Achinyamata Ofanana ndi Mame Opatsa Mpumulo
“Idzani Kuno kwa Ine . . . Ndipo Ndidzakupumulitsani Inu”
Achinyamata Ofanana ndi Mame Opatsa Mpumulo
MOSAKAYIKIRA, Yesu Kristu pamene anati, “idzani kuno kwa Ine . . . ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu,” anali kuuzanso otsatira ake achinyamata. (Mateyu 11:28) Anthu atayamba kupita ndi ana awo kwa iye, ophunzira ake anawaletsa. Koma Yesu anati: “Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse.” Mpaka Yesu “anatiyangata, natidalitsa.” (Marko 10:14-16) Sitingachite kufunsa, Yesu ankaona ana kukhala ofunika kwambiri.
Baibulo limatiuza za anyamata ndi atsikana okhulupirika komanso ana aang’ono, amene anapereka zitsanzo zabwino kwambiri potumikira Mulungu. Buku la Masalmo linalosera za “khamu la anyamata” opatsa mpumulo ngati mame. Limanenanso za “anyamata” ndi “anamwali” akutamanda dzina la Yehova.—Salmo 110:3, NW; 148:12, 13.
Malo Amene Achinyamata Amakula Bwino
N’koyenera kuyerekezera achinyamata ndi mame, chifukwa mame amatchulidwa pofuna kutanthauza kusasoŵa kanthu komanso kupindula. (Genesis 27:28) Mame amakhala ofeŵa ndiponso osangalatsa. M’masiku a kukhalapo kwa Kristu ano, Akristu ambiri achinyamata akudzipereka mofunitsitsa ndiponso mwachangu. Monga mame opatsa mpumulo, anyamata ndi atsikana ambiri amatumikira Mulungu ndiponso amathandiza olambira anzawo mosangalala.—Salmo 71:17.
Akristu achinyamata amapatsa mpumulo ena; iwonso amapeza mpumulo muutumiki wawo. Gulu la Mulungu ndi malo amene iwo angakule bwino. Anyamata ndi atsikana amakhala paubwenzi wabwino ndi Mulungu ngati atsatira miyezo ya pamwamba ya makhalidwe abwino. (Salmo 119:9) Mu mpingo, amagwiranso ntchito zabwino ndipo amapeza mabwenzi abwino—zinthu zomwe zimathandiza munthu kukhala ndi moyo wosangalatsa ndiponso watanthauzo.
‘Zochiritsa ndi Zolimbikitsa’
Kodi Akristu achinyamata mumaona kuti muli ngati “mame”? Tamvani Tania, mtsikana amene amagwira ntchito mwachangu pampingo ndipo mwezi uliwonse amathera mosangalala maola oposa 70 mu utumiki. Kodi amamva bwanji? Iye akuti: “Ndimapeza mpumulo ndiponso ndimalimbikitsidwa. Kutsogozedwa ndi Yehova ndi gulu lake la padziko lapansi pamoyo wanga kwakhala ‘kochiritsa ndi kolimbikitsa’ kwa ine.”—Miyambo 3:8, NW.
Ariel, mtsikana wina amene ndi mtumiki wanthaŵi zonse, amayamikira chakudya chauzimu chimene amalandira ku mpingo. Iye akuti: “Ndikapita ku misonkhano Yakobo 2:23.
ya mpingo, yachigawo, yadera ndi yapadera ndimadya pa gome lauzimu la Yehova, zimenezi zimandipatsa mpumulo wauzimu. Ndipo kudziŵa kuti ndili ndi antchito anzanga padziko lonse lapansi kumandilimbikitsa.” Pofotokoza chimene chimam’patsa kwambiri mpumulo anati: “Kukhala paubwenzi ndi Yehova kumandipatsa mpumulo waukulu, makamaka ndikamva kapena kuona momwe dongosolo lino likuvulazira anthu.”—Abishai yemwe ali ndi zaka 20 akutumikira monga mtumiki wanthaŵi zonse ndiponso monga mtumiki wotumikira pa mpingo. Pofotokoza zimene waona akuti: “Ndimasangalala chifukwa ndimadziŵa momwe ndingathetsere mavuto ambiri amene achinyamata amakumana nawo masiku ano. Choonadi cha m’Baibulo chandithandiza kuonetsetsa zimene ndikufunika kuchita kuti nditumikire Yehova ndi mtima wonse.”
Kumayambiriro kwa unyamata wake, Antoine anali munthu wamtima wapachala. Nthaŵi ina anamenya mwana wasukulu mnzake ndi mpando, ndiponso anabaya wina ndi pensulo. Antoine sanali munthu wopatsa mpumulo. Koma malangizo a m’Baibulo anasintha khalidwe lake. Tsopano ali ndi zaka 19 ndipo ndi mtumiki wotumikira ndiponso mtumiki wanthaŵi zonse mu mpingo, ndipo akuti: “Ndikuthokoza Yehova pondilola kuti ndimudziŵe ndiponso pondithandiza kuzindikira kufunika kokhala wodziletsa ndi kusintha khalidwe langa. Chifukwa cha zimenezi, ndapeŵa mavuto ambiri.”
Anthu ena amaona khalidwe lopatsa mpumulo la Akristu achinyamata. Matteo ndi Mboni yachinyamata ku Italy. Aphunzitsi ake anaika lamulo lakuti aliyense m’kalasimo wopezeka akutukwana azipereka ndalama. Nthaŵi ina, anawo anapempha aphunzitsiwo kuti lamulo limenelo lithe chifukwa “n’kosatheka kukhala wosatukwana.” Matteo akuti: “Koma aphunzitsi anati zimene anawo ankanena zinali zabodza, ndipo anapereka chitsanzo cha ine, wa Mboni za Yehova, anandiyamikira pamaso pa kalasi yonse chifukwa chakuti sindinkatukwana.”
Ku Thailand m’kalasi ina ya ana a mphulupulu, aphunzitsi anauza Racha yemwe ndi wazaka 11 kuti aimirire kutsogolo kwa kalasiyo ndipo anamuyamikira chifukwa cha khalidwe lake labwino, ndiyeno anati: “N’chifukwa chiyani enanu simutengera khalidwe la uyu? Amalimbikira sukulu ndipo ndi wakhalidwe labwino.” Ndiyeno anauza anawo kuti: “Ndikukhulupirira kuti mungafunikire kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova, monga Racha, kuti mukhale ana akhalidwe.”
N’zosangalatsa kuona Akristu ambiri achinyamata akum’dziŵa bwino Yehova ndi kuchita zimene amafuna. Ana abwino ameneŵa amasonyeza nzeru zoposa msinkhu wawo. Mulungu angawathandize kuti ziwayendere bwino pamoyo wawo uno komanso kuwapatsa tsogolo labwino kwambiri m’dziko latsopano likudzalo. (1 Timoteo 4:8) Achinyamata achikristu amapatsa mpumulo, mosiyana ndi dongosolo la zinthu losakonda zinthu zauzimu lino limene ladzaza ndi achinyamata osakhutira ndi osasangalala!