Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muyenda ndi Mulungu?

Kodi Muyenda ndi Mulungu?

Kodi Muyenda ndi Mulungu?

‘Yendani modzichepetsa ndi Mulungu wanu.’​—MIKA 6:8.

1, 2. Kodi tingayerekezere motani mmene Yehova amamvera akamationa ndi mmene limamvera kholo lomwe likuphunzitsa mwana kuyenda?

M WANA wamng’ono akuimirira miyendo ili njenjenje, n’kugwira manja amene kholo lake lam’tansira ndipo akuyenda kwa nthawi yoyamba. Zingaoneke ngati zopanda ntchito kwenikweni, koma sichoncho kwa mayi ndi bambo a mwanayo. Imeneyi ndi nthawi yopatsa chiyembekezo poganizira za tsogolo la mwanayo. Iwo amayembekezera mwachidwi kuti m’miyezi ndiponso zaka zomwe zikubwera, adzayenda ndi mwana wawoyo, atagwirana naye manja. Iwo amayembekezera kudzatsogolera ndiponso kudzam’thandiza mwanayo tsogolo lake lonse.

2 Umu ndi mmenenso Yehova Mulungu amamvera ndi ana ake a padziko lapansi. Nthawi ina ananena izi zokhudza anthu ake Aisrayeli, kapena kuti Efraimu: “Ndinaphunzitsa Efraimu kuyenda, ndinawafungata m’manja mwanga . . . Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za chikondi.” (Hoseya 11:3, 4) Apa, Yehova anadzifotokoza monga kholo lachikondi lomwe moleza mtima laphunzitsa mwana wake kuyenda, mwinanso kumunyamula akagwa. Yehova, Kholo labwino kwambiri, ndi wokonzeka kutiphunzitsa kuyenda. Amasangalalanso kuyenda nafe limodzi pamene tikuzolowera kuyenda. Monga momwe likusonyezera lemba lotsogolera nkhani ino, tingathe kuyenda ndi Mulungu. (Mika 6:8) Koma kodi kuyenda ndi Mulungu kumatanthauzanji? N’chifukwa chiyani tifunika kuyenda naye? Zingatheke motani kuyenda naye? Ndipo ndi madalitso otani amene munthu amapeza poyenda ndi Mulungu? Tiyeni tikambirane mafunso anayiwa limodzi ndi limodzi.

Kodi Kuyenda ndi Mulungu Kumatanthauzanji?

3, 4. (a) Kodi n’chiyani chomwe chili chochititsa chidwi ndi chithunzithunzi cha kuyenda ndi Mulungu? (b) Kodi kuyenda ndi Mulungu kumatanthauzanji?

3 N’zoona kuti n’zosatheka kuti munthu ayende zenizeni ndi Yehova, yemwe ndi mzimu. (Eksodo 33:20; Yohane 4:24) Motero Baibulo likamanena za anthu akuyenda ndi Mulungu, limakhala likuphiphiritsa. Limapereka fanizo labwino kwambiri lomwe munthu wa dziko kapena chikhalidwe chilichonse sangalephere kumva ndiponso limene lingagwiritsidwe ntchito m’nyengo iliyonse. Ndipo kodi n’kuti kapena ndi nyengo iti imene anthu sangamvetse mfundo ya munthu akuyenda ndi mnzake? Kodi si zoona kuti fanizo limeneli limatipatsa chithunzithunzi cha chikondi komanso mgwirizano wolimba? Malingaliro amenewa amatithandizako kuzindikira kuti kuyenda ndi Mulungu kumatanthauzanji. Komabe, tiyeni tione zimenezi mwatsatanetsatane.

4 Kumbukirani za Enoke ndi Nowa, anthu amene anali okhulupirika. N’chifukwa chiyani amafotokozedwa kuti anayenda ndi Mulungu? (Genesis 5:24; 6:9) M’Baibulo, mawu akuti “kuyenda” kawirikawiri amatanthauza kuchita zinthu motsatira njira inayake. Enoke ndi Nowa anasankha kukhala moyo wogwirizana ndi chifuniro cha Yehova Mulungu. Mosiyana ndi anthu amene analipo m’masiku awo, iwo anadalira Yehova kuti ndiye awatsogolere ndipo anali kumvera malangizo ake. Anali kum’dalira. Kodi izi zikutanthauza kuti Yehova anali kuwasankhira zochita? Ayi. Yehova anapatsa anthu ufulu wosankha ndipo amafuna kuti tizigwiritsa ntchito mphatso imeneyi mogwirizana ndi “nzeru” zathu. (Aroma 12:1, Malembo Oyera) Koma posankha zochita, timadzichepetsa ndi kulola nzeru zakuya za Yehova kutsogolera nzeru zathuzo. (Miyambo 3:5, 6; Yesaya 55:8, 9) Moyo wathu ukakhala wotero, timakhala tikuyendera limodzi ndi Yehova.

5. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ananena za kuwonjezera mkono pa moyo wa munthu?

5 Baibulo nthawi zambiri limayerekezera moyo ndi ulendo. M’mavesi ena kuyerekezera kumeneku kumakhala kochita kuonekeratu, koma m’mavesi ena sizikhala choncho. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuwonjezera pa msinkhu [kapena kuti pa moyo] wake mkono umodzi?” (Mateyu 6:27) M’vesili muli mawu ena omwe angazunguze munthu. N’chifukwa chiyani Yesu ananena za kuwonjezera “mkono umodzi,” womwe ndi muyeso wa mtunda, pa moyo wa munthu, womwe umayesedwa ndi nthawi? * N’zoonekeratu kuti Yesu apa anali kuyerekezera moyo ndi ulendo. Ndi fanizoli, Yesu anaphunzitsa kuti kuda nkhawa sikungakuthandizeni kuwonjezera ngakhale phazi limodzi pa ulendo wanu pa moyo. Ndiyeno, kodi tinene kuti palibe chimene tingachite kuti titalikitse mtunda wa ulendowu? Ayi, sichoncho. Zimenezi zikutifikitsa pa funso lathu lachiwiri loti, N’chifukwa chiyani tifunika kuyenda ndi Mulungu?

N’chifukwa Chiyani Tifunika Kuyenda ndi Mulungu?

6, 7. Kodi n’chiyani chimene anthu opanda ungwiro amafunikira kwambiri, ndipo n’chifukwa chiyani tingachite bwino kudalira Yehova kuti atithandize pavuto limenelo?

6 Chimodzi mwa zifukwa zimene tifunikira kuyenda ndi Yehova Mulungu chafotokozedwa pa Yeremiya 10:23. Lembali limati: “Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” Motero anthufe sitingathe ndipo si udindo wathu kulongosola moyo wathu. Sitingachitirenso mwina ayi, tikufunika kulangizidwa basi. Anthu amene amaumirira kuchita zawozawo, osafuna kutsogoleredwa ndi Mulungu, amachita zimene Adamu ndi Hava anachita, zomwe ndi zolakwika. Banja loyambirirali linadzitengera lokha mphamvu zosankha chabwino ndi choipa. (Genesis 3:1-6) “Sikuli” kwa ife kukhala ndi mphamvu zimenezi.

7 Kodi inu simukuona kufunika kotsogoleredwa m’moyo wanu? Tsiku ndi tsiku timafunika kusankha zochita, zina zikuluzikulu ndipo zina zing’onozing’ono. Zina mwa zosankhazi n’zovuta ndipo zingakhudze tsogolo lathu, komanso tsogolo la anthu ena amene timawakonda. Ndiyeno tayerekezani kuti munthu wina wakale kwambiri ndiponso wanzeru zakuya koposa akufuna kutipatsa malangizo abwino ofotokoza mmene tingapangire zosankhazo! N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri masiku ano amakonda kukhulupirira maganizo awo ndi kudzitsogolera okha. Amanyalanyaza mfundo yoona yopezeka pa Miyambo 28:26, pamene timawerenga kuti: “Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa; koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.” Yehova amafuna kuti tipewe mavuto omwe tingakumane nawo chifukwa chokhulupirira mtima wa munthu, womwe ndi wonyenga. (Yeremiya 17:9) Amafuna kuti tiyende mwanzeru, timukhulupirire monga Mtsogoleri ndi Mlangizi wathu wanzeru. Tikatero, moyo wathu umakhala wotetezeka, wokhutiritsa, ndiponso waphindu.

