Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Achinyamatanu Mukupita Patsogolo Mwauzimu?

Kodi Achinyamatanu Mukupita Patsogolo Mwauzimu?

Kodi Achinyamatanu Mukupita Patsogolo Mwauzimu?

“NGAKHALE kuti ndinkapezeka pa misonkhano yachikristu, ndinalibe cholinga chotumikira Yehova ndi mtima wonse,” anatero Hideo pokumbukira nthaŵi imene anali kusekondale. “Nthaŵi zambiri ndinkadziyerekezera ndili wotchuka kwa anzanga a m’kalasi, ndikuyenda mwamatama pa msewu ndi chibwenzi changa. Ndinalibe zolinga zodziŵika, ndipo ndinalibenso cholinga chopita patsogolo mwauzimu.” Mofanana ndi Hideo, achinyamata ambiri amangokhala opanda zolinga zothandiza m’moyo ndiponso sapita patsogolo.

Ngati ndinu wachinyamata, mosakaika mumasangalala mukamachita masewero kapena zinthu zina zimene mumakonda. Koma zikakhala zinthu zauzimu, mwina simungasangalale chotero. Kodi zingatheke kusangalala ndi zinthu zauzimu? Taganizirani za mawu a wamasalmo awa: “Mboni [“zikumbutso,” NW] za Yehova ziri zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru. . . . Malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.” (Salmo 19:7, 8) Mawu a Mulungu angathandize “opusa” kuti achite zinthu mwanzeru, ‘n’kuwapenyetsa maso.’ Ndithudi, mungasangalale ndi zinthu zauzimu. Koma kodi n’chiyani chimene chikufunika kuti musangalale? Kodi mungayambire pati?

Khalani ndi Mtima Wofuna Kutumikira Mulungu

Poyamba, inuyo panokha muyenera kufunitsitsa. Taganizirani za nkhani ya Yosiya, mfumu yachinyamata ya Ayuda. Pamene buku la Chilamulo cha Yehova linapezeka m’kachisi, Yosiya ananena kuti liwerengedwe ndipo zimene anamvazo zinamukhudza mtima. Zotsatira zake n’zakuti: “Yosiya [a]nachotsa zonyansa zonse m’maiko onse okhala a ana a Israyeli.” (2 Mbiri 34:14-21, 33) Kuŵerenga Mawu a Mulungu kunam’chititsa Yosiya kuchita zambiri popititsa patsogolo kulambira koyera.

Inunso mukhoza kukulitsa mtima wofuna kutumikira Yehova ngati nthaŵi zonse muŵerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha za zimene mwaŵerenga. Zimenezo n’zimene zinalimbikitsa Hideo. Iye anayamba kucheza ndi mpainiya wachikulire, mtumiki wa nthaŵi zonse wa Mboni za Yehova. Mpainiyayo anali wophunzira Baibulo wakhama ndipo ankayesetsa kugwiritsa ntchito zimene amaphunzirazo pa moyo wake. Atalimbikitsidwa ndi chitsanzo cha mpainiyayo, Hideo anayamba kuchitanso chimodzimodzi ndipo anayamba kufunitsitsa kutumikira Mulungu komanso anthu ena. Kupita kwake patsogolo mwauzimu kunachititsa moyo wake kukhala n’cholinga.

Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kungalimbikitse achinyamata. Takahiro akufotokoza kuti: “Nthaŵi zonse pamene ndikukagona ndikakumbukira kuti tsiku limenelo sindinaŵerenge Baibulo, ndinkadzuka n’kuŵerenga kaye. Zotsatira zake n’zakuti ndinkaona kuti Yehova akunditsogolera. Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndi kumene kunandithandiza kwambiri kuti ndipite patsogolo mwauzimu. Chifukwa chakuti ndinkafunitsitsa kuchita nawo mokwanira utumiki wa Yehova, ndinayamba upainiya wa nthaŵi zonse nditangomaliza sukulu ya sekondale. Ndipo ndikusangalala nawo kwambiri.”

