Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungapeze Kuti Moyo Wauzimu Weniweni?

Kodi Mungapeze Kuti Moyo Wauzimu Weniweni?

Kodi Mungapeze Kuti Moyo Wauzimu Weniweni?

RODOLPHE anafunsa mwadala kuti: “Ngati mudzatsatira chipembedzo chifukwa chabe choti achibale onse akuchitsatira, bwanji osangosankha chipembedzo cha Asetiki chimene makolo akale anali kutsatira zaka 2000 zapitazo?” Zimenezi zinapangitsa wachinyamata yemwe anali kumvetsera kumwetulira.

Rodolphe anati: “Ubwenzi wanga ndi Mulungu ndi wofunika kwambiri kwa ine. Ndikutsutsiratu mfundo yoti nditsatire ziphunzitso za chipembedzo mwa mwambo kokha chifukwa choti achibale anga omwe anakhala ndi moyo zaka makumi kapena mazana zapitazo anatsatira chipembedzo chimenechi.” Rodolphe anapenda zinthu mosamalitsa; iye sanafune kuona nkhani yofunika imeneyi monga chinthu chongolandira kwa makolo.

Ngakhale kuti kupatsirana chipembedzo kwa mibadwo kukutha masiku ano, anthu ambiri amatsatirabe chipembedzo cha banja lawo. Komano kodi ndi bwino nthaŵi zonse kutsatira chipembedzo cha makolo ako? Kodi Baibulo limati chiyani?

Atakhala zaka 40 mu chipululu, Yoswa, amene analowa m’malo mwa Mose, anapatsa Aisrayeli mwayi wosankha. Iye anati: “Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzam’tumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m’dziko lawo; koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.”​—Yoswa 24:15.

Limodzi mwa makolo amene Yoswa anali kunena anali Tera, bambo wa Abrahamu, amene anakhala mu mzinda wa Uri, umene panthaŵiyo unali kum’maŵa kwa mtsinje wa Firate. Baibulo silinena zambiri zokhudza Tera, kusiyapo mfundo yakuti anali kulambira milungu ina. (Yoswa 24:2) Mwana wake Abrahamu ngakhale kuti sanali kudziŵa zambiri zokhudza chifuno cha Mulungu, analolera kusiya mzinda wa kwawo nthaŵi imene Yehova anam’lamula kutero. Inde, Abrahamu anasankha chipembedzo chosiyana ndi cha bambo ake. Chifukwa choti anachita zimenezi, Abrahamu analandira madalitso amene Mulungu anam’lonjeza ndipo anakhala munthu amene zipembedzo zambiri zimam’dziŵa monga “tate wa onse akukhulupirira Mulungu.”​—Aroma 4:11, Today’s English Version.

Baibulo limafotokozanso bwino kwambiri nkhani ya Rute, kholo la Yesu Kristu. Rute, mkazi wachimoabu amene anakwatiwa ndi Mwiisrayeli, anakhala mkazi wamasiye ndipo anafunika kusankha: kukhala m’dziko la kwawo kapena kubwerera ndi mpongozi wake ku Israyeli. Poona kufunika kwambiri kwa kulambira Yehova poyerekeza ndi kulambira mafano komwe makolo ake ankachita, Rute anauza mpongozi wake kuti: “Anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga.”​—Rute 1:16, 17.

Pofotokoza za kufunika kwa nkhani imeneyi m’mabuku ovomerezedwa a Baibulo, buku lakuti Dictionnaire de la Bible linafotokoza kuti nkhani imeneyi ikusonyeza “mmene mkazi wobadwira ku dziko lina, pakati pa anthu akunja osagwirizana ndiponso odedwa ndi Aisrayeli, . . . anakhalira kholo la Mfumu yoyera Davide mwa kufuna kwa Mulungu, chifukwa cha kukonda kwake mtundu wa Yehova ndiponso kumulambira iye.” Rute sanazengereze kusankha chipembedzo chosiyana ndi cha makolo ake ndipo chifukwa cha kusankha motere, analandira dalitso la Mulungu.

Nkhani yofotokoza chiyambi chachikristu imalongosola momveka bwino kwambiri zifukwa zimene ophunzira a Yesu anakanira zipembedzo za makolo awo akale. Mtumwi Petro, pokamba nkhani imene inakhudza anthu mtima kwambiri, anapempha omvera ake kuti ‘adzipulumutse ku mbadwo uno wokhotakhota’ mwa kulapa machimo awo ndi kubatizidwa m’dzina la Yesu Kristu. (Machitidwe 2:37-41) Chimodzi mwa zitsanzo zabwino kwambiri chinali cha Sauli, Myuda wozunza Akristu. Pamene anali kupita ku Damasiko, anaona masomphenya a Kristu. Zitachitika zimenezi Sauli anakhala Mkristu ndipo anadzatchedwa mtumwi Paulo.​—Machitidwe 9:1-9.