8. Kodi mwachibadwa timapita kuti chifukwa cha uchimo ndi kupanda ungwiro, komano Yehova amatifunira zotani?

8 Chifukwa china chimene timafunikira kuyenda ndi Mulungu chikukhudza mtunda wa ulendo womwe tikufuna kuyenda. Baibulo limatchula mfundo ina yomvetsa chisoni kwambiri. Tinganene kuti anthu onse opanda ungwiro akupita kumodzi. Pofotokoza mavuto amene amadza ndi ukalamba, lemba la Mlaliki 12:5 limati: “Munthu apita kwawo kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja.” Kodi “kwawo kwamuyaya” kumeneku ndi kuti? Uku ndi kumanda, komwe timapitako mwachibadwa chifukwa cha uchimo ndi kupanda ungwiro. (Aroma 6:23) Komatu Yehova amatifunira zambiri, osati moyo wa mavuto kungoyambira pa kubadwa mpaka kufa ayi. (Yobu 14:1) Ngati tikuyenda ndi Mulungu tingakhale ndi chiyembekezo choyenda kwamuyaya, zomwe ndi zogwirizana ndi mmene tinapangidwira. Kodi izi si zimene mumafuna? Ndiyetu n’zosachita kufunsa kuti muyenera kuyenda ndi Atate wanu.

Kodi Tingayende Bwanji ndi Mulungu?

9. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova nthawi zina ankabisikira anthu ake, koma malinga ndi Yesaya 30:20 iye anawatsimikizira zotani?

9 Funso lachitatu m’nkhani yathuyi ndi lofunika kuliganizira mozama kwambiri. Funsoli ndi lakuti, Kodi tingayende bwanji ndi Mulungu? Yankho lake timalipeza pa Yesaya 30:20, 21, pomwe timawerenga kuti: ‘Mphunzitsi wako [Wamkulu] sadzabisikanso, koma maso ako adzaona Mphunzitsi wako [Wamkulu]; ndipo makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.’ M’ndime yolimbikitsa imeneyi, n’kutheka kuti mawu a Yehova opezeka mu vesi 20 anakumbutsa anthu ake kuti akamupandukira, zimakhala ngati kuti iye anali kuwabisikira. (Yesaya 1:15; 59:2) Koma pano, Yehova sakufotokozedwa kuti wabisala, koma ataima poyera, pamaso pa anthu ake okhulupirika. Tingathe kuganiza za mlangizi ataima patsogolo pa ophunzira ake, ndi kuwasonyeza zimene iye akufuna kuti iwo aphunzire.

10. Kodi mawu a Mphunzitsi wanu Wamkulu ‘mungawamve kumbuyo kwanu’ m’lingaliro lotani?

10 Mu vesi 21, akutipatsa chithunzithunzi china. Yehova akufotokozedwa ngati kuti akuyenda kumbuyo kwa anthu ake, ndi kumawapatsa malangizo a njira yoyenera kudzera. Akatswiri amaphunziro a Baibulo amati n’kutheka kuti mawu amenewa anafotokozedwa malinga ndi mmene mbusa nthawi zina amalondolera nkhosa zake pambuyo, n’kumakuwa pozilangiza ndiponso poziletsa kulowera njira yolakwika. Kodi chithunzithunzi chimenechi chikugwira ntchito motani kwa ifeyo? Tikamafufuza malangizo m’Mawu a Mulungu, timakhala tikuwerenga mawu amene analembedwa kalekale. Amakhala ngati akuchokera kumbuyo kwathu, kapena kuti nthawi yakale kwambiri. Koma ngakhale zili choncho, ndi mawu othandiza panopo monga mmene analili pamene ankalembedwa. Malangizo a m’Baibulo angatitsogolere pa zosankha zathu za tsiku ndi tsiku, ndipo angatithandize kukonza tsogolo lathu. (Salmo 119:105) Tikachita khama kufunafuna malangizo oterowo ndi kuwagwiritsa ntchito, Yehova amakhala Mtsogoleri wathu. Timakhala tikuyenda ndi Mulungu.

11. Malinga ndi Yeremiya 6:16, kodi Yehova anafuna anthu ake achite chiyani, koma iwo anatani?

11 Kodi timaloladi kuti Mawu a Mulungu atitsogolere pafupi choncho? Ndi bwino kumadzipenda nthawi zina. Taonani vesi lomwe lingatithandize kuchita zimenezi: “Yehova atero, Imani m’njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m’menemo muli njira yabwino, muyende m’menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.” (Yeremiya 6:16) Mawu amenewa akhoza kutikumbutsa za munthu amene ali paulendo ndipo waima pamphambano kuti afunsire njira. Mwauzimu, anthu opanduka a Yehova ku Israyeli ankafunika zimenezi. Ankafunikira kupeza njira yobwererera ku “mayendedwe [awo] akale.” “Njira yabwino” imeneyo inali njira imene makolo awo okhulupirika anayendamo, njira yomwe mtunduwo unasiya, komwe kunali kupusa. N’zomvetsa chisoni kuti Aisrayeli anachita liuma ndipo sanalabadire zimene Yehova anawakumbutsazi. Vesi lomweli likupitiriza motere: “Koma anati, Sitidzayendamo.” Komabe mosiyana ndi Aisrayeli, masiku ano anthu a Mulungu alabadira malangizo amenewa.