Kuwonjezera pa kuŵerenga Baibulo, kodi n’chiyaninso chingakulimbikitseni kutamanda Yehova? Tomohiro anaphunzitsidwa choonadi cha Baibulo ndi mayi ake. Iye anati: “Nditaphunzira mokwanira buku lakuti Life Does Have a Purpose ndili ndi zaka 19 m’pamene ndinamvetsetsa kwambiri chikondi cha Yehova ndi nsembe ya dipo ya Yesu. Kuyamikira chikondi cha Mulungu kumeneko kunandilimbikitsa kuti ndichite zambiri mu utumiki wa Yehova.” (2 Akorinto 5:14, 15) Mofanana ndi Tomohiro, achinyamata ambiri alimbikitsidwa kupita patsogolo mwauzimu chifukwa cha kuphunzira Baibulo mwakhama paokha.

Komabe, bwanji ngati pambuyo pochita zonsezi simukumvabe kuchokera pansi pamtima kuti mukufunitsitsa kutumikira Yehova? Kodi mungapite kwa ndani kuti akuthandizeni? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe . . . ndiye Mulungu.” (Afilipi 2:13) Ngati mupemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni, adzakupatsani mzimu wake woyera, umene sudzangokupatsani mphamvu zoti ‘muchite’ zokha, komanso zoti ‘mufune.’ Zimenezi zikutanthauza kuti mzimu wa Mulungu udzalimbikitsa cholinga chanu choti muchite zonse zimene mungathe mu utumiki wa Yehova ndipo udzakuthandizani kuti mukule mwauzimu. Chotero, dalirani mphamvu za Yehova ndipo limbani mtima!

Khalani ndi Zolinga Zanuzanu

Mukatsimikiza kuti mukufunitsitsa kutumikira Yehova mokwanira, muyenera kukhala ndi zolinga zanuzanu kuti mupite patsogolo mwauzimu. Mana, mtsikana wamng’ono wachikristu anati: “Chimene chinandithandiza ndi kukhala ndi zolinga. Mmalo moti ndizibwerera m’mbuyo, ndinayamba kupita patsogolo molimba mtima. Popeza ndinali ndi zolinga m’maganizo, ndinapemphera kwa Yehova kuti anditsogolere, ndipo ndinapita patsogolo popanda chododometsa.”

Zolinga zanu ziyenera kukhala zoti mukhoza kuzikwanitsadi. Kuŵerenga chaputala chimodzi cha Baibulo tsiku lililonse chikhoza kukhala cholinga chabwino. Mukhozanso kuyamba kuchita kafukufuku pa nkhani ina yake. Kuti tikupatseni chitsanzo cha m’mene mungachitire zimenezi pogwiritsa ntchito zofalitsa zimene muli nazo m’Chichewa, mukhoza kuphunzira mozama za makhalidwe anayi aakulu a Yehova amene afotokozedwa mwatsatanetsatane m’buku la Yandikirani kwa Yehova. Mosakayikira kufufuzako kudzakuthandizani kuti muyandikire kwa Yehova ndiponso kudzakuthandizani kukhala wofunitsitsa kum’chitira zambiri. Zolinga zina zimene mungakwanitse ndi kuyankha, ngakhale kamodzi kokha, pa misonkhano yachikristu imene anthu amayankhapo. Mukhozanso kudziŵana bwino ndi winawake mumpingo pa msonkhano uliwonse, ndiponso osalola kuti tsiku lingodutsa osapemphera kwa Yehova kapena kuuzako ena za iye.

Ngati simunalembetsebe mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, chimenecho chingakhalenso cholinga chanu chabwino. Kodi mwakhala mukuchita nawo ntchito yolalikira? Ngati simunayambe, mungayesetse kuti mukhale wofalitsa wosabatizidwa. Kuganizira mofatsa za ubale wanu ndi Yehova ndi kudzipatula kwa iye chingakhale cholinga chotsatira. Achinyamata ambiri amayesetsa kukhala mogwirizana ndi kudzipatulira kwawo mwa kuchita utumiki wa nthaŵi zonse.

