Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata Amene Amakondweretsa Mtima wa Yehova

Achinyamata Amene Amakondweretsa Mtima wa Yehova

Achinyamata Amene Amakondweretsa Mtima wa Yehova

“Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.”​—MIYAMBO 27:11.

Nkhani zophunzira zimenezi akonzera makamaka achinyamata a Mboni za Yehova. Motero, tikukulimbikitsani achinyamata kuphunzira mosamala nkhanizi ndi kupereka ndemanga momasuka pamene zikuphunziridwa ku mpingo pa Phunziro la Nsanja ya Olonda.

1, 2. (a) Fotokozani ngati kukopeka chabe ndi zinthu za m’dziko kumatanthauza kuti simukuyenerera kukhala Mkristu. (Aroma 7:21) (b) Kodi mukuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Asafu? (Onani bokosi pa tsamba 13.)

TAYEREKEZERANI kuti mukufuna kugula zovala. Pamene mukuyang’anayang’ana, mukuona chovala chomwe kungochiona kumene chakusangalatsani kwambiri. Mtundu wake komanso sitayelo yake ndi yabwino kwabasi kwa inu, ndipo mtengo wake ndi wosaboola m’thumba. Komano mutachiyanga’anitsitsa chovalacho mukudabwa kwambiri kuona kuti nsalu ya m’mbali mwake ndi yoperepeseka, ndiponso sanachisoke bwino chovalacho. Ngakhale kuti ndi chosangalatsa, sanachikonze bwino. Kodi mudzawononga ndalama zanu kugula chovala chosalimbacho?

2 Yerekezerani zimenezi ndi zinthu zimene mungakumane nazo monga wachinyamata wachikristu. Kungoona koyamba, zinthu za m’dziko lapansili, mofanana ndi chovala, zingaoneke ngati zosangalatsa kwambiri. Mwachitsanzo, anzanu kusukulu angamapite ku mapwando osangalatsa, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa, kupanga zibwenzi zachisawawa, ndiponso kugonana anthu oti sanakwatirane. Kodi nthaŵi zina mumakopeka ndi zinthu zimenezi? Kodi mumalakalaka mutangolaŵako chabe umene eniwo amati ufulu? Ngati ndi choncho, musafulumire kuganiza kuti ndinu woipa ndiponso kuti simukuyenerera kukhala Mkristu. Ndipotu, Baibulo limavomereza kuti dzikoli lingakope mwamphamvu, ngakhale munthu amene akufuna kusangalatsa Mulungu.​—2 Timoteo 4:10.

3. (a) N’chifukwa chiyani n’kopanda phindu kuchita nawo zinthu za m’dzikoli? (b) Kodi Mkristu wina anafotokoza bwanji kupanda pake kochita zinthu za m’dzikoli?

3 Tsopano liyang’anitsitseni dzikoli monga mmene mungachitire ndi chovala chimene munafuna kugula. Dzifunseni kuti, ‘Kodi nsalu ya dzikoli ikuoneka bwanji nanga aisoka motani?’ Baibulo limanena kuti “dziko lapansi lipita.” (1 Yohane 2:17) Chisangalalo chilichonse chimene chingapezeke m’dzikoli ngakhale chitakhala chabwino bwanji, n’chosakhalitsa. Ndiponso, mtengo wa makhalidwe osagwirizana ndi Mulungu ndi waukulu kwambiri. Ndi woboola m’thumba. Mkristu wina amene anavutika ndi zimene iye anatcha “zopweteka zimene zinakhalapo chifukwa chogwiritsa ntchito molakwika unyamata,” anati: “Dziko lingaoneke ngati losangalatsa ndiponso lokopa. Ndipo limafuna kuti muzikhulupirira kuti mungasangalale nalo mmene mungafunire popanda zopweteka. Koma zimenezi n’zosatheka. Dziko lidzakudyerani masuku pamutu, ndipo likathana nanu, lidzakutayani.” * Nanga n’kuwonongeranji unyamata wanu mwa kuchita zinthu zosapindulitsa moyo wanu zoterozo?

Zimene Zingakutetezeni kwa “Woipayo”

4, 5. (a) Kodi Yesu atangotsala pang’ono kumwalira anapempha chiyani kwa Yehova? (b) N’chifukwa chiyani pempholi linali loyenerera?

