“Chipulumutso N’cha Yehova”
“Chipulumutso N’cha Yehova”
M’DZIKO mukakhala mavuto ndiponso pakakhala kusamvana pakati pa mayiko, anthu amadalira boma lawo kuti liwateteze. Nalo bomalo limakonza mapulogalamu olimbikitsa anthu kuti akhale kumbali yake. Mapulogalamu amenewo amalimbikitsa kwambiri mzimu wokonda dziko lako ndipo zimenezi zimalimbikitsa kuchita miyambo yosonyeza kukonda dziko.
M’dziko mukagwa vuto mwadzidzidzi, kukonda kwambiri dziko lawo nthaŵi zambiri kumachititsa anthu kukhala ogwirizana ndiponso amphamvu ndipo kungalimbikitse mtima wogwirira ntchito limodzi ndi woganizirana. Komabe, nkhani ina mu magazini ya The New York Times, inati: “Kukondetsa dziko lako kungayambitse mavuto” popeza “kukangolekereredwa anthu angakusonyeze molakwika.” Kusonyeza kukonda dziko lako kungasinthe n’kusokoneza ufulu wa anthu ndiponso ufulu wachipembedzo wa nzika zina za m’dzikolo. Makamaka Akristu oona amakumana ndi vuto lakuti aswe zikhulupiriro zawo. Kodi amatani zimenezi zikabuka m’dziko limene iwo akukhala? Kodi ndi mfundo za m’Malemba ziti zimene zimawathandiza kuchita mwanzeru ndi kukhulupirikabe kwa Mulungu?
“Usazipembedzere Izo”
Nthaŵi zina, anthu amachitira sawatcha mbendera posonyeza kukonda kwambiri dziko lawo. Koma nthaŵi zambiri, pa mbendera pamakhala zifanizo za zinthu zakumwamba, monga nyenyezi, pamodzinso ndi zinthu zapadziko lapansi. Mulungu anafotokoza mmene amaonera kupembedza zinthu zimenezo pamene analamula anthu ake kuti: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje [“amene ndimafuna kundilambira ine ndekha,” NW].”—Eksodo 20:4, 5.
Kodi kuchitira sawatcha mbendera imene ikuimira Boma kapena kuigwadira kumatsutsanadi ndi lamulo la Yehova Mulungu lomulambira iye yekha? N’zoona kuti Aisrayeli akale anali ndi ‘zizindikiro,’ zimene mafuko okhala m’magulu amafuko atatuatatu anali kusonkhanirapo ali m’chipululu. (Numeri 2:1, 2) Pofotokoza za mawu a Chihebri a zizindikiro zoterozo, buku laumboni la McClintock ndi Strong limati: “Koma mawu amenewo sanali kutanthauza mmene timadziŵira ‘chizindikiro’ cha mbendera.” Ndiponso, zizindikiro za Aisrayeli sanali kuzitenga ngati zopatulika, ndipo panalibe mwambo uliwonse umene unkachitika pozigwiritsa ntchito. Zinkagwira ntchito monga zizindikiro chabe, kuwasonyeza anthu malo oti asonkhane.
Zizindikiro za akerubi m’chihema ndi m’kachisi wa Solomo kwenikweni zinangosonyeza chithunzi cha akerubi akumwamba. (Eksodo 25:18; 26:1, 31, 33; 1 Mafumu 6:23, 28, 29; Ahebri 9:23, 24) Umboni wakuti zizindikiro zimenezi sanayenere kuzilambira ndi woti anthu ambiri sanali kuziona, ndipotu angelo sayenera kulambiridwa.—Akolose 2:18; Chivumbulutso 19:10; 22:8, 9.
Taganizaninso za chifanizo cha njoka ya mkuwa chimene mneneri Mose anapanga Aisrayeli ali m’chipululu. Chifanizo chimenecho Numeri 21:4-9; Yohane 3:14, 15) Sanali kuchilemekeza kapena kuchilambira. Komabe, patapita zaka zambiri Mose atamwalira, Aisrayeli analakwitsa n’kuyamba kulambira chizindikiro chimenecho, mpaka kufika pochifukizira zonunkhira. Motero, Hezekiya mfumu ya Yuda anachiphwanya.—2 Mafumu 18:1-4.
chinali chizindikiro chabe ndiponso chinapereka ulosi. (Kodi mbendera za dziko zangokhala zizindikiro chabe zimene zimagwira ntchito ina yake yothandiza? Kodi zimaimira chiyani? Wolemba mabuku wina, J. Paul Williams anati: “Posonyeza kukonda dziko lako, mbendera ndiyo chizindikiro chachikulu cha chikhulupiriro ndipo ndi imene imagwiritsidwa ntchito kwambiri polambira.” Buku lakuti The Encyclopedia Americana limati: “Mbendera ndi yopatulika monga mmene ulili mtanda.” Mbendera imaimira boma. Motero, kuigwadira kapena kuichitira sawatcha ndiwo mwambo wachipembedzo wolemekeza Boma. Kuchita zimenezi kumasonyeza kulitenga boma kukhala mpulumutsi ndipo sizigwirizana ndi zimene Baibulo limanena pankhani ya kulambira mafano.