Ngakhale kuti n’kwabwino kukhala ndi zolinga m’moyo, samalani kuti musayambe kuchita mpikisano. Mungasangalale kwambiri ndi zimene mukuchita ngati simukudziyerekezera ndi ena.​—Agalatiya 5:26; 6:4.

Mwina mukuganiza kuti simukudziŵa zambiri, ndipo zikukuvutani kukhala ndi zolinga zimene mungakwanitse. Ngati ndi choncho, tsatirani uphungu wa Baibulo wakuti: “Tchera makutu ako, numvere mawu a anzeru.” (Miyambo 22:17) Pemphani thandizo kwa makolo anu kapena Akristu ena okhwima. Koma pa nkhani imeneyi, makolo ndi ena ayenera kukhala olimbikitsa komanso omvetsa zinthu. Kukakamiza achinyamata kukwaniritsa zolinga zimene ena awaikira kungawachititse kusasangalala ndipo mmalo mowalimbikitsa, kukhoza kuwononga zolinga zawo. Zimenezi zinachitikirapo mtsikana wina, amene anati: “Makolo anga anandiikira zolinga zambiri, monga kulembetsa mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, kupita nawo mu utumiki wakumunda, kubatizidwa, ndi kukhala mpainiya. Ndinayesetsa kwambiri kuti ndikwanitse cholinga chilichonse. Ndikakwanitsa cholinga chimodzi, makolo anga sankandiyamikira, koma mmalo mwake ankandiikira cholinga china kuti ndichikwanitsenso. Zotsatira zake n’zoti ndinakakamizika kuti ndikwanitse zolingazo. Ndinatopa ndipo ndinamva ngati palibe chimene ndachita.” Kodi chinalakwika n’chiyani? Zolinga zonsezo zinali zabwino, koma sizinali zake. Kuti mupambane, inuyo muyenera kufunitsitsa panokha kudziikira zolinga!

Taganizirani za Yesu Kristu. Atabwera pa dziko lapansi, ankadziŵa zimene Atate ake, Yehova, ankafuna kuti iye achite. Kuchita chifuniro cha Yehova sichinali cholinga chabe kwa Yesu, koma ntchito imene anafunika kuikwaniritsa. Kodi Yesu anauona bwanji utumiki wake? Iye anati: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yohane 4:34) Yesu anasangalala kuchita chifuniro cha Yehova ndipo anachita zinthu mogwirizana ndi zimene Atate ake ankayembekezera. Chinali ngati chakudya kwa Yesu. Anasangalala ndi kukhutira pomaliza ntchito imene ankafunika kuigwira. (Ahebri 10:5-10 10:5-10) Nanunso mungasangalale ngati panokha muli wofunitsitsadi kuchita zimene makolo anu akukulimbikitsani.

Musaleme Pakuchita Zabwino

Mukakhala ndi cholinga mmaganizo, yesetsani kuti muchikwaniritse. Lemba la Agalatiya 6:9 limati: “Tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.” Musangodalira pa mphamvu kapena luso lanu lokha. Mosakaikira mudzakumana ndi zothetsa nzeru ndipo nthaŵi zina mungaone ngati mukulephera. Koma Baibulo limatitsimikizira kuti: “Umlemekeze [Mulungu] m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:6) Yehova adzakuthandizani pamene mukuyesetsa zolimba kuti mukwaniritse zolinga zanu zauzimu.

Inde, mwakukulitsa cholinga chotumikira Yehova ndiponso mwakukhala ndi zolinga zauzimu, mudzatha kusonyeza ‘kupita kwanu patsogolo kwa anthu onse.’ (1 Timoteo 4:15, NW) Mukatero mudzasangalala ndi moyo watanthauzo mu utumiki wa Mulungu.

[Chithunzi patsamba 9]

Kuŵerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha za zimene mwaŵerenga kungakulimbikitseni kutumikira Yehova

[Chithunzi patsamba 10]

Yesu anachita zimene Atate ake ankayembekezera