Yendani mwa Chikhulupiriro Osati mwa Zooneka Ndi Maso
Yendani mwa Chikhulupiriro Osati mwa Zooneka Ndi Maso
“Tiyendayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe.”—2 AKORINTO 5:7.
1. Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti mtumwi Paulo ankayenda mwa chikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso?
ICHI chinali chaka cha 55 C.E. Munthu wina amene dzina lake lakale linali Sauli, yemwe anazunzapo Akristu, anali atayamba Chikristu zaka 20 zapitazo. Kwa nthawi yonseyi iye sanalole kuti chikhulupiriro chake mwa Mulungu chifooke. Ngakhale kuti anali asanaone zinthu zakumwamba ndi maso ake, iye anali wolimbabe m’chikhulupiriro. Motero, mtumwi Paulo analemba mawu otsatirawa kwa Akristu odzozedwa, okhala ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba: “Tiyendayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe.”—2 Akorinto 5:7.
2, 3. (a) Kodi timasonyeza bwanji kuti tikuyenda mwa chikhulupiriro? (b) Kodi kuyenda mwa zooneka ndi maso n’kutani?
2 Kuti tiyende mwa chikhulupiriro timafunika kukhulupirira Mulungu ndi mtima wonse kuti iye angathe kutsogolera moyo wathu. Sitiyenera kukayika ngakhale pang’ono kuti amadziwa zimene zingatithandizedi. (Salmo 119:66) M’moyo wathu, tikamasankha zochita ndiponso tikamachita zinthu tasankhazo, tiziganizira za “zinthu zimene sitiziona.” (Ahebri 11:1, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Zina mwa zinthu zosaonekazi ndi “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano.” (2 Petro 3:13) Komano tikamayenda mwa zooneka ndi maso, ndiye kuti moyo wathu umakhala wongoganizira zinthu zooneka, zokhudzika ndi zinanso zotere. Moyo woterewu n’ngoopsa chifukwa ungatichititse kusaganizira n’komwe za chifuniro cha Mulungu.—Salmo 81:12; Mlaliki 11:9.
3 Kaya ndife a “kagulu kankhosa,” okhala ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba, kapena a “nkhosa zina” okhala ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi, tonsefe tiyenera kumvera malangizo akuti tiziyenda mwa chikhulupiriro osati mwa zooneka ndi maso. (Luka 12:32; Yohane 10:16) Tiyeni tione mmene kutsatira malangizo ouziridwawa kungatitetezere kuti tisamakopeke ndi “zosangalatsa zosakhalitsa za uchimo,” kuti tipewe msampha wa chuma, ndiponso kuti tisaiwale kuti mapeto a dongosolo la zinthu lino ayandikira. Ndiponso tiona kuti kodi kuyenda mwa zooneka ndi maso n’koopsa m’njira zotani.—Ahebri 11:25, NW.
Kukana ‘Zosangalatsa Zosakhalitsa Zauchimo’
4. Kodi Mose anasankha kutani, ndipo n’chifukwa chiyani anatero?
4 Taganizirani moyo umene Mose, mwana wa Amramu akanatha kukhala nawo. Iye analeredwa limodzi ndi ana achifumu ku Aigupto wakale, motero akanatha kukhala munthu waulamuliro, wachuma ndiponso wamphamvu. Mose akanatha kumaganiza kuti: ‘Ndaphunzitsidwa bwino nzeru zapamwamba za ku Aigupto, ndiponso ndine wamphamvu m’mawu ndi m’zintchito zanga. Ngati n’takhalabe m’nyumba yachifumuyi, ndingathe kudzapulumutsa Ahebri anzanga ndi mphamvu zangazi.’ (Machitidwe 7:22) Koma Mose sanaganize choncho, m’malo mwake anasankha “kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu.” N’chifukwa chiyani anatero? N’chiyani chinam’chititsa Mose kusiya zonse zimene akanapeza ku Aigupto? Baibulo limatiyankha kuti: “Ndi chikhulupiriro [Mose] anasiya Aigupto, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.” (Ahebri 11:24-27) Chimene chinathandiza Mose kukana kusangalala kwa kanthawi pochita uchimo ndicho kukhulupirira kuti Yehova amapereka mphoto kwa ochita zolungama.
