Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Nditsatireni Ine Nthaŵi Zonse’

‘Nditsatireni Ine Nthaŵi Zonse’

‘Nditsatireni Ine Nthaŵi Zonse’

“Kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Kristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.”​—1 PETRO 2:21.

1, 2. N’chifukwa chiyani chitsanzo changwiro cha Yesu si chapamwamba kwambiri moti sitingathe kuchitsanzira?

YESU KRISTU anali Mphunzitsi wamkulu woposa wina aliyense amene anakhalako. Ndiponso, iye anali wangwiro, sanachimwe m’moyo wake wonse pamene anali munthu. (1 Petro 2:22) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti chitsanzo cha Yesu monga mphunzitsi n’chapamwamba kwambiri moti ife anthu opanda ungwiro sitingathe kuchitsanzira? Ayi.

2 Monga tinaonera m’nkhani yapitayo, chinthu chofunika kwambiri pa kuphunzitsa kwa Yesu chinali chikondi. Ndipo chikondi ndi chinthu choti tonsefe tikhoza kukhala nacho. Mawu a Mulungu nthaŵi zambiri amatilimbikitsa kukulitsa ndiponso kuwonjezera kukonda kwathu anthu ena. (Afilipi 1:9; Akolose 3:14) Yehova safuna kuti zolengedwa zake zichite zinthu zomwe izo sizingathe. Ndipo, popeza “Mulungu ndiye chikondi” ndipo anatipanga m’chifaniziro chake, tinganene kuti anatikonza kuti tizisonyeza chikondi. (1 Yohane 4:8; Genesis 1:27) Motero, tikamaŵerenga mawu a mtumwi Petro amene ali m’lemba limene latsogolera nkhani ino, tingavomere mtima uli m’malo kuti tingakwanitse kutero. Tingathe kutsatira mapazi a Kristu. Ndipo, tingamvere mawu a Yesu mwiniyo akuti: ‘Nditsatireni ine [“nthaŵi zonse,” NW].’ (Luka 9:23) Tiyeni tikambirane mmene tingatsanzirire chikondi chimene Kristu anasonyeza, choyamba pa choonadi chimene anaphunzitsa, ndipo kenako kwa anthu amene anawaphunzitsa.

Kukonda Choonadi Chimene Timaphunzira

3. N’chifukwa chiyani ambiri amavutika kuphunzira, koma kodi ndi langizo lotani limene lili pa Miyambo 2:1-5?

3 Kuti tikonde choonadi chimene timaphunzitsa ena, tiyenera kukonda kuphunzira choonadicho ifeyo. Masiku ano, kukonda kuphunzira si chinthu chapafupi. Zinthu monga kusaphunzira mokwanira ndi zizoloŵezi zoipa zimene ena amakhala nazo paunyamata zimachititsa ambiri kusakonda kuphunzira. Komabe, n’kofunika kwambiri kuti tiziphunzira kwa Yehova. Miyambo 2:1-5 amati: “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziŵadi Mulungu.”

4. Kodi “kulozetsa” mtima kumatanthauza chiyani, ndipo ndi kuona zinthu kotani kumene kungatithandize kuchita zimenezo?

4 Onani kuti m’vesi 1 mpaka 4, akutilimbikitsa mobwerezabwereza kuti tichite khama osati kuti ‘tingolandira’ ndi “kusunga” basi koma kutinso ‘tifunefune’ ndi ‘kupwaira.’ Kodi n’chiyani chingatilimbikitse kuti tichite zonsezi? Chabwino, onani mawuwo akuti “kulozetsa mtima wako kukuzindikira.” Buku lina linati langizo limeneli “si pempho lakuti munthu amvetsere chabe ayi; likufuna kuti munthu akhale ndi maganizo ena ake: kufuna ndi mtima wonse kulandira zimene akuphunzirazo.” Ndiyeno kodi n’chiyani chingatichititse kulandira ndi kufunitsitsa kuphunzira zimene Yehova amatiphunzitsa? Chimene chingatichititse zimenezi ndi mmene timaonera zinthu. Tiyenera kuona “kum’dziŵadi Mulungu” kukhala ngati “siliva” ndiponso ngati “chuma chobisika.”

