Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi pa Genesis 3:22, Yehova anali kunena ndani pamene anati “mmodzi wa ife”?

Zikuoneka kuti Yehova Mulungu anali kunena za iye ndi Mwana wake wobadwa yekha pamene anati: “Munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:22) Tiyeni tione chifukwa chake tikutero.

Yehova ananena mawu ameneŵa ataweruza banja loyambirira. Ena atenga mawu akuti “mmodzi wa ife” monga kudzilemekeza kumene mafumu amachita. Koma ponena za pa Genesis 1:26 ndi Genesis 3:22, katswiri wamaphunziro a Baibulo Donald E. Gowan anati: “M’Chipangano Chakale mulibe umboni wotsimikizira zimene anthu ambiri amafotokoza kuti, n’kulankhula kwa mafumu komadzinena kuti ‘ife,’ n’kungodzilemekeza chabe munthu payekha, n’kulankhula kosonyeza kuti munthu amadzimva, kapenanso n’kusonyeza kuti pali anthu angapo mwa Mulungu mmodzi. . . . Koma palibe mfundo iliyonse pa mfundo zimenezi imene ilidi yokwanira kutsimikizira kuti mawu a pa Genesis 3:22 akuti ‘mmodzi wa ife’ amasonyeza kuti Mulungu ankadzinena yekha.”

Kodi Yehova anali kunena Satana Mdyerekezi, amene anayamba kudzisankhira yekha “zabwino ndi zoipa” ndiponso amene anachititsa anthu oyambirira kuchita zomwezo? Zimenezi si zomveka. Apa Yehova anagwiritsa ntchito mawu akuti ‘mmodzi wa ife.’ Satana sanalinso pagulu la angelo okhulupirika a Yehova, choncho sakanaphatikizidwa ndi amene anali kumbali ya Yehova.

Kodi Mulungu anali kunena angelo okhulupirika? Sitinganene motsimikiza. Komabe, tingapeze yankho poona kufanana kwa mawu a pa Genesis 1:26 ndi pa Genesis 3:22. Pa Genesis 1:26, timaŵerenga kuti Yehova anati: ‘Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu.’ Kodi mawu ameneŵa anali kulankhula ndi ndani? Mtumwi Paulo ponena za mngelo amene anadzasanduka munthu wangwiro Yesu, anati: “Amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse; pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko.” (Akolose 1:15, 16) Inde, n’zomveka kuti pa Genesis 1:26, Yehova anali kulankhula ndi Mwana wake wobadwa yekha, “mmisiri,” amene anali pambali pake pamene anali kulenga kumwamba ndi dziko lapansi. (Miyambo 8:22-31) Popeza mawuŵa akufanana ndi mawu a pa Genesis 3:22, zikusonyeza kuti Yehova anali kulankhulanso ndi amene anali naye pafupi kwambiri, Mwana wake wobadwa yekha.

Mwachionekere Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anali kudziŵa “zabwino ndi zoipa.” Chifukwa chakuti anakhala kwanthaŵi yaitali ndiponso pafupi kwambiri ndi Yehova, ndithudi anaphunzira mokwanira maganizo a Atate wake, mfundo zawo, ndiponso kachitidwe kawo ka zinthu. Pokhutira kuti Mwana wake anali kuzidziŵadi bwino zimenezi ndiponso kuti ankazitsatira ndi mtima wonse, Yehova ayenera kuti anam’patsako ufulu wosamalira nkhani zina popanda kum’funsa Iye mwachidunji pankhani iliyonse. Choncho Mwana pamenepa ankatha kudziŵa chabwino ndi choipa komanso anali ndi ulamuliro wochita zimenezo. Komabe, mosiyana ndi Satana, Adamu, ndiponso Hava, iye sanachite zinthu zosiyana ndi za Yehova.