Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tonsefe Timafuna Kuyamikiridwa

Tonsefe Timafuna Kuyamikiridwa

Tonsefe Timafuna Kuyamikiridwa

PATSIKULO zinthu zinali zitamuyendera bwino kwambiri mwana wamkazi. Ngakhale kuti nthaŵi zina ankafunika kudzudzulidwa, patsikuli, anasonyeza khalidwe labwino kwambiri. Koma usiku umenewo, mwanayo atakam’goneka, amayi ake anamumva akulira. Atam’funsa chimene chavuta, iye anafunsa, kwinaku akugwetsa misozi, kuti: “Kodi lero sindinali mwana wabwino?”

Funso limenelo linawakhudza kwambiri mayiwo. Nthaŵi zonse sankachedwa kum’dzudzula akalakwa. Komano patsikuli, ngakhale kuti anaona kuti mwanayo wayesetsa kusonyeza khalidwe labwino, mayiwo sanamuyamikire ngakhale pang’ono.

Sikuti ndi ana aakazi okha amene amafuna kuyamikiridwa ndi kulimbikitsidwa. Tonsefe timafuna kuyamikiridwa ndi kulimbikitsidwa monganso mmene timafunira kuti ena atilangize ndi kutiwongolera tikalakwitsa.

Timamva bwanji munthu akatiyamikira mochokera pansi pa mtima? Kodi sizitisangalatsa ndi kutilimbikitsa? Mwachionekere timamva kuti winawake waona zomwe tachita ndipo amatiganizira. Wina akatiyamikira zimatitsimizira kuti tachita zinthu zaphindu, ndipo zimatilimbikitsa kuti tidzalimbikirenso m’tsogolo. N’zosadabwitsa kuti nthaŵi zambiri, wina akatiyamikira mochokera pansi pa mtima, timakopeka ndi munthu woteroyo amene wapatula nthaŵi kuti atiuze zinazake zolimbikitsa.​—Miyambo 15:23.

Yesu Kristu anadziŵa za kufunika koyamikira anthu ena. M’fanizo la matalente, mbuye (amene akuimira Yesu mwiniwakeyo) anayamikira aliyense wa akapolo aŵiri okhulupirika. Anawayamikira mwa kuwauza kuti: “Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika.” Ndi zolimbikitsatu zimenezi! Ngakhale kuti aliyense wa akapolowo anali ndi luso losiyana kwambiri ndi la mnzake komanso anachita zinthu zosiyanasiyana, onse anawayamikira mofanana.​—Mateyu 25:19-23.

Chotero tiyeni tikumbukire mayi wa mwana uja. Tisayembekezere kuti ena achite kulira tisanawayamikire. M’malo mwake, tingakonze zoti tizifufuza mipata yoti tiyamikirire anthu ena. Inde, tili ndi zifukwa zomveka zoyamikirira ena mochokera pansi pa mtima tikapeza mwayi wotero.