Kondani Phunziro Laumwini la Mawu a Mulungu
Kondani Phunziro Laumwini la Mawu a Mulungu
“Ndidzalingalira [“Ndidzasinkhasinkha,” NW] ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.”—SALMO 77:12.
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kupatula nthaŵi yosinkhasinkha? (b) Kodi ‘kusinkhasinkha’ kumatanthauza chiyani?
IFE monga ophunzira a Yesu Kristu, tiyenera kudera nkhaŵa kwambiri ubale wathu ndi Mulungu ndi zolinga zathu pom’tumikira. Komabe, masiku ano anthu ambiri amakhala otanganidwa kwambiri moti sapatula nthaŵi yosinkhasinkha. Atengeka kwambiri ndi kukondetsa chuma, kutanganidwa ndi zogulagula, ndiponso kukonda zosangalatsa zopanda pake. Kodi tingatani kuti tipeŵe kuchita zinthu zosapindulitsa ngati zimenezi? Monga mmene timapatulira nthaŵi yeniyeni yochitira zinthu zina zofunika kwambiri monga kudya ndi kugona, tiyeneranso kupeza nthaŵi tsiku lililonse yosinkhasinkha zimene Yehova amachita.—Deuteronomo 8:3; Mateyu 4:4.
2 Kodi mumakhala pansi n’kusinkhasinkha? Kodi kusinkhasinkha n’kutani? Kusinkhasinkha kumatanthauza kuganizira mozama zimene taphunzira poŵerenga kapena kumva. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani kwa ife?
3. Kodi kupita patsogolo mwauzimu kukugwirizana kwambiri ndi chiyani?
3 Mwa zina, zimenezi ziyenera kutikumbutsa zimene mtumwi Paulo analembera mtumiki mnzake Timoteo kuti: “Kufikira ndidza ine, usamalire kuŵerenga, kuchenjeza, kulangiza. . . . Izi uzisamalitse [“uzisinkhesinkhe,” NW]; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako [“kupita kwako patsogolo,” NW] kuonekere kwa onse.” Inde, iye anafunika kupita patsogolo, ndipo mawu a Paulo anasonyeza kuti panali kugwirizana kwambiri pakati pa kusinkhasinkha zinthu zauzimu ndi kupita patsogolo. N’chimodzimodzinso masiku ano. Kuti tipindule ndi kupita patsogolo, tiyenera kupitiriza ‘kusinkhasinkha’ ndi ‘kukhala’ m’zimene Mawu a Mulungu amafotokoza.—1 Timoteo 4:13-15.
4. Kodi ndi zida ziti zimene mungagwiritse ntchito kuti zikuthandizeni kusinkhasinkha Mawu a Yehova nthaŵi zonse?
4 Nthaŵi yanu yabwino yosinkhasinkha imadalira inu ndi zimene banja lanu limachita nthaŵi zonse. Ambiri amasinkhasinkha lemba la m’Baibulo kum’maŵa pamene amaŵerenga m’kabuku kakuti Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Ndipotu, antchito odzipereka pafupifupi 20,000 a pa Beteli pa dziko lonse amayamba tsiku mwa kukambirana lemba la m’Baibulo la tsikulo kwa mphindi 15. Ngakhale kuti m’maŵa uliwonse a m’banja la Beteli amene amapereka ndemanga ndi ochepa, ena onse amasinkhasinkha zimene enawo akufotokoza ndi kuŵerenga. Mboni zina zimasinkhasinkha Mawu a Yehova popita kuntchito. Zimamvera makaseti a Baibulo ndiponso a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zimene zimapezeka m’zinenero zina. Akazi ambiri amene amakhala pakhomo amachita zimenezi akamagwira ntchito zapakhomo. Inde, iwo amatsanzira wamasalmo Asafu, amene analemba kuti: “Ndidzakumbukira zimene adazichita Ambuye; inde, ndidzakumbukira Salmo 77:11, 12.