5, 6. (a) N’chiyani chingachitike m’kupita kwa nthaŵi, ndipo tingatani kuti tipeŵe zimenezo? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kuwonjezera chuma cha zimene tadziŵa kuchokera m’Baibulo?

5 Kuona zinthu koteroko n’kosavuta. Mwachitsanzo, “kum’dziŵadi Mulungu” kumene mwachita kale mosakayikira kukuphatikizapo kudziŵa choonadi chakuti Yehova ali n’cholinga choti anthu okhulupirika adzakhale ndi moyo kosatha m’Paradaiso pa dziko lapansi. (Salmo 37:28, 29) Mutaphunzira koyamba choonadi chimenecho, mosakayikira munachiona kukhala chuma chenicheni, mfundo imene inachititsa maganizo ndi mtima wanu kudzaza ndi chiyembekezo ndi chimwemwe. Bwanji pakalipano? Popeza tsopano papita nthaŵi, kodi kuyamikira chuma chanu kwazirala? Ngati ndi choncho, yesani kuchita zinthu ziŵiri. Choyamba, yambiraninso kuyamikira, ndiko kuti, ganizani nthaŵi zonse chifukwa chake mukuona kuti choonadi chimene Yehova wakuphunzitsani n’cha mtengo wapatali, ngakhale chimene munaphunzira zaka zambiri zapitazo.

6 Chachiŵiri, pitirizani kuwonjezera chuma chanu. Ndipo, ngati mwamwayi mwakumba n’kupeza mwala wamtengo wapatali, kodi mungangouika m’thumba nthaŵi yomweyo n’kumapita mutakhutira? Kapena kodi mudzakumbabe kuti muone ngati pali miyala ina? Mawu a Mulungu n’ngodzala ndi choonadi cha mtengo wapatali chomwe chikufanana ndi siliva ndi chuma chobisika. Zilibe kanthu kuti kaya mwapeza choonadi cha mtengo wapatali chotani, mungapezenso china. (Aroma 11:33) Mukaphunzira mfundo ya choonadi yatsopano, dzifunseni kuti: ‘N’chiyani chikuchititsa mfundo imeneyi kukhala ya mtengo wapatali? Kodi ikundithandiza kuzindikira mwakuya makhalidwe a Yehova kapena zolinga zake? Kodi ikundipatsa malangizo abwino amene angandithandize kutsatira mapazi a Yesu?’ Kusinkhasinkha mafunso amenewo kudzakuthandizani kukulitsa kukonda kwanu mfundo za choonadi zimene Yehova wakuphunzitsani.

Kukonda Choonadi Chimene Timaphunzitsa

7, 8. Kodi ndi njira zina ziti zimene tingasonyezere ena kuti timakonda choonadi chimene taphunzira m’Baibulo? Perekani chitsanzo.

7 Pamene tikuphunzitsa ena, kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda choonadi chimene taphunzira m’Mawu a Mulungu? Potsatira chitsanzo cha Yesu, timadalira kwambiri Baibulo polalikira ndi kuphunzitsa. Posachedwapa, anthu a Mulungu padziko lonse alimbikitsidwa kugwiritsa ntchito kwambiri Baibulo polalikira kwa anthu onse. Pamene mukugwiritsa ntchito langizo limeneli, yesani kupeza njira zimene zingathandize mwininyumbayo kudziŵa kuti inuyo mumalemekeza uthenga wa m’Baibulo umene mukumuuzawo.​—Mateyu 13:52.

