Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ukwati Wosayembekezeka wa Boazi ndi Rute

Ukwati Wosayembekezeka wa Boazi ndi Rute

Ukwati Wosayembekezeka wa Boazi ndi Rute

TSIKU lina cha ku Betelehemu pabwalo popunthira tirigu panali kuchitika zinthu zambirimbiri. Inali nthaŵi ya masika ndipo patsikuli panali ntchito yambiri. Kununkhira kwa tirigu wokazinga kunadziŵitsa antchito amene anali ndi njala kuti inali nthaŵi yoti adye. Aliyense anadyera thukuta lake.

Boazi yemwe anali mwini munda ndiponso wolemera, anadya ndi kumwa mpaka kukhuta ndipo anapumula m’mbali mwa mulu wa tirigu. Ndiye atatha kukolola patsiku limenelo, aliyense anayang’ana malo abwino oti agone. Boazi atakhuta, anadzifunda n’kufa nato tulo.

Kukumana Mwachinsinsi

Pakati pausiku, Boazi anadzuka akumva kuzizira ndiponso akunjenjemera. Anadabwa kuona kuti wina wamuvundukula dala mapazi ake, ndipo chapompo pagona munthu wina. Popeza kuti unali usiku ndipo sanadziŵe kuti anali ndani, anafunsa kuti: “Ndiwe yani?” Mawu a munthu wamkazi anayankha kuti: “Ndine Rute mdzakazi wanu; mufunde mdzakazi wanu chofunda chanu, pakuti inu ndinu wondiombolera cholowa.”​—Rute 3:1-9.

Anthuwa analankhulana mu mdima popanda wina kuwamva. Akazi sankapezeka okha chonchi popunthirapo. (Rute 3:14) Komabe, Boazi atam’pempha, Rute anagonabe ku mapazi ake mpaka kutatsala pang’ono kufika mbandakucha ndipo anadzuka n’kumapita, motero anapeŵa zonenanena za anthu zopanda umboni.

Kodi kukumana kumeneku kunali kwa anthu oti ali pachibwenzi? Kodi mwamuna wolemera ndi wachikulire ameneyu anatengeka mtima kwambiri ndi Rute, mkazi wamasiye, wosauka, ndi wachitsikana wa dziko limene silinali lachiisrayeli? Kapena kodi usiku umenewo Boazi anam’pezerera Rute chifukwa cha mavuto ake ndiponso popeza anali wosungulumwa? Yankho la mafunso ameneŵa n’lakuti ayi. Zimene zinachitika kwenikweni zili chitsanzo cha kukhulupirika ndiponso kukonda Mulungu. Ndipo nkhani yonse ndi yokhudzanso mtima kwambiri.

Koma kodi Rute anali ndani? Kodi cholinga chake chinali chotani? Ndipo kodi munthu wolemera ameneyu, Boazi, anali ndani?

“Mkazi Waulemu”

Zaka zingapo izi zisanachitike, ku Yuda kunagwa chilala. Banja lachiisrayeli la anthu anayi​—Elimeleki; mkazi wake, Naomi; ndi ana awo aŵiri, Maloni ndi Kilioni​—linasamukira ku Moabu, dziko la chonde. Anawo anakwatira akazi aŵiri achimoabu, Rute ndi Olipa. Amuna atatuŵa atamwalira ku Moabu, akazi atatuwa anamva kuti zinthu tsopano zinali bwino ku Israyeli. Chotero Naomi amene tsopano anali wamasiye, wowawidwa mtima, wopanda ana kapena zidzukulu, anaganiza zobwerera ku dziko la kwawo.​—Rute 1:1-14.

Ali paulendo wa ku Israyeli, Naomi anam’limbikitsa Olipa kubwerera kwawo. Ndiyeno Naomi anauza Rute kuti: “Taona mbale wako wabwerera kwa anthu a kwawo, ndi kwa mulungu wake, bwerera um’tsate mbale wako.” Koma Rute anati: “Musandiumirize kuti ndikusiyeni, . . . pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, . . . anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga; kumene mudzafera inu ine ndidzafera komweko, ndi kuikidwa komweko.” (Rute 1:15-17) Choncho akazi aŵiri amasiye osauka ameneŵa anabwerera ku Betelehemu. Kumeneko, anthu amene anali kukhala nawo pafupi anachita chidwi ndi mmene Rute ankakondera ndi kusamalilira apongozi ake, moti anthuwo ankati Rute ‘anaposa ana aamuna asanu ndi aŵiri pothandiza [Naomi].’ Ena ankati ndi “mkazi waulemu.”​—Rute 3:11; 4:15.

Ku Betelehemu atayamba kukolola Barele, Rute anati kwa Naomi: “Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha la ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomera mtima.”​—Rute 2:2.

Mwamwayi anapita ku munda wa Boazi, wachibale wa apongozi ake aamuna, Elimeleki. Anapempha kwa woyang’anira mundawo kuti atole nawo khunkha. Kulimbikira kwake ntchito potola khunkha kunali kochititsa chidwi, ndipo woyang’anirayo anakamuyamikira kwa Boazi.​—Rute 1:22–2:7.