zodabwitsa zanu zoyambira kale. Ndipo ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.”—Kukhala ndi Maganizo Abwino Kumapindulitsa
5. N’chifukwa chiyani phunziro laumwini liyenera kukhala lofunika kwambiri kwa ife?
5 M’nyengo yathu ino ya ma TV, mavidiyo, ndi makompyuta, anthu ambiri saŵerenga kwambiri monga zinalili kale. Mboni za Yehova siziyenera kutero. Ndipotu, kuŵerenga Baibulo kuli ngati njira ya kumoyo imene imatifikitsa kwa Yehova. Zaka zambirimbiri zapitazo, Yoswa analoŵa m’malo mwa Mose kukhala mtsogoleri wa Israyeli. Kuti Yehova amudalitse, Yoswa anafunika kudziŵerengera yekha Mawu a Mulungu. (Yoswa 1:8; Salmo 1:1, 2) Masiku anonso tifunika kuchita zimenezi. Komabe, ena chifukwa cha kusaphunzira kwambiri, amavutika kuŵerenga ndiponso amaona kuti n’kotopetsa. Motero, kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizifuna kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu? Yankho lake tingalipeze m’mawu a Mfumu Solomo amene ali pa Miyambo 2:1-6. Tatsegulani Baibulo lanu ndi kuŵerenga mavesi ameneŵa. Ndiyeno tikambirana pamodzi.
6. Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani pankhani ya kudziŵa za Mulungu?
6 Poyamba, tikupeza langizo lakuti: “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; . . . ” (Miyambo 2:1, 2) Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu ameneŵa? Tikuphunzira kuti tonsefe, aliyense payekha, tili ndi udindo wophunzira Mawu a Mulungu. Onani mawuwo akuti “ukalandira mawu anga.” Zimenezi zikutanthauza kuti munthu adzafunika kuchitapo kanthu chifukwa si anthu onse amene amaganizira za Mawu a Mulungu. Kuti tikonde kuŵerenga Mawu a Mulungu, tiyenera kufunitsitsa kulandira mawu a Yehova ndi kuwaona monga chuma chimene sitifuna kuti chititayike. Sitiyenera kulola kuti zochita zathu za tsiku ndi tsiku zititangwanitse kwambiri kapena kutipatutsa moti n’kuyamba kunyalanyaza Mawu a Mulungu, kapena kuwakayikira kumene.—Aroma 3:3, 4.
7. N’chifukwa chiyani tiyenera kupezeka ndi kutchera khutu pa misonkhano yachikristu ngati n’kotheka?
7 Kodi ‘timatcheradi makutu’ ndi kumvetsera mosamala Mawu a Mulungu akamafotokozedwa pa misonkhano yathu yachikristu? (Aefeso 4:20, 21) Kodi ‘timalozetsa mtima’ wathu kuti tizindikire? Mwina wokambayo angakhale woti si waluso kwambiri, koma pamene akufotokoza Mawu a Mulungu, iye ndi woyenerera kumumvetsera mosamalitsa. Inde, kuti titchere khutu ku nzeru za Yehova, tiyenera kupezeka pa misonkhano yachikristu ngati n’kotheka. (Miyambo 18:1) Tangoganizani mmene aliyense amene ayenera kuti sanakhale nawo pa msonkhano wa m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu pa Pentekoste wa 33 C.E. anakhumudwira! Ngakhale kuti misonkhano yathu si yapadera monga mmene unalili msonkhano umenewo, buku lathu lalikulu lophunzirira, Baibulo, limafotokozedwa pa misonkhanoyi. Motero, msonkhano uliwonse ungatipindulitse mwauzimu ngati titchera khutu ndi kumaŵerenga nawo m’mabaibulo athu.—Machitidwe 2:1-4; Ahebri 10:24, 25.
8, 9. (a) Kodi phunziro laumwini limafuna kuti tizitani? (b) Kodi mtengo wa golidi mungauyerekezere bwanji ndi kumvetsa ndiponso kudziŵa za Mulungu?
8 Mawu otsatira a mfumu yanzeruyo akuti: “Ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; . . . ” (Miyambo 2:3) Kodi mawu ameneŵa akutisonyeza maganizo otani? Akutisonyeza maganizo ofunitsitsa kumvetsa Mawu a Yehova. Akusonyeza kuti tiyenera kufuna kuphunzira n’cholinga choti tikhale ozindikira, kuti tidziŵe chifuniro cha Yehova. Izi mosakayika zimafuna khama, ndipo zikutifikitsa pa mawu otsatira a Solomo pamodzi ndi fanizo lake.—Aefeso 5:15-17.