12, 13. (a) Kodi otsatira odzozedwa a Kristu alabadira motani lemba la Yeremiya 6:16? (b) Kodi tingadzipende motani pankhani ya njira yomwe tikuyendamo masiku ano?

12 Kuyambira chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, otsatira odzozedwa a Kristu aona malangizo a pa Yeremiya 6:16 ngati opita kwa iwo. Monga gulu, iwo atsogolera njira yobwererera ndi mtima wonse ku “mayendedwe akale.” Mosiyana ndi Matchalitchi Achikristu ampatuko, iwo ayesetsa kutsatira “chitsanzo cha mawu a moyo” chimene Yesu Kristu anakhazikitsa ndipo omutsatira ake oyambirira analimbikitsa. (2 Timoteo 1:13) Mpaka pano, odzozedwa amathandizana komanso amathandiza anzawo a “nkhosa zina” kukhala moyo wabwino ndi wosangalala womwe Matchalitchi Achikristu anausiya.​—Yohane 10:16.

13 Mwa kupereka chakudya chauzimu pa nthawi yake, gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru lathandiza anthu ambiri kupeza “mayendedwe akale” ndiponso kuyenda ndi Mulungu. (Mateyu 24:45-47) Kodi inu ndi mmodzi wa anthu amenewo? Ngati ndi choncho, kodi mungatani kuti musasiye njira imeneyi, n’kulowera njira yanuyanu? N’chinthu chanzeru kuti nthawi ndi nthawi muzipenda mmene mukuyendera pamoyo wanu. Ngati mumawerenga bwinobwino Baibulo ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo ndiponso kufika pa misonkhano yomwe odzozedwa amakonza masiku ano, ndiye kuti mukuphunzitsidwa kuyenda ndi Mulungu. Ndipo mukamatsatira modzichepetsa malangizo amene mwalandira, ndiye kuti mukuyendadi ndi Mulungu, ndipo mukutsatira “mayendedwe akale.”

Yendani Monga Ngati ‘Mukuona Wosaonekayo’

14. Ngati Yehova ndi weniweni kwa ife, kodi tingasonyeze motani zimenezo pa zomwe timasankha kuchita?

14 Kuti tiyende ndi Yehova, iye ayenera kukhala weniweni kwa ife. Kumbukirani kuti Yehova anatsimikizira Aisrayeli akale okhulupirika kuti iye sadzawabisikira. Masiku anonso amadziulula kwa anthu ake monga Mphunzitsi Wamkulu. Kodi kwa inuyo, Yehova ndi weniweni choncho, moti amakhala ngati ali patsogolo panu ndi kumakulangizani? Chikhulupiriro ngati chimenechi ndi chimene chikufunika kuti tiyende ndi Mulungu. Mose anali ndi chikhulupiriro choterocho, “pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.” (Ahebri 11:27) Ngati Yehova ndi weniweni kwa ife, ndiye kuti tiziganizira maganizo ake pamene tikusankha zochita. Mwachitsanzo, sitingaganizeko n’komwe zochita tchimo ndiyeno n’kuyesa kulibisa kwa akulu mumpingo kapena kwa anthu a m’banja mwathu. M’malo mwake, timayesetsa kuyenda ndi Mulungu ngakhale panthawi yomwe munthu aliyense sakutiona. Mofanana ndi Mfumu Davide yakalekale, ndife otsimikiza mtima kuti: “Ndidzayenda m’nyumba [mwanga] ndi mtima wangwiro.”​—Salmo 101:2.

15. Kodi kusonkhana ndi abale ndi alongo athu achikristu kungatithandize bwanji kuona kuti Yehova ndi weniweni?

15 Yehova amamvetsa kuti ndife opanda ungwiro, anthu amatupi anyama ndi mwazi ndipo nthawi zina zimativuta kukhulupirira zimene sitingaone. (Salmo 103:14) Amachita zinthu zambiri potithandiza kuthana ndi vuto limeneli. Mwachitsanzo, iye wasonkhanitsa “anthu a dzina lake” kuchokera m’mitundu yonse ya dziko lapansi. (Machitidwe 15:14) Pamene tikutumikira limodzi mogwirizana, timalimbikitsana. Kumva mmene Yehova wathandizira mbale kapena mlongo wathu wauzimu kuthana ndi vuto kapena mayesero enaake kumatithandiza kuona kuti Mulungu ndi weniweni kwa ifeyo.​—1 Petro 5:9.