Woteteza ndi Wothandiza

Boazi anali wolambira Yehova wodzipereka. M’mawa uliwonse, Boazi popereka moni kwa anthu amene ankamuchekera tirigu ankati: “Yehova akhale nanu,” ndipo iwo ankayankha kuti: “Yehova akudalitseni.” (Rute 2:4) Boazi ataona kuti Rute anali wolimbikira ntchito ndiponso atamva zoti ndi wokhulupirika kwa Naomi, anakonza zoti Rute azikunkha mwapadera. Mwachidule tingati anamuuza kuti: ‘Uzikunkha m’munda mwanga; palibe chifukwa chopitira kwina. Umirira adzakazi anga; udzakhala nawo bwinobwino. Ndawauza anyamata kuti asakukhudze. Ukamva ludzu, azikakutungira madzi abwino.’​—Rute 2:8, 9.

Rute anagwada pansi nati: ‘Mwandikomera mtima chifukwa ninji, popeza ndine mlendo?’ Boazi anayankha kuti: ‘Ndinamva bwino zonse unachitira mpongozi wako atafa mwamuna wako​—kuti unasiya atate wako ndi amako, achibale ako, ndi dziko lako, kudzakhala ndi anthu amene sunawadziŵa iwe kale. Yehova akubwezere ntchito yako. Akupatse mphotho yokwanira.’​—Rute 2:10-12.

Boazi sanachite izi n’cholinga chomukopa kuti akhale naye pachibwenzi. Anali kumuyamikira mochokera pansi pamtima. Rute anadzichepetsa kwambiri ndi kumuthokoza chifukwa cha mawu ake olimbikitsawa. Anadziona kuti sakuyenera zimenezi ndipo anapitiriza kulimbikira ntchito kwambiri kuposa mmene ankachitira. Ndiyeno panthaŵi ya chakudya, Boazi anamupempha Rute kuti: ‘Sendera, idya mkate; nusunse nthongo yako m’vinyo wosasayo.’ Anadya mpaka kukhuta ndiponso anasunga chakudya choti apite nacho kunyumba akapatse Naomi.​—Rute 2:14.

Pofika madzulo, Rute anali atakunkha Balere wokwana lichero limodzi. Anatenga pamodzi ndi chakudya chimene anasunga chija kupita nacho kunyumba kukapatsa Naomi. (Rute 2:15-18) Naomi pochita chidwi ndi kuchuluka kwa khunkha, anafunsa kuti: “Unakatola kuti khunkha lero? . . . Adalitsike iye amene anakusamalira.” Atamva kuti ndi kwa Boazi, Naomi anati: “Yehova am’dalitse amene sanaleka kuwachitira zokoma amoyo ndi akufa. . . . Munthuyu ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera cholowa.”​—Rute 2:19, 20.

Kupeza “Popumulako”

Pofuna kupezera mpongozi wakeyo “popumulako,” kapena kuti nyumba, Naomi anapezerapo mwayi pa zimene zinachitikazi kukonza zopempha wowombola, malinga ndi Chilamulo cha Mulungu. (Levitiko 25:25; Deuteronomo 25:5, 6) Tsopano Naomi anamulangiza Rute zochita ndipo anatero mogwira mtima ndi mochititsa chidwi, kuti Boazi akakopeke naye. Atakonzeka ndiponso atalangizidwa bwino, Rute anapita usiku popunthirapo pa Boazi. Anamupeza ali mtulo. Anamuvundukula mapazi ake n’kumadikira kuti adzuke.​—Rute 3:1-7.

Boazi atadzuka, zochita za Rute zimene zinali ndi tanthauzo mosakayikira zinampangitsa kuzindikira kuti pempho lake linali lalikulu moti ‘anamufunda mdzakazi wake chofunda chake.’ Zochita za Rute zinapangitsa Myuda wachikulireyo kuzindikira udindo wake monga woombola, popeza anali wachibale wa mwamuna wa Rute, Maloni amene anamwalira.​—Rute 3:9.

Kufika kwa Rute usiku kunali kodzidzimutsa. Komabe zimene Boazi anachita zinasonyeza kuti zimene Rute ananena zoti iye ndi woombola, sizinali zachilendo kwenikweni. Boazi anali wofunitsitsa kuchita zimene Rute anapempha.

Mawu a Rute ayenera kuti anasonyeza kuti anali ndi mantha ndithu, zimene zinachititsa Boazi kumutsimikizira kuti: “Tsopano, mwana wanga, usaope; ndidzakuchitira zonse unenazi; pakuti onse a pa mudzi wa anthu a mtundu wanga adziŵa kuti iwe ndiwe mkazi waulemu.”​—Rute 3:11.

Tikuona kuti Boazi anaona zochita za Rute kukhala zoyenera kwambiri pa mawu ake akuti: “Yehova akudalitse, mwana wanga. Chokoma chako wachichita potsiriza pano, chiposa chakuyamba chija.” (Rute 3:10) Poyamba, Rute anachitira zokoma Naomi. Potsiriza, modzipereka anadzidziŵikitsa kwa Boazi, mwamuna wachikulire zedi, popeza anali woombola. Anali wofunitsitsa kubereka mwana m’dzina la Maloni, mwamuna wake amene anamwalira, ndiponso kwa Naomi.

