane nalo. Angathe kutipatsa nzeru zopiririra ‘mayesero a mitundumitundu.’ (Yakobo 1:2-5) Mbusa amagwiritsa ntchito ndodo yake osati kungothamangitsira zilombo komanso kulishila nkhosa zake kuti zipite kwabwino. Yehova ‘angatilishe,’ mwina kudzera mwa olambira anzathu, kuti titsatire malangizo a m’Baibulo amene angatithandize kwambiri pa mavuto athu. Kuwonjezera apo, Yehova angatipatse mphamvu kuti tithe kupirira. (Afilipi 4:13) Kudzera mwa mzimu wake woyera, iye angatipatse “ukulu woposa wamphamvu,” kapena kuti mphamvu zoposa zachibadwa. (2 Akorinto 4:7) Mzimu wa Mulungu ungatithandize kupirira chiyeso chilichonse chomwe Satana angatiyese nacho. (1 Akorinto 10:13) Kodi sizolimbikitsa kudziwa kuti Yehova ndi wokonzeka nthawi zonse kuti atithandize?
16 Inde, kaya tikhale m’chigwa chotani cha mdima, sitiyendamo tokhatokha. Mbusa wathu amakhala nafe, ndipo amatithandiza m’njira zimene poyambirira ifeyo sitingazimvetse bwinobwino. Taonani chitsanzo cha Mkristu wina yemwe ndi mkulu mumpingo ndipo anam’peza ndi chotupa m’bongo. Iye anati: “Kunena zoona, poyamba ndinkaganiza kuti Yehova wandikwiyira kapenanso kuti sandikonda. Koma sindinafune m’pang’ono pomwe kuchoka kumbali ya Yehova. M’malo mwake, ndinamufotokozera mavuto anga. Ndipo Yehova anandithandiza, n’kumandilimbikitsa nthawi zambiri kudzera mwa abale ndi alongo anga achikristu. Ambiri anali kundibenthulira nzeru zosonyeza mmene iwo apiririra matenda aakulu. Zonena zawo zabwino zinandikumbutsa kuti panalibe chachilendo ndi vuto langalo. Thandizo lawo labwino kwambiri, kuphatikizaponso zimene ankandichitira mokoma mtima, zinanditsimikizira kuti Yehova sanandikwiyire. N’zoona kuti ndiyenera kupitiriza kulimbana ndi matenda angawa, ndipo sindikudziwa kuti zidzatha bwanji. Koma sindikukayika n’komwe kuti Yehova ali nane ndipo adzapitiriza kundithandiza m’mavuto anga onse.”
“Mundiyalikira Gome Pamaso Panga”
17. Pa Salmo 23:5, kodi Davide akumufotokoza motani Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani izi sizikutsutsana ndi fanizo la mbusa lija?
17 Davide tsopano akupereka chifukwa chachitatu chokhulupirira Mbusa wake: Yehova Salmo 23:5) M’vesi ili, Davide anafotokoza Mbusa wake kukhala wochereza alendo wowolowa manja, amene wakonza chakudya ndi zakumwa zamwanaalirenji. Sikuti pali kutsutsana pakati pa mafanizo awiriwa, la mbusa wachikondi ndi la wochereza alendo wowolowa manja. Ndipotu, mbusa wabwino amayenera kudziwa kumene angapeze busa lamsipu wabwino ndi madzi okwanira kumwa nkhosa zake kuti ‘zisasowe’ kanthu kalikonse.—Salmo 23:1, 2.
amadyetsa nkhosa zake, ndipo amazipatsa chakudya chamwanaalirenji. Davide analemba kuti: “Mundiyalikira gome pamaso panga m’kuona kwa adani anga: Mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.” (18. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova ndi wochereza alendo wowolowa manja?