Akristu oyambirira ambiri sizinawachitikire zimenezi. Komabe, onse anasiya Chiyuda kapena kulambira milungu yakunja yosiyanasiyana. Anthu amene anatsatira Chikristu anachita zimenezi akudziŵa bwino zoona zake ndipo nthaŵi zambiri zinkachitika pambuyo pa kukambirana kwanthaŵi yaitali za ntchito ya Yesu monga Mesiya. (Machitidwe 8:26-40; 13:16-43; 17:22-34) Akristu oyambirira ameneŵa anadziŵa bwino kufunika kosintha miyoyo yawo. Onse, Ayuda ndi Akunja omwe anaitanidwa, koma uthenga unali wofanana. Kuti asangalatse Mulungu, anafunika kutsatira njira yatsopano ya kulambira ya Akristu.

Zimene Tikufunika Kusankha

M’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino panafunika kulimba mtima kuti munthu asiye chipembedzo cha makolo monga Chiyuda, kulambira mfumu kapena kulambira milungu yachikunja, kuti aloŵe chipembedzo chimene chinali kunyozedwa ndi Ayuda komanso Aroma. Posapita nthaŵi kusankha kotere kunali kuchititsa ena kuzunzidwa mwankhanza. Masiku ano, pamafunikanso kulimba mtima kuti “munthu akane kutengeka kwambiri ndi kutsatira zimene ena akuchita,” monga momwe Hippolyte Simon, bishopu wachikatolika, wa ku Clermont-Ferrand ananenera m’ buku lake lakuti Vers une France païenne? (Kodi Dziko la France Likufuna Kukhala Lachikunja?) Pamafunika kulimba mtima kuti ukhale m’gulu lachipembedzo laling’ono la Mboni za Yehova limene nthaŵi zina limatsutsidwa.

Paul wachinyamata wa ku Bastia, pachilumba cha Corsica, amene analeredwa m’chipembedzo cha Katolika nthaŵi zina ankachita nawo ntchito za pa tchalitchi monga kugulitsa makeke kuti apeze ndalama za gulu lothandiza anthu la Akatolika. Chifukwa chofuna kudziŵa bwino Baibulo, anavomera kuti azikambirana ndi Mboni za Yehova nthaŵi zonse. M’kupita kwanthaŵi anazindikira kuti zimene anali kuphunzira zidzam’pindulitsa kwanthaŵi yaitali. Motero, Paul anavomereza kotheratu mfundo za Baibulo ndipo anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Makolo ake anavomereza zimene iye anasankha ndipo zimenezi sizinasinthe kugwirizana kwawo kwa pamtima m’banja lawo.

Amélie amakhala kumwera kwa France. Mibadwo inayi ya am’banja lake ndi Mboni za Yehova. N’chifukwa chiyani anasankha chipembedzo cha makolo ake? Iye anati: “Munthu sakhala wa Mboni za Yehova chifukwa choti makolo ake kapena agogo ake ali kapena anali Mboni za Yehova. M’malo mwake, munthu umadzafika ponena kuti ‘Ichi n’chipembedzo changa chifukwa zimenezi n’zomwe ineyo ndikukhulupirira.’” Mofanana ndi Mboni za Yehova zina zachinyamata, Amélie amadziŵa kuti kukhulupirira kwambiri ziphunzitso za chipembedzo chake kwam’chititsa kukhala ndi cholinga pamoyo ndiponso kukhala wosangalala nthaŵi zonse.

Chifukwa Chake Tiyenera Kutsatira Miyezo ya Mulungu

Buku la Miyambo, chaputala 6, vesi 20, limalimbikitsa amene akufuna kusangalatsa Mulungu kuti: “Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mako.” M’malo moti achinyamata azingomvera mwachimbulimbuli, malangizo ameneŵa akuwauza kutsatira miyezo ya Mulungu mwa kukulitsa chikhulupiriro chawo ndiponso mwa kuima kumbali ya Mulungu. Mtumwi Paulo anauza anzake kuti ‘aziyesa zonse,’ kufufuza ngati zimene anali kuphunzitsidwa zinali zogwirizana ndi Mawu a Mulungu ndi chifuno Chake, ndiponso kutsatira zimenezo.​—1 Atesalonika 5:21.

Mboni za Yehova zoposa sikisi miliyoni, achinyamata ndi achikulire omwe kaya analeredwa m’banja lachikristu kapena ayi, anasankha motero. Mwa kuphunzira Baibulo mosamalitsa, anapeza mayankho odalirika a mafunso awo okhudza cholinga cha moyo ndiponso anamvetsa bwino kwambiri za chifuno cha Mulungu kwa anthu. Atadziŵa zimenezi, anatsatira miyezo ya Mulungu ndiponso kuyesetsa kuchita chifuniro cha Mulungu.

Kaya mumaŵerenga magazini ino nthaŵi zonse kapena ayi, bwanji osalola Mboni za Yehova kukuthandizani kupenda moyo wauzimu m’Baibulo? Mwa njira imeneyi, mudzatha ‘kulawa, ndi kuona kuti Yehova ndiye wabwino’ ndiponso mudzadziŵa zinthu zimene ngati muzigwiritsira ntchito, zidzakuthandizani kuti mudzapeze moyo wosatha.​—Salmo 34:8; Yohane 17:3.

[Chithunzi patsamba 5]

Mibadwo inayi ya banja la Mboni za Yehova ku France

[Chithunzi patsamba 7]

Rute anasankha kutumikira Yehova m’malo mwa milungu ya makolo ake