N’chifukwa Chiyani Kupepesa Kumavuta?
N’chifukwa Chiyani Kupepesa Kumavuta?
MU July 2000, gulu lopanga malamulo ku California, m’dziko la United States linavomereza lamulo loti munthu azikhala wopanda mlandu ngati wapepesa kwa munthu yemwe wavulala pangozi imene yachitika ali limodzi. N’chifukwa chiyani anavomereza lamuloli? Anali ataona kuti nthaŵi zambiri anthu sapepesa, munthu akavulala kapena zinthu zikawonongeka pangozi, poopa kuti ku khoti angakaoneke kuti anavomera mlandu. Komanso, anthu amene akuganiza kuti akufunika kupepesedwa mofulumira angathe kukalipa, ndipo ngozi ing’onong’ono ingathe kukhala mkangano waukulu.
Ndi zoona kuti m’posafunika kupepesa chifukwa cha ngozi imene mwachititsa si inu. Ndipo nthaŵi zina kungakhale kwanzeru kusamala ndi zimene mukulankhula. Mwambi wina wakale umati: “Pochuluka mawu zolakwa sizisoŵeka; koma wokhala chete achita mwanzeru.” (Miyambo 10:19; 27:12) Komabe mungathe kusonyeza ulemu ndiponso kuthandizapo.
Koma kodi si zoona kuti anthu ambiri asiya kupepesa, ngakhale pa zinthu zoti sizingakhudze a khoti? Panyumba, mkazi
angadandaule kuti, ‘Mwamuna wanga sapepesa ngakhale pang’ono.’ Pantchito, kapitawo angadandaule kuti, ‘Antchito anga savomereza kulakwa kwawo, ndipo nthaŵi zambiri sapepesa n’komwe.’ Ku sukulu, mphunzitsi anganene kuti, ‘Ana sakuphunzitsidwa kunena kuti pepani, ndikhululukireni.’Chifukwa chimodzi chimene anthu sapepesera chingakhale chakuti amaopa kuti sawamvera. Mwina munthu sangafotokoze zakukhosi kwake povutika ndi maganizo akuti mwina samukomera mtima. Ndipo munthu amene walakwiridwayo angathe kupeweratu munthu womulakwirayo, zimene zingapangitse kuti kukhale kovuta kuti anthuwo agwirizanenso.
Chifukwa chinanso chimene ena sapepesera chingakhale kusaganizira mmene anthu ena akumvera. Mwina anganene kuti, ‘Kupepesa sikudzakonza chinthu chimene ndalakwitsa kale.’ Pali anthu enanso amene sapepesa polingalira zimene zingachitike. Amasinkhasinkha kuti, ‘Kodi ndidzaoneka wolakwa ndi kuuzidwa kuti ndipereke chipukuta misozi?’ Komabe chinthu chachikulu cholepheretsa munthu kuvomera kuti walakwa ndicho kunyada. Munthu wonyada kwambiri amene sanganene kuti “Pepani” angakhale akuganiza kuti, ‘Sindikufuna kuoneka wofooka mwa kuvomera cholakwa changa. Zimenezi zingachepetse ulemu umene anthu amandipatsa.’
Pangakhale zifukwa zosiyanasiyana zolepheretsa anthu ambiri kunena mawu opepesa. Koma kodi kupepesa n’kofunikadi? Kodi kuli ndi phindu lotani?
[Chithunzi patsamba 3]
“Ana sakuphunzitsidwa kunena kuti pepani, ndikhululukireni”
[Chithunzi patsamba 3]
“Mwamuna wanga sapepesa n’komwe”
[Chithunzi patsamba 3]
“Antchito anga savomereza kulakwa kwawo”