Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungakonde Kumufunsa Chiyani Mulungu?

Kodi Mungakonde Kumufunsa Chiyani Mulungu?

Kodi Mungakonde Kumufunsa Chiyani Mulungu?

ANTHU padziko lonse ali ndi mafunso ofunikadi mayankho okhudza moyo. Kodi inunso muli ndi mafunso oterowo? Ena afunsa aphunzitsi a zipembedzo mafunso awowo koma sanawayankhe zogwira mtima. Ena asinkhasinkha mafunso ameneŵa paokha. Ena apemphera kwa Mulungu kuti awathandize. Kodi n’zothekadi kuti Mulungu ayankhe mafunso anu okhudza nkhani zimene zimakuvutitsani maganizo? Ena mwa mafunso amene anthu ambiri anena kuti akanakonda kufunsa Mulungu ndi aŵa.

Mulungu, kodi ndinu ndani kwenikweni?

Chikhalidwe, chipembedzo cha makolo, ndiponso zosankha za anthu zimakhudza mmene anthuwo amamuonera Mulungu. Ena amatchula dzina la Mulungu pamene ena amangomutcha Mulungu basi. Kodi ndi nkhani yaikulu kumutchula kapena kusamutchula dzina lake? Kodi pali Mulungu m’modzi yekha woona amene amatiuza za iye ndiponso dzina lake?

N’chifukwa chiyani anthu tikuvutika kwambiri?

Kutayirira kwa munthu kapena khalidwe lake loipa zikawononga thanzi lake kapena kumuloŵetsa mu umphaŵi, iye angadandaule. Koma angadziŵe chifukwa chake akuvutika.

Komabe, anthu ena ankhaninkhani amavutika kwambiri pamene iwo sanalakwe chilichonse. Ena akudwala matenda osachiritsika. Ena akuvutika kwambiri kuti apeze malo okhala ndiponso chakudya chokwanira banja lawo. Anthu ambiri akuvutika ndi umbanda, nkhondo, chiwawa chosaneneka, masoka achilengedwe, kapena kusoŵa chilungamo kwa anthu a maudindo.

M’pake kuti ambiri amafunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani mavuto ameneŵa afala kwambiri chonchi? N’chifukwa chiyani Mulungu akulolera kuti tizivutika motere?’

N’chifukwa chiyani ndili ndi moyo? Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?

Nthaŵi zambiri munthu amayamba kudzifunsa mafunso ameneŵa chifukwa cha kukhumudwa ngati zochita zake za tsiku ndi tsiku sizikum’thandiza kusangalala kwenikweni ndi moyo, ndipo ndi ambiri amene zimawachitikira zimenezi. Anthu ena ambirimbiri amakhulupirira kuti Mulungu analinganiziratu mmene moyo wa munthu aliyense udzakhalira. Kodi zimenezo n’zoona? Ngati Mulungu ali nanudi cholinga chapadera, mosakayika mungakonde kuchidziŵa.

Mwa mabuku onse amene ali padziko lapansi, pali buku limodzi limene limafotokoza momveka bwino kuti analiuzira Mulungu. Monga mungayembekezere uthenga wochokeradi kwa Mulungu wopita kwa anthu onse mmene uyenera kukhalira, buku limeneli likupezeka m’zinenero zambiri kuposa buku lina lililonse. Buku limeneli ndi Baibulo Lopatulika. M’bukuli, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, Mulungu mwiniwakeyo, akufotokoza kuti iye ndani ndipo dzina lake ndani. Kodi mukulidziŵa dzina lakelo? Kodi mumadziŵa zimene Baibulo limanena pa mfundo yoti Mulungu ndi wotani? Kodi mukudziŵa zimene limanena pankhani ya zimene Mulungu amafuna kwa inu?

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

COVER: Chad Ehlers/​Index Stock Photography

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Mountain: Chad Ehlers/​Index Stock Photography