8 Mwachitsanzo, zigaŵenga zitangoukira kumene ku mzinda wa New York chaka chatha, mlongo wina wachikristu anali kuŵerengera anthu amene anakumana nawo mu utumiki wake lemba la Salmo 46:1, 11. Ankayamba kuwafunsa anthuwo mmene akupiririra zotsatira za tsoka limene linangochitika kumenelo. Mlongoyo anali kumvetsera mwatcheru pamene anthuwo anali kuyankha ndipo anali kuwayamikira, ndiyeno n’kunena kuti: “Kodi ndingaŵerenge nanu lemba limene ine landitonthoza kwambiri m’nthaŵi yovutayi?” Ndi ochepa okha amene anakana, ndipo anakambirana bwino ndi anthu ambiri. Polankhula ndi achinyamata, mlongoyu nthaŵi zambiri amati: “Ndakhala ndikuphunzitsa Baibulo kwa zaka 50 tsopano, ndipo kodi mukudziŵa? Sindinakumanepo ndi vuto lililonse limene bukuli silingathetse.” Mwa kulankhula moona mtima komanso ndi mtima wonse, timasonyeza anthu kuti timalemekeza ndi kukonda zimene taphunzira m’Mawu a Mulungu.​—Salmo 119:97, 105.

9, 10. N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kugwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunso okhudza zikhulupiriro zathu?

9 Anthu akatifunsa mafunso okhudza zikhulupiriro zathu, timakhala ndi mwayi wabwino wosonyeza kuti timakonda Mawu a Mulungu. Potsatira chitsanzo cha Yesu, sitimangoyankha za m’mutu mwathu ayi. (Miyambo 3:5, 6) M’malo mwake, timagwiritsa ntchito Baibulo poyankha. Kodi mumaopa kuti wina adzakufunsani funso limene simudzatha kuliyankha? Taonani njira ziŵiri zothandiza zimene mungatsatire.

10 Chitani zomwe mungathe kuti mukhale wokonzeka. Mtumwi Petro analemba kuti: “Mumpatulikitse Ambuye Kristu m’mitima yanu; okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Kodi ndinu wokonzeka kupereka umboni wa zimene mumakhulupirira? Mwachitsanzo, ngati munthu wina akufuna kudziŵa chifukwa chake simuchita nawo miyambo kapena zochitika zina zosagwirizana ndi malemba, musangonena kuti, “Chipembedzo changa chimaletsa zimenezo.” Kuyankha motero kungasonyeze kuti anthu ena ndi amene amakusankhirani zochita ndipo muyenera kuti muli m’kagulu kenakake ka chipembedzo. Zingakhale bwino kunena kuti, “Mawu a Mulungu, Baibulo, amaletsa zimenezo” kapena kuti, “Sizingasangalatse Mulungu wanga.” Ndiyeno fotokozani mogwira mtima chifukwa chake.​—Aroma 12:1.

11. Kodi ndi chida chiti chothandiza pofufuza chimene chingatithandize kukhala okonzeka kuyankha mafunso okhudza choonadi cha m’Mawu a Mulungu?

11 Ngati mukuona kuti simunakonzeke, bwanji osapatula nthaŵi n’kuphunzira buku la Kukambitsirana za m’Malemba? * Sankhani nkhani zazikulu zingapo zimene zikuoneka kuti anthu angathe kufunsa, ndiyeno loŵezani pamtima mfundo zina za m’Malemba. Khalani ndi buku la Kukambitsirana ndi Baibulo nthaŵi zonse. Musazengereze kugwiritsa ntchito zonsezi, kumuuza wofunsayo kuti muli ndi chida chimene chimathandiza pofufuza ndipo kuti mukufuna kuchigwiritsa ntchito kuti mupeze mayankho a m’Baibulo pa mafunsowo.

12. Kodi tingayankhe bwanji ngati sitikudziŵa yankho la funso lina lake lokhudza Baibulo?

12 Musade nkhaŵa kwambiri. Palibe munthu wopanda ungwiro amene angathe kuyankha funso lililonse. Motero, ngati munthu wakufunsani funso lokhudza Baibulo limene simungathe kuyankha, munganene kuti: “Zikomo kwambiri chifukwa cha funso lanu losangalatsa. Koma ndisakunamizeni, sindikudziŵa yankho lake, komabe ndikukhulupirira kuti Baibulo limayankha funso limenelo. Ndimakonda kufufuza Baibulo, motero ndikafufuza funso lanu ndiyeno ndidzabweranso kudzakuyankhani.” Kuyankha moona mtima ndiponso modzichepetsa koteroko, kungathandize kuti mudzakambiranenso ulendo wina.​—Miyambo 11:2.