4 Pozindikira kuti dongosolo lino la zinthu silingapereke chinthu chabwino chilichonse, achinyamata a Mboni za Yehova amayesetsa kupeŵa kupanga ubwenzi ndi dzikoli. (Yakobo 4:4) Kodi ndinu m’modzi mwa achinyamata okhulupirika oterowo? Ngati ndi choncho, muyenera kuyamikiridwa. N’zoona kuti n’zovuta kukana kuchita zimene anzanu amachita ndiponso kuoneka kuti ndinu wosiyana ndi iwo, koma thandizo lilipo.

5 Yesu atangotsala pang’ono kumwalira, anapempha Yehova kuti ‘awasunge’ ophunzira ake “kuletsa woipayo.” (Yohane 17:15) Yesu anapempha zimenezi pa chifukwa chabwino. Iye anadziŵa kuti kukhulupirika sikudzakhala kophweka kwa otsatira ake, mosasamala kanthu za usinkhu wawo. Chifukwa chiyani? Chimodzi mwa zifukwa zake n’chakuti, monga mmene Yesu ananenera, ophunzira ake anali oti adzalimbana ndi mdani wamphamvu, wosaoneka, yemwe ndi “woipayo,” Satana Mdyerekezi. Baibulo limanena kuti wolengedwa wauzimu woipa ameneyu, “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.”​—1 Petro 5:8.

6. Kodi tikudziŵa bwanji kuti Satana sachitira chifundo achinyamata?

6 Kuyambira kale, Satana amasangalala kwambri kuvutitsa anthu kwadzaoneni. Tangoganizirani mavuto aakulu zedi amene Satana anam’bweretsera Yobu ndi banja lake. (Yobu 1:13-19; 2:7) Mwina mungakumbukire zinthu zimene zachitika pa nthaŵi ya moyo wanu zimene zasonyeza mzimu wachiwawa wa Satana. Mdyerekezi, akuzembera anthu kuti awagwire, ndipo pa kufunafuna kwake kulikwira, iye sachitira chifundo achinyamata. Mwachitsanzo, kumayambiriro kwa zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, Herode anakonza zakupha ana onse aamuna ku Betelehemu amene anali ndi zaka ziŵiri kapena kucheperapo. (Mateyu 2:16) Mwachionekere, Satana ndi amene anam’chititsa Herode kuti atero, ndipo cholinga chinali chakuti awononge mwana amene tsiku lina adzakhala Mesiya wolonjezedwa wa Mulungu ndipo adzapereka chiweruzo cha Mulungu pa Satanayo. (Genesis 3:15) Inde, Satana sachitira chifundo achinyamata. Cholinga chake chenicheni n’chakuti alikwire anthu ambiri monga momwe angathere. Zimenezi akuzichita kwambiri makamaka pakalipano, chifukwa anam’chotsa kumwamba ndi kum’ponya padziko lapansi, “wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.”​—Chivumbulutso 12:9, 12.

7. (a) Kodi Yehova akusiyana kwambiri ndi Satana motani? (b) Kodi Yehova amaona bwanji kusangalala kwanu ndi moyo?

7 Mosiyana kwambiri ndi Satana yemwe ali ndi “udani waukulu,” Yehova ali ndi “mtima wachifundo.” (Luka 1:78) Iye ndiye mwini wake wa chikondi. Ndipotu, Mlengi wathu amasonyeza kwambiri khalidwe limeneli moti Baibulo limati: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Inde, pali kusiyana kwakukulu pakati pa mulungu wa dongosolo lino la zinthu ndi Mulungu amene inu muli ndi mwayi wom’lambira. Pamene Satana amafunafuna kulikwira, Yehova ‘safuna kuti ena awonongeke.’ (2 Petro 3:9) Moyo wa munthu aliyense, kuphatikizapo wanu, amauona kukhala wamtengo wapatali. Yehova akamakulangizani kudzera m’Mawu ake kuti musakhale a dziko lapansi, sikuti akufuna kukuletsani kusangalala ndi moyo wanu kapena kukusokonezerani ufulu wanu. (Yohane 15:19) M’malo mwake, iye amakusungani kuletsa woipayo. Atate wanu wakumwamba akufuna kuti mukhale ndi chinthu chabwino kwambiri kusiyana ndi zosangalatsa zakanthaŵi za dzikoli. Iye akufuna kuti mudzapeze “moyo weniweniwo,” womwe ndi moyo wosatha m’paradaiso pa dziko lapansi. (1 Timoteo 6:17-19) Yehova akufuna kuti zinthu zikuyendereni bwino, ndipo akukulimbikitsani kuti zimenezi zichitikedi. (1 Timoteo 2:4) Ndiponso, Yehova akukupemphani chinthu china chapadera. Kodi chinthu chake n’chiyani?