Malemba amanena mosapita m’mbali kuti: “Chipulumutso n’cha Yehova.” (Salmo 3:8) Mabungwe a anthu kapena zizindikiro zawo sizingapulumutse. Mtumwi Paulo analangiza Akristu anzake kuti: “Okondedwa anga, thaŵani kupembedza mafano.” (1 Akorinto 10:14) Akristu oyambirira sanali kuchita nawo zina zilizonse zokhudza kulambira Boma. M’buku lakuti Those About to Die, Daniel P. Mannix anati: “Akristu anakana . . . kupereka nsembe kwa mzimu wa mfumu [ya Roma]—zomwe zikufanana ndi kukana kuchitira sawatcha mbendera masiku ano.” Ndi mmene Akristu oona akuchitira masiku ano. Pofuna kulambira Yehova yekha, amapeŵa kuchitira sawatcha mbendera ya dziko lililonse. Mwakuchita zimenezi, amaika Mulungu patsogolo komabe amalemekeza maboma ndi olamulira ake. Inde, amadziŵa kuti ali ndi udindo womvera “maulamuliro aakulu” a boma. (Aroma 13:1-7) Nanga kodi Malemba amati chiyani pankhani yoimba nyimbo zosonyeza kukonda kwambiri dziko lako, monga ngati nyimbo za fuko?
Kodi Nyimbo za Fuko N’chiyani?
“Nyimbo za fuko ndi nyimbo zosonyeza kukonda kwambiri dziko lako ndipo nthaŵi zambiri m’nyimbozo anthu amapempha Mulungu kuti awatsogolere ndi kuwateteza anthuwo kapena olamulira awo,” limatero buku lakuti The Encyclopedia Americana. Kunena zoona, nyimbo ya fuko ndi nyimbo yotamanda Mulungu kapena yopempherera dziko. Nthaŵi zonse nyimboyi imapempha kuti zinthu ziziyenda bwino m’dziko ndiponso kuti likhale kwa nthaŵi yaitali. Kodi Akristu ayenera kuchita nawo mapemphero oterowo?
Mneneri Yeremiya ankakhala pakati pa anthu amene ankati amatumikira Mulungu. Koma Yehova anamulamula kuti: “Iwe usapempherere anthu aŵa, usawakwezere iwo mfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe.” (Yeremiya 7:16; 11:14; 14:11) N’chifukwa chiyani anamulamula Yeremiya zimenezi? Chifukwa chakuti anthu m’dzikolo anali kuba, kupha, kuchita chigololo, kulumbira zonama, ndi kulambira mafano.—Yeremiya 7:9.
Yesu anapereka chitsanzo pamene ananena kuti: “Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine.” (Yohane 17:9) Malemba amanena kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo” ndipo “lipita.” (1 Yohane 2:17; 5:19) Nanga Akristu oona angapemphererenji dziko loterolo kuti zinthu ziziyenda bwino ndiponso kuti likhalitse?
N’zoona kuti si nyimbo za fuko zonse zimene zimakhala ndi mapemphero kwa Mulungu. Buku lakuti Encyclopædia Britannica limati: “Mfundo za m’nyimbo za fuko ndi zosiyanasiyana, zingakhale zopempherera mfumu, zosimba za nkhondo zofunika za dzikolo kapena kuukira . . . zingasonyeze kukondetsa kwambiri dziko lako.” Koma kodi anthu amene amafuna kusangalatsa Mulungu angatamande nkhondo kapena kusintha zinthu kwa dziko lililonse? Yesaya analosera za olambira oona kuti: “Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape.” (Yesaya 2:4) Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Pakuyendayenda m’thupi, sitichita nkhondo monga mwa thupi, pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi.’—2 Akorinto 10:3, 4.
Nthaŵi zambiri, nyimbo za fuko zimasonyeza malingaliro a kunyada kapena kuona ngati dziko lawo limaposa lina lililonse. Malemba savomereza maganizo oterowo. Mtumwi Paulo polankhula kwa Areopagi anati: “[Yehova Mulungu] ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.” (Machitidwe 17:26) Mtumwi Petro anati: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”—Machitidwe 10:34, 35.
