Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Uthenga Wabwino Ukubala Zipatso ku São Tomé ndi Príncipe

Uthenga Wabwino Ukubala Zipatso ku São Tomé ndi Príncipe

Uthenga Wabwino Ukubala Zipatso ku São Tomé ndi Príncipe

MWINA anthu ambiri sanamvepo za São Tomé ndi Príncipe. Zilumba zimenezi sizitchulidwatchulidwa m’timabuku totsatsa malonda a malo amene anthu angachitireko tchuti. Pa mapu a dziko lonse lapansi, zilumbazi zimaoneka ngati timadontho tating’ono kwambiri pa Gulf of Guinea ku gombe la kumadzulo kwa Africa. São Tomé ali cha pamzere wongoyerekeza wodula dziko lonse lapansi paŵiri kuchokera kumpoto mpaka kum’mwera wotchedwa equator ndipo Príncipe ali kumpoto chakum’maŵa pang’ono kwa São Tomé. Popeza kumagwa mvula yambiri ndiponso n’kotentha, kuli nkhalango zachilengedwe zosangalatsa, zimene zili m’mphepete mwa mapiri ena aatali kuposa mamita 2,000.

Pazilumba za m’madera otentha zimenezi, zomwe zili ndi madzi obiriŵira ndiponso zili ndi mitengo ya mgwalangwa, pali anthu ochezeka ndiponso achikondi omwe ali ndi chikhalidwe chosangalatsa kwambiri chifukwa ngosakanikirana; kuli anthu a ku Africa kuno ndiponso a ku Ulaya. Ntchito yaikulu ya anthu okwana 170,000 a kumeneko ndi yaulimi wa cacao, omwe ndi malonda aakulu a dzikolo kumaiko ena, kapena ulimi wa mbewu zina ndi usodzi. M’zaka zaposachedwapa, kwakhala kovuta ngakhale kupeza chakudya cha patsiku.

Komabe, zaka khumi zomaliza za m’ma 1900 munachitika chinthu chimene chakhudza kwambiri moyo wa anthu ambiri pazilumba zimenezi. Mu June 1993, Mboni za Yehova zinalembetsa mwalamulo ku boma la São Tomé ndi Príncipe, ndipo ameneŵa anali mapeto a nthaŵi yaitali ndiponso yovuta kwa Mboni za Yehova pazilumba zimenezi.

Mbewu Zifesedwa Movutikira

Zikuoneka kuti Mboni yoyamba inapita ku dziko limeneli kumayambiriro a m’ma 1950 pamene akaidi a m’mayiko ena a mu Africa muno omwe anali mu ulamuliro wa Portugal anali kutumizidwa kukagwira ntchito ku misasa yozunzira anthu ku zilumbazi. Mboni ina ya ku Africa kuno, mpainiya, kapena kuti mtumiki wa nthaŵi zonse, inathamangitsidwa ku Mozambique chifukwa chakuti inali kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’dzikolo. Mboni imeneyi inapitiriza kulalikira mwachangu, ndipo pasanathe miyezi isanu ndi umodzi, panapezeka anthu ena 13 amene analinso kufalitsa uthenga wabwino. Kenako, kunafika Mboni zina za ku Angola zimene zinalinso ndi mlandu womwewo. Panthaŵi imene zinali paukaidi, zinagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuuza anthu kumeneko uthenga wabwino.

Pofika 1966 abale onse amene anali paukaidi ku São Tomé anali atabwerera kwawo. Kagulu ka ofalitsa Ufumu kamene kanatsala kanapitiriza kulalikira molimba mtima. Anazunzidwa, kumenyedwa, ndiponso kuikidwa m’ndende chifukwa anali kusonkhana pamodzi n’kumaphunzira Baibulo, ndipo panalibe aliyense wowayendera kapena kuwalimbikitsa. Mu 1975, dzikoli linalandira ufulu wodzilamulira kuchoka ku dziko la Portugal, ndipo pang’ono ndi pang’ono mbewu za choonadi cha Ufumu zinayamba kubala zipatso.