‘Kondweretsa Mtima Wanga’

8, 9. (a) Kodi ndi mphatso yotani imene mungapatse Yehova? (b) Kodi Satana amatonza bwanji Yehova, monga mmene zikuonekera m’nkhani ya Yobu?

8 Kodi munagulirapo mphatso mnzanu wapamtima ndiyeno n’kumuona mnzanuyo akumwetulira kwambiri chifukwa chodabwa ndiponso kusangalala atalandira mphatsoyo? Muyenera kuti munaganizira kwa nthaŵi yaitali kuti ndi mphatso yotani imene ingakhale yoyenerera kwa munthuyo. Tsopano ganizirani funso ili: Kodi ndi mphatso yotani imene mungapereke kwa Mlengi wanu, Yehova Mulungu? Poyamba, mfundo yakuti Mulungu n’kumupatsa mphatso ingaoneke yachilendo. Kodi Mulungu Wamphamvuyonse angafune chiyani kwa munthu? Kodi mungam’patse chiyani chimene iye alibe kale? Baibulo limayankha pa Miyambo 27:11 kuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.”

9 Monga muyenera kuti mukudziŵa mwa kuphunzira kwanu Baibulo, Satana Mdyerekezi ndi amene akutonza Yehova. Iye amanena kuti munthu aliyense amene amatumikira Mulungu amatero osati chifukwa cha chikondi koma chifukwa cha dyera. Iye amati ngati anthuwo atakumana ndi mavuto, mosataya nthaŵi adzasiya kulambira koona. Mwachitsanzo, taonani zimene Satana anauza Yehova za munthu wolungama, Yobu. Anati: “Kodi simunam’chinga iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pom’zinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoŵeta zake zachuluka m’dziko. Koma mutambasule dzanja lanu ndi kum’khudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pankhope panu.”​—Yobu 1:10, 11.

10. (a) Kodi tikudziŵa bwanji kuti Satana anakayikira kukhulupirika kwa anthu onse osati kwa Yobu yekha? (b) Kodi nkhani ya ulamuliro imeneyi ikukukhudzani bwanji?

10 Monga mmene zikuonekera m’nkhani ya m’Baibulo imeneyi, Satana anakayikira osati kukhulupirika kwa Yobu yekha komanso kwa ena onse amene amatumikira Mulungu, kuphatikizapo inuyo. Ndipotu, pofotokoza za anthu onse, Satana anauza Yehova kuti: “Khungu kulipa khungu, inde munthu [osati Yobu yekha koma aliyense] adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.” (Yobu 2:4) Kodi mukuona mbali yanu pankhani yofunika kwambiri imeneyi? Monga mmene lemba la Miyambo 27:11 lasonyezera, Yehova akunena kuti pali chinachake chimene mungapereke kwa iye, chimene chingathandize kuti amuyankhe nacho wotonzayo, Satana. Tangoganizani! Wolamulira wa Chilengedwe Chonse akukupemphani kuthandiza nawo poyankha nkhani yaikulu kwambiri kuposa ina iliyonse. Inde, muli ndi udindo ndiponso mwayi waukulu. Kodi mungachite zimene Yehova akukupemphani? Yobu anatero. (Yobu 2:9, 10) Yesu anateronso pamodzi ndi anthu ena ambirimbiri kuyambira kale mpaka pano, kuphatikizapo achinyamata ambiri. (Afilipi 2:8; Chivumbulutso 6:9) Inunso mungachite chimodzimodzi. Komabe, dziŵani kuti n’zosatheka kukhala opanda mbali pankhani imeneyi. Mwa zochita zanu, mudzasonyeza kuti muli ku mbali yotonza ya Satana kapena kumbali ya yankho la Yehova. Kodi mudzasankha kukhala mbali iti?

Yehova Amakusamalirani

11, 12. Kodi zimamukhudza Yehova mukasankha kum’tumikira kapena ayi? Fotokozani.

