Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi pangachitidwe chinachake ngati Mkristu wodzozedwa yemwe akudwala sangathe kupezekapo pamene mpingo ukuchita mwambo wa Mgonero wa Ambuye?

Inde. Chinachake chingachitidwe ndipo chiyenera kuchitidwa posonyeza kuganizira Mkristu wodzozedwa yemwe akudwala ndipo mwina sachoka pamphasa, ndiyeno chifukwa cha zimenezi sangathe kupezekapo pamene mpingo ukuchita Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Zikatere, bungwe la akulu lingakonze kuti mkulu kapena mwamuna wina wachikristu wokhwima mwauzimu atenge mkate ndi vinyo, zizindikiro za pa Chikumbutso, kupititsa kwa wokhulupirira mnzawoyo usiku womwewo umene mwambowo wachitika, ndipo akafikitse dzuwa lisanatuluke.

Mkulu kapena mbale amene wapita kwa Mkristu wodzozedwayo angapereke ndemanga zachidule ndi kuŵerenga malemba oyenerera, koma zimenezi zingadalire mmene alili. Angatsanzire chitsanzo cha Yesu pamene anayambitsa Mgonero wa Ambuye. Mwachitsanzo, akhoza kuŵerenga Mateyu 26:26 n’kupemphera ndiyeno n’kupereka mkate wopanda chotupitsawo. Kenako, mbale amene wabweretsa zizindikiroyo angaŵerenge Mateyu chaputala 26, vesi 27 ndi 28, n’kupempheranso ndiyeno n’kupereka vinyo. Angafotokoze mwachidule zimene chizindikiro chilichonse chikuimira, ndipo ayenera kumaliza ndi pemphero.

N’zoona kuti munthu ayenera kuyesetsa mmene angathere kuti apezekepo pamene mpingo ukuchita mwambo wa Mgonero wa Ambuye. Koma kodi n’chiyani chimene Mkristu wodzozedwa amene akudwala kwambiri, ali kuchipatala, kapena ali ndi vuto lina lake angachite ngati kutakhala kovutitsitsa kuti achite Chikumbutso dzuŵa litaloŵa pa Nisani 14? Wodzozedwa woteroyo angatsatire zimene zinkachitika m’Chilamulo cha Mose ndipo angachite mwambowo payekha patapita masiku 30.​—Numeri 9:9-14.