Kukonda Anthu Amene Timawaphunzitsa

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi maganizo abwino kwa anthu amene timawalalikira?

13 Yesu anakonda anthu amene anawaphunzitsa. Kodi tingamutsanzire bwanji pankhani imeneyi? Tisakhale ndi mtima wosaganizira anthu amene tili nawo pafupi. N’zoona kuti “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse” ikuyandikira kwambiri, ndipo anthu miyandamiyanda adzawonongeka. (Chivumbulutso 16:14; Yeremiya 25:33) Komabe, sitikudziŵa kuti ndani amene adzapulumuke ndipo ndani adzafe. Chiweruzo chimenecho chidzachitika m’tsogolo ndipo Yesu Kristu, amene Yehova wamuika, ndi amene adzaweruze. Tiziona munthu aliyense kuti akhoza kukhala mtumiki wa Yehova mpaka pamene chiweruzochi chidzaperekedwa.​—Mateyu 19:24-26; 25:31-33; Machitidwe 17:31.

14. (a) Kodi tingadzipende bwanji kuti tione ngati timamvera chisoni anthu? (b) Kodi ndi njira zothandiza ziti zimene tingasonyezere kuti timamvera chisoni ndi kuganizira ena?

14 Ndiyeno, monga anachitira Yesu, tiyenera kumvera chisoni anthu. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimamvera chisoni anthu amene anyengedwa ndi mabodza a zipembedzo za dzikoli, ndale, ndiponso a zamalonda? Ngati sakulabadira uthenga umene tikuwauza, kodi ndimayesetsa kumvetsa chifukwa chake akutero? Kodi ndimazindikira kuti ine, kapena ena amene akutumikira Yehova mokhulupirika pakalipano analinso osalabadira kale? Kodi ndasintha kalalikidwe kanga kuti kagwirizane ndi mmene anthuwo akuchitira? Kapena kodi ndimangowanyalanyaza anthu ameneŵa poganiza kuti sadzasintha?’ (Chivumbulutso 12:9) Anthu akamaona kuti timawamveradi chisoni, n’kosavuta kuti alabadire uthenga wathu. (1 Petro 3:8) Kumva chisoni kungatichititsenso kuganizira kwambiri anthu amene timakumana nawo mu utumiki. Tingasunge mafunso ndi nkhaŵa zawo. Pobwererako, tingawasonyeze kuti takhala tikuganizira zimene ananena pamene tinabwera ulendo watha. Ndipo ngati ali ndi zina zimene zikufunika thandizo mwamsanga, tingawathandize.

15. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyang’ana mbali zabwino za anthu, ndipo tingachite bwanji zimenezo?

15 Monga Yesu, timayang’ana mbali zabwino za anthu. Mwina mkazi yemwe alibe mwamuna akuchita khama loyamikirika polera ana ake. Mwina mwamuna wina akuyesetsa zolimba kusamalira banja lake. Munthu wokalamba akuchita chidwi ndi zinthu zauzimu. Kodi timaona zimenezi mwa anthu amene timakumana nawo ndiyeno n’kuwayamikira? Kuchita zimenezi kumathandiza kuti tigwirizane nawo ndipo zingatsegule mpata wolalikira za Ufumu.​—Machitidwe 26:2, 3.