11 Kodi zimene mwasankha kuchita zimakhudza Yehova? Kodi anthu okwanira sanasonyeze kale kukhulupirika zimene zingamuthandize kumuyankha mokwanira Satana? N’zoona kuti Mdyerekezi ananena kuti palibe amene amatumikira Yehova chifukwa chomukonda, kuneneza kumene kwatsimikiziridwa kale kuti kunali kwabodza. Komabe, Yehova akufuna kuti inuyo mukhale ku mbali yake pankhani ya ulamuliroyi chifukwa amakusamalirani monga munthu panokha. Yesu anati: “Sichili chifuniro cha Atate wanu wa kumwamba kuti mmodzi wa aang’ono awa atayike.”​—Mateyu 18:14.

12 Inde, Yehova amaona zimene mwasankha kuchita. Kuposanso pamenepo, zimene mwasankhazo zimamukhudza. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti zinthu zabwino kapena zoipa zimene anthu amachita zimamukhudza kwambiri. Mwachitsanzo, pamene Aisrayeli anapanduka mobwerezabwereza, “zinam’pweteka” Yehova. (Salmo 78:40, 41, NW) Chigumula cha m’nthaŵi ya Nowa chisanachitike, pamene “kuipa kwa anthu kunali kwakukulu,” Yehova “anavutika m’mtima mwake.” (Genesis 6:5, 6) Taganizirani tanthauzo la zimenezi. Ngati mungasankhe kuchita zinthu zoipa, mudzachititsa Mlengi wanu kupwetekedwa. Zimenezi sizikutanthauza kuti Mulungu ndi wofooka kapena kutengeka maganizo kumamulamulira ayi. M’malo mwake, iye amakukondani ndipo amasamala za moyo wanu. Koma ngati muchita zabwino, mtima wa Yehova umakondwera. Amasangalala osati kokha chifukwa chakuti wapeza yankho lina kwa Satana komanso chifukwa chakuti tsopano angakhale Wokubwezerani Mphoto. Ndipo iye amafuna kuchita zimenezi. (Ahebri 11:6) Inde, Yehova Mulungu ndi Atate wanu wachikondi.

Madalitso Aakulu Pakalipano

13. Kodi kutumikira Yehova kumabweretsa bwanji madalitso ngakhale pakalipano?

13 Madalitso amene amakhalapo chifukwa chotumikira Yehova sikuti tidzalandira m’tsogolo mokha ayi. Achinyamata ambiri a Mboni za Yehova amadalitsidwa ndi chimwemwe ndiponso chisangalalo pakalipano, ndipo amatero pa chifukwa chomveka. Wamasalmo analemba kuti: “Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima.” (Salmo 19:8) Yehova amadziŵa zinthu zabwino kwa ife kuposa mmene angadziŵire munthu wina aliyense. Yehova ananena mwa mneneri Yesaya kuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”​—Yesaya 48:17, 18.

14. Kodi mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni bwanji kupeŵa kupweteka kwa ngongole?

14 Kutsatira mfundo za m’Baibulo kudzakuthandizani kupeŵa mavuto ambiri ndi chisoni chochuluka. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti amene amakonda ndalama “adzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.” (1 Timoteo 6:9, 10) Kodi ena mwa anzanu zawachitikira zinthu zopweteka monga mmene lembali likufotokozera? Anyamata ndi atsikana ena ali ndi ngongole zazikulu chifukwa chofuna kuti akhale ndi zovala zatsopano zodula ndiponso zipangizo zatsopano zapamwamba. Kulemetsedwa ndi kubweza ngongole kwa nthaŵi yaitali pa chiwongola dzanja chachikulu chifukwa cha zinthu zimene simungakwanitse kugula, ndi ukapolo wopweteka kwambiri.​—Miyambo 22:7.

15. Kodi mfundo za m’Baibulo zimakutetezani bwanji ku zopweteka zimene zimakhalapo chifukwa cha chiwerewere?

15 Taganiziraninso nkhani ya chiwerewere. Chaka chilichonse padziko lonse, atsikana aang’ono osakwatiwa amatenga mimba. Ena amabereka mwana amene safuna kumulera ndiponso sangathe kutero. Ena amataya mimba ndiyeno amakumana ndi zotsatirapo zake, kuvutika mumtima. Ndiyenso pali anyamata ndi atsikana ena amene amatenga matenda opatsirana m’njira ya chiwerewere, monga Edzi. Komanso, kwa munthu amene amadziŵa Yehova chopweteka kuposa zonsezo ndicho kuwonongeka kwa ubwenzi wake ndi Yehova. * (Agalatiya 5:19-21) N’chifukwa chake Baibulo limati: “Thaŵani dama.”​—1 Akorinto 6:18.

