Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi n’chifukwa chiyani Nsanja ya Olonda ya April 1, 2002, patsamba 11, ndime 7, inanena kuti ubatizo wa m’madzi wa Ayuda amene anakhulupirira pa Pentekoste wa mu 33 C.E. unasonyeza “kudzipatulira kwa Mulungu kudzera mwa Kristu,” paokha pamene m’mbuyomu timakhulupirira kuti ubatizo wa Ayuda kuyambira mu 33 C.E. mpaka mu 36 C.E. sumafunika kuti munthu adzipatulire payekha?
Mu 1513 B.C.E., Yehova Mulungu anapatsa Aisrayeli mwayi wokhala mtundu woyera kwa iye ngati ‘akamvera mawu ake ndi kusunga chipangano chake.’ Iwo anayankha kuti: “Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita.”—Eksodo 19:3-8; 24:1-8.
Mwa kuvomera kuti adzasunga pangano la Chilamulo cha Mose, Aisrayeliwo anadzipatulira kwa Mulungu. Ana a m’tsogolo Achiyuda anadzabadwira mu mtundu wodzipatulira kwa Mulungu umenewu. Komabe, ubatizo wa Ayuda amene anasanduka otsatira a Yesu Kristu kuyambira pa Pentekoste wa mu 33 C.E. kumka m’tsogolo unatanthauza zambiri osati kungodzipereka chabe kwa Mulungu monga munthu wobadwira mu mtundu wodzipatulira. Ubatizowu umaimira kudzipatulira kwawo kwa Yehova Mulungu ndipo umayambitsa ubwenzi watsopano ndi iye kudzera mwa Yesu Kristu. Kodi zimenezi zinatheka bwanji?
Pambuyo pa kutsanulidwa kwa mzimu woyera pa ophunzira pafupifupi 120 amene anasonkhana m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu pa Pentekoste wa mu 33 C.E., mtumwi Petro anaimirira n’kuyamba kulalikira kwa gulu la Ayuda ndi anthu oloŵa Chiyuda amene anasonkhana kuti adzaone chimene chinachitika. Atapereka umboni wokwanira, iye anauza Ayuda amene anali kumva chisoni m’mitima mwawowo kuti: “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu.” Pokhudzidwa ndi zimene Petro ananena pambuyo pake, “iwo amene analandira mawu ake anabatizidwa; ndipo anawonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.”—Machitidwe 2:1-41.
Kodi Ayuda amene anabatizidwa atamva mawu a Petro sanali anthu a mtundu wodzipatulira kale kwa Mulungu? Kodi sanali kale mabwenzi a Mulungu chifukwa chokhala anthu odzipatulira kwa iye? Ayi. Mtumwi Paulo analemba kuti ‘Mulungu anachotsa Chilamulo mwa kuchikhomera pa mtengo wozunzirapo.’ (Akolose 2:14, NW) Pamene Kristu anafa mu 33 C.E., Yehova Mulungu anachotsa pangano la Chilamulo, lomwe linali maziko amene ankachititsa Aisrayeli kukhala mabwenzi Ake odzipatulira kwa iye. Mtundu umene unakana Mwana wa Mulungu tsopano unakanidwa ndi Mulungu mwiniwakeyo. Mtundu wa “Israyeli monga mwa thupi” sukanathanso kunena kuti unali mtundu wodzipatulira kwa Mulungu.—1 Akorinto 10:18; Mateyu 21:43.
Pangano la Chilamulo linathetsedwa mu 33 C.E., koma nthaŵi ya Mulungu yoyanja ndi kusamalira Ayuda mwapadera sinathere pamenepo. * Nthaŵi imeneyo inapitirirabe mpaka mu 36 C.E., pamene Petro analalikira kwa Mtaliyana woopa Mulungu Korneliyo ndi banja lake, komanso kwa anthu ena Akunja. (Machitidwe 10:1-48) Kodi maziko owonjezerera nthaŵi ya chiyanjo imeneyi anali chiyani?
Danieli 9:27 amati: “[Mesiya] adzapangana chipangano cholimba ndi ambiri sabata limodzi.” Pangano limene linakhalapobe kwa zaka zisanu ndi ziŵiri, kapena “sabata limodzi,” kuyambira pa ubatizo wa Yesu ndi kuyambika kwa utumiki wake wapoyera monga Mesiya mu 29 C.E. linali pangano la Abrahamu. Kuti munthu akhale nawo m’pangano limenelo, anangofunikira kukhala mbadwa yachihebri ya Abrahamu. Pangano la mbali imodzi limenelo silinkam’pangitsa munthu kukhala paubwenzi wodzipatulira kwa Yehova. Choncho, Ayuda okhulupirira amene ankabatizidwa pambuyo pa nkhani ya Petro ya pa Pentekoste wa mu 33 C.E., ngakhale kuti anali kuonedwa mwapadera chifukwa chobadwa ali Ayuda, iwo sanali pa ubwenzi ndi Mulungu monga anthu ake odzipatulira pambuyo pa kutha kwa pangano la Chilamulo. Anafunika kuti adzipatulire kwa Mulungu paokha.
Ayuda komanso anthu oloŵa Chiyuda amene anabatizidwa pa tsiku la Pentekoste wa mu 33 C.E. anafunikiranso kudzipatulira paokha kwa Mulungu pa chifukwa china. Mtumwi Petro analimbikitsa omvetsera ake kuti alape n’kubatizidwa m’dzina la Yesu. Kuti achite zimenezi anafunikira kusiya zinthu za dziko n’kuvomereza kuti Yesu ndiye Ambuye ndi Mesiya, Mkulu wa Ansembe, ndiponso ndi amene ali kudzanja lamanja la Mulungu kumwamba. Anayenera kuitanira pa dzina la Yehova Mulungu kuti apulumuke kudzera mwa Kristu Yesu, kutanthauza kuti anayenera kukhulupirira Kristu n’kuvomereza kuti iye ndiye Mtsogoleri wawo. Maziko onse okhalira ndi ubwenzi ndi Mulungu komanso kukhululukidwa machimo tsopano anali atasintha. Aliyense wa Ayuda okhulupirirawo payekha anafunika kuvomereza zinthu zatsopano zimenezi. Motani? Mwa kudzipatulira kwa Mulungu n’kusonyeza zimenezi poyera mwa kumizidwa m’madzi m’dzina la Yesu Kristu. Ubatizo wa m’madzi unali chizindikiro cha kudzipatulira kwawo kwa Mulungu, ndipo unawachititsa kukhala pa ubwenzi watsopano ndi iye kudzera mwa Yesu Kristu.—Machitidwe 2:21, 33-36; 3:19-23.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Pamene Yesu Kristu anakwera kumwamba n’kupereka kwa Yehova Mulungu mtengo wa moyo wake waumunthu woperekedwa nsembe, pangano la Chilamulo cha Mose linathetsedwa, ndipo maziko a “pangano latsopano” lonenedweratulo anakhazikitsidwa.—Yeremiya 31:31-34.