Kupita Patsogolo Ndiponso Ntchito Yomanga

Mu 1993 m’mwezi womwewo umene Mboni zinalembetsa mwalamulo, panali ofalitsa Ufumu okwana 100. Chaka chomwecho, apainiya apadera a ku Portugal anafika m’dzikolo. Anthu a kumeneko anawakonda apainiya ameneŵa chifukwa choti anali kuyesetsa kuphunzira chinenero cha Portuguese Creole. Ndiyeno ntchito yofunika kwambiri inali yoyang’ana malo a Nyumba ya Ufumu. Mlongo wina dzina lake Maria atamva za vutoli, anapereka theka la malo pamene panali nyumba yake yaing’ono. Malowo anali aakulu ndithu poti n’kukwana Nyumba ya Ufumu yaikulu. Maria sanali kudziŵa kuti popeza analibe achibale amene anali moyo, anthu ofuna kutukula malo anali kuŵenderera malo akewo. Tsiku lina munthu wina wamalonda wotchuka zedi anapita kukalankhula ndi Maria.

Iye anamuchenjeza kuti: “Zimene mwachita si zabwino ayi. Ndamva kuti mwapatsa anthu malo anu. Simukudziŵa kuti mungagulitse ndalama zambiri chifukwa chakuti ali muno m’tauni mwenimweni?”

Maria anafunsa kuti: “Ndikanapatsa inu, mukanandipatsa ndalama zingati?” Mwamunayo atangokhala chete osayankha, Maria anati: “Ngakhale munakandipatsa ndalama zonse za padziko lonse, n’zosakwana chifukwa ndalama sizingagule moyo.”

Mwamuna uja anafunsa kuti: “Mulibe ana inu, si choncho kodi?”

Pofuna kuthetsa nkhaniyo, Maria anati: “Malowo ndi a Yehova. Anandibwereka kwa zaka zambiri, ndipo tsopano ndam’bwezera. Ndikuyembekeza mwachidwi kudzakhala ndi moyo kosatha.” Ndiyeno anamufunsa mwamuna uja kuti: “Kapena muli ndi moyo wosatha umene mungandipatse?” Ananyamuka kumapita popanda kunena chilichonse.

Chotsatira chake chinali chakuti nyumba yabwino kwambiri ya nsanjika imodzi inamangidwa mothandizidwa ndi abale odziŵa ntchito a ku Portugal. Ili ndi zipinda zapansi, Nyumba ya Ufumu yaikulu, ndiponso nyumba zogonamo. Ilinso ndi zipinda zochitiramo sukulu ya akulu, atumiki otumikira, ndiponso apainiya. Panopo mipingo iŵiri imachitira misonkhano yawo m’nyumbayi, zimene zapangitsa kuti ikhale malo abwino kwambiri ophunzitsirapo kulambira koona mu likulu la dzikoli.

Ku Mé-Zochi, kunali mpingo wa ofalitsa achangu okwana 60. Popeza misonkhano inali kuchitikira mu Nyumba ya Ufumu yachisakasa imene inali m’munda wa nthochi, zinali zoonekeratu kuti pamafunika kumanga Nyumba ya Ufumu yabwino. Anakauza zimenezi khonsolo ya mzindawo, ndipo akuluakulu aboma okoma mtima anapereka malo abwino m’mphepete mwa msewu waukulu. Nyumba ya Ufumu yabwino inamangidwa m’miyezi iŵiri mothandizidwa ndi abale a ku Portugal, pogwiritsa ntchito njira yomanga mofulumira. Anthu akumeneko sanakhulupirire zimene anaona. Munthu wina wa zomangamanga wa ku Sweden amene amagwira ntchito yomanga m’tauniyo anadabwa kuona abale ndi alongo akugwira ntchito. Iye anati: “N’zochititsa chidwi izi. Mboni za Yehova, kuno ku Mé-Zochi, kumanga nyumba pogwiritsa ntchito njira yomanga mofulumira! Umu ndi mmene tiyenera kugwirira ntchito yathu.” Nyumba ya Ufumu imeneyi anaipatulira pa June 12, 1999, ndipo panali anthu 232. Holo imeneyi imachititsa chidwi kwambiri alendo obwera m’tauni ya Mé-Zochi.