5. Kodi chitsanzo cha Mose chimatilimbikitsa bwanji?
5 Nthawi zambiri nafenso timavutika kusankha zoyenerera kuchita pa nkhani monga izi: ‘Kodi ndisiye makhalidwe kapena zizolowezi zinazake zimene sizili zogwirizana kwenikweni ndi mfundo za m’Baibulo? Kodi ndilolere kulowa ntchito yomwe ikuoneka kuti ingandipezetse bwino koma yomwe ingathe kundilowetsa pansi mwauzimu?’ Chitsanzo cha Mose chimatithandiza kuti tisasankhe kuchita zinthu zosonyeza nzeru za m’dziko lino zosatha kuona patali; m’malo mwake chimatithandiza kuti tizikhulupirira nzeru zoona patali za Yehova Mulungu, “wosaonekayo.” Monga Mose, tiyesetse kusamala ubwenzi wathu ndi Yehova kuposa china chilichonse chimene dzikoli lingatipatse.
6, 7. (a) Kodi Esau anasonyeza bwanji kuti anasankha kuyenda mwa zooneka ndi maso? (b) Kodi Esau ndi chitsanzo chotichenjeza za chiyani?
6 Zimene anachita Mose n’zosiyana ndi zimene anachita Esau, mwana wa kholo lakale Isake. Esau anasankha kusangalala nthawi yomweyo. (Genesis 25:30-34) ‘Ponyoza zinthu zauzimu,’ Esau anagulitsa ufulu wake monga woyamba kubadwa ndi “mtanda umodzi wa chakudya.” (Ahebri 12:16) Iye sanaganizire mmene zogulitsa ufulu wakewo zidzakhudzire ubwenzi wake ndi Yehova ndiponso mmene zidzakhudzire mbadwa zake. Iye sanaone zinthu mwauzimu. Esau anatseka maso ake n’kusaona malonjezo a Mulungu amtengo wapatali, ndipo anawaona ngati osafunika kwenikweni. Iye anayenda mwa zooneka ndi maso, osati mwa chikhulupiriro.
7 Esau ndi chitsanzo chotichenjeza ifeyo masiku ano. (1 Akorinto 10:11) Tikamaganiza zochita zinazake, kaya zazing’ono kaya zazikulu, sitiyenera kunyengedwa ndi mfundo zokopa za dziko la Satanali, limene limalimbikitsa anthu kuti chilichonse chimene akufuna azichipeza nthawi yomweyo. Tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi kamtima ka Esau kamaonekera pa zinthu zina zimene ndimachita? Kodi ndikachita zimene ndikufuna panopo ndiye kuti zinthu zauzimu ndiziika pambuyo? Kodi zimene ndimasankha kuchita zingathe kusokoneza ubwenzi wanga ndi Mulungu ndiponso mphoto yanga yam’tsogolo? Kodi ena ndikuwapatsa chitsanzo chotani? Yehova amatidalitsa ngati zimene timasankha kuchita zikusonyeza kuti timayamikira zinthu zopatulika.—Miyambo 10:22.
Kupewa Msampha wa Chuma
8. Kodi ndi chenjezo lotani limene Akristu a ku Laodikaya analandira, ndipo ifeyo likutikhudza bwanji?
8 Cha kumapeto kwa zaka 100 zoyambirira, Yesu Kristu ali mu ulemerero wake kumwamba, anapereka uthenga ku mpingo wa ku Laodikaya ku Asiyamina kudzera mu vumbulutso lomwe anaonetsa mtumwi Yohane. Umenewu unali uthenga wochenjeza za kukonda chuma. Ngakhale kuti Akristu a ku Laodikaya anali olemera, iwo anali osauka mwauzimu. M’malo mopitiriza kuyenda mwa chikhulupiriro, iwo analola chuma kuwatseka maso awo auzimu. (Chivumbulutso 3:14-18) Masiku anonso kukonda chuma kumatseka maso athu mwauzimu. Kumafooketsa chikhulupiriro chathu n’kutichititsa kuleka ‘kuthamanga mwachipiriro’ liwiro la moyo. (Ahebri 12:1) Tikapanda kusamala, “zokondweretsa za moyo” zingathe kuphimba zinthu zauzimu moti mpaka zinthu zauzimuzo zingathe ‘kutsamwiratu.’—Luka 8:14.