Kudzichepetsa N’kofunika Posonyeza Chikondi

16. N’chifukwa chiyani n’kofunika kukhala ofatsa ndiponso aulemu kwa anthu amene timawalalikira?

16 Kukonda anthu amene timawaphunzitsa kudzatichititsa kumvera chenjezo lanzeru la m’Baibulo lakuti: “Chidziŵitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.” (1 Akorinto 8:1) Yesu anali kudziŵa zambiri, koma sanadzitukumule. Choncho, pouza ena zikhulupiriro zanu, peŵani kulankhula mosonyeza ngati mukufuna kukangana nawo, ndipo musasonyeze kuti ndinu wodziŵa kwambiri kuposa iwo. Cholinga chathu ndicho kuwafika anthu pamtima ndi kuwakopera ku choonadi chimene timachikonda kwambiri. (Akolose 4:6) Kumbukirani kuti Petro polangiza Akristu kuti akhale okonzeka kupanga chodzikanira, anakumbutsanso kuti tizichita zimenezo “ndi chifatso ndi mantha [“ulemu waukulu,” NW].” (1 Petro 3:15) Ngati tili ofatsa ndi aulemu, tingakopere anthu kwa Mulungu amene timam’tumikira.

17, 18. (a) Kodi tingatani ena akamatinena kuti tilibe ziyeneretso zokhala atumiki? (b) N’chifukwa chiyani kudziŵa zinenero zakale za Baibulo n’kosafunikira kwenikweni kwa ophunzira Baibulo?

17 Palibe chifukwa chowagometsera anthu ndi zimene tikudziŵa kapena maphunziro athu. Ngati ena m’gawo lanu amakana kumvetsera munthu amene alibe digiri inayake ya ku yunivesite kapena mayina aulemu a ku yunivesite, musalole kuti maganizo awo akufooketseni. Yesu sanasamale zimene otsutsa anali kunena zoti iye sanaphunzire m’sukulu zapamwamba za arabi za m’nthaŵi yake. Ndiponso iye sanagonjere malingaliro olakwika otchuka mwa kugometsa anthu ndi nzeru zake zapamwamba.​—Yohane 7:15.

18 Kudzichepetsa ndi chikondi n’zofunika kwambiri kwa atumiki achikristu kuposa maphunziro ena alionse a kusukulu. Yehova, Mphunzitsi Wamkulu, ndiye amene amatiyeneretsa kuti titumikire. (2 Akorinto 3:5, 6) Ndipo ngakhale atsogoleri ena a Matchalitchi Achikristu anene zotani, sitifunikira kuphunzira zinenero zoyambirira za Baibulo kuti tikhale aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Yehova anauzira Baibulo kuti lilembedwe momveka, mwachindunji moti pafupifupi aliyense angamvetse choonadi chake cha mtengo wapatali. Mfundo za choonadi zimenezo sizisintha ngakhale atalimasulira m’zinenero zambirimbiri. Motero, kudziŵa zinenero zakale, ngakhale kuti nthaŵi zina n’kothandiza, sikofunika.Ndiponso, kunyada chifukwa chokhala ndi luso lodziŵa zinenero kungachititse munthu kusakhala ndi khalidwe lomwe ndi lofunika kwambiri kwa Akristu oona​—khalidwe la kuphunzitsika.​—1 Timoteo 6:4.

19. N’chifukwa chiyani tingati utumiki wathu wachikristu ndi ntchito yofunika kwambiri?

19 N’zosakayikitsa kuti utumiki wathu wachikristu ndi ntchito yofuna kudzichepetsa. Nthaŵi zambiri timakumana ndi anthu otsutsa, osalabadira, ngakhalenso ena amene amatizunza. (Yohane 15:20) Komabe, mwakuchita utumiki wathu mokhulupirika, timachita ntchito yofunika kwambiri. Ngati tipitiriza kutumikira ena modzichepetsa m’ntchito imeneyi, timatsanzira chikondi chimene Yesu Kristu anasonyeza kwa anthu. Taganizani: Ngati titati tilalikire kwa anthu chikwi chimodzi osalabadira kapena otsutsa kuti tipeze munthu mmodzi wonga nkhosa, kodi sipomveka kuchita khama? Mpomveka! Choncho, mwa kulimbikira kuchita ntchitoyi, osagwa ulesi, tikutumikira mokhulupirika anthu onga nkhosa amene tikufunikirabe kuwaphunzitsa. Mosakayikira, Yehova ndi Yesu adzaonetsetsa kuti anthu ena ambiri ofunika ngati amenewo adzapezeke ndi kuthandizidwa mapeto asanafike.​—Hagai 2:7.

