Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mukhoza Kulimbana ndi Vuto la Kusatsimikizika kwa Zinthu

Mukhoza Kulimbana ndi Vuto la Kusatsimikizika kwa Zinthu

Mukhoza Kulimbana ndi Vuto la Kusatsimikizika kwa Zinthu

“ZOTSIMIKIZIKA!” “Zosakayikitsa!” “Zodalirika!” Mosakayikira inu mwamvapo mawu ngati amenewo kambirimbiri. Koma pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku, zinthu zambiri n’zosatsimikizika. Za mawa sizidziŵika moti nthaŵi zambiri timadabwa ngati pali chilichonse chimene tingakhale otsimikiziradi kuti chichitika. Moyo wathu ndi wodzala ndi zinthu zokayikitsa ndiponso zosatsimikizika.

Mosadabwitsa, anthu ambiri amafuna kuti iwowo ndi mabanja awo akhale otetezeka ndi achimwemwe. Amagwira ntchito mwakhama kuti apeze zinthu zimene amaganiza kuti ziwachititsa kukhala achimwemwe ndi otetezeka. Zinthu zimenezi nthaŵi zambiri zimakhala ndalama ndi katundu. Komabe, chivomezi, mphepo yamkuntho, ngozi, kapena upandu wachiwawa ungawononge zinthu zimenezo m’kanthaŵi kochepa. Matenda aakulu, kutha kwa ukwati, kapena kutha kwa ntchito kungasinthe miyoyo ya anthu mwadzidzidzi. N’zoona kuti zinthu ngati zimenezo mwina sizingakuchitikireni inuyo. Komabe, kungodziŵa kuti chinthu chinachake choipa kwambiri chingachitike nthaŵi ina iliyonse kumatidetsa nkhaŵa ndi kutivutitsa maganizo. Koma mavuto amene alipo si okhawo ayi.

Mawu akuti kusatsimikizika ndi ofanana ndi mawu akuti kukayikitsa, ndipo mtanthauzira mawu wina amamasulira mawu akuti “kayika” motere: “Khala wosatsimikiza poganiza kapena pochita chinthu.” Kuwonjezera apo, buku lotchedwa Managing Your Mind linati “kusatsimikiza za chinthu chinachake chofunika kwambiri kumachititsa kuti anthu ambiri azikhala ndi nkhaŵa.” Ngati kukayikira sikukutha kungachititse nkhaŵa, kugwiritsidwa mwala, ndi kukwiya. Zoonadi, kudera nkhaŵa za chomwe chingachitike kapena chimene sichingachitike kungatidwalitse m’maganizo ndi m’thupi mwathu.

Poopa zimenezi, anthu ena sadera nkhaŵa n’komwe za chilichonse. Amafanana ndi mnyamata wa ku Brazil amene ananena kuti: “Pali chifukwa chanji chodera nkhaŵa zimene zichitike? Tiyenera kuganizira za lero, osati za mawa.” Maganizo oika moyo pangozi amenewo akuti “tidye timwe pakuti mawa timwalira” angangotichititsa kuti tikhumudwe, tivutike maganizo, ndipo pamapeto pake tife. (1 Akorinto 15:32) Chinthu chabwino koposa chimene tingachite ndiye kudalira Mlengi, Yehova Mulungu, amene Baibulo limati “alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.” (Yakobo 1:17) Tikamaŵerenga mozama Mawu a Mulungu, Baibulo, tidzapeza malangizo abwino a mmene tingalimbanire ndi kusatsimikizika kwa moyo. Lingatithandizenso kumvetsetsa chifukwa chake zinthu zambiri zili zosatsimikizika.

Chimene Chimachititsa Kuti Tikhale Osatsimikiza

Malemba amafotokoza bwino zinthu zimene zimachitika pa moyo ndipo amatithandiza kuona moyenera kusatsimikizika ndi kusintha kwa zinthu. Ngakhale kuti maubwenzi athu ndi achibale athu, mmene anthu ena amationera, nzeru zathu, thanzi lathu, ndi zina zotero zingatithandizeko kukhala otetezeka, Baibulo limasonyeza kuti sitingayembekezere kuti zinthu zidzangokhalabe choncho, kapena kuyembekezera kukhala ndi moyo wopanda mavuto. Mfumu yanzeru Solomo inati: “Omwe athamanga msanga sapambana m’liwiro, ngakhale olimba sapambana m’nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziŵitsa sawakomera mtima.” Chifukwa chiyani? Chifukwa “yense angoona zom’gwera m’nthaŵi mwake.” Choncho Solomo anachenjeza kuti: “Monga nsomba zigwidwa m’ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthaŵi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.”​—Mlaliki 9:11, 12.

Yesu Kristu nayenso analankhulapo za nthaŵi imene mbadwo wonse wa anthu udzakhala wosadziŵa chomwe chichitike ndiponso wankhaŵa kwambiri. M’mawu omveka bwino kwambiri, iye anati: “Kudzakhala zizindikiro pa dzuŵa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi padziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkukumo wake wa nyanja ndi mafunde ake; anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zilinkudza kudziko lapansi; pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.” Komabe Yesu ananena mawu olimbikitsa kwa anthu oona mtima masiku ano pamene anati: “Pakuona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.” (Luka 21:25-27, 31) Mofanana ndi zimenezo, m’malo moopa m’tsogolo mosadziŵika bwino, tili ndi chikhulupiriro mwa Mulungu chimene chimatithandiza kuti tisamangoganiza za kusatsimikizika kwa zinthu koma tiziyembekezera m’tsogolo mochititsa chidwi ndiponso motetezeka.

Kukhala ndi “Chiyembekezo Chokwanira”

Ngakhale kuti sitingakhale otsimikiza za chinthu chilichonse chimene timamva, kuŵerenga, kapena kuona, tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira Mlengi. Iye sikuti wangokhala chabe Wamkulukulu, komanso ndi Atate wachikondi amene amasamalira ana ake a padziko lapansi. Ponena za mawu ake, Mulungu anati: “Sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m’mene ndinawatumizira.”​—Yesaya 55:11.

Yesu Kristu anaphunzitsa choonadi chochokera kwa Mulungu ndipo ambiri amene anamumva akulankhula anakhulupiriradi ndi mtima wonse zimene ananenazo. Mwachitsanzo, gulu la Asamariya oona mtima anauza mkazi amene anamvetsera Yesu koyamba kuti: “Tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziŵa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.” (Yohane 4:42) N’chimodzimodzinso masiku ano. Ngakhale kuti tikukhala mu nthaŵi zosatsimikizika, sitiyenera kukayikira zimene tiyenera kukhulupirira.

Pankhani ya zikhulupiriro zachipembedzo, anthu ambiri amanena kuti m’malo moyesera kumvetsetsa zinthu, tiyenera kungokhulupirira basi. Koma munthu wina wolemba Baibulo, Luka, anali ndi maganizo osiyana ndi amenewo. Anachita kafukufuku ndiponso ananena zinthu zolondola n’cholinga choti ena ‘adziŵitse zoona zake za mawu’ amene analemba. (Luka 1:4) Popeza achibale ndi anzathu amene sakhulupirira zinthu zimene timakhulupirira angamade nkhaŵa kuti pomalizira pake tidzagwiritsidwa fuwa lamoto ndiponso tidzakhumudwa, n’zofunika kwambiri kuti tizitha kuikira kumbuyo chikhulupiriro chathu. (1 Petro 3:15) Ngati tikudziŵa bwinobwino chifukwa chimene timakhulupirira zinthu zimene timakhulupirirazo, m’pamene tingathe kuthandiza ena kudalira Mulungu. Baibulo limamufotokoza Yehova motere: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.”​—Deuteronomo 32:4.

Taonani mawu omalizawo akuti: “Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” Kodi tili ndi zifukwa zotani zokhulupirira zimenezi? Mtumwi Petro anakhulupirira kwambiri mfundo imeneyi. Anauza wolamulira wachiroma ndi banja lake kuti: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Petro ananena mawu ameneŵa chifukwa anali atangoona kumene mmene Mulungu anayendetsera zinthu kuti banja lachikunja, limene kale linkaoneka ngati lodetsedwa ndiponso losavomerezeka, likhale lovomerezeka kwa Iye. Mofanana ndi Petro, nafenso tingatsimikize kuti Mulungu alibe tsankho ndiponso kuti ndi wachilungamo tikaona tokha “khamu lalikulu” la anthu opitirira sikisi miliyoni ochokera m’mayiko oposa 230 padziko lonse lapansi amene asiya moyo wawo wakale n’kuyamba kuyenda pa njira yachilungamo.​—Chivumbulutso 7:9; Yesaya 2:2-4.

Monga Akristu oona, sitifuna kukhala otengeka maganizo kwambiri kapena oumirira zinthu, koma odzichepetsa ndi omvetsetsa zinthu. Komabe, sikuti ndife osatsimikizira zimene timakhulupirira ndi zimene tikuyembekezera m’tsogolo. M’kalata imene analembera Akristu m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, mtumwi Paulo anati: “Tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga ku chiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro.” (Ahebri 6:11) Mofanana ndi Akristu amenewo, uthenga wabwino wa m’Baibulo watipatsa “chiyembekezo chokwanira.” Chiyembekezo chimenecho, chimene n’chochokera m’Mawu a Mulungu, “sichichititsa manyazi, [“sichikhumudwitsa,” NW],” mogwirizana ndi zimene Paulo anafotokoza.​—Aroma 5:5.

Kuwonjezera pamenepo, timakhulupirira kwambiri kuti kuphunzitsa ena uthenga wabwino wa m’Baibulo kungawathandize kukhala otetezeka ndiponso otsimikizira zinthu zauzimu, ngakhale zokhudza maganizo ndi thupi lawo. Tingagwirizane ndi Paulo amene ananena kuti: “Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m’mawu mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’kuchuluka kwakukulu.”​—1 Atesalonika 1:5.

Madalitso Amene Timapeza Chifukwa Chokhala Otetezeka Mwauzimu

Ngakhale kuti sitingayembekezere kukhala otetezeka kotheratu pa moyo wathu masiku ano, pali zimene tingachite zimene zingatithandize kukhala ndi moyo wotsimikizika ndi wotetezeka. Mwachitsanzo, kusonkhana nthaŵi zonse ndi mpingo wachikristu pa misonkhano kumatithandiza kukhala ndi moyo wotsimikizika chifukwa kumeneko timaphunzirako mfundo zoona ndi zodalirika ndiponso makhalidwe abwino. Paulo analemba kuti: “Lamulira iwo achuma m’nthaŵi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo.” (1 Timoteo 6:17) Chifukwa cha kuphunzira kudalira Yehova osati katundu wawo kapena zosangulutsa, zimene sizikhalitsa, anthu ambiri athetsa nkhaŵa ndi kugwiritsidwa mwala kumene anali nako kale.​—Mateyu 6:19-21.

Mu mpingo, tilinso ndi abale amene amatikonda, ndipo amatithandiza ndi kutichirikiza m’njira zosiyanasiyana. Panthaŵi ina mu utumiki wake, mtumwi Paulo ndi anthu amene ankayenda nawo ‘anathodwa kwakukulu’ ndipo ‘anada nkhaŵa ngakhale za moyo wawo.’ Kodi Paulo anapeza kuti chilimbikitso ndi chithandizo? N’zoona kuti chikhulupiriro chake mwa Mulungu sichinazilale m’pang’ono pomwe. Komabe, analimbikitsidwa ndi kutonthozedwa ndi Akristu anzake amene anamuthandiza. (2 Akorinto 1:8, 9; 7:5-7) Masiku ano, kukachitika masoka achilengedwe kapena ngozi za mtundu wina, nthaŵi zambiri abale athu achikristu ndi amene amakhala oyamba kubwera kudzathandiza popereka zinthu zofunika pamoyo ndiponso zauzimu kwa Akristu anzawo komanso anthu ena amene akufunika kuthandizidwa.

Njira ina imene ingatithandize kulimbana ndi kusatsimikizika kwa moyo ndiyo pemphero. Nthaŵi zonse tikakhala pa mavuto amene sitimawayembekezera tingapemphe Atate wathu wachikondi wakumwamba kuti atithandize. “Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m’nyengo za nsautso.” (Salmo 9:9) Makolo akhoza kulephera kuteteza ana awo. Koma Mulungu ndi wokonzeka kutithandiza kuti tilimbane ndi nkhaŵa zathu ndi kusatsimikizika kwa zinthu. Tikamusenzetsa Yehova nkhaŵa zathu m’pemphero, tingakhale otsimikiza kuti angathe “kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza.”​—Aefeso 3:20.

Kodi mumapemphera kwa Mulungu nthaŵi zonse? Kodi mukukhulupirira kuti Mulungu amamva mapemphero anu? Mtsikana wina ku São Paulo anati: “Mayi anga anandiuza kuti ndizipemphera kwa Mulungu. Koma ndinadzifunsa ndekha kuti: ‘N’chifukwa chiyani ndiyenera kulankhula ndi munthu amene sindikumudziŵa n’komwe?’ Kenaka lemba la Miyambo 18:10 linandithandiza kuzindikira kuti timafunika kuti Mulungu atithandize ndipo tiyenera kulankhula naye m’pemphero.” Lemba limenelo limati: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.” Indedi, kodi tingayambe bwanji kukhulupirira ndi kudalira Yehova ngati tilibe chizoloŵezi cholankhulana naye? Kuti atidalitse potiteteza mwauzimu, tiyenera kukhala ndi chizoloŵezi chopemphera kuchokera pansi pa mtima tsiku lililonse. Yesu anati: “Dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.”​—Luka 21:36.

Chinanso chimene tingakhale otsimikiza ndicho chiyembekezo chathu mwa Ufumu wa Mulungu. Taonani mawu a pa Danieli 2:44: “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.” Chiyembekezo chimenecho n’chodalirika ndipo tingakhale otsimikizira zimenezo. Malonjezo a anthu nthaŵi zambiri sakwaniritsidwa, koma nthaŵi zonse tingadalire mawu a Yehova. M’malo mokhala wosadalirika, Mulungu ali ngati thanthwe limene tingalidalire. Tingamve ngati mmene anamvera Davide, amene ananena kuti: “Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzam’khulupirira; chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa ku chiwawa.”​—2 Samueli 22:3.

Buku limene talitchula koyambirira lija lakuti Managing Your Mind linanenanso kuti: “Munthu akamaganizira kwambiri zinthu zoipa zimene zingachitike, m’pamene zimaonekanso kuti zingachitikedi, ndiponso m’pamene zimakhala zovuta kwambiri kudziŵa zimene angachite kuti alimbane nazo.” Choncho, kodi pali chifukwa chanji chololera kulemedwa ndi nkhaŵa ndi kusatsimikizika kwa zinthu za padzikoli? M’malo mwake, chotsani kusatsimikizika kwa zinthu za m’dzikoli mwa kuganizira zinthu zotsimikizika zimene Mulungu amatipatsa. Mwa kupitirizabe kukhulupirira malonjezo a Yehova amene sangalephere kukwaniritsidwa, ndife otsimikiza kuti: “Amene aliyense akhulupirira iye, sadzachita manyazi [“sadzakhumudwa,” NW].”​—Aroma 10:11.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti m’tsogolo anthu adzadalitsidwa

[Mawu Otsindika patsamba 30]

“Amene aliyense akhulupirira iye, sadzakhumudwa.”

[Chithunzi patsamba 31]

Uthenga wabwino wa Ufumu umathandiza anthu kukhala otetezeka