Ambiri, chifukwa cha kumvetsa kwawo Baibulo, amasankha okha kukana kuchitira sawatcha mbendera kapena kuimba nawo nyimbo zosonyeza kukondetsa dziko lawo. Koma kodi amatani pakachitika zinthu zimene zingapangitse kukumana ndi zoterezi?
Kanani Mwaulemu
Mfumu Nebukadinezara ya Babulo wakale inaimika fano lalikulu la golidi m’chigwa cha Dura pofuna kulimbikitsa umodzi mu ufumu wake. Ndiyeno anakonza mwambo wopatulira fanolo kumene anaitanira akalonga, akazembe, ziwanga, oweruza, ndi akuluakulu ena a boma. Onse osonkhanawo anafunika kugwadira fanolo ndi kulilambira nyimbo ikayamba. Ena mwa amene anafunika kukapezekako anali Ahebri achinyamata atatu, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego. Kodi anasonyeza bwanji kuti sanali kuchita nawo mwambo wachipembedzowu? Nyimbo itayamba ndipo onse osonkhanawo atagwadira fanolo, Ahebri atatuwo anangoima chilili.—Danieli 3:1-12.
Masiku ano, nthaŵi zambiri anthu amachitira sawatcha mbendera mwa kuwongola mkono kapena kugwira pamphumi kapena pamtima. Nthaŵi zina, pamakhala kaimidwe kenakake kapadera. M’mayiko ena, ana kusukulu amafunika kugwada ndi kupsopsona mbenderayo. Akristu oona amasonyeza mwaulemu kuti sachita nawo mwa kungoima duu pamene ena akuchitira sawatcha mbenderayo.
Bwanji ngati mmene mwambo wa mbenderawo ukuchitikira zikusonyeza kuti ngakhale kungoima chabe ukuchita nawo mwambowo? Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mwana wina
pasukulu amusankha kuti aimire sukulu yonseyo ndiyeno akuchitira sawatcha mbendera panja pamlongoti umene aimangirirapo pamene ana a sukulu ena onse ayenera kuima njo m’kalasi. Kuima chabe kotereku kukusonyeza kuvomereza kuti wophunzira amene akukachitira sawatcha mbendera uja akukuimira munthuwe. Motero, kuimako kukusonyeza kuti munthu wachita nawo mwambowo. Zikakhala chonchi, amene akufuna kuti angosonyeza ulemu koma osachita nawo adzangokhala pansi phee. Bwanji ngati pamene mwambowo ukuyambika n’kuti anthu onse m’kalasilo ataimirira? Zikakhala chonchi, kuimirirabe sikusonyeza kuti tikuchita nawo mwambowo.Tiyerekeze kuti munthuwe sanakuuze kuti uchitire sawatcha mbendera koma kungoinyamula chabe, kaya pa perete kapena m’kalasi kapenanso pena paliponse, kuti ena aichitire sawatcha. M’malo ‘mothaŵa kulambira mafano’ monga mmene malemba amalamulira, kuchita zimenezi kudzatanthauza kukhala pachimake pa mwambowo. Zimenezi n’chimodzimodzinso ndi kuyenda nawo pa perete wosonyeza kukonda dziko lako. Popeza kuchita zimenezi kumasonyeza kuthandizira nawo zimene anthu ochita peretewo akulemekeza, Akristu oona amakana zimenezi mosamala.
Akamaimba nyimbo ya fuko, nthaŵi zambiri munthu amangofunika kuima kuti asonyeze kuti akugwirizana ndi malingaliro a m’nyimboyo. Zikatero, Akristu amangokhala pansi. Koma ngati pamene akuimba nyimboyo n’kuti ataima kale, palibe chifukwa chokhalira pansi. Sikuti anaima chifukwa cha nyimboyo. Komanso, ngati anthu akufunika kuima ndi kuimba nyimboyo, kungoima chabe posonyeza ulemu koma osaimba nawo sikungatanthauze kuti tagwirizana nawo malingaliro a m’nyimboyo.