9. Kodi kukhutira ndiponso kuyamikira chakudya chauzimu kumatiteteza motani?
9 Kuti tithe kudziteteza mwauzimu tizikhutira, osamafuna kulemera kapena kufuna kuti 1 Akorinto 7:31; 1 Timoteo 6:6-8) Tikamayenda mwa chikhulupiriro osati mwa zooneka ndi maso, timasangalala naye paradaiso wauzimu amene alipoyu. Kodi mitima yathu siitisonkhezera ‘kuimba ndi mtima wosangalala’ pamene tikudya chakudya chauzimu chopatsa thanzi. (Yesaya 65:13, 14) Ndiponsotu, timasangalala kwambiri kuchezerana ndi anthu amene amasonyeza chipatso cha mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) Motero, m’pofunikadi kuti tizikhutira ndiponso kusangalala ndi zinthu zauzimu zimene Yehova akutipatsa.
chilichonse cha m’dzikoli chisatipite. (10. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso otani?
10 Pali mafunso ena awa amene tiyenera kudzifunsa: Kodi zinthu zosakhala zauzimu ndimaziona kuti n’zofunika motani m’moyo wanga? Kodi chuma chimene ndili nacho ndimangosangalala nacho basi kapena ndimachigwiritsira ntchito popititsa patsogolo kulambira koona? Kodi chimandisangalatsa kwambiri n’chiyani? Kuphunzira Baibulo komanso kukhala ndi abale pa misonkhano, kapena kupumako Loweruka ndi Lamlungu osachita zinthu zokhudzana ndi maudindo achikristu? Kodi nthawi zambiri ndimakonda kukasangalala Loweruka ndi Lamlungu m’malo mogwiritsira ntchito nthawi imeneyi kulalikira ndi kuchita zinthu zina zokhudza kulambira koona?’ Tikamayenda mwa chikhulupiriro ndiye kuti tikukhala otanganidwa ndi ntchito ya Ufumu, komanso tikukhulupirira malonjezo a Yehova ndi mtima wonse.—1 Akorinto 15:58.
Kukumbukira Kuti Mapeto Ayandikira
11. Kodi kuyenda mwa chikhulupiriro kumatithandiza bwanji kusaiwala kuti mapeto ayandikira?
11 Kuyenda mwa chikhulupiriro kumatithandiza kupewa maganizo a anthu akuti mapeto ali kutali kwambiri ndiponso kuti sadzabwera n’komwe. Mosiyana ndi anthu okayikira amene amanyoza maulosi a m’Baibulo, ifeyo timaona mmene zochitika za padziko lonse zikukwaniritsira zimene Mawu a Mulungu ananena kuti zidzachitika m’masiku athu ano. (2 Petro 3:3, 4) Mwachitsanzo, kodi maganizo ndiponso makhalidwe a anthu ambiri masiku ano sapereka umboni wakuti tikukhala “masiku otsiriza”? (2 Timoteo 3:1-5) Ndi maso achikhulupiriro, timatha kuona kuti nkhani zimene zikuchitika masiku ano sikuti n’zongofanana ndi za m’mbuyo monsemu. M’malo mwake zikupanga “chizindikiro cha kufika [kwa Kristu] ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano.”—Mateyu 24:1-14.
12. Kodi mawu a Yesu opezeka pa Luka 21:20, 21 anakwaniritsidwa bwanji?
12 Taganizirani nkhani ina ya kale, yomwe ili yofanana ndi nkhani zimene zikuchitika masiku ano. Ali padziko lapansi, Yesu Kristu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali m’kati mwa uwo atuluke.” (Luka 21:20, 21) Pokwaniritsa ulosi umenewu, magulu ankhondo a Aroma, molamulidwa ndi Seshasi Galasi anazungulira Yerusalemu m’chaka cha 66 C.E. Koma asilikaliwa anachoka msanga, ndipo ichi chinali chizindikiro ndiponso unali mwayi kwa Akristu a kumeneku kuti “athawire kumapiri.” Mu 70 C.E., magulu ankhondo aja anabweranso n’kuwononga mzinda wa Yerusalemu ndiponso kachisi wake. Josephus ananena kuti panafa Ayuda opitirira wani miliyoni, ndipo Ayuda 97,000 anagwidwa ukapolo. Apa, Mulungu anaweruza dongosolo la zinthu la Ayudalo. Anthu amene ankayenda mwa chikhulupiriro n’kumvera chenjezo la Yesu anapulumuka zoopsazi.
13, 14. (a) Kodi m’tsogolomu muchitika zotani? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala atcheru kuona kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo?