16. Kodi kuphunzira za Yesu kungatithandize bwanji kuyenda ndi Mulungu?

16 Koposa zonsezi, Yehova watipatsa chitsanzo cha Mwana wake. Yesu anati: “Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” (Yohane 14:6) Kuphunzira mmene Yesu anakhalira padziko lapansi pano ndi imodzi mwa njira zabwino kwambiri zotithandizira kuona kuti Yehova ndi weniweni kwa ife. Chilichonse chimene Yesu ananena kapena kuchita chinasonyeza bwino kwambiri khalidwe ndi njira za Atate wake wakumwamba. (Yohane 14:9) Tikamasankha zoti tichite, tiziganizira mozama zimene Yesu akanachita pankhaniyo. Zosankha zathu zikamasonyeza kuti taziganizira mofatsa ndiponso tapempherera nkhaniyo, ndiye kuti tikutsatira mapazi a Kristu. (1 Petro 2:21) Mwa kuchita zimenezi timakhala tikuyenda ndi Mulungu.

Kodi Mungapeze Madalitso Otani?

17. Ngati tiyenda m’njira ya Yehova, kodi miyoyo yathu idzapeza “mpumulo” wotani?

17 Moyo umakhala wokhutiritsa kwambiri pamene munthu akuyenda ndi Yehova Mulungu. Kumbukirani zimene Yehova analonjeza anthu ake pankhani ya kufunafuna “njira yabwino.” Anati: “Muyende m’menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.” (Yeremiya 6:16) Kodi “mpumulo” umenewu ukutanthauza chiyani? Kodi ukutanthauza moyo wodzala ndi zosangalatsa? Ayi. Yehova amapereka chinthu china chabwino kwambiri, chimene anthu achuma kwambiri sachipeza kawirikawiri. Kupeza mpumulo m’moyo wanu ndiko kukhala ndi mtendere wa mumtima, kukhala mwachimwemwe, mokhutitsidwa, ndiponso mokhutira mwauzimu. Mpumulo umenewu ukutanthauza kuti mungathe kukhala ndi chikhulupiriro chakuti mwasankha kuyenda m’njira yabwino kwambiri. Mtendere wa m’maganizo umenewu ndi wosowa m’dziko la mavutoli.

18. Kodi Yehova akufuna kukupatsani dalitso lotani, ndipo mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?

18 N’zoona kuti moyo pawokha ndi dalitso lalikulu kwambiri. Ngakhale kukhala moyo waufupi kuli bwino kusiyana n’kusakhalapo n’komwe. Koma Yehova sanafune kuti moyo wanu ukhale waufupi, kungochoka pa chinyamata n’kufika m’mavuto a ukalamba. Ayi, Yehova amafuna kuti mudzapeze dalitso lalikulu kwambiri kuposa onse. Akufuna kuti muyende naye kwamuyaya. Zimenezi zafotokozedwa bwino pa Mika 4:5, kuti: “Mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mlungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthawi yomka muyaya.” Kodi mukufuna kudzapeza dalitso limeneli? Kodi mukufuna kudzakhala moyo umene Yehova akuutcha mochititsa chidwi kuti “moyo weniweniwo”? (1 Timoteo 6:19) Ndiyetu onetsetsani kuti mwatsimikiza kuyenda ndi Yehova lero, mawa, ndiponso tsiku lililonse m’tsogolomu mpaka muyaya!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Mabaibulo ena amachotsa mawu oti “mkono” m’vesili n’kuikapo muyeso wa nthawi, monga “kamphindi” (The Emphatic Diaglott) kapena “mphindi imodzi” (A Translation in the Language of the People, la Charles B. Williams). Koma mawu amene anagwiritsidwa ntchito m’malemba oyambirira amatanthauza muyeso wa masentimita pafupifupi 45.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi kuyenda ndi Mulungu kumatanthauzanji?

• N’chifukwa chiyani mukuona kuti mufunika kuyenda ndi Mulungu?

• Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuyenda ndi Mulungu?

• Kodi anthu amene akuyenda ndi Mulungu amapeza madalitso otani?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 23]

Kudzera m’Baibulo, timamva mawu a Yehova kumbuyo kwathu akuti, “Njira ndi iyi”

[Chithunzi patsamba 25]

Pamisonkhano timalandira chakudya chauzimu panthawi yake