‘Khalani ndi Chikumbumtima Chabwino’
Atafotokoza kupanda ntchito kwa mafano amene anthu amapanga n’kumalambira, wamasalmo Salmo 115:4-8) Motero, n’zosachita kufunsa kuti kulembedwa ntchito imene mwachindunji imaphatikizapo kupanga zinthu zimene anthu amalambira, monga mbendera za dziko, n’kosaloleka kwa olambira Yehova. (1 Yohane 5:21) Pangabukenso zochitika zina kuntchito ngati Mkristu mwaulemu amasonyeza kuti salambira mbendera kapena zimene imaimira koma Yehova yekha.
anati: “Adzafanana nawo iwo akuwapanga; ndi onse akuwakhulupirira.” (Mwachitsanzo, bwana angauze wantchito kuti akweze kapena kutsitsa mbendera imene ili panyumba ina. Kaya munthuyo achita zimenezo kapena ayi zingadalire mmene iye akuonera zinthu panthaŵi imeneyo. Ngati kukweza kapena kutsitsa mbenderayo ndi mbali ya mwambo wapadera, pamene anthu adzaima njo kapena kuchitira sawatcha mbendera, ndiye kuti kuchita zimenezi kudzasonyeza kuti munthuyo akuchita nawo mwambowo.
Koma ngati palibe mwambo uliwonse pokweza kapena kutsitsa mbenderayo, ndiye kuti kuchita zimenezi kungangofanana ndi kuchita ntchito zina monga kukonza nyumbayo kuti izigwiritsidwa ntchito, kutsegula ndi kutseka zitseko ndiponso kutsegula ndi kutseka mawindo. Zikakhala chonchi, mbenderayo imangokhala chizindikiro cha Boma basi, ndipo kuikweza kapena kuitsitsa monga imodzi mwa ntchito zimene munthu amachita nthaŵi zonse ndi nkhani imene munthu angasankhe malinga ndi chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo. (Agalatiya 6:5) Chikumbumtima cha wina chingamulimbikitse kuuza womuyang’anira wake kuti auze wantchito wina kuti azikweza kapena kutsitsa mbenderayo. Mkristu wina angaone kuti chikumbumtima chake chingamulole kukweza kapena kutsitsa mbenderayo ngati palibe mwambo uliwonse. Kaya tisankha kuchita chiyani, olambira oona ayenera “kukhala nacho chikumbumtima chabwino” kwa Mulungu.—1 Petro 3:16.
Malemba saletsa kugwira ntchito kapena kukhala pamalo a anthu onse, monga pa maofesi oyang’anira tauni ndi pasukulu pamene pali mbendera. Mbendera ingakhalenso pa sitampa, pa laisensi ya galimoto, kapena pa zinthu zina zimene boma limapanga. Kugwiritsa ntchito zinthu zimenezo sikusonyeza kuti tikuzilambira. Chofunika kwambiri apa si kukhalapo kwa mbenderayo kapena chizindikiro chake, koma mmene munthu amachitira nayo.
Nthaŵi zambiri anthu amaikanso mbendera pa mawindo, zitseko, magalimoto, madesiki ndi pa zinthu zina. Anthu amathanso kugula zovala zimene zili ndi chizindikiro cha mbendera. M’mayiko ena n’zoletsedwa kuvala zovala zoterozo. Ngakhale kuti kuchita zimenezo sikungakhale kuswa lamulo, kodi zingasonyeze chiyani pankhani ya mmene munthuyo amaonera dziko? Ponena za otsatira ake, Yesu Kristu anati: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Chimenenso sitiyenera kuiŵala ndi mmene kuchita zimenezo kungakhudzire okhulupirira anzathu. Kodi zivulaza chikumbumtima chawo? Kodi zifooketsa kutsimikiza mtima kwawo koti akhalebe olimba m’chikhulupiriro? Paulo analangiza Akristu kuti: “Mutsimikizire zinthu zofunika kwambiri, kuti mukhale opanda cholakwa ndi osakhumudwitsa ena.”—Afilipi 1:10, NW.
“Waulere pa Onse”
Pamene zochitika m’dzikoli zikuipiraipira ‘m’nthaŵi zoŵaŵitsa’ zino, n’zachidziŵikire kuti malingaliro a kukondetsa dziko lako angakulirekulire. (2 Timoteo 3:1) Amene amakonda Mulungu asaiŵale kuti chipulumutso n’cha Yehova yekha basi. Tiyenera kulambira iye yekha basi. Atumwi a Yesu atauzidwa kuti achite zinthu zina zotsutsana ndi chifuniro cha Yehova, anayankha kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 5:29.
Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse.” (2 Timoteo 2:24) Motero, Akristu amayesetsa kukhala amtendere, aulemu, ndiponso ofatsa pamene akudalira chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo posankha zochita pankhani yochitira sawatcha mbendera ndi kuimba nyimbo ya fuko.
[Chithunzi patsamba 23]
Ahebri atatu anasankha molimba mtima koma mwaulemu kusangalatsa Mulungu
[Chithunzi patsamba 24]
Kodi Mkristu angatani pa mwambo wosonyeza kukonda kwambiri dziko lake?