9 Iye akupitiriza kuti: ‘Ukafunafuna [luntha] ngati siliva, ndi kulipwaira ngati chuma chobisika; . . . ’ (Miyambo 2:4) Zimenezi zikutichititsa kuganiza za ntchito za migodi za amuna amene kwa zaka zambiri akhala akufunafuna siliva ndi golidi, miyala imene amati ndi yamtengo wapatali. Anthu aphana chifukwa cha golidi. Ena akhala akufunafuna golidi moyo wawo wonse. Koma kodi golidi ali ndi mtengo wotani? Ngati mutasochera m’chipululu ndipo mwatsala pang’ono kufa ndi ludzu, kodi mungakonde chiyani: golidi kapena madzi? Komatu, anthu afunafuna golidi mwakhama kwambiri, ngakhale kuti mtengo wake ndi wosakhalitsa ndiponso umasinthasintha! * Kuli bwanji nanga kufunafuna nzeru, kuzindikira, ndi kufuna kumvetsa za Mulungu ndi chifuniro chake! Inde, tiyenera kuchita zimenezo mwakhama kwambiri. Koma kodi tingapindule chiyani ndi kufufuza koteroko?—Salmo 19:7-10; Miyambo 3:13-18.
10. Kodi tingadziŵe chiyani ngati tiphunzira Mawu a Mulungu?
10 Solomo akupitiriza kufotokoza kuti: “Pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziŵadi Mulungu.” (Miyambo 2:5) Ndi mfundo yochititsa chidwitu imeneyi, mfundo yakuti ife anthu ochimwa ‘tingam’dziŵedi Mulungu,’ Yehova, Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse! (Salmo 73:28; Machitidwe 4:24) Afilosofi ndi ena amene amatchedwa anthu anzeru a dzikoli ayesetsa kwa zaka zambirimbiri kuti amvetse nkhani zovuta kumva zokhudza moyo ndiponso chilengedwe. Koma iwo alephera “kum’dziŵadi Mulungu.” Chifukwa chiyani? Ngakhale kuti chidziŵitso cha Mulungu chakhala chilipo kwa zaka zambirimbiri m’Mawu a Mulungu, Baibulo, iwo achikana n’kumati sichinafotokozedwe mozama ndipo motero amalephera kuvomereza ndi kuchimvetsa.—1 Akorinto 1:18-21.
11. Kodi timapindula chiyani ndi phunziro laumwini?
11 Solomo akufotokozanso mfundo ina yakuti: “Yehova apatsa nzeru; kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.” (Miyambo 2:6) Yehova amapatsa nzeru, chidziŵitso, ndi kuzindikira mwaufulu ndiponso moolowa manja kwa aliyense amene akufunafuna zinthu zimenezi. Inde, tili ndi zifukwa zokwanira zokondera phunziro laumwini la Mawu a Mulungu, ngakhale ngati zimenezo zitafuna kuti tichite khama, kudziletsa, ndiponso kudzipereka. Ndipotu ife tili ndi mabaibulo osindikizidwa kale ndipo sitifunika kuchita kukopera pamanja tokha monga ankachitira ena kale!—Deuteronomo 17:18, 19.
Kuyenda Moyenera Yehova
12. Kodi cholinga chathu pofuna kum’dziŵadi Mulungu chiyenera kukhala chiyani?
12 Kodi cholinga chathu pochita phunziro laumwini chizikhala chotani? Kodi ndicho kuti tioneke ngati abwinopo kusiyana ndi ena? Kapena Mateyu 11:28-30) Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Chidziŵitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.” (1 Akorinto 8:1) Motero, tiyenera kukhala ndi mtima wodzichepetsa wonga umene Mose anasonyeza pamene anauza Yehova kuti: “Mundidziŵitsetu njira zanu, kuti ndikudziŵeni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu.” (Eksodo 33:13) Inde, tizifuna kupeza chidziŵitso n’cholinga chosangalatsa Mulungu, osati n’cholinga chogometsa anthu. Tifunika kukhala atumiki a Mulungu oyenera ndiponso odzichepetsa. Kodi tingakwanitse bwanji zimenezo?
kuti tisonyeze kuti timadziŵa zambiri? Kapenanso kuti tikhale anthu odziŵa kwambiri Baibulo? Ayi. Cholinga chathu n’chakuti tizichita zinthu monga Akristu, kukhala okonzeka nthaŵi zonse kuthandiza ena, kuwapatsa mpumulo monga anachitira Kristu. (13. Kodi n’chiyani chikufunika kuti munthu akhale mtumiki wa Mulungu woyenerera?