Kutumikira “Mulungu Wachimwemwe”

16. (a) Kodi tikudziŵa bwanji kuti Yehova amafuna kuti musangalale ndi unyamata wanu? (b) N’chifukwa chiyani Yehova amapereka malangizo oti muwatsatire?

16 Baibulo limati Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Amafuna kuti inunso mukhale wachimwemwe. Ndipotu, Mawu ake enieniwo amati: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe.” (Mlaliki 11:9) Koma Yehova amaona patali osati za pakalipano zokha ndipo amadziŵa zotsatirapo zokhalitsa za khalidwe labwino ndi loipa lomwe. N’chifukwa chake amakulangizani kuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo.”​—Mlaliki 12:1.

17, 18. Kodi Mkristu wina wachinyamata anafotokoza bwanji chimwemwe chimene ali nacho potumikira Yehova, ndipo inu mungapeze bwanji chimwemwe choterocho?

17 Masiku ano, achinyamata ambiri apeza chimwemwe chachikulu potumikira Yehova. Mwachitsanzo, Lina wa zaka 15 anati: “Ndili ndi chidaliro ndiponso ndimadziona kuti ndine wofunika. Ndili ndi thupi lathanzi chifukwa chopeŵa kusuta ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ndimalandira malangizo amtengo wapatali kumpingo amene amandithandiza kulimbana ndi zinthu zoipa za Satana. Ndimasangalala chifukwa cha macheza olimbikitsa amene amakhala ku Nyumba ya Ufumu. Ndipo choposa zonsezi, ndikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha pa dziko lapansi.”

18 Mofanana ndi Lina, Akristu achinyamata ambiri akumenyera nkhondo zolimba chikhulupiriro, ndipo zimenezi zimawabweretsera chimwemwe. Amazindikira kuti moyo wawo, ngakhale kuti nthaŵi zina umakhala wa mavuto ambiri, uli ndi cholinga chenicheni ndiponso uli ndi tsogolo lenileni. Motero, pitirizani kutumikira Mulungu amene amakufunirani zabwino. Kondweretsani mtima wake, ndipo adzakuthandizani kuti musangalale pakalipano ndiponso mpaka kalekale.​—Salmo 5:11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Onani nkhani yakuti “The Truth Gave Me Back My Life,” ya mu Galamukani! yachingelezi ya October 22, 1996.

^ ndime 15 N’zosangalatsa kudziŵa kuti munthu akalapa, kusiya kuchita zoipa ndi kuvomereza machimo ake, Yehova “adzakhululukira koposa.”​—Yesaya 55:7.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ndi ngozi yotani imene mumakumana nayo kuchokera kwa “woipayo,” Satana?

• Kodi mungakondweretse bwanji mtima wa Yehova?

• Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova amakusamalirani?

• Kodi ndi madalitso ena ati amene amapezeka chifukwa chotumikira Yehova?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 13]

Munthu Wolungama Anatsala Pang’ono Kugwa

Asafu anali woimba nyimbo wachilevi wodziŵika kwambiri pa kachisi wa Yehova kale mu Israyeli. Iye mpaka analemba nyimbo zimene anthu anali kugwiritsira ntchito polambira. Komabe, ngakhale kuti anali ndi mwayi wapadera umenewu wotumikira, nthaŵi ina Asafu anakopeka ndi khalidwe losasangalatsa Mulungu la anthu ena ofanana naye msinkhu, amene ankaoneka kuti anali kuswa malamulo a Mulungu koma osakumana ndi mavuto alionse. Kenako Asafu anavomereza kuti: “Ndikadagwa; mapazi anga akadaterereka. Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa.”​—Salmo 73:2, 3.

Ndiyeno, Asafu anapita ku kachisi wa Mulungu ndipo anapempherera nkhaniyo. Atayambanso kuona zinthu mwauzimu, iye anazindikira kuti Yehova amadana ndi zoipa ndipo kuti m’kupita kwa nthaŵi, oipa ndi olungama adzatuta zimene afesa. (Salmo 73:17-20; Agalatiya 6:7, 8) Inde, oipa ali poterera. Mapeto ake, iwo adzagwa pamene Yehova adzawononga dongosolo lino losaopa Mulungu.​—Chivumbulutso 21:8.

[Zithunzi patsamba 15]

Yehova amakufunirani zabwino pamene Satana ali ndi cholinga choti akulikwireni

[Chithunzi patsamba 16]

Achinyamata ambiri akusangalala kwambiri potumikira Yehova ndi Akristu anzawo