Woombola Akana

M’maŵa mwake, Boazi anapempha wachibale, amene anangomutcha kuti “uje,” amene anali wachibale kwambiri wa Naomi poyerekezera ndi Boazi. Pamaso pa anthu a m’mudzimo ndiponso akuluakulu ena a m’mudzimo, Boazi anati: ‘Ndati ndikuululire za udindo wako woombola kwa Naomi kadziko kamene kanali ka mwamuna wake Elimeleki, popeza ayenera kugulitsa.’ Boazi anapitiriza kuti: ‘Uwombola?’ Ukapanda kuombola, ndidzaombola.’ Ndiyeno uje uja anasonyeza kuti awombola.​—Rute 4:1-4.

Koma ujeyo sanadziŵe kuti chitsatire n’chiyani. Tsopano Boazi anati pamaso pa mboni zonse: “Tsiku lomwelo ugula mundawo pa dzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmoabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa cholowa chake.” Poopa kuwononganso ndi cholowa chake chomwe, wachibaleyo anakana udindo wake woombola, nati: “Sinditha kuombola.”​—Rute 4:5, 6.

Malinga ndi mwambo wawo, mwamuna wokana kuombola anafunika kuvula nsapato yake ndi kupatsa mnansi wake. Choncho pamene woombolayo anauza Boazi kuti, ‘udzigulire wekha kadzikoko,’ anavulanso nsapato yake. Ndiyeno Boazi anati kwa akulu ndi anthu onse: “Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, pa dzanja la Naomi. Ndiponso Rute Mmoabu, mkazi wa Maloni ndam’gula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa cholowa chake . . . inu ndinu mboni lero lino.”​—Rute 4:7-10.

Anthu onse amene anali kuchipata anati kwa Boazi: “Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m’nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israyeli, iwo aŵiri; nuchite iwe moyenera m’Efrata, mumveke m’Betelehemu.”​—Rute 4:11, 12.

Anthuwo atam’funira zabwino, Boazi anatenga Rute kukhala mkazi wake. Anam’balira mwana wamwamuna dzina lake Obedi, ndipo chifukwa cha chimenechi Rute ndi Boazi anakhala makolo a Mfumu Davide ndipo kenako a Yesu Kristu.​—Rute 4:13-17; Mateyu 1:5, 6, 16.

“Mphotho Yokwanira”

Mu nkhani yonse, kuyambira mmene anali kuwapatsira moni mwachikondi antchito ake mpaka kuvomera udindo wosunga dzina la banja la Elimeleki, Boazi anasonyeza kukhala mwamuna wabwino kwambiri yemwe ankachita zinthu zothandiza ndiponso waudindo wake. Komanso, anali mwamuna wodziletsa, wachikhulupiriro, ndi wokhulupirika. Boazi analinso woolowa manja, wachifundo, wodzisunga, ndiponso womvera kwambiri malamulo a Yehova.

Tikutha kuona kuti Rute anali kukonda Yehova, anachitira zokoma Naomi, anali kulimbikira ntchito ndiponso anali wodzichepetsa. N’zosadabwitsa kuti anthu anali kumuona kuti anali “mkazi waulemu.” Sankadya “zakudya za ulesi,” ndipo chifukwa cholimbikira ntchito, ankapeza zinthu zokadyera pamodzi ndi apongozi ake amene anali osoŵa. (Miyambo 31:27, 31) Pomugwirira ntchito Naomi, Rute ayenera kuti anapeza chimwemwe chimene chimabwera chifukwa chopatsa.​—Machitidwe 20:35; 1 Timoteo 5:4, 8.

Ndi zitsanzo zabwino kwambiri zimene timapeza mu buku la Rute. Yehova amam’kumbukira Naomi. Rute analandira “mphoto yokwanira” monga kholo la Yesu Kristu. Boazi anadalitsidwa ndi “mkazi waulemu.” Ife timapeza zitsanzo za chikhulupiriro mwa aliyense wa anthu ameneŵa.

[Bokosi patsamba 26]

Kuyembekezera Zabwino

Ngati mukuona kuti muli m’mavuto, mungapeze chiyembekezo mu nkhani ya Rute. Tikuonanso kuti nkhani ya Rute ndi mathero ofunika kwambiri a buku la Oweruza. Buku la Rute limanena momwe Yehova anagwiritsira ntchito mkazi wamasiye wodzichepetsa wa mtundu wachilendo wa Moabu kutulutsa mfumu ya anthu ake. Poona zochitika za m’buku la Oweruza, chikhulupiriro cha Rute chinawala ngati muuni m’nthaŵi imeneyo.

Mwa kuŵerenga nkhani ya Rute, mungakhale ndi chidaliro chakuti kaya zinthu zivute bwanji, Mulungu nthaŵi zonse amasamalira anthu ake ndipo amachita zofuna zake.