13 Paulo analangiza Timoteo mmene angakondweretsere Mulungu. Anati: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.” (2 Timoteo 2:15) Mawu akuti “wolunjika nawo bwino” akuchokera ku verebu lachigiriki lokhala ndi mawu angapo limene poyambirira linkatanthauza “kudula mosakhotetsa.” (Kingdom Interlinear) Anthu ena amati mawu ameneŵa amasonyeza ganizo la telala akudula nsalu motsatira sitayelo yake, kapena mlimi akulima mizere m’munda mwake, ndi zina zotero. M’mbali zonsezi, zimene achite pomaliza pake siziyenera kukhala zokhotakhota. Mfundo ndi yakuti, Timoteo kuti akhale mtumiki wa Mulungu woyenera ndiponso wovomerezeka anafunika ‘kuchita changu,’ kuonetsetsa kuti zimene anali kuphunzitsa ndiponso khalidwe lake zinali zogwirizana ndi mawu a choonadi.—1 Timoteo 4:16.
14. Kodi phunziro lathu laumwini liyenera kukhudza bwanji zimene timachita ndi kulankhula?
14 Paulo anafotokozanso mfundo yomweyi pamene analimbikitsa Akristu a ku Kolose ‘kuti ayende moyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo,’ mwa “kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m’chizindikiritso cha Mulungu.” (Akolose 1:10) Pano Paulo akugwirizanitsa kukhala woyenera kwa Ambuye ndi “kubala zipatso m’ntchito yonse yabwino” ndiponso “kukula m’chizindikiritso cha Mulungu.” M’mawu ena, zimene Yehova amaona kuti n’zofunika si kuyamikira kwathu chidziŵitso kokha ayi komanso kutsatira kwathu kwambiri Mawu a Mulungu pa zimene timachita ndi zimene timalankhula. (Aroma 2:21, 22) Zimenezi zikutanthauza kuti phunziro lathu laumwini liyenera kukhudza mmene timaganizira ndi khalidwe lathu ngati tikufuna kusangalatsa Mulungu.
15. Kodi tingatani kuti titeteze ndi kulamulira maganizo athu?
15 Masiku ano, Satana ndi wotanganidwa kuti awononge moyo wathu wauzimu mwa kulimbikitsa nkhondo ya maganizo. (Aroma 7:14-25) Motero, tiyenera kuteteza ndi kulamulira maganizo athu kuti tikhale oyenera kwa Mulungu wathu, Yehova. Chida chimene tili nacho ndicho “chidziŵitso cha Mulungu” chimene chingathe “kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu.” Chimenechi ndi chifukwa chachikulu choikira maganizo pa phunziro la Baibulo la tsiku ndi tsiku, popeza tikufuna kuti tipeŵe kuganizira zinthu zadyera, zopanda pake.—2 Akorinto 10:5.
Zothandizira Kumvetsa
16. Kodi tingapindule bwanji Yehova akamatiphunzitsa?
16 Zimene Yehova amaphunzitsa zimapindulitsa Yesaya 48:17) Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuyenda m’njira yake yopindulitsa? Choyamba, tili ndi Mawu ake ouziridwa, Baibulo Lopatulika. Limeneli ndi buku lalikulu lophunzirira limene timaligwiritsa ntchito nthaŵi zonse. N’chifukwa chake n’koyenera kutchera khutu pa misonkhano yachikristu titatsegula Baibulo lathu. Phindu lochita zimenezo tingalione m’nkhani ya mdindo wa ku Aitiopiya, imene ili pa Machitidwe chaputala 8.
mwauzimu ndiponso mwakuthupi. Sindizo maphunziro aumulungu osasangalatsa kapena opanda phindu lenileni. N’chifukwa chake timaŵerenga kuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.” (17. N’chiyani chinachitika pa nkhani ya mdindo wa ku Aitiopiya, ndipo zimenezi zikusonyeza chiyani?
17 Mdindo wa ku Aitiopiya anali wotembenukira ku Chiyuda. Anali kukhulupirira kwambiri Mulungu, ndipo anaphunzira Malemba. Iye, akuyenda mu galeta wake, anali kuŵerenga lemba la Yesaya, pamene Filipo anamuthamangira ndi kum’funsa kuti: “Kodi muzindikira chimene muŵerenga?” Kodi mdindoyo anayankha kuti chiyani? Anayankha kuti: “Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? Ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye.” Ndiyeno Filipo, motsogoleredwa ndi mzimu woyera, anathandiza mdindoyo kumvetsa ulosi wa Yesaya. (Machitidwe 8:27-35) Kodi zimenezi zikusonyeza chiyani? Zikusonyeza kuti kuŵerenga kwathu Baibulo patokha n’kosakwanira. Yehova, mwa mzimu wake, amagwiritsa ntchito gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kutithandiza kumvetsa Mawu ake panthaŵi yoyenera. Kodi amachita bwanji zimenezi?—Mateyu 24:45-47; Luka 12:42.