13 Zinthu zofanana ndi zimenezi zatsalanso pang’ono kuchitika masiku ano. Mayiko a m’bungwe la United Nations adzathandiza nawo pa chiweruzo cha Mulungu. Mofanana ndi asilikali ankhondo a Aroma omwe anali ndi ntchito yokhazikitsa Mtendere wa Aroma (Pax Romana), bungwe la United Nations nalonso cholinga chake ndicho kukhazikitsa mtendere. Ngakhale kuti magulu ankhondo a Aroma anayesetsa kuti pakhale bata padziko lonse lodziwika panthawiyo, iwowa ndiwo anawononga Yerusalemu. Masiku anonso, ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti magulu a asilikali a m’bungwe la United Nations adzaona kuti zipembedzo zimabweretsa chisokonezo ndipo adzawononga Yerusalemu wa nthawi ino, amene ali Matchalitchi Achikristu, kuphatikizaponso Babulo Wamkulu yense. (Chivumbulutso 17:12-17) Inde, ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga uwonongedwa posachedwapa.
14 Panthawi ya kuwonongedwa kwa zipembedzo zonyenga m’pamene padzayambire chisautso chachikulu. Kumapeto kwa chisautso chachikulu, mbali zina zimene zidzatsalire za dongosolo lino la zinthu zidzawonongedwa. (Mateyu 24:29, 30; Chivumbulutso 16:14, 16) Kuyenda mwa chikhulupiriro kumatithandiza kukhala atcheru kuti tione kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo. Sitinyengedwa ndi maganizo akuti mabungwe opangidwa ndi anthu, monga bungwe la United Nations, ndiwo njira ya Mulungu yobweretsera mtendere weniweni ndi bata. Motero, kodi moyo wathu suyenera kusonyeza kuti sitikukayika ngakhale pang’ono kuti “tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.”?—Zefaniya 1:14.
Kodi Kuyenda mwa Zooneka ndi Maso N’koopsa Motani?
15. Ngakhale kuti mtundu wa Israyeli unadalitsidwa ndi Mulungu, kodi unagwa mu msampha wotani?
15 Zimene zinawachitikira Aisrayeli akale zimasonyeza kuti kuyenda mwa zooneka ndi maso n’koopsa chifukwa kumafooketsa chikhulupiriro chathu. Aisrayeliwo anaona Miliri Khumi imene inanyozetsa milungu ya ku Aigupto ndipo kenaka anapulumutsidwa mozizwitsa powoloka Nyanja Yofiira. Komabe, iwo anaswa lamulo la Mulungu n’kupanga fano la mwana wang’ombe wagolide kenaka n’kumalilambira. Chifukwa cholephera kuugwira mtima anatopa kudikirira Mose, amene “anachedwa kutsika m’phiri.” (Eksodo 32:1-4) Motero anayamba kulambira fano looneka ndi maso. Chifukwa choyenda mwa zooneka ndi maso iwo ananyoza Yehova moti ‘anthu pafupifupi zikwi zitatu’ anaphedwa. (Eksodo 32:25-29) Zimamvetsatu chisoni kwambiri masiku ano kuona wolambira Yehova akuchita zinthu mosonyeza kuti sakhulupirira Yehova ndiponso kuti amakayika kuti iye angathe kukwaniritsa malonjezo ake.
16. Kodi Aisrayeli anakhudzidwa bwanji ndi zinthu zooneka ndi maso?
16 Aisrayeli anasokonezeka m’njira zinanso chifukwa cha zooneka ndi maso. Kuyenda mwa zooneka ndi maso kunawachititsa kuopa adani awo. (Numeri 13:28, 32; Deuteronomo 1:28) Kunawachititsa kuti aziderera Mose pa udindo wake wopatsidwa ndi Mulungu ndiponso kuti azidandaula za moyo wawo. Kusowa chikhulupiriro kotere kunawachititsa kuti aziona kuti dziko la Aigupto, lomwe linali lolamulidwa ndi ziwanda, linali bwinoko poyerekezera ndi Dziko Lolonjezedwa. (Numeri 14:1-4; Salmo 106:24) Yehova ayenera kuti anapwetekedwa mtima kwambiri poona chipongwe chachikuluchi chomwe anthu ake anam’chitira iye, Mfumu yawo yosaoneka.