18 Kodi Mbusa wathu nayenso ndi wochereza alendo wowolowa manja? N’zosachita kufunsa zimenezo. Tangoganizirani za chakudya chauzimu chabwino, chochuluka, ndiponso chosiyanasiyana chomwe timalandira. Kudzera mwa gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, Yehova watipatsa mabuku othandiza kwambiri ndiponso maphunziro abwino kwambiri pa misonkhano ya mpingo, yadera, yapadera, ndi yachigawo. Zonsezi zimatithandiza kuti tisakhale osowa mwauzimu. (Mateyu 24:45-47) Sitiperewedwa chakudya chauzimu ngakhale pang’ono. “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wafalitsa Mabaibulo ndiponso mabuku othandiza kuphunzira Baibulo okwana mamiliyoni ambiri, ndipo tikunena pano mabukuwa akupezeka m’zinenero 413. Yehova wapereka chakudya chauzimu chimenechi mosiyanasiyana, kuyambira pa “mkaka,” womwe ndi ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo, mpaka kufika pa “chakudya chotafuna,” chomwe ndi mfundo zakuya za m’Baibulo. (Ahebri 5:11-14) Chifukwa cha zimenezi, tikakumana ndi mavuto kapena pamene tikufunika kusankha zochita, tikhoza kupeza thandizo loyenerera. Kodi tikanatani padakapanda chakudya chauzimu chimenechi? Mbusa wathu alidi wochereza alendo wowolowa manja kwambiri!—Yesaya 25:6; 65:13.
“Ndidzakhala M’nyumba ya Yehova”
19, 20. (a) Pa Salmo 23:6, kodi Davide akufotokoza chikhulupiriro chotani, ndipo tingatani kuti nafe tikhale ndi chikhulupiriro choterocho? (b) Kodi m’nkhani yotsatirayi mwafotokozedwa zotani?
19 Ataganizira zochita za Mbusa wake ndi Womupatsa Zinthu, Davide akumaliza motere: “Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga: Ndipo ndidzakhala m’nyumba ya Yehova masiku onse.” (Salmo 23:6) Tsopano Davide akulankhula ndi mtima woyamikira kwambiri ndiponso mwachikhulupiriro. Ali ndi mtima woyamikira pokumbukira kale lake ndipo ali ndi chikhulupiriro poganizira za tsogolo lake. Davide yemwe anakhalapo mbusa akuona kuti ndi wotetezeka, atadziwa kuti malinga ngati ali paubwenzi ndi Mbusa wake wakumwamba, ngati kuti akukhala m’nyumba Yake, Yehova adzam’samalira bwino nthawi zonse.
20 Tikuyamikira kwambiri mawu abwino opezeka mu Salmo la 23. Palibenso njira ina yomwe Davide akanafotokozera bwino mmene Yehova amatsogolera, amatetezera, ndiponso mmene amadyetsera nkhosa zake! Mawu abwino a Davide ali m’Baibulo pofuna kutithandiza kukhulupirira kuti nafenso tingadalire Yehova monga Mbusa wathu. Inde, malinga ngati tili paubwenzi wolimba ndi Yehova, iye adzatisamalira monga Mbusa wachikondi “masiku onse,” ngakhalenso kwamuyaya. Komabe, monga nkhosa zake, tili ndi udindo woyenda ndi Mbusa wathu wamkuluyu, Yehova. M’nkhani yotsatirayi tiona zimene zimafunika pa udindo umenewu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 13 Davide analemba masalmo ambiri omwe anatamandamo Yehova chifukwa chom’pulumutsa kungozi zosiyanasiyana.—Mwachitsanzo, onani timawu tapamwamba ta Masalimo 18, 34, 56, 57, 59, ndi 63.
^ ndime 15 Onani nkhani yakuti “Kodi Tiyembekezere Kuti Mulungu Adzachitapo Kanthu Motani?” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2003.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani zili zoyenerera kuti Davide anayerekeza Yehova ndi mbusa?
• Kodi Yehova amatitsogolera bwanji moganizira kuperewera kwathu?
• Kodi Yehova amatithandiza m’njira zotani kupirira mayesero?
• Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yehova ndi wochereza alendo wowolowa manja?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 18]
Mofanana ndi mbusa ku Israyeli, Yehova amatsogolera nkhosa zake