18. Kodi gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru limatithandiza bwanji?
18 Ngakhale kuti gulu la kapolo alifokoza kuti ndi ‘lokhulupirika ndi lanzeru,’ Yesu sananene kuti ilo silingalakwitse. Gulu la abale odzozedwa okhulupirika limeneli lapangidwabe ndi Akristu opanda ungwiro. Ngakhale ali ndi zolinga zabwino motani, iwo angalakwitse, monganso mmene amuna otereŵa nthaŵi zina anachitira m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino. (Machitidwe 10:9-15; Agalatiya 2:8, 11-14) Komabe, zolinga zawo n’zabwino, ndipo Yehova akuwagwiritsa ntchito kutigaŵira zothandizira kuphunzira Baibulo kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu m’Mawu a Mulungu ndi malonjezo ake. Chida chachikulu chogwiritsa ntchito pa phunziro laumwini chimene kapoloyo watipatsa ndicho Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures. Panopa tsopano likupezeka lonse kapena mbali yake m’zinenero 42, ndipo lasindikizidwa makope osiyanasiyana okwana 114 miliyoni. Kodi tingaligwiritse ntchito bwanji mogwira mtima pa phunziro lathu laumwini?—2 Timoteo 3:14-17.
19. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zili m’Baibulo la New World Translation—With References zimene zingakuthandizeni pa phunziro laumwini?
19 Mwachitsanzo, taonani mmene Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures—With References lilili. Lili ndi madanga a maumboni a malemba, mawu a mmunsi, mlozera Salmo 149:1-9; Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10.
mawu wachidule wotchedwa “Bible Words Indexed” ndi “Footnote Words Indexed,” ndiponso Mawu Owonjezera amene amafotokoza mwatsatanetsatane nkhani zokwana 43, kuphatikizapo mapu ndi matchati. Mulinso “Mawu Oyamba” amene amafotokoza magwero osiyanasiyana amene anawagwiritsa ntchito potembenuza Baibulo lapadera limeneli. Ngati lili m’chinenero chimene mumatha kumva, yesetsani kuzoloŵera mbali zimene tazifotokozazi ndi kuzigwiritsa ntchito. Mulimonse mmene zingakhalire, Baibulo ndiye poyambira pulogalamu yathu yophunzira, ndipo Baibulo la New World Translation limatsindika moyenera dzina la Mulungu pamene limasonyeza ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.—20. Kodi ndi mafunso ati okhudza phunziro laumwini amene tsopano akufunika kuwayankha?
20 Tsopano tingafunse kuti: ‘Kodi timafunikiranso thandizo lina liti kuti timvetse Baibulo? Kodi tingapeze bwanji nthaŵi yochita phunziro laumwini? Kodi tingatani kuti kuphunzira kwathu kukhale kogwira mtima? Kodi kuphunzira kwathu kuyenera kukhudza bwanji ena?’ Nkhani yotsatirayi idzapenda mbali zofunika kwambiri zimenezi za kupita kwathu patsogolo kwachikristu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Kuyambira mu 1979 mtengo wa golidi wakhala ukusinthasintha. Mu 1980, mtengo wa golidi unali madola 850 pa magalamu 31 alionse koma mu 1999 mtengowu unatsika n’kufika pa madola 252.80 pa magalamu 31 alionse.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi ‘kusinkhasinkha’ n’kutani?
• Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani pankhani yophunzira Mawu a Mulungu?
• Kodi tiyenera kukhala ndi zolinga zotani pochita phunziro laumwini?
• Kodi tili ndi zinthu ziti zimene zingatithandize kumvetsa Baibulo?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 15]
A m’banja la Beteli amaona kuti zimawalimbikitsa kwambiri mwauzimu kuyamba tsiku lililonse mwa kukambirana lemba la m’Baibulo
[Zithunzi patsamba 15]
Nthaŵi ya mtengo wapatali ingagwiritsidwe ntchito mwa kumvetsera matepi a Baibulo pamene tili paulendo
[Chithunzi patsamba 16]
Amuna ankagwira ntchito mwamphamvu ndiponso kwa nthaŵi yaitali kuti apeze golidi. Kodi mumachita khama kwambiri kuphunzira Mawu a Mulungu?
[Mawu a Chithunzi]
Mwa chilolezo cha California State Parks, 2002
[Zithunzi patsamba 17]
Baibulo ndi chuma chimene chingatithandize kukapeza moyo wosatha