17. Kodi mu nthawi ya Samueli n’chiyani chinawachititsa Aisrayeli kusafuna kutsatira malangizo a Yehova?
17 Ndiponso m’nthawi ya mneneri Samueli, mtundu woyanjidwa ndi Mulungu wa Israyeli unakodwanso mumsampha woyenda mwa zooneka ndi maso. Anthuwo anayamba kufuna kukhala ndi mfumu yoti azitha kuiona. Ngakhale kuti Yehova anasonyeza kuti anali Mfumu yawo, zimenezi sizinawachititse kuti ayambe kuyenda mwa chikhulupiriro. (1 Samueli 8:4-9) Iwo anadzipweteketsa okha chifukwa anachita zopanda nzeru posafuna kutsatira malangizo angwiro a Yehova, koma m’malo mwake anasankha kukhala ngati mitundu yowazungulira.—1 Samueli 8:19, 20.
18. Kodi tingaphunzire zotani pankhani ya kuopsa kwa kuyenda mwa zooneka ndi maso?
18 Atumiki a Yehova a masiku anofe, timaona kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu n’ngwamtengo wapatali kwambiri. Timafunitsitsa kuphunzira ndi kugwiritsira ntchito zinthu zofunikira zimene timaphunzira pa zochitika za m’mbuyomo. (Aroma 15:4) Panthawi imene Aisrayeli ankayenda mwa zooneka ndi maso, anaiwala kuti Mulungu akuwatsogolera kudzera mwa Mose. Ifenso tikapanda kusamala, tingathe kuiwala kuti Yehova Mulungu pamodzi ndi Mose Wamkulu, Yesu Kristu, akutsogolera mpingo wachikristu masiku ano. (Chivumbulutso 1:12-16) Tiyenera kusamala kuti tisamaone gulu la Yehova la padziko lapansi m’njira yaumunthu. Tikamatero tingathe kukhala ndi mzimu wokonda kudandaula ndiponso kusayamikira anthu oimira Yehova komanso kusayamikira chakudya chauzimu choperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mateyu 24:45.
Tsimikizani Mtima Kuyenda mwa Chikhulupiriro
19, 20. Kodi inuyo mwatsimikiza mtima kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani mwatero?
19 Baibulo limanena kuti: “Kulimbana kwathu sitilimbana nawo mwazi ndi thupi, komatu nawo maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a choipa m’zakumwamba.” (Aefeso 6:12) Mdani wathu wamkulu ndi Satana Mdyerekezi. Iyeyu cholinga chake n’chakuti awononge chikhulupiriro chathu mwa Yehova. Amayesetsa kutikopa m’njira ina iliyonse kuti tisiye kutumikira Mulungu. (1 Petro 5:8) Kodi n’chiyani chingatiteteze kuti tisamakopeke ndi zinthu zooneka ndi maso za m’dziko la Satana lino? Si china ayi koma kuyenda mwa chikhulupiriro osati mwa zooneka ndi maso. Kukhulupirira malonjezo a Yehova kungatiteteze kuti ‘chikhulupiriro chathu chisasweke ngati ngalawa.’ (1 Timoteo 1:19) Motero, tiyeni tiyesetse kuyenda mwa chikhulupiriro, osakayika ngakhale pang’ono kuti Yehova azitidalitsa. Ndipotu tisaleke kupemphera kuti tidzathe kupulumuka zinthu zonse zimene zichitike posachedwapa.—Luka 21:36.
20 Pamene tikuyenda mwa chikhulupiriro osati mwa zooneka ndi maso, tili ndi Chitsanzo chabwino kwambiri. Baibulo limati: “Kristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.” (1 Petro 2:21) Nkhani yotsatirayi ifotokoza mmene tingapitirizire kuyenda monga iye anayendera.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi mwaphunzirapo chiyani pa chitsanzo cha Mose ndi Esau, pankhani ya kuyenda mwa chikhulupiriro osati mwa zooneka ndi maso?
• Kodi njira yopewera kukonda chuma ndi yotani?
• Kodi kuyenda mwa chikhulupiriro kumatithandiza bwanji kupewa maganizo akuti mapeto adakali kutali?
• N’chifukwa chiyani kuyenda mwa zooneka ndi maso kuli koopsa?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 17]
Mose anayenda mwa chikhulupiriro
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi nthawi zambiri mumalephera kuchita zinthu zauzimu chifukwa cha zosangalatsa?
[Chithunzi patsamba 20]
Kodi kumvera Mawu a Mulungu kumakutetezani bwanji?