Msonkhano Wosaiŵalika

Chochitika chosaiŵalika kwa Mboni za Yehova ku São Tomé ndi Príncipe ndi Msonkhano Wachigawo wa masiku atatu wakuti “Chiphunzitso Chaumulungu” umene unachitika mu January 1994​—msonkhano woyamba kuchitika ku zilumba zimenezi. Unachitikira mu holo yabwino kwambiri ya m’dzikoli yokhala ndi zipangizo zoziziritsira mpweya. Kodi mungathe kungolingalira mmene ofalitsa Ufumu okwana 116 anasangalalira kuona gulu la anthu 405 ndiponso nthaŵi yoyamba kuonera maseŵero a m’Baibulo komanso kulandira zofalitsa zatsopano zimene zinatuluka pamsonkhanowo? Kugombe n’kumene kunabatizidwira anthu 20 amene anadzipatulira.

Chinthu chachilendo chimene chinakopa anthu ndi mabaji apadera amene nthumwi za pamsonkhanowo zinavala. Kupezekapo kwa alendo 25 a ku Portugal ndi Angola kunapangitsa kuti msonkhanowo ukhale ngati wamayiko. Abalewo sanachedwe kukulitsa chikondi chachikristu, ndipo anthu ambiri anali kugwetsa misozi pa chigawo chomaliza pamene anali kutsanzikana.​—Yohane 13:35.

Atolankhani a wailesi yaboma ya National Radio anafika pa msonkhanowo ndipo analankhula ndi woyang’anira msonkhanowo. Anaulutsanso mbali zina za nkhani zosiyanasiyana za msonkhanowo. Unalidi wosaiŵalika, ndipo unathandiza Mboni zokhulupirika zimene zakhala kwazokhazokha kwa nthaŵi yaitali zimenezi, kuona kuti zili pafupi kwambiri ndi gulu looneka la Yehova.

Kubala Zipatso Kuti Yehova Atamandidwe

Uthenga wa Ufumu ukamabala zipatso, umathandiza anthu kukhala ndi khalidwe labwino limene limapangitsa kuti Yehova atamandidwe ndiponso alemekezedwe. (Tito 2:10) Mtsikana wina anali kusangalala kwambiri ndi zimene anali kuphunzira pa phunziro lake la Baibulo la mlungu ndi mlungu. Koma, bambo ake anali kumuletsa kupezeka pa misonkhano yampingo. Atawafotokozera mwaulemu kufunika kwa misonkhano yachikristu ndiponso kuti anali kufunitsitsa kumapezekapo, bambowo nthaŵi yomweyo anam’thamangitsa panyumbapo. Mwina anali kuganiza kuti achita zimene atsikana ambiri amachita​—kungoloŵerera mwamuna amene azimuthandiza. Bambo ake atamva kuti anali ndi makhalidwe abwino, wodzisunga monga Mkristu, anamuitana kudzakhala panyumbapo ndipo anam’patsa ufulu wonse wotumikira Yehova.

Chitsanzo china ndi cha mtsogoleri wa gulu lina loimba. Anali kumva chisoni chifukwa cha khalidwe lake loipa. Akufunafuna cholinga cha moyo, anayenderedwa ndi Mboni. Atayamba kugwiritsa ntchito miyezo ya makhalidwe ya m’Baibulo pamoyo wake, anthu m’tauniyo anali kumangokamba za iye. Posakhalitsa anaona kufunika kosiya kucheza ndi anthu onse olakwika. (1 Akorinto 15:33) Ndiyeno anachita chinthu chofunika kwambiri, anabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwake kwa Yehova.