20. Kodi ndi njira zina ziti zimene tingaphunzitsire mwa kuchita zimene tikuphunzitsanzo?

20 Kuphunzitsa mwa kuchita zimene tikuphunzitsazo ndi njira ina yosonyezera kufuna kwathu ndi mtima wonse kutumikira ena. Mwachitsanzo, tikufuna kuphunzitsa anthu kuti kutumikira Yehova, “Mulungu wachimwemwe,” ndiko chinthu chabwino kwambiri pa moyo wa munthu kuposa china chilichonse. (1 Timoteo 1:11, NW) Akamaona khalidwe lathu ndi mmene timachitira zinthu ndi anansi athu, ophunzira anzathu kusukulu, ndi amene timagwira nawo ntchito, kodi angaone kuti ndife achimwemwe ndiponso osangalala? Mofananamo, timaphunzitsa ophunzira Baibulo kuti mpingo wachikristu ndiwo malo a chikondi m’dziko losaganizirana ndiponso loopsa lino. Kodi ophunzira athuwo angaone mosavuta kuti timakonda anthu onse mumpingomo ndi kuyesetsa kukhala pa mtendere wina ndi nzake?​—1 Petro 4:8.

21, 22. (a) Kodi kudzipenda pankhani ya utumiki wathu kungatichititse kugwiritsira ntchito mwayi wotani? (b) Kodi nkhani za mu Nsanja ya Olonda yotsatira zidzafotokoza chiyani?

21 Kukonda utumiki wathu nthaŵi zina kungatichititse kudzipendanso tokha. Kuchita zimenezo moona mtima kwachititsa ena kuona kuti ali ndi mwayi wotha kuwonjezera utumiki wawo mwa kuchita utumiki wa nthaŵi zonse kapena kupita kukatumikira ku madera kumene kukufunika atumiki ambiri. Ena aganiza zophunzira chinenero chachilendo kuti atumikire alendo obwera m’dzikolo amene ali m’gawo lawo. Ngati mipata imeneyi muli nayo, iganizireni mosamalitsa ndiponso mwapemphero. Kutumikira kumabweretsa chimwemwe, chisangalalo ndiponso mtendere wa maganizo.​—Mlaliki 5:12.

22 Mulimonse mmene zingakhalire, tiyeni tipitirize kutsanzira Yesu Kristu mwa kukulitsa kukonda kwathu choonadi chimene timaphunzitsa ndi kukonda anthu amene timawaphunzitsawo. Kukulitsa ndi kusonyeza chikondi m’mbali ziŵiri zimenezi kudzatithandiza kuika maziko oti tikhale aphunzitsi ofanana ndi Kristu. Komabe, kodi tingamange bwanji pa maziko amenewo? Mu Nsanja ya Olonda yotsatira, nkhani zotsatizana zidzafotokoza njira zina zachindunji zophunzitsira zimene Yesu anagwiritsa ntchito.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tikutsimikiza bwanji kuti chitsanzo cha Yesu monga mphunzitsi si chapamwamba moti sitingathe kuchitsanzira?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda choonadi chimene taphunzira m’Baibulo?

• N’chifukwa chiyani n’kofunika kukhalabe wodzichepetsa pamene tikupitiriza kudziŵa zambiri?

• Kodi ndi njira zina ziti zimene tingasonyezere kuti timakonda anthu amene tikuyesetsa kuwaphunzitsa?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 16]

Chitani zomwe mungathe kuti mukhale wokonzeka

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Ngati mumaona kuti “kum’dziŵadi Mulungu” n’kwa mtengo wapatali mungagwiritse ntchito Baibulo mogwira mtima

[Chithunzi patsamba 18]

Timasonyeza kukonda anthu mwa kuwauza uthenga wabwino