Achinyamata angapo anali kufuna chipembedzo choona. Zimenezi zinawapangitsa kukambirana ndi apasitala a mipingo yosiyanasiyana ya evangelical, koma chotsatira chake chinali chakuti amangowawonjezera kusokonezeka maganizo ndiponso kukhumudwa. Ndiyeno, anayamba kupemphapempha ndiponso kunyoza chilichonse chokhudza chipembedzo.

Tsiku lina, mmishonale wina wa Mboni za Yehova, anali paulendo wokachititsa phunziro la Baibulo, ndipo anafika pamene panali anyamata ameneŵa. Gululi linafuna kuti mmishonaleyu ayankhe mafunso angapo ndipo anapita naye kuseri kwa nyumba, n’kumuuza kuti akhale pa kampando. Ndiyeno anayamba kum’funsa mafunso ambirimbiri ankhani zokhudza mzimu wa munthu, moto wa helo, moyo wakumwamba, ndiponso kutha kwa dziko. Mboniyo inayankha mafunso awo onse pogwiritsa ntchito Baibulo limene mtsogoleri wa anyamatawo anam’patsa. Patatha ola limodzi, mtsogoleriyo, yemwe dzina lake ndi Law, anati kwa mmishonaleyo: “Pokuitanani kuti mubwere mudzayankhe mafunso, cholinga chathu chinali kuti tikunyozeni, monga tanyozera anthu a zipembedzo zina. Timaganiza kuti palibe angayankhe mafunso ameneŵa. Koma inu mwayankha, ndipo mwagwiritsa ntchito Baibulo lokha. Tsopano tandiuzani, kodi ndingatani kuti ndiphunzire zambiri ponena za Baibulo?” Law anayamba kuphunzira Baibulo, ndipo posapita nthaŵi anayamba kupezeka pamisonkhano. Patangopita nthaŵi pang’ono, anachoka m’gulu lija ndipo anasiya khalidwe lake lachiwawa. Pasanathe chaka, anapatulira moyo wake kwa Yehova ndipo anabatizidwa. Tsopano ndi mtumiki wotumikira.

Khalidwe lina limene anthu a pazilumbazi amalikonda kwambiri ndi longokhalira limodzi popanda kulembetsa ukwati. Ambiri akhalira limodzi kwa zaka zambiri, ndipo ali ndi ana. Amaona kuti ndi chinthu chovuta kuchita zimene Mulungu amafuna pankhaniyi. N’zosangalatsa kuona mmene Mawu a Mulungu anathandizira munthu wina kuthana ndi vuto limeneli.​—2 Akorinto 10:4-6; Ahebri 4:12.

Antonio anamvetsa kuti ayenera kulembetsa ukwati wake ndipo anakonza zochita zimenezo akakolola chimanga kuti apeze ndalama zochitira phwando laukwati. Tsiku lina akuganiza zokolola chimangacho m’maŵa, akuba anaba chimangacho. Anaganiza zodikira kuti adzachite zimenezo akadzakolola chimanga chaka chotsatira, ndipo chimanga chimenechonso akuba anamubera. Atayesanso kupeza ndalama zochitira ukwati wake koma n’kulephera, Antonio anazindikira amene kwenikweni anali kuchititsa zimenezi. Iye anati: “Satana saseŵera nanenso. Pakutha pa mwezi umodzi ndi theka, tikhala titakwatirana, kaya padzakhala phwando laukwati kapena ayi.” Anaterodi, ndipo anadabwa kwambiri kuona kuti mabwenzi awo anawapatsa nkhuku, abakha, ndiponso mbuzi kuti achitire phwando laukwati. Atalembetsa ukwati wawo, Antonio ndi mkazi wake​—pamodzi ndi ana awo asanu ndi mmodzi​—anabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova.

Ku Chilumba cha Príncipe

M’zaka za posachedwapa woyang’anira dera ndi apainiya a ku São Tomé akhala akuyendera mwa apo ndi apo anthu okwana 6,000 a ku Príncipe. Anthu a pachilumba chimenechi anali kulandira bwino kwambiri alendo ndiponso ofunitsitsa kumvetsera zimene Mboni zinene. Mwamuna wina atatha kuŵerenga thirakiti limene apainiya anamusiyira, m’maŵa mwake anafunafuna apainiyawo n’kuwauza kuti akufuna kuti awathandize kugaŵira mathirakiti. Apainiyawo anafotokoza kuti imeneyo ndi ntchito yawo, koma mwamunayo anaumirira kuti apita nawo ku khomo lililonse limene apainiyawo apite kuti azikawadziŵikitsa apainiyawo kwa eninyumba ndi kuwapempha kuti amvetsere mosamalitsa. Pomalizira mwamuna uja anawasiya apainiya aja, koma anawayamikira chifukwa cha ntchito yofunika imene anali kugwira.

Mu 1998 apainiya aŵiri a ku São Tomé anasamukira ku Príncipe, ndipo pasanapite nthaŵi anali kuchititsa maphunziro a Baibulo a panyumba okwana 17. Ntchito inapitirira kupita patsogolo, ndipo posakhalitsa pa Phunziro la Buku la Mpingo nthaŵi zambiri panali kufika anthu ngati 16, ndipo anthu oposa 30 ankapezeka pankhani ya onse. Anakauza khonsolo ya mzindawo kuti akufuna malo osonkhanira, ndipo chosangalatsa n’chakuti anawapatsa malo omangapo Nyumba ya Ufumu. Abale a ku São Tomé anadzipereka kumanga Nyumba ya Ufumu yaing’ono yokhala ndi mogona apainiya apadera aŵiri.

Ndithudi uthenga wabwino ukubala zipatso zambiri ndiponso ukufalikira pazilumba za kwaokhaokha zimenezi. (Akolose 1:5, 6) Mu January 1990 ku São Tomé ndi Príncipe kunali ofalitsa 46. Mu chaka chautumiki cha 2002, chiŵerengero cha olengeza Ufumu chinafika pa 388. Ofalitsa oposa mmodzi pa asanu alionse ali mu utumiki wa nthaŵi zonse, ndipo akuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba pafupifupi 1,400. Opezeka pa Chikumbutso chaka cha 2001 anali anthu 1,907, kuposa ziŵerengero zonse za mbuyomo. Inde, pa zilumba zotentha zimenezi, mawu a Yehova akuthamanga ndipo akulemekezedwa.​—2 Atesalonika 3:1.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 12]

Mapulogalamu Otchuka a Pawailesi

Buku limene anthu a pazilumba zimenezi amakonda kwambiri ndi lakuti Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza. * M’milungu iŵiri iliyonse, pawailesi yaboma ya National Radio amaulutsa pulogalamu ya mphindi 15 ya mutu umenewu. Si mmene zimasangalatsira kumva woulutsa pulogalamuyi akufunsa kuti, “Achinyamata, kodi mungadziŵe motani ngati chili chikondi chenicheni kapena kungotengeka maganizo?” ndiyeno amaŵerenga ndime za m’bukuli. (Onani mutu 31.) Pulogalamu inanso yofanana ndi imeneyi imaulutsa ndime zimene asankha m’buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 33 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 33 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 9]

Nyumba ya Ufumu yoyamba ku São Tomé mu 1994

[Zithunzi patsamba 10]

1. Nyumba ya Ufumu yomangidwa mofulumira ku Mé-Zochi

2. Msonkhano wachigawo wosaiŵalika unachitikira mu holo iyi

3. Anthu achimwemwe amene anabatizidwa pa msonkhano wachigawo

[Mawu a Chithunzi patsamba